chchichewa survivors-se 20200608
TRANSCRIPT
OpulumukaKusindikiza kwa PaderaCHICHEWA: SURVIVORS-SE
1
Malonje kwa Wopulumuka!
Buku lino ndi lanu. Lili ndi fundo zambiri ndiponso
zinthu zoti muchite zambiri. Likuthandizani kuchira ndi kukula.
Mliri wa COVID-19 wakhudza munthu aliyense m’njira zosiyanasiyana.
Choncho buku lanuli ndi losiyana ndi mabuku a anthu ena onse.
Limeneli ndi lanulanu!
Dzina langa ndi
Ine ndine Wopulumuka
2 3
Kukhala ModzitetezaMwina mukumadandaula kapena
kuchita mantha.Sikuti mukulakwitsa kutero ayi.
Munthu wopulumuka pa ngozi nthawi zina amachitanso mantha.M’dziko lonse lapansi muli zinthu
zambiri zodabwitsa. Komanso muli zina zochititsa mantha kwambiri. Monga
kusefukira kwa madzi, nkhondo, ngozi za galimoto ndipo tsopano kwabwera mliri pa dziko lonse (matenda amene akufalikira ponseponse mofulumira kwambiri amene asanduka mliri).
Lembani zinthu zingapo zomwe zikukudandaulitsani za mliri wa COVID-19:
4 5
Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda!Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.
Ndikanathawira kutalindi kukakhala m’chipululu.
Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo;kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”
Pali munthu wina amene ankachita mantha kwambiri pamene
ankalemba zomwe ankazifuna.
Salimo 55:6–8
6 7
Kodi inu munakhalapo ndi maganizo monga amenewa?
Kodi pamene mukuchita mantha mumafuna chitakuchitikirani chiyani?
Pamene ndili ndi mantha, ndimalakalaka…
Lembani kapena jambulani chomwe mukufuna apa.
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu
wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife m’mavuto athu onse,
kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse
ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu.
2 Akorinto 1:3–4
Have you ever made a wish like this? What do you wish when you are afraid?
Give praise to the God and Father of our Lord Jesus Christ!
He is the Father who gives tender love. All comfort comes from him.
He comforts us in all our troubles. Now we can comfort
others when they are in trouble.We ourselves receive comfort from God.
2 Corinthians 1:3–5Write or draw your wish here.
8 9
Malangizo kwa Opulumuka
Pempherani: Nthawi zonse pamene mukuchita mantha muziyankhula ndi Mulungu. Iye adzakhala malo anu achitetezo.
Chitanipo Kanthu!
Pekani nyimbo.Nyimbo ndi zabwino kwambiri
pakuti zimathandiza anthu kuchotsa mantha.
Nayi nyimbo yochokera m’Baibulo
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
Salimo 27:1
Sambani m’manja ndi sopo pafupipafupi.
Imani motalikirana ndi anthu ena.
Onetsetsani kuti simukukhudza maso anu, mphuno yanu ndi pakamwa panu.
Ngati thupi lanu likupweteka, ngati mukutsokomola kapena mukubanika popuma, wuzani makolo anu kapena amene akukuyang’anirani kuti awuze dotolo.
Muzichita masewero m’nyumba ndi a pa banja panu m’malo mokaswera ndi anzanu kunja.
Dzitetezeni ku kachirombo ka corona:
10 11
Kupempha Thandizo
N’kutheka kuti mwathedwa nzeru.Sikuti mukulakwitsa kutero.
Opulumuka amafunanso thandizo nthawi zina.
Zimakhala zopweteka kwambiri pamene munthu ukulephera kutuluka m’nyumba kapena kusowa wosewera naye. Mumakhala wosangalala kapena
wokwiya. Zimavuta kuti mufotokoze bwino momwe mukumvera mu mtima mwanu.
Zimakhala zovuta kulandira thandizo kuchokera kwa anthu ena.
Anthu ambiri akufuna kukuthandizani. Koma sangathe kutero chifukwa sakudziwa
zomwe mukuzisowa, choncho…AWUZENI!
12 13
“Chifukwa chake pempherani motere:“ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe,
Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike
pansi pano monga kumwamba.Mutipatse chakudya chathu chalero.
Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira
amangawa athu.Ndipo musatitengere kokatiyesa;
koma mutipulumutse kwa woyipayo.”
Mateyu 6:9–13
Iye anati,
Pemphani kwa Mulungu chomwe mukufuna!
Yesu anatiphunzitsa momwe tingapemphere thandizo kwa Mulungu.
14 15
Tili ndi mwayi wopempha thandizo nthawi zonse kwa Mulungu.
Tengani pemphero lomwe lili pa peji yotsatirayi kukhala pemphero lanu
ndipo onjezerani mawu anu.
Yehova ndiye mphamvu zanga ndi chishango changa;mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa.
Mtima wanga umalumphalumpha
chifukwa cha chimwemwendipo ndidzayamika
Iye m’nyimbo.
Salimo 28:7
Mulungu Atate wokondedwa,ndikuthokoza chifukwa
mumandikonda ine kwambiri.Lero ndikumva mu mtima mwanga
chifukwa cha
ndipo ndikufuna thandizo lanu. Chonde
Zikomo chifukwa
16 17
Malangizo kwa Opulumuka
Fotokozerani anthu zomwe mukusowa pa moyo wanu.Afotokozereni anthu momwe angakuthandizireni.
Pemphero lodzipempherera nokha.Pemphani Mulungu kuti akusungeni ndi kuteteza banja lanu.Thokozani Mulungu chifukwa chokusamalirani.
Khalani wothandiza wina. Yang’anani munthu amene akusowa thandizo.
Mutha kuthandiza amene ali pafupi ndi nyumba yanu,
posamalira m’nyumba mwawo, kapena kutsuka mbale zawo.
Munthu umamva bwino ukamathandiza ena!Kumbukirani kupempha thandizo pamene mukufuna kuthandizidwa.
Chitanipo Kanthu!
18 19
Salimo 10:14
Kufuna Chitonthozo
Mwina muli ndi chisoni.Sikuti mukulakwitsa kutero.Opulumuka amamvanso chisoni nthawi zina.
Mwina mukumusowa mnzanu amene anamwalira.
Mwina mukuganiza kwambiri za mmene zinthu zinalili kale. Mwina simukutha kumvetsa
zomwe zikukuchitikirani.
Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa,
mumaganizira zochitapo kanthu.
20 21
Odala ndi amene ali achisoni,chifukwa adzatonthozedwa.Odala ndi amene ali ofatsa,
chifukwa adzalandira dziko lapansi.Odala ndi amene akumva njala
ndi ludzu la chilungamo,chifukwa adzakhutitsidwa.
Odala ndi amene ali ndi chifundo,chifukwa adzawachitira chifundo.Odala ndi amene ali oyera mtima,
chifukwa adzaona Mulungu.Ndi odala amene amabweretsa mtendere,
chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.Odala ndi amene akuzunzidwa
chifukwa cha chilungamo,pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”
Mateyu 5:4–10
Ambuye Yesu anati,
22 23
Kodi ndi ziti zomwe mumakonda kuchita?
Kodi mumakonda kuthamanga mwaliwiro? Kodi mumakonda kusaka tizirombo tooneka modabwitsa?
Kodi mumakonda kujambula?
Lembani mndandanda wa Zinthu Zofunika Kuchita. Lembani zomwe mumakonda kuchita.
Zinthu Zofunika Kuchita
24 25
Malangizo kwa Opulumuka
Uzani munthu amene mumamukonda zomwe inu mukumva mu mtima mwanu. Zimathandiza kufotokozera wina maganizo anu ndi zomwe mukumva mu mtima mwanu.
Muuzeni Mulungu za chisoni chanu. Mupempheni kuti akutonthozeni. Yembekezerani dalitso.
Chitanipo kanthu pa Zinthu Zofunika Kuchita zija.
Chitanipo Kanthu!
Pangani Bokosi la Zochitika.
Pezani bokosi.
Kongoletsani bokosilo ndi penti kapena chekenirani ndi chilichonse chokongoletsa.
M’bokosimo muyikemo zinthu zosangalatsa. Zinthu za fungo labwino lomwe mumalikonda, zinthu zokoma, zomveka bwino.
Pamene muli ndi chisoni, tengani Bokosi la Zochitika ndipo muyambe kuseweretsa zinthu zomwe zimakusangalatsanizo.
26 27
Zisiyeni Zipite
Mwina mwakwiya.Sikuti mukulakwitsa kutero.Nthawi zina Opulumuka amakwiyanso.
Mwina mukuona kuti zinthu sizikuyenera kutero.Mwina mwakwiya chifukwa simukuloledwa kutuluka m’nyumba. Mwina mukanakonda zinthu zikanachitika mwa mtundu wina.
Jambulani nkhope ya munthu wokwiya apa, ngati inu mwakwiya.
GRRRRR!
28 29
N’zosalakwika kukwiya,koma ndi zabwino kwambiri kuchotsa mkwiyo.
Nthawi zonse tikuyenera kukhululukira munthu wina pa zomwe watichitira zimene
zikutipweteka mu mtima. Choncho tikuyenera kuchotsa mkwiyo wathu.
ndi kuchotsa mkwiyo.Ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri,
muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira.
Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake.
Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.
Akolose 3:12–13
Kukhala moyo umene Mulungu amafuna
zikutanthauza kukhala ndi mphamvu zokhululukira anthu.
30 31
Nthawi zina pamafunika kufuula kwambiri kuti muchotse mkwiyo wanu.
Pangani Chinthu Chofuulira.
2. Gunditsani pakamwa panu mbali imodziyi.3. Dzanja lanu ligwire mbali ina ya chinthuchi. 4. Mukokere mpweya m’kati.5. Fuulani kwambiri monga momwe mungathere.
1. Pindani bukuli motere.
32 33
Malangizo kwa OpulumukaKhululukirani anthu. Pemphani Mulungu kuti akupatseni mphamvu zokhululukira anthu amene anakulakwirani.
Chotsani mkwiyo. Gwiritsani ntchito Chinthu chanu Chofuulira chija.
Chitanipo kanthu!Njira yosavuta yopewera mkwiyo.
Muganize inuyo kuti ndinu munthu winayo. Kodi zikusintha ndi ziti pa moyo wanu pamene mukuona zinthu monga mmene akuonera winayo?
Mukokere mpweya m’kati musanayankhe.
Gonani mokwanira.
Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali
chikwiyire.Aefeso 4:26
Pitani kakhululukireni!
34 35
Kulumikizana ndi Ena
Mwina mukudziona kuti muli nokha.Sikuti mukulakwitsa kutero.Opulumuka nthawi zina amadziona ngati ali okha.
Mwina mukuona kuti dzikoli lakukulirani ndipo inu mukudziona kuchepa kwambiri.
Mwina mukumusowa mnzanu amene mumamukonda.Mwina muli kutali ndi abwenzi anu kapena banja lanu.
Ngati mwamusowa wina wake, lembani dzina la munthuyo pano.
Mulikongoletse dzinalo kuti lioneka ngati munthuyo ali pamenepo.
Pangani kuti dzinalo likongole kwambiri kapena lioneka ngati chidole,
kapena LIKULE KWAMBIRI kapena lichepe kwambiri.
36 37
Iye ndi Atate wa ana amasiye, mtetezi wa amayi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala m’malo oyera.
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa m’mabanja.
Kuyambira pachiyambi cha dziko, Mulungu anati sikwabwino kuti ife tikhale tokha.
Khalani bwenzi!
Salimo 68:5–6
Zimatengera gulu lonse kuti munthu akhale moyo wabwino.
38 39
Ngati mukuona kuti muli nokha, yambani kucheza ndi anthu amene akuyandikirani.
Zolemba zanu zikhale zosangalatsa kwambiri!
Njira ina yabwino kwambiri yoyambira kucheza ndi anthu ndi kuwalembera kalata.
Mawu amene mulembewo adzakhala njira yolumikizirana ndi munthu wina.
Mutha kulemba mawu Owathokoza,
mawu a Chilimbikitso,
mawu akuti, Ndakusowani kapena mawu akuti,
Kodi sukufuna kukhala ndi kachidole kokhala ngati nyama ya kuthengo?
40 41
Malangizo kwa OpulumukaYang’anani mbali zonse ndipo yamikani Mulungu chifukwa cha anthu abwino amene mukukhala nawo.
Pezani ndi kulumikizana ndi munthu wina polemberana naye.
Chitanipo kanthu!
Phunzirani kukonda anthu amene mukukhala nawo ndi chikondi monga ichi:
Chikondi n’choleza mtima, chikondi n’chokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga,
sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza
nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira
nthawi zonse. Chikondi n’chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime
adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.1 Korinto 13:4–8
42 43
Pamene Zonse Zatha Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
N’chifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.
Salimo 46:1–3
Inu simukudzwa kuti mliri umenewu ukhalapo mpaka liti.Koma mungathe kudalira Mulungu kuti akudutsitsani.Koma nthawi ino, mutha kuyamba kukonzekera zomwe
mukufuna kudzachita pamene izi zonse zatha!Lembani zinthu zomwe mukufuna kudzachita
44 45
Baibulo likutiwuza kuti:
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma
athe kukhala ndi moyo wosatha.
Yohane 3:16.
Yesu anafa pa mtanda chifukwa cha machimo athu, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa patatha
masiku atatu ndipo ali ndi moyo mpaka lero!
Yesaya 53:4
Yesu akufuna kuti inu mumudalire ndi kupereka moyo wanu kwa Iye kuti Iyeyo azikhala ndi inu nthawi zonse. Ngati ndinu wokonzeka kupereka moyo wanu
kwa Yesu, pempherani pemphero ili.
Ambuye Yesu,
ine ndikudziwa kuti mumandikonda ndipo munandifera pa mtanda.
Ndikupepesa chifukwa cha zinthu zoyipa zimene ndakhala ndikuchita, ndipo kuyambira lero ndikufuna kukhala moyo wokondweretsa Inu.
Lamulirani moyo wanga pamene ndikuphunzira kutsatira Inu.
Zikomo chifukwa chokhala Mpulumutsi wanga!
Ameni.
Iye anamva zowawa m’malo mwa ife;ndipo anasautsidwa m’malo mwathu.
46 47
48
OpulumukaTM Kusindikiza kwa PaderaMwini © 2020 ndi Biblica, Inc.
Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
The SurvivorsTM Special Edition (Chichewa)Copyright © 2020 by Biblica, Inc.
All rights reserved worldwide.
Mawu a Mulungu achokera mu m'Baibulo laMawu a Mulungu Mu Chichewa ChaleroTM
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.
Zizindikiro izi “Biblica”, Biblica Logo, “International Bible Society” ndi zovomerezeka ku Amerika ndi Bungwe la Biblica.
ISBN: 978-1-62337-395-5