uthenga wabwino wochokera kwa mulungu - jw.orgdownload.jw.org/files/media_books/50/fg_cn.pdfni...

32
UTHENGA WABWINO WOCHOKERA K WA MULUNGU

Upload: vuthuy

Post on 10-Mar-2018

593 views

Category:

Documents


37 download

TRANSCRIPT

UTHENGAWABWINOWOCHOKERA KWA

MULUNGU

Printed by WatchTower Bible andTract Society of South Africa NPC1 Robert Broom Drive East,Rangeview, Krugersdorp, 1739, R.S.A.Made in the Republic of South AfricaLopangidwa ku Republic of South Africa

UthengaWabwino Wochokera kwa MulunguGood News From God!Kosindikizidwa mu February 2018Chichewa (fg-CN)˘ 2012WATCH TOWER BIBLE AND TRACTSOCIETYOF PENNSYLVANIAOfalitsa

Kabukuka sitigulitsa. Timapereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulopadziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amaperekamwa kufuna kwawo.Ngati mukufuna kupereka ndalama, pitani pa webusaiti yathu ya jw.org/ny.

Malemba onse m’kabuku kano akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika,lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.Photo Credits: Page 6, top, Dead Sea Scroll: Shrine of the Book, Photo ˘ The IsraelMuseum, Jerusalem; page 6, middle, and page 32, upper right, Greek Codex: FromTheCodex Alexandrinus in Reduced Photographic Facsimile, 1909, by permission of the BritishLibrary; page 16, Hitler: Based on U.S. National Archives photo

Kabuku kano kakuthandizani kuti muzisangalalamukama-phunziraMawu aMulungu, Baibulo. Kumapeto kwa ndimeiliyonse kuli malemba am’Baibulo omwe angakuthandizenikudziwa yankho la funso limene lalembedwa ndimawu akudakwambiri lomwe lili pamwamba pa ndimeyo.

Pamenemukuwerengamalemba am’Baibulo, ganiziranimmenemalembawo akuyankhiramafunsowo. Aliyense waMboni za Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani kumvetsabwinoMalembawo.D Werengani Luka 24:32, 45.

Zimene mungachite kuti mupindule ndi kabukuka:

D Werengani Yohane 17:3.

Dziwani izi: Mabuku omwe atchulidwa m’kabuku kano ndi ofalitsidwa ndi Mboni zaYehova.

Mmene mungapezere malemba m’Baibulo lanu.Lemba lililonse limakhalandi dzina la buku limenemukufunika kupeza m’Baibulo.

Nambala yoyambaikuimira chaputala cham’bukulo chomwemukufunika kupeza.

Kenako nambalakapena manambalaotsatira akuimiravesi kapena mavesiamene mukufunikakuwerenga.

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙˙

˙

˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙

˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙

˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙ ˙

°

°

°

mukumana ndi masautso, koma limba-ni mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.”

17 Yesu atalankhula zinthu zimene-zi, anakweza maso ake kumwa-

mba ndi kunena kuti: “Atate, nthawi ya-fika, lemekezani mwana wanu, kutimwana wanu akulemekezeni. 2 Inumwamupatsa ulamuliro pa anthu onse,kuti onse amene inu mwamupatsa, awa-patse moyo wosatha.3 Pakuti moyo wo-satha adzaupeza akamaphunzira ndi ku-dziwa za inu, Mulungu yekhayo ameneali woona, ndi za Yesu Khristu, ame-ne inu munamutuma. 4 Ndakulemeke-zani padziko lapansi, popeza ndatsiriza

YOHANE 16:33—17:24

3

1. Kodi Mulungu akutiuza uthenga wotani?

Mulungu akufuna kuti anthu azisangalala ndi moyo padziko la-pansi pano. Iye analenga dziko lapansi ndi chilichonse chimene chilim’dzikoli chifukwa chakuti amakonda anthu. Posachedwapa Mulunguadzachotsa zinthu zonse zimene zikuyambitsa mavuto pakati pa anthukuti anthu m’dziko lililonse azikhala mosangalala. D Werengani Ye-remiya 29:11.

Palibe boma limene lakwanitsa kuthetsa chiwawa, matenda kapenaimfa. Komabe pali uthenga wabwino. Uthenga wake ndi wakuti posa-chedwapa, Mulungu athetsa maboma onse a anthu ndipo m’malomwake akhazikitsa boma lake. Anthu amene azidzalamuliridwa ndiboma la Mulungu adzakhala mwamtendere komanso adzakhala ndithanzi labwino. D Werengani Yesaya 25:8; 33:24; Danieli 2:44.

2. N’chifukwa chiyani uthenga wabwino ukufunika kulengezedwamwamsanga?

Mavuto amene anthu akukumana nawo sangathe pokhapokhaMulungu atachotsa anthu oipa padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) Ndiye-no kodi anthu oipawo adzawachotsa liti padzikoli? Mawu a Mulunguanalosera za mavuto amene anthu akukumana nawo masiku ano.Choncho, zinthu zoipa zimene zikuchitikazi ndi umboni wakuti nthawiyoti Mulungu awononge oipa ili pafupi kwambiri. D Werengani2 Timoteyo 3:1-5.

3. Kodi tikuyenera kuchita chiyani?

Tiyenera kuphunzira za Mulungu kudzera m’Mawu ake, Baibulo.Baibulo lili ngati kalata imene bambo wachikondi walembera ana ake.Bukuli limatiuza zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino pa-nopa, komanso kuti tidzapeze moyo wosatha padziko lapansi m’tso-golo muno. N’zoona kuti anthu ena atakuonani mukuphunzira Baibu-lo kuti mulimvetse bwino, sangasangalale. Koma musalole kuti winaaliyense akulepheretseni kuphunzira Mawu a Mulungu amene angaku-thandizeni kudzapeza moyo wosatha m’tsogolo. D Werengani Mi-yambo 29:25; Chivumbulutso 14:6, 7.

1Kodi Uthenga WabwinoN’chiyani?

4

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Mulungu?

Mulungu woona ndi amene analenga zinthu zonse. Iye alibe chi-yambi komanso alibe mapeto. (Salimo 90:2) Uthenga wabwino ume-ne uli m’Baibulo unachokera kwa iyeyo. (1 Timoteyo 1:11) Popezakuti Mulungu ndi amene anatipatsa moyo, iye yekha ndi amene tiye-nera kumulambira. D Werengani Chivumbulutso 4:11.

2. Kodi Mulungu ndi wotani kwenikweni?

Palibe munthu amene anaonapo Mulungu chifukwa chakuti Mu-lungu ndi Mzimu. Izi zikutanthauza kuti iye ndi wapamwamba kwa-mbiri kuposa cholengedwa chilichonse cha padziko lapansi. (Yohane1:18; 4:24) Komabe, tingathe kudziwa makhalidwe a Mulungu tikao-na zinthu zimene iye analenga. Mwachitsanzo, Mulungu analengamaluwa komanso zipatso za mitundu yosiyanasiyana zimene zimaso-nyeza kuti iye ndi wachikondi komanso wanzeru. Ndipo zinthu zambi-ri zakuthambo zimene analenga zimasonyeza kuti iye ndi wampha-mvu. D Werengani Aroma 1:20.

Tikamawerenga Baibulo tingaphunzire zambiri zokhudza makha-lidwe a Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza zimene Mulunguamakonda komanso zimene amadana nazo, zimene amachita kwaanthu, ndiponso mmene amachitira zinthu pa nkhani zosiyanasiyana.D Werengani Salimo 103:7-10.

3. Kodi Mulungu ali ndi dzina?

Yesu ananena kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyere-tsedwe.” (Mateyu 6:9) Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mayina ambiriaulemu, koma dzina lake lenileni ndi limodzi lokha. Dzinali limalembe-dwa m’njira zosiyanasiyana, m’zinenero zosiyanasiyananso. Mwachi-tsanzo, m’Chichewa timati “Yehova,” koma anthu ena amangoti “Ya-hweh.” D Werengani Salimo 83:18.

M’Mabaibulo ambiri anachotsamo dzina la Mulungu ndipo m’ma-lomwake anaikamo mayina audindo chabe akuti Ambuye kapenaMulungu. Koma Baibulo litangolembedwa kumene, dzina la Mulungulinkapezeka m’malo pafupifupi 7,000. Ndipotu pamene Yesu anka-

2 Kodi Mulungu Ndani?

5

phunzitsa anthu zokhudzaMulungu, anawathandiza kuti adziwensodzina laMulungu. D Werengani Yohane 17:26.

4. Kodi Yehova amasamala za ife?Kodi mmene mavuto achulukiramu, zi-

kusonyeza kuti Yehova ndi Mulungu amenesasamala za ife? Anthu ena amanena kutiMulungu amatibweretsera mavuto pofunakutiyesa, koma zimenezi si zoona.D Werengani Yakobo 1:13.

Mulungu amatilemekeza ndipo anatipatsa ufulu wosankha zimenetikufuna. Kunena zoona, timayamikira kwambiri kuti tili ndi ufulu wo-sankha kulambiraMulungu. (Yoswa 24:15) Komabe anthu ambiriamasankha kuchitira ena zinthu zoipa, ndipo izi zachititsa kuti anthuambiri azivutika. Yehova amakhumudwa akamaona kupanda chilu-ngamo kotereku. D Werengani Genesis 6:5, 6.

Yehova ndi Mulungu amene amasamala za ife. Iye amafuna kutitizisangalala ndi moyo. Choncho, posachedwapa athetsa mavutoonse komanso awononga anthu onse amene amayambitsa mavuto-wo. Koma padakali pano, Mulungu ali ndi chifukwa chomveka cholo-lera kuti anthu avutike kwa kanthawi kochepa. Mu Phunziro 8, tidza-kambirana za chifukwa chimenechi. D Werengani 2 Petulo 2:9; 3:7,13.

5. Kodi tingatani kuti timuyandikire Mulungu?Yehova akutipempha kuti timuyandikire polankhula naye m’pe-

mphero. Iye amasamalira munthu aliyense payekha. (Salimo 65:2;145:18) Yehova ndi wokonzeka kutikhululukira. Ndipotu iye amaonatikamayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa, ngakhale kuti nthawizina timalephera. Choncho, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro,n’zotheka ndithu kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. D WerenganiSalimo 103:12-14; Yakobo 4:8.

Popeza kuti Yehova watipatsa moyo, tiyenera kumukonda kwambi-ri kuposa mmene timakondera wina aliyense. (Maliko 12:30)Muka-masonyeza kuti mumakondaMulungu popitiriza kuphunzira za iyeyo,komanso pochita zimene akufuna, mudzamuyandikira kwambiri.D Werengani 1 Timoteyo 2:4; 1 Yohane 5:3.

Mofanana ndibambo wachiko-ndiyu,Mulungu

wakonza zothetsamavuto athu kutitisadzavutikensompaka kalekale

1. Kodi Mlembi Wamkulu wa Baibulo ndani?

Uthenga wabwino wakuti anthu adzakhala kwamuyaya pa-dziko lapansi ukupezeka m’Baibulo. (Salimo 37:29) M’Baibulomuli mabuku ang’onoang’ono okwana 66, ndipo polemba mabu-ku amenewa, Mulungu anagwiritsa ntchito amuna okhulupirikaokwana 40. Mabuku asanu oyambirira analembedwa ndi Mosezaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Ndipo buku lomaliza linalembe-dwa ndi mtumwi Yohane zaka zoposa 1,900 zapitazo. Kodi anthuolemba Baibulowo ankalemba maganizo a ndani? Mulungu anka-lankhula ndi anthu amene analemba Baibulowo kudzera mwamzimu woyera. (2 Samueli 23:2) Choncho, iwo analemba maga-nizo a Mulungu, osati maganizo awo. Pa chifukwa chimenechi,Yehova ndiye Mlembi Wamkulu wa Baibulo. D Werengani 2 Ti-moteyo 3:16; 2 Petulo 1:20, 21.

2. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Baibulo limanena zoona?

Tikudziwa kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu chifukwachakuti limalosera za m’tsogolo molondola komanso mwatsata-netsatane. Palibe munthu aliyense amene angachite zimenezi. (Yo-swa 23:14) Ndi Mulungu Wamphamvuyonse yekha amene ama-tha kudziwiratu zimene zidzachitikire anthu m’tsogolo.D Werengani Yesaya 42:9; 46:10.

Choncho n’zosadabwitsa kuti buku lochokera kwa Mulungundi lapadera kwambiri. Mabaibulo mabiliyoni ochuluka afalitsi-dwa m’zinenero mahandiredi ambiri. Ngakhale kuti Baibulo ndilakale kwambiri, limagwirizana ndi mfundo zolondola za sayansi.Komanso anthu 40 amene analemba Baibuloli sanalembe mfu-ndo zotsutsana.� Kuwonjezera pamenepo, zimene Baibulo lima-nena pa nkhani ya chikondi n’zapadera kwambiri, ndipo sizinga-chokere kwa wina aliyense koma kwa Mulungu woona yekha,

� Onani kabuku kakuti Buku la Anthu Onse.

3 Kodi Uthenga Wabwino NdiWochokeradi kwa Mulungu?

6

yemwe ndi Mulungu wachikondi. Ndipotu Baibulo lidakali ndimphamvu yosintha moyo wa anthu kuti ukhale wabwino. Pogani-zira mfundo zimenezi, anthu mamiliyoni ambiri sakayikira kuti Ba-ibulo ndi Mawu aMulungu. D Werengani 1 Atesalonika 2:13.

3. Kodi m’Baibulo muli nkhani zotani?Imodzi mwa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo ndi yakuti Mu-

lungu ali ndi cholinga chapadera chokhudza anthu. Malembaamafotokoza mmene anthu anatayira mwayi wokhala m’paradai-so padziko lapansi pano kalelo, komanso amafotokoza mmeneMulungu adzabwezeretsere paradaiso ameneyo. D WerenganiChivumbulutso 21:4, 5.

M’Mawu aMulungu mulinso malamulo, mfundo za makhali-dwe abwino komanso malangizo. Kuwonjezera pamenepo, m’Bai-bulo muli nkhani zokhudza zimene Mulungu ankachitira anthu,ndipo tikamawerenga nkhanizi timaona makhalidwe ameneMu-lungu ali nawo. Choncho Baibulo lingakuthandizeni kuti mu-m’dziwe bwino Mulungu. Limafotokoza zimene mungachite kutimukhale bwenzi lake. D Werengani Salimo 19:7,11; Yakobo2:23; 4:8.

4. Kodi mungatani kuti muzilimvetsa bwino Baibulo?Kabuku kano kakuthandizani kuti mulimvetse bwino Baibulo,

ndipo kakufotokoza malemba potsatira njira imene Yesu ankagwi-ritsa ntchito. Nthawi zonse, Yesu ankagwiritsa ntchito malembapophunzitsa, ndipo ankafotokoza ‘tanthauzo la Malembawo.’D Werengani Luka 24:27, 45.

Palibe chinthu chosangalatsa kuposa uthenga wabwino wo-chokera kwaMulungu. Komabe, anthu ena safuna kumva uthe-nga umenewu, ndipo ena amakwiya chifukwa cha uthengawu.Koma zimenezi zisakufooketseni, chifukwa ngati mukufuna kudza-peza moyo wosatha mukuyenera kuphunzira kuti mum’dziwe bwi-no Mulungu. D Werengani Yohane 17:3.

Kuti mumve zambiri, werengani mutu 2 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

7

1. Kodi moyo wa Yesu unayamba bwanji?

Mosiyana ndi munthu wina aliyense, Yesu anakhalapo ku-mwamba asanabwere padziko lapansi, ndipo anali ndi thupi lau-zimu. (Yohane 8:23) Iye anali woyamba pa zinthu zonse zimeneMulungu analenga, ndipo anathandiza Mulungu pa ntchito yo-lenga zinthu zina zonse. Ndi Yesu yekha amene Yehova anamule-nga mwachindunji, ndipo mpake kuti amatchedwa Mwana “wo-badwa yekha” wa Mulungu. (Yohane 1:14) Pa nthawi ina Yesuankalankhula m’malo mwa Mulungu, choncho amatchedwansokuti “Mawu.” D Werengani Miyambo 8:22, 23, 30; Akolose1:15,16.

2. N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?

Mulungu anatumiza Mwana wake padziko lapansi posamutsamoyo wake kumwamba, n’kuuika m’mimba mwa namwali winawachiyuda, dzina lake Mariya. Choncho Yesu analibe bambowomubereka. (Luka 1:30-35) Yesu anabwera padziko lapansi(1) kudzaphunzitsa anthu choonadi chokhudza Mulungu,(2) kudzatisonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire chifunirocha Mulungu ngakhale pamene tili m’mavuto, komanso (3) ku-dzapereka moyo wake wangwiro kuti ukhale “dipo.” D Were-ngani Mateyu 20:28.

3. N’chifukwa chiyani tikufunikira dipo?

Dipo ndi malipiro amene munthu amapereka pofuna ku-wombola munthu wina kuti asaphedwe. (Ekisodo 21:29, 30) Pa-

mene Mulungu ankalenga anthu,analibe cholinga choti anthuwoazikalamba komanso kufa. Tiku-dziwa bwanji zimenezi? Tikudziwazimenezi chifukwa chakuti Mulu-ngu anauza munthu woyamba,Adamu, kuti akadzachita “tchi-mo,” malinga n’kunena kwa Bai-

4 Kodi Yesu Khristu Ndani?

Kodi ndi makhalidweati a Yesu omwe anka-chititsa kuti anthuazimasuka naye?—MATEYU 11:29;

MALIKO 10:13-16.

bulo, adzafa. Choncho Adamu akanapanda kuchimwa, sakana-fa. (Genesis 2:16,17; 5:5) Malinga ndi zimene Baibulo limanena,imfa ‘inalowa’ m’dziko kudzera mwa Adamu. Choncho Adamuanapatsira ana ake onse uchimo, womwe chilango chake ndiimfa. N’chifukwa chake tikufunikira dipo lotiwombola kuti tisa-dzalandire chilango cha imfa chimene tinatengera kwa Adamu.D Werengani Aroma 5:12; 6:23.

Kodi ndani amene akanapereka dipo lotiwombola ku imfa?Panopa munthu aliyense akamwalira, amakhala ngati waperekamalipiro a machimo ake okha. Munthu wopanda ungwiro sa-ngathe kupereka dipo lowombola anthu ena. D WerenganiSalimo 49:7-9.

4. N’chifukwa chiyani Yesu anafa?Mosiyana ndi ife, Yesu anali wangwiro. Choncho sanafunike

kufa chifukwa cha machimo ake, popeza sanachite tchimo lililo-nse. M’malomwake, Yesu anafa chifukwa cha machimo a anthuena. Mulungu anasonyeza kuti amakonda kwambiri anthu potu-miza Mwana wake kuti adzatifere. Nayenso Yesu anasonyeza kutiamatikonda chifukwa anamvera Atate wake pololera kuperekamoyo wake kuti atiwombole ku machimo athu. D WerenganiYohane 3:16; Aroma 5:18,19.

5. Kodi panopa Yesu akuchita chiyani?Pamene anali padziko lapansi, Yesu anachiritsa odwala, ana-

ukitsa akufa komanso anathandiza anthu amene anali m’mavu-to osiyanasiyana. Iye anachita zimenezi pofuna kusonyeza zime-ne adzachite m’tsogolo kwa anthu onse omvera. (Mateyu 15:30, 31; Yohane 5:28) Yesu atafa, Mulungu anamuukitsa ndi thu-pi lauzimu. (1 Petulo 3:18) Kenako Yesu anadikira kudzanja la-manja la Mulungu kufikira pamene Yehova anamupatsa mpha-mvu zoti alamulire padziko lonse lapansi mongaMfumu.(Aheberi 10:12,13) Panopa Yesu akulamulira mongaMfumu ku-mwamba ndipo otsatira ake akulengeza uthenga wabwinowupadziko lonse lapansi. D Werengani Danieli 7:13,14; Mateyu24:14.

Posachedwapa, Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake mo-ngaMfumu pothetsa mavuto onse komanso powononga anthuonse amene amayambitsa mavutowo. Anthu onse amene ama-khulupirira Yesu komanso kumumvera adzasangalala ndi moyom’paradaiso padziko lapansi. D Werengani Salimo 37:9-11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 4 ndi 5 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

9

10

1. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi?Yehova analenga dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. Choncho

anthufe kwathu ndi padzikoli. Cholinga cha Mulungu polenga anthuawiri oyambirira, Adamu ndi Hava, sichinali chakuti iwo akakhalekumwamba, chifukwa iye anali atalenga kale angelo n’kuwaika ku-mwambako. (Yobu 38:4, 7) M’malomwake, Mulungu anaika mu-nthu woyambirirayo m’paradaiso wokongola kwambiri, wotchedwamunda wa Edeni. (Genesis 2:15-17) Cholinga cha Yehova chinalichakuti munthuyo, pamodzi ndi ana amene akanabereka, akhale ndimoyo wosatha padziko lapansili. D Werengani Salimo 37:29;115:16.

Poyamba, munda wa Edeni wokha ndi womwe unaliparadaiso. Koma Mulungu ankafuna kuti banja loyambiriralo libere-ke ana, n’kuchuluka padziko lonse lapansi. M’kupita kwa nthawi,iwo akanadzaza dziko lonse lapansi, ndipo dziko lonseli likanakhalaparadaiso. (Genesis 1:28) Choncho dziko lapansili silidzawononge-dwa, ndipo anthu adzapitiriza kukhalamo. D Werengani Salimo104:5.

2. N’chifukwa chiyani dziko lapansili silili paradaiso panopa?Adamu ndi Hava sanamvere Yehova Mulungu, ndipo iye anawatu-

lutsa m’munda wa Edeni. Chifukwa cha zimenezi, iwo anataya mwa-yi wokhala m’paradaiso, ndipo palibe munthu amene angakwanitsekubweretsanso paradaiso. Baibulo limati: “Dziko lapansi lapereke-dwa m’manja mwa woipa.”—Yobu 9:24. D Werengani Genesis 3:23, 24.

Kodi Yehova wasintha cholinga chimene analengera anthu? Ayi,sanasinthe. Iye ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo sangalepherekuchita zimene akufuna. (Yesaya 45:18) Yehova adzathandiza anthukuti akhale ndi moyo wosatha komanso wosangalala ngati mmeneiyeyo anafunira poyamba. D Werengani Salimo 37:11, 34.

3. Kodi chidzachitike n’chiyani kuti dzikoli likhalenso Paradaiso?Yesu Khristu akulamulira monga Mfumu yoikidwa ndi

Mulungu ndipo posachedwapa dzikoli likhalanso paradaiso. Pa

5 Kodi MulunguAli Ndi Cholinga ChotaniChokhudza Dziko Lapansili?

nkhondo yotchedwa Aramagedo, Yesu adzatsogolera angelo a Mulu-ngu powononga onse amene amatsutsana ndi Mulungu. KenakoYesu adzatsekera Satana m’ndende kwa zaka 1,000. Oipa akamadza-wonongedwa, anthu aMulungu adzapulumuka chifukwa Yesu adza-watsogolera ndiponso kuwateteza. Iwo adzasangalala ndi moyo wo-satha m’Paradaiso padziko lapansi. D Werengani Chivumbulutso20:1-3; 21:3, 4.

4. Kodi mavuto a anthu adzatha liti?Kodi Mulungu adzathetsa liti mavuto onse padziko lapansili? Yesu

anapereka “chizindikiro” chimene chidzasonyeze kuti mapeto a dzi-koli atsala pang’ono kufika. Zinthu zimene zikuchitika padzikoli ma-siku ano n’zoopsa kwambiri ndipo zikuika moyo wa anthu pangozi.Koma zonsezi zikungosonyeza kuti tsopano tikukhala m’nyengo ya“mapeto a nthawi ino.” D Werengani Mateyu 24:3, 7-14, 21, 22.

Yesu adzathetsa mavuto onse mu ulamuliro wake wa zaka 1,000pamene azidzalamulira dziko lapansili ali kumwamba. (Yesaya 9:6, 7; 11:9) Kuwonjezera pa udindo wake mongaMfumu, Yesu adza-tumikiranso mongaMkulu wa Ansembe ndipo adzafafaniza machi-mo a anthu omwe amakondaMulungu. Choncho kudzera mwaYesu, Mulungu adzathetsa matenda, ukalamba ndiponso imfa.D Werengani Yesaya 25:8; 33:24.

5. Kodi ndani amene adzakhale m’Paradaiso m’tsogolo muno?Anthu omvera Mulungu ndi omwe adzakhale m’Paradaiso. (1 Yo-

hane 2:17) Yesu anatumiza otsatira ake kuti akafufuze anthu ofatsandi kuwaphunzitsa zimene angachite kuti Mulungu aziwakonda.Masiku ano, Yehova akuthandiza anthu mamiliyoni ambiri kutiadzakhale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) KuNyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, anthu amaphunzira zimeneangachite kuti akhale amuna ndi abambo abwino, kapenanso kutiakhale akazi ndi amayi abwino. Ana ndi makolo amalambira Mulu-ngu pamodzi ndipo amaphunzira zimene angachite kuti apeze ma-dalitso chifukwa cha uthenga wabwino. D Werengani Mika 4:1-4.

Mukapita ku Nyumba yaUfumu,mukapeza anthuamene amakondaMulu-ngu komanso ameneamafunitsitsa kuphunzirazimene angachite kuti azi-mukondweretsa

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 wa buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

11

1. Kodi pali uthenga wabwino wotani wokhudza anthu ameneanamwalira?

Pamene Yesu ankafika m’tauni ya Betaniya, yomwe inali pafupindi mzinda wa Yerusalemu, panali patadutsa masiku anayi mnzakeLazaro atamwalira. Kenako Yesu pamodzi ndi Malita ndi Mariya,omwe anali azichemwali ake a Lazaro, anapita kumanda kumenemchimwene wawoyo anaikidwa. Posapita nthawi, kumandako ku-nadzaza anthu. Kenako Yesu anaukitsa Lazaro, ndipo mukhoza ku-ona m’maganizo mwanu chisangalalo chimene Malita ndi Mariyaanali nacho ataona kuti m’bale wawo waukitsidwa. D Were-ngani Yohane 11:21-24, 38-44.

Malita anali akudziwa kale za uthenga wabwino wokhudzaanthu amene anamwalira. Iye ankadziwa kuti Yehova adzaukitsaakufa ndipo adzakhalanso ndi moyo padziko lapansili. D Were-ngani Yobu 14:14,15.

2. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

Anthu anapangidwa kuchokera kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19)Anthufe si mizimu imene ikukhala m’matupi okhala ndi minofu.Koma ndife zolengedwa zooneka, zokhala ndi thupi, ndipo mkatimwathu mulibe chinthu chomwe chimapitirizabe kukhala ndimoyo tikamwalira. Munthu akamwalira, ubongo wake umafanso,ndipo zinthu zonse zimene ankaganiza zimathera pomwepo. N’chi-fukwa chaketu Lazaro sananene chilichonse chokhudza zimene zi-nkamuchitikira pa nthawi imene anamwalira, popeza munthu aka-fa sadziwa chilichonse. D Werengani Salimo 146:4; Mlaliki 9:5,6,10.

6 Kodi Pali ChiyembekezoChotani Chokhudza AnthuAmene Anamwalira?

Mulungu anauzaAdamu kuti:“Popeza ndiwefumbi, kufumbikoudzabwerera.”—GENESIS 3:19.

12

Kodi anthu oipa akamwalira, Mulungu amawawotcha ndimoto? Popeza Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti munthuakafa sadziwa chilichonse, mfundo yakuti Mulungu amawotchaanthu ndi yabodza, ndipo imangochititsa kuti anthu aziimbaMu-lungumlandu wa zinthu zimene iye sachita n’komwe. NdipotuMu-lungu amanyansidwa kwambiri anthu akamazunza anzawo powa-wotcha ndi moto kapena akamamunamizira kuti iye amachitazimenezi. D Werengani Yeremiya 7:31.

3. Kodi anthu amene anamwalira angathe kulankhula nafe?Anthu akufa sangalankhule kapena kumva. (Salimo 115:17)

Komabe pali angelo ena oipa ndipo amalankhula ndi anthu pona-mizira kuti ndi anthu amene anamwalira. (2 Petulo 2:4) NdipotuYehova amaletsa kulankhula ndi anthu akufa. D Werengani De-uteronomo 18:10,11.

4. Kodi ndi anthu ati amene adzaukitsidwe?Anthumamiliyoni ambirimbiri amene ali m’manda adzauka

n’kukhalanso ndi moyo padziko lapansi. Ngakhalenso anthu enaamene sankamudziwaMulungu ndipo ankachita zoipa adzaukitsi-dwa. D Werengani Luka 23:43; Machitidwe 24:15.

Anthu amene adzaukitsidwe adzakhala ndi mwayi woti aphu-nzire zaMulungu ndi kusonyeza kuti akukhulupirira Yesu pomu-mvera. (Chivumbulutso 20:11-13) Oukitsidwawo akamadzachitazinthu zabwino adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosathapadziko lapansi. D Werengani Yohane 5:28, 29.

5. Kodi mfundo yakuti akufa adzaukitsidwa ikutiuza chiyani zaYehova?

N’zotheka kuti akufa adzaukitsidwe chifukwaMulungu anatu-mizaMwana wake kudzatifera. Choncho tikaganizira mfundo ime-neyi timaona kuti Yehova ndi wachikondi komanso kukomamtimakwake n’kwakukulu. Kodi akufa akadzauka, inuyo mukufunitsitsakudzaonana ndi ndani? D Werengani Yohane 3:16; Aroma6:23.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6, 7 ndi 10 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

13

14

1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?Ufumu waMulungu ndi boma lakumwamba. Boma limeneli li-

dzalowa m’malo mwamaboma onse ndipoMulungu adzagwiritsantchito boma limeneli pokwaniritsa chifuniro chake kumwambandi padziko lapansi. Uthenga wonena za Ufumu waMulungu ndiwabwino. Anthu akufunikira boma labwino, ndipo posachedwapaUfumu waMulungu, womwe ndi boma labwino uyamba kulamuli-ra. Bomali lidzagwirizanitsa anthu onse okhala padziko lapansi.D Werengani Danieli 2:44; Mateyu 6:9,10; 24:14.

Ufumu uliwonse umakhala ndi mfumu yake. Choncho, Yehovaanaika Mwana wake, Yesu Khristu, kuti akhale Mfumu ya Ufumuwake. D Werengani Chivumbulutso 11:15.

2. N’chifukwa chiyani Yesu ali Mfumu yoyenerera?Mwana waMulungu ndi Mfumu yoyenerera chifukwa chakuti

ndi wachifundo ndipo amachita zabwino nthawi zonse. (Mateyu11:28-30) Komanso ali ndi mphamvuzambiri moti angathe kuthandizaanthu. Izi zili choncho chifukwa chaku-ti azidzalamulira dziko lapansi ali ku-mwamba. Iye ataukitsidwa, anapitakumwamba n’kukakhala kudzanja la-manja la Yehova poyembekezera kutiamupatse ufumu. (Aheberi 10:12,13)KenakoMulungu anapatsa Yesu mpha-mvu kuti ayambe kulamulira. D We-rengani Danieli 7:13,14.

3. Kodi ndani amene azidzalamulira limodzi ndi Yesu?Pali gulu lina la “oyera” amene azidzalamulira limodzi ndi Yesu

kumwamba. (Danieli 7:27) Oyera oyambirira kusankhidwa analiatumwi okhulupirika a Yesu. Mpaka pano Yehova akusankhabeamuna ndi akazi okhulupirika kuti akhale m’gulu la oyera limeneli.

7 Kodi Ufumu wa MulunguN’chiyani?

Kodi n’chiyanichimenechimachititsakuti YesuakhaleMfumuyoyenerera?—MALIKO 1:40-42.

Mofanana ndi Yesu, anthu amenewa amaukitsidwa ndi matupi au-zimu. D Werengani Yohane 14:1-3; 1 Akorinto 15:42-44.

Kodi ndi anthu angati amene adzapite kumwamba? Yesu anane-na kuti anthu opita kumwambawa ndi “kagulu ka nkhosa.” (Luka12:32) Onse pamodzi adzakwana 144,000, ndipo adzalamulira dzi-ko lapansi limodzi ndi Yesu. D Werengani Chivumbulutso 14:1.

4. Kodi chinachitika n’chiyani Yesu atayamba kulamulira?Ufumu waMulungu unayamba kulamulira m’chaka cha 1914.�

Chinthu choyamba chimene Yesu anachita atakhala Mfumu chinalikuchotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba n’kuwaponyera pa-dziko lapansi. Zitatero Satana anakwiya kwambiri ndipo anayambakubweretsa mavuto kwa anthu padziko lonse lapansi. (Chivumbu-lutso 12:7-10,12) Kungoyambira pa nthawi imeneyo, mavuto ame-ne anthu akukumana nawo akhala akuwonjezereka kwambiri. Cho-ncho, nkhondo, njala, miliri komanso zivomezi, zonsezi ndi mbaliya “chizindikiro” chosonyeza kuti posachedwapa Ufumu waMulu-ngu uyamba kulamulira dziko lapansi. D Werengani Luka 21:7,10,11, 31.

5. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zinthu zotani?Kudzera m’ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse,

Ufumu waMulungu wayamba kale kugwirizanitsa khamu lalikulu laanthu ochokera m’mitundu yonse. Anthu ofatsa mamiliyoni ambiriakubwera kumbali ya Ufumu waMulungu, womwe wolamulirawake ndi Yesu. Ufumu umenewu udzateteza anthuwo pamene dzi-ko loipali lizidzawonongedwa. Choncho aliyense amene akufunakupeza madalitso mu Ufumu waMulungu, ayenera kumvera Yesumonga wolamulira wake. D Werengani Chivumbulutso 7:9,14,16,17.

Mkati mwa zaka 1,000, Ufumu umenewu udzakwaniritsa choli-nga choyambirira chaMulungu chokhudza anthu. Dziko lonse la-pansi lidzakhala paradaiso, ndipo pamapeto pake Yesu adzabweze-ra Ufumuwom’manja mwa Atate wake. (1 Akorinto 15:24-26)Kodi pali winawake amene mungakonde kumuuza za Ufumu waMulungu? D Werengani Salimo 37:10,11, 29.

� Kuti mumve zambiri zokhudza ulosi wa m’Baibulo wonena za chaka cha1914, werengani tsamba 217 mpaka 220 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphu-nzitsa.

Kuti mumve zambiri, werengani mutu 8 ndi 9 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

15

1. Kodi zinthu zoipa zinayamba bwanji?Zinthu zoipa zinayamba padziko lapansi pamene Satana ananena

bodza loyamba. Poyamba Satana anali mngelo wangwiro, koma “sana-khazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Choncho anayamba kulakalakakulambiridwa. Zimenezi sizinali zoyenera chifukwaMulungu yekha ndi-ye woyenera kulambiridwa. Pofuna kukwaniritsa cholinga chake, Sata-na ananamiza mkazi woyamba, Hava, n’kumunyengerera kuti amumve-re m’malo momvera Mulungu. Kenako Adamu nayenso sanamvereMulungu, ndipo anachita zimene Hava anachita. Zimenezi zinachititsakuti anthu azivutika komanso kufa. D Werengani Genesis 3:1-6,19.

Satana anayamba kugalukira ulamuliro waMulungu kapena kutiudindo wake mongaWam’mwambamwamba, pamene anauza Havakuti asamvere Mulungu. Anthu ambiri m’dzikoli ali kumbali ya Satanandipo akukana kuti Mulungu akhale Wolamulira wawo. Choncho, Sa-tana wakhala “wolamulira wa dziko.” D Werengani Yohane 14:30;1 Yohane 5:19.

2. Kodi zinthu zimene Mulungu analenga n’zimene zinali ndi vuto?Zonse zimene Mulungu amapanga zimakhala zangwiro zokhazokha.

Mwachitsanzo, Mulungu analenga anthu komanso angelo angwiroamene akanatha kumumvera popanda chovuta chilichonse. (Deutero-nomo 32:4, 5) Potilenga, Mulungu anatipatsa ufulu wosankha kuchitachabwino kapena choipa. Ufulu umenewu umatipatsa mwayi wosonye-za chikondi chathu kwaMulungu. D Werengani Yakobo 1:13-15;1 Yohane 5:3.

3. N’chifukwa chiyani Mulungu walolakuti anthu azivutika mpaka pano?

Kwa nthawi yochepa, Yehova walolakuti anthu komanso angelo ena apa-ndukire ufumu wake. Chifukwa chiyaniwachita zimenezi? Iye wachita zimenezikuti anthu aone okha kuti ndi ulamulirowaMulungu wokha umene ungathetsemavuto a anthu. (Mlaliki 7:29; 8:9) Tso-pano padutsa zaka 6,000 anthu akudzi-lamulira okha, ndipo zikuonekeratu kuti

8 N’chifukwa Chiyani MulunguWalola Zinthu Zoipa KomansoKuti Anthu Azivutika?

Mulungu wape-reka nthawiyokwanira yotianthu adzilamulireokha pofuna kuso-nyeza kuti paokha,sangakwanitse ku-thetsamavuto awo

ulamuliro wa anthu walephera kuthetsa nkhondo, uchigawenga, kupa-nda chilungamo, komanso matenda. D Werengani Yeremiya 10:23;Aroma 9:17.

Mosiyana ndi ulamuliro wa anthu, ulamuliro waMulungu uma-thandiza anthu amene ali kumbali yake. (Yesaya 48:17,18) Posache-dwapa Yehova athetsa maboma onse a anthu, ndipo anthu okhawoamene asankha kuti Mulungu aziwalamulira, adzakhala padziko lapa-nsi.—Yesaya 11:9. D Werengani Danieli 2:44.

4. Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kwatipatsa mpata wochitachiyani?

Satana ananena kuti anthu amatumikira Yehova chifukwa cha dyerabasi. Kodi mungakonde kutsutsa bodza limeneli? Mungathe kulitsutsa.Kuleza mtima kwaMulungu kwatipatsa mpata woti tisonyeze ngati ti-makonda ulamuliro waMulungu kapena wa anthu. Zimene timachitapa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku n’zomwe zimasonyeza ulamuliroumene tasankha. D Werengani Yobu 1:8-12; Miyambo 27:11.

5. Kodi tingasankhe bwanji Mulungu kuti akhale Wolamulira wathu?Tingasankhe Mulungu kuti akhale Wolamulira wathu pofufuza

chipembedzo choona n’kumachita zimene chipembedzo choonachochimafuna mogwirizana ndi Mawu aMulungu, Baibulo. (Yohane 4:23)Tingakane Satana kuti akhale wolamulirawathu potengera chitsanzo cha Yesu ameneanapewa kulowerera mu ndale komanso ku-menya nkhondo. D Werengani Yohane17:14.

Satana akugwiritsa ntchito mphamvuzake polimbikitsa anthu kuti azichita chiwe-rewere ndi makhalidwe ena oipa. Tikamape-wa makhalidwe amenewa, anzathu kapenaachibale ena angayambe kutinyoza kapenakutitsutsa. (1 Petulo 4:3, 4) Zikatero tingafunike kusankha zimene tiku-ona kuti n’zabwino. Kodi tidzapitiriza kugwirizana ndi anthu ameneamakondaMulungu? Kodi tidzamvera malamulo ake anzeru, amene-nso amasonyeza mmene amatikondera? Ngati titachita zimenezi, tidza-sonyeza kuti Satana ananama ponena kuti munthu aliyense sangamvereMulungu pamene akukumana ndi mavuto. D Werengani 1 Akorinto6:9,10; 15:33.

Mulungu amakonda kwambiri anthu, ndipo umenewu ndi umboniwakuti adzathetsa mavuto komanso zinthu zonse zoipa. Choncho aliye-nse amene amakhulupirira zimenezi, adzasangalala ndi moyo wosathapadziko lapansi kwamuyaya. D Werengani Yohane 3:16.

Zimenetimasankha kuchitazimasonyeza ngati

tikufuna kutiMulungu akhale

Wolamulira wathukapena ayi

Kuti mumve zambiri, werengani mutu 11 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

17

18

1. Kodi kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza bwanjikuti banja likhale losangalala?

Yehova, Mulungu wachimwemwe, amafuna kuti mabanjaazikhala osangalala, ndipo umenewu ndi uthenga wabwino. (1 Ti-moteyo 1:11) Iye ndi amene anayambitsa ukwati. Kukwatirana mo-tsatira malamulo kumathandiza kuti banja likhale losangalala chi-fukwa chakuti limakhala malo abwino olereramo ana. ChonchoAkhristu ayenera kulemekeza malamulo a boma okhudza kulembe-tsa ukwati. D Werengani Luka 2:1, 4, 5.

Kodi Mulungu amaona bwanji ukwati? Mulungu amafuna kutimwamuna ndi mkazi okwatirana azikhala limodzi moyo wawo wo-nse. Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi amene ali pabanja,onse azikhala okhulupirika m’banjamo. (Aheberi 13:4) Iye amada-na ndi kuthetsa ukwati. (Malaki 2:16) Komabe amalola kuti Mkhri-stu athetse ukwati wake n’kukwatirana ndi munthu wina ngatimnzake m’banjamo wachita chigololo. D Werengani Mateyu19:3-6, 9.

2. Kodi mwamuna ndi mkazi wake ayenera kumakhala motani?Yehova analenga mwamuna ndi mkazi kuti azithandizana m’ba-

nja. (Genesis 2:18) Mwamuna, yemwe ndi mutu wa banja, ali ndiudindo waukulu wopezera banja lake zinthu zofunika komanso ku-liphunzitsa zokhudza Mulungu. Mwamuna ayenera kusonyeza chi-kondi chololera kuvutikira mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi wakeayenera kukondana kwambiri komanso kulemekezana. Popeza kutionse, mwamuna ndi mkazi, ndi anthu opanda ungwiro, ayenerakuphunzira kukhululukirana ndipo zimenezi zidzawathandiza kutiazikhala osangalala m’banja. D Werengani Aefeso 4:31, 32; 5:22-25, 33; 1 Petulo 3:7.

3. Ngati banja silikuyenda bwino, kodi ndi bwinokungolithawa?

Ngati mukuona kuti m’banja mwanu muli mavuto, aliyense wainu ayesetse kusonyeza mnzake chikondi. (1 Akorinto 13:4, 5)

9 Kodi Mungatani Kuti BanjaLanu Likhale Losangalala?

Mawu aMulungu salimbikitsa anthu okwatirana kuti azipatukanan’cholinga chothana ndi mavuto am’banja mwawo. D Were-ngani 1 Akorinto 7:10-13.

4. Ananu, kodi Mulungu amafuna kuti muzichita chiyani?Yehova amafuna kuti ananumuzikhala osangalala. Iye wakupa-

tsani malangizo abwino kwambiri okuthandizani kuti muzisangala-la pamene muli achinyamata. Mulungu akufuna kuti mupindulendi nzeru za makolo anu komanso zinthu zimene iwowo akumananazo pamoyo. (Akolose 3:20) Yehova, yemwe ndi Mlengi wanu,akufunanso kuti muzisangalala pochita zinthu zimene iye komansoMwana wake akufuna. D Werengani Mlaliki 11:9–12:1; Mateyu19:13-15; 21:15,16.

5. Inu makolo, kodi mungatani kuti ana anu azikhalaosangalala?

Muyenera kuyesetsa kuwapezera chakudya, pokhala ndiponsozovala. (1 Timoteyo 5:8) Koma kuti ana anuwo azikhala osangala-la, muyeneranso kuwaphunzitsa kukondaMulungu ndiponso kute-ngera chitsanzo chake. (Aefeso 6:4) Ngati inuyo mumakondaMu-lungu, chitsanzo chanu chidzathandiza kwambiri ana anu kutinawonso azikonda kwambiri Mulungu. Mukamalangiza ana anupogwiritsa ntchitoMawu aMulungu, mungawathandize kwambirianawo kuti aziona zinthu moyenera. D Werengani Deuterono-mo 6:4-7; Miyambo 22:6.

Zimakhala zothandiza kwambiri kwa anamukamawalimbikitsakomanso kuwayamikira. Koma akalakwitsa amafunika kuwapatsachilango kapena kuwadzudzula. Zimenezi zingathandize kuti ana-wo azipewamakhalidwe omwe angachititse kuti azikhala osasa-ngalala. (Miyambo 22:15) Komabe, si bwino kupatsa mwanachilango chokhwima kwambiri kapena kumulangamwankhanza.D Werengani Akolose 3:21.

AMboni za Yehova ali ndi mabuku osiyanasiyana omwe choli-nga chake n’kuthandiza makolo komanso ana. Mfundo za m’ma-buku amenewa ndi zochokera m’Baibulo. D Werengani Salimo19:7,11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

19

1. Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?

Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chokha, ndipootsatira ake anali m’chipembedzo chimenecho. Chipembedzocho chilingati msewu womwe ukulowera ku moyo wosatha. Ponena za msewuumenewu, Yesu ananena kuti: “Amene akuupeza ndi anthu owerenge-ka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomereza anthu okhawo amene aku-mulambira mogwirizana ndi mfundo zochokera m’Mawu ake Baibu-lo, omwe ndi choonadi. Anthu onse omwe ndi olambira oonaamakhulupirira zinthu zofanana. D Werengani Yohane 4:23, 24;14:6; Aefeso 4:4, 5.

2. Kodi Yesu ananena chiyanichokhudza Akhristu onyenga?

Yesu anachenjeza kuti aneneri onye-nga adzayamba kuphunzitsa zinthu zabodza pakati pa Akhristu. Pa-maso chabe, aneneri onyenga amenewa amaoneka ngati amalambiraMulungu m’njira yoyenera. Komanso amanena kuti zipembedzo zawondi zachikhristu. Komabe, munthu angathe kuwazindikira kuti siAkhristu oona. Kodi angawazindikire bwanji? Angawazindikire chifu-kwa chakuti ndi chipembedzo choona chokha chimene anthu ake ndiAkhristu enieni ndipo makhalidwe awo komanso zochita zawo zima-khala zabwino. D Werengani Mateyu 7:13-23.

3. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mudziwe olambira oona?

Taonani zinthu zisanu zomwe ndi zizindikiro za olambira oona aMulungu:

˛ Olambira oona amalemekeza Baibulo monga Mawu a Mulu-ngu. Iwo amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo.

Choncho chipembedzo choona chima-siyana ndi chipembedzo chimene chi-mayendera maganizo a anthu. (Mateyu15:7-9) Komanso olambira oona sa-mangophunzitsa chabe koma amaye-setsa kuchita zinthu mogwirizana ndi

10 Kodi Chipembedzo ChoonaMungachidziwe Bwanji?

“Chenjerani ndianeneri onyenga.”—MATEYU 7:15.

“Amanena poyerakuti amadziwaMulungu, komaamamukana ndizochita zawo.”—TITO 1:16.

zimene amaphunzitsazo. D Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo3:16,17.

˛ Otsatira a Yesu enieni amalemekeza dzina laMulungu lakutiYehova. Yesu analemekeza dzina laMulungu polidziwikitsa kwa anthuena. Iye anathandiza anthu ena kudziwaMulungu komanso anawa-phunzitsa kupemphera kuti dzina laMulungu liyeretsedwe. (Mateyu6:9)M’dera limene mukukhala, kodi ndi chipembedzo chiti chomwechimauza anthu ena za dzina laMulungu? D Werengani Yohane17:26; Aroma 10:13,14.

˛ Akhristu enieni amalalikira za Ufumu waMulungu.Mulunguanatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzalalikire uthenga wabwino waUfumu. Tsogolo la anthu likudalira pa Ufumu waMulungu wokhawomwe udzabweretse madalitso ambiri. Yesu ankauza anthu za Ufu-mu umenewumpaka pa tsiku la imfa yake. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye ananenanso kuti otsatira ake azilalikira za Ufumuwo. Ndi-yeno kodi munthu wina atakupezani n’kumakuuzani za Ufumu waMulungu, mungaganize kuti munthu ameneyu ndi wachipembedzochiti? D Werengani Mateyu 24:14.

˛ Otsatira a Yesu sali mbali ya dziko loipali.Otsatira a Yesu mu-ngawadziwe chifukwa chakuti iwo salowerera nkhani zandale kapenamikangano imene imachitika m’madera amene iwo akukhala. (Yohane17:16; 18:36) Komanso samatengera makhalidwe ndi maganizo oipaam’dzikoli. D Werengani Yakobo 4:4.

˛ Akhristu enieni amakondana kuchokera pansi pa mtima. Iwoamaphunzira m’Mawu aMulungu kuti ayenera kulemekeza anthu amitundu yonse. Ngakhale kuti zipembedzo zonyenga zakhala zikulo-werera nkhondomayiko osiyanasiyana akamamenyana, olambiraoona amakana kuchita zimenezi. (Mika 4:1-3)M’malomwake, Akhri-stu oona amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chumachawo kuti athandize ena komanso kuwalimbikitsa. D WerenganiYohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20.

4. Kodi tsopano mwachidziwa chipembedzo choona?Kodi ndi chipembedzo chiti chomwemfundo zake zonse zimacho-

kera m’Mawu aMulungu, chimalemekeza dzina laMulungu komansochimalalikira zoti ndi Ufumu waMulungu wokha womwe ungabwere-tse madalitso kwa a anthu padziko lapansi? Kodi ndi gulu liti la anthulomwe limakondana kuchokera pansi pa mtima komanso lomwe li-makana kumenya nkhondo? Tikukhulupirira kuti mwalidziwa tsopa-no. D Werengani 1 Yohane 3:10-12.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

21

1. N’chifukwa chiyani timafunikira malangizo?Mlengi wathu ndi wanzeru kwambiri kuposa ifeyo. Popeza kuti

iye ndi Atate wachikondi, amatisamalira. Komanso sanatilenge kutitizidzilamulira tokha. (Yeremiya 10:23) Mofanana ndi mwana wa-mng’ono yemwe amadalira makolo ake kuti azimuuza zochita, to-nsefe timafunika kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Yesaya 48:17,18)Choncho mfundo za m’Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulu-ngu. D Werengani 2 Timoteyo 3:16.

Malamulo a Yehova ndi othandiza kwa ife. Malamulowa amati-phunzitsa zimene tiyenera kuchita kuti tizikhala osangalala koma-nso zimene tingachite kuti tidzapeze madalitso osatha m’tsogolo.Choncho popeza Mulungu ndi amene anatilenga tiyenera kumu-mvera nthawi zonse. D Werengani Salimo 19:7,11; Chivumbu-lutso 4:11.

2. Kodi mfundo za m’Baibulo n’zosiyana bwanji ndimalamulo?

Nthawi zambiri, malamulo amagwira ntchito pa nthawiinayake kapena pa zochitika zinazake. (Deuteronomo 22:8) Mfu-ndo za m’Baibulo ndi mfundo za choonadi zofunika kwambiri zi-mene sizisintha. Ndipotu malamulo ambiri a Mulungu amachoke-ra pa mfundo za m’Baibulo. Timafunika kugwiritsa ntchito lusolathu la kuganiza kuti timvetse bwino mfundo zimenezi ndi kuzigwi-ritsa ntchito pa moyo wathu. (Miyambo 2:10-12) Mwachitsanzo,m’Baibulo timapezamo mfundo yoti moyo ndi mphatso yochokerakwa Mulungu. Kuganizira mfundo imeneyi kungatithandize kuti ti-zichita zinthu zotithandiza kupewa ngozi tikakhala kuntchito, ku-nyumba kapena m’galimoto. D Werengani Machitidwe 17:28.

3. Kodi ndi mfundo ziwiri ziti zam’Baibulo zomwe ndi zofunikakwambiri?

Yesu anatchula malamulo awiria Mulungu ndipo m’malamuloamenewa timapezamo mfundo zo-

11 Kodi Timapindula Bwanjindi Mfundo za M’Baibulo?

Kodi mfundo zam’Baibulo zingati-thandize bwanjikupewa ngozi?—SALIMO 36:9.

funika kwambiri. Lamulo loyamba limasonyeza cholinga chachiku-lu pamoyo wamunthu, chomwe ndi kudziwaMulungu ndi kumu-tumikira mokhulupirika. Tiyenera kugwiritsa ntchito mfundoyoyamba imeneyi nthawi zonse tikafuna kusankha zochita pamoyowathu. (Miyambo 3:6) Aliyense amene amagwiritsa ntchito mfu-ndo imeneyi amakhala pa ubwenzi ndi Mulungu, amakhala wosa-ngalala komanso adzapeza moyo wosatha. D Werengani Mate-yu 22:36-38.

Lamulo lachiwiri lilinso ndi mfundo zothandiza kuti tizitha ku-khala bwino ndi anzathu. (1 Akorinto 13:4-7) Munthu angasonye-ze kuti akugwiritsira ntchito mfundo imeneyi potsanzira mmeneMulungu amachitira zinthu ndi anthu. D Werengani Mateyu7:12; 22:39, 40.

4. Kodi timapindula bwanji ndi mfundo za m’Baibulo?Mfundo za m’Baibulo zimathandiza kuti mabanja akhale ogwi-

rizana komanso kuti anthu m’banjamo azikondana. (Akolose 3:12-14)Mawu aMulungu amatetezanso mabanja chifukwa amanenakuti anthu akakwatirana ayenera kukhala limodzi moyo wawo wo-nse. D Werengani Genesis 2:24.

Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zinthu zingatiyendere bwi-no komanso tingapewe kuvutika maganizo. Mwachitsanzo, ma-bwana akafuna kulemba anthu ntchito, amafuna anthu ameneamatsatira mfundo za m’Baibulo, monga kuonamtima komansokulimbikira ntchito. (Miyambo 10:4, 26; Aheberi 13:18) Mawu aMulungu amatiphunzitsanso kuti tiyenera kukhala okhutira ndi zi-mene tili nazo komanso kuona kuti ubwenzi wathu ndi Mulungundi wofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi. D WerenganiMateyu 6:24, 25, 33; 1 Timoteyo 6:8-10.

Mfundo zopezeka m’Malemba zingatithandizenso kuti tikhalendi thanzi labwino. (Miyambo 14:30; 22:24, 25) Mwachitsanzo,lamulo laMulungu loletsa kuledzera limatiteteza kuti tisadwalematenda oopsa komanso kuti tisachite ngozi. (Miyambo 23:20,29, 30) Yehova saletsa anthu kumwamowa pang’ono, koma safu-na kuti aziledzera. (Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10)Mfundo zaMulungu zimatithandiza kupewamakhalidwe ndi maganizo oipa.(Salimo 119:97-100) Koma sikuti Akhristu oona amatsatiramfundo zaMulungu pongofuna kuti zinthu ziwayendere bwino.Iwo amachita zimenezi chifukwa chakuti amalemekeza Yehova.D Werengani Mateyu 5:14-16.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 12 ndi 13 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

23

24

1. Kodi Mulungu amamvetsera mapemphero onse?

Mulungu akuuza anthu amitundu yonse kuti amuyandikirekudzera m’pemphero. (Salimo 65:2) Komabe sikuti iye ama-mvetsera kapena kuyankha mapemphero onse. Mwachitsa-nzo, mapemphero a mwamuna amene amachitira nkhanzamkazi wake angatsekerezedwe. (1 Petulo 3:7) Komanso pame-ne Aisiraeli ankapitirizabe kuchita zinthu zoipa, Mulungu ana-kana kumva mapemphero awo. Kunena zoona, ndi mwayi wa-ukulu kwambiri kulankhula ndi Mulungu m’pemphero.Ndipotu Mulungu amamva mapemphero, ngakhale a munthuamene wachita tchimo lalikulu, ngati munthuyo walapa.D Werengani Yesaya 1:15; 55:7.

2. Kodi tiyenera kupemphera motani?

Pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu. Choncho tiye-nera kupemphera kwa Yehova yekha, yemwe ndi Mlengi wa-thu. (Mateyu 4:10; 6:9) Komanso tikudziwa kuti ndife opa-nda ungwiro, choncho tiyenera kupemphera m’dzina la Yesupopeza kuti iye anatifera chifukwa cha machimo athu. (Yo-hane 14:6) Yehova safuna kuti tizingobwereza mapempheroamene tinawaloweza kapena amene analembedwa penapa-ke. Iye amafuna kuti tizipemphera kuchokera pansi pa mti-ma. D Werengani Mateyu 6:7; Afilipi 4:6, 7.

Mlengi wathu amamva ngakhale mapemphero a mumti-ma. (1 Samueli 1:12,13) Iye amafuna kuti tizipempheranthawi zonse. Mwachitsanzo, tingapemphere pogona, po-dzuka, tisanayambe kudya chakudya, kapena pamene taku-mana ndi mavuto. D Werengani Salimo 55:22; Mateyu15:36.

12 Kodi Mungatani KutiMuyandikire Mulungu?

3. N’chifukwa chiyani Akhristu amasonkhana pamodzi?Kuyandikira Mulungu si chinthu chophweka chifukwa choti

m’dziko limene tikukhalamoli muli anthu omwe sakhulupiriraMulungu ndipo amanyoza lonjezo lake loti padziko lapansipadzakhala mtendere. (2 Timoteyo 3:1, 4; 2 Petulo 3:3,13)Choncho timafunika kusonkhana ndi abale athu kuti tizilimbi-kitsana. D Werengani Aheberi 10:24, 25.

Kucheza ndi anthu okondaMulungu kumatithandiza kutitimuyandikire. Misonkhano yaMboni za Yehova imatipatsamwayi woti tilimbikitsidwe ndi chikhulupiriro chimene anza-thu ali nacho. D Werengani Aroma 1:11,12.

4. Kodi mungatani kuti muyandikire Mulungu?Kuganizira mozama zimene mwaphunzira kuchokera

m’Mawu aMulungu kungakuthandizeni kuti muyandikire Ye-hova. Muyenera kuganiziranso zimene iye wachita, malangizoamene wapereka komanso malonjezo ake. Kupemphera ko-manso kuganizira zimenezi mozama, kungakuthandizeni kutimuziyamikira kuchokera pansi pa mtima chikondi chaMulu-ngu komanso nzeru zake. D Werengani Yoswa 1:8; Salimo1:1-3.

Munthu angayandikire Mulungu pokhapokha ngati ama-mudalira komanso kumukhulupirira. Komabe chikhulupirirochimafunika kuchilimbitsa nthawi zonse. Choncho muzichili-mbitsa nthawi zonse poganizira zifukwa zimene zimakuchiti-tsani kuvomereza zimene mumaphunzira. D WerenganiMateyu 4:4; Aheberi 11:1, 6.

5. Kodi kuyandikira Mulungu kungakuthandizeni bwanji?Yehova amakonda anthu omwe amamukonda. Iye anga-

wateteze ku chinthu chilichonse chomwe chingawononge chi-khulupiriro chawo komanso chiyembekezo chawo cha moyowosatha. (Salimo 91:1, 2, 7-10) Komanso amatichenjeza kutitisamachite zinthu zomwe zingawononge thanzi lathu koma-nso zomwe zingatibweretsere mavuto. Yehova amatiphunzitsakuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. D Were-ngani Salimo 73:27, 28; Yakobo 4:4, 8.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

25

26

1. Kodi zipembedzo zonse n’zabwino?M’zipembedzo zonse mumapezeka anthu ena oona mtima.

Uthenga wabwino ndi wakuti Mulungu amaona anthu oterowondipo amawakonda. Komabe, chomvetsa chisoni n’chakutianthu akugwiritsa ntchito chipembedzo pochita zinthu zoipa.(2 Akorinto 4:3, 4; 11:13-15)Mogwirizana ndi zimene malipotiena amanena, zipembedzo zina zafika poyamba kuchita nawozauchigawenga, kupha anthu ambirimbiri nthawi imodzi, kulo-werera nkhondo komanso kuchitira ana nkhanza. Zimenezi zi-makhumudwitsa kwambiri anthu amene amakhulupirira Mulu-ngu moona mtima. D Werengani Mateyu 24:3-5,11,12.

Pamene chipembedzo choona chikulemekeza Mulungu, chi-pembedzo chonyenga chikuchita zinthu zosamusangalatsa. Chi-pembedzo chonyenga chimaphunzitsa mfundo zosachokeram’Baibulo, monga ziphunzitso zabodza zokhudza Mulungu ndi-ponso zimene zimachitika munthu akafa. Koma Yehova akufunakuti anthu adziwe zoona zokhudza iyeyo. D Werengani Ezeki-eli 18:4; 1 Timoteyo 2:3-5.

2. Kodi pali uthenga wabwino wotani wokhudzazipembedzo?

Mulungu sapusitsidwa ndi zipembedzo zomwe zimanena kutizimamukonda pamene kwenikweni zimakonda dziko la Satanali.(Yakobo 4:4)Mawu aMulungu amanena kuti zipembedzo zo-nse zonyenga zimatchedwa “BabuloWamkulu.” Dzina limenelilinachokera pa dzina la mzinda wakale wa Babulo, kumene chi-pembedzo chonyenga chinayambira pambuyo pa Chigumulacha m’nthawi ya Nowa. Posachedwapa, Mulungu awononga zi-pembedzo zonyenga zomwenso zimachitira anthu nkhanza.D Werengani Chivumbulutso 17:1, 2, 5,16,17; 18:8.

Palinso uthenga wina wabwino. Yehova sanaiwale anthuoona mtima amene ali m’zipembedzo zonyenga padziko lonse,omwe akufunitsitsa kumulambira. Iye akugwirizanitsa anthu

13 Kodi Pali UthengaWabwino Wotani WokhudzaZipembedzo?

amenewa powaphunzitsa choonadi. D Werengani Mika 4:2, 5.

3. Kodi anthu amene akufunadi kulambira Mulungu woonaayenera kuchita chiyani?

Yehova amakonda anthu amene amakonda choonadi koma-nso amene amakonda zinthu zabwino. Iye akuwalimbikitsa kutiachoke m’chipembedzo chonyenga. Anthu amene amakondaMulungu akusinthadi mofunitsitsa kuti akondweretse Mulungu-yo. D Werengani Chivumbulutso 18:4.

Mu nthawi ya atumwi, anthu a mitima yabwino anasangalalakwambiri atamva uthenga wabwino womwe atumwiwo ankala-likira. Iwo anaphunzira zinthu zatsopano kuchokera kwa Yeho-va, n’kuyamba kukhala ndi moyo wosangalala komanso ali ndichiyembekezo chabwino. Anthu amenewa ndi chitsanzo cha-bwino kwa ife masiku ano chifukwa anamvera uthenga wabwi-no ndipo anachita zimenezi posonyeza kuti kumvera Yehova ndichinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo. D Werengani1 Atesalonika 1:8, 9; 2:13.

Yehova akulandira anthu onse amene achoka kuchipembe-dzo chonyenga kuti akhale limodzi ndi anthu amene amamula-mbira. Mukamvera Yehova n’kubwera m’gulu lake, mudzakhalanaye pa ubwenzi, mudzapeza anthu okukondani omwemuzi-dzalambira nawo Yehova komanso mudzapeza moyo wosatha.D Werengani Maliko 10:29, 30; 2 Akorinto 6:17,18.

4. Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti padziko lonse anthuakhale osangalala?

Zoti chipembedzo chonyenga chiwonongedwa posachedwa-pa ndi uthenga wabwino. Zimenezi zidzachititsa kuti anthu asa-maponderezedwenso padziko lonse. Ndipo chipembedzo cho-nyenga sichidzasocheretsa anthu komanso kuwagawanitsa.Anthu onse adzagwirizana polambira Mulungu woona mmodzi.D Werengani Chivumbulutso 18:20, 21; 21:3, 4.

Chipembedzochoona chikugwiri-

zanitsa anthu

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 ndi 16, m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

27

28

1. N’chifukwa chiyani Mulungu anakonza zoti Aisiraeli akaleakhale gulu la anthu ake?

Mulungu anakonza zoti mbadwa za Abulahamu zikhale mtunduwaukulu wa anthu ndipo anawapatsa malamulo osiyanasiyana.Mtunduwo anaupatsa dzina lakuti “Isiraeli” ndipo anausankha kutiuzimulambira m’njira yovomerezeka ndiponso kuti uzitsatira mawuake. (Salimo 147:19, 20) Ndipo anthu ena ochokera m’mitundu yo-nse akanatha kupeza madalitso kuchokera mumtundu wa Isiraeli.D Werengani Genesis 22:18.

Mulungu anasankha Aisiraeli kuti akhale mboni zake. Mbiri yawoyakale imasonyeza bwino mfundo yakuti, zinthu zimawayendera bwi-no anthu akamamvera malamulo a Mulungu. (Deuteronomo 4:6)Motero kudzera mwa Aisiraeli, anthu enanso anali ndi mwayi wodzi-wa Mulungu woona. D Werengani Yesaya 43:10,12.

2. N’chifukwa chiyani Akhristu enieni ndi gulu lochita zinthumwadongosolo?

Patapita nthawi, Aisiraeli anasiya kumvera Mulungu ndipo iye ana-siyanso kuwakonda. Choncho, Yehova anakonza zoti pakhale mpingowachikhristu womwe unawalowa m’malo. (Mateyu 21:43; 23:37, 38)Masiku ano, m’malo mwa Aisiraeli, Akhristu oona amatumikira Yeho-va monga mboni zake. D Werengani Machitidwe 15:14,17.

Yesu anakonza zoti otsatira ake akhale gulu limene lizilalikira ndikuphunzitsa anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira ake. (Ma-teyu 10:7,11; 24:14; 28:19, 20) Masiku ano, pamene tili m’nyengo yamapeto a nthawi ino, ntchitoyi ikufika pachimake. Ndipo kwa nthawiyoyamba m’mbiri yonse, Yehova wasankha anthu mamiliyoni ambiriochokera m’mitundu yonse kuti agwirizane n’kukhala olambira akeoona. (Chivumbulutso 7:9,10) Akhristu oona ndi gulu logwirizanandipo anthu ake amalimbikitsana ndiponso amathandizana. Padzikolonse, iwo amakhala ndi pulogalamu yofanana yophunzirira Baibulopamisonkhano yawo. D Werengani Aheberi 10:24, 25.

14 N’chifukwa Chiyani MulunguAli ndi Gulu?

3. Kodi gulu la masiku ano la Mboni za Yehova linayamba bwanji?Gulu la m’nthawi yathu ino laMboni za Yehova linayambam’zaka

za m’ma 1870. Pa nthawiyo, kagulu ka anthu ochepa omwe ankaphu-nzira Baibulo kanatulukira mfundo za m’Baibulo za choonadi zomwezinali zitabisika kwa nthawi yaitali. Anthu am’kaguluko anadziwa zotiYesu anakhazikitsa mpingo wachikhristu monga gulu loti lizilalikira.Choncho iwo anayamba ntchito yapadera yolalikira za Ufumu padzi-ko lonse. Mu 1931, iwo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova.D Werengani Machitidwe 1:8; 2:1, 4; 5:42.

4. Kodi gulu la Mboni za Yehova limayenda bwanji?M’nthawi ya atumwi, mipingo yachikhristu yomwe inali m’mayiko

ambiri inkapindula ndi malangizo ochokera ku bungwe lolamulira li-mene linkachita zinthu mozindikira kuti Yesu ndi Mutu wampingo.(Machitidwe 16:4, 5)Masiku anonso anthu aMboni za Yehova padzi-ko lonse amapindula ndi malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira,lomwe lapangidwa ndi akulu amene akhala akutumikiraMulungukwa nthawi yaitali. Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito imeneikuchitika m’maofesi a nthambi aMboni za Yehova. Anthu omweakutumikira m’maofesi amenewa amagwira ntchito monga yomasuli-ra mabuku ophunzirira Baibulo, kuwasindikiza ndiponso kuwatumizam’mipingo yosiyanasiyana, ndipo mabuku amenewa akumasuliridwam’zinenero zoposa 600. Choncho, ntchito imeneyi imathandiza kutiBungwe Lolamulira lizitha kulimbikitsa ndiponso kupereka malangizoa m’Malemba kumipingo yoposa 100,000 padziko lonse. Ndipo mu-mpingo uliwonse, amuna oyenerera amatumikira monga akulu kape-na kuti oyang’anira. Amuna amenewa amasamalira nkhosa zaMulu-ngu mwachikondi. D Werengani 1 Petulo 5:2, 3.

Mboni za Yehova ndi gulu limene limalalikira uthenga wabwinondiponso limaphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Mofana-na ndi zimene atumwi ankachita, ifenso timalalikira kunyumba ndinyumba. (Machitidwe 20:20) Komanso timadzipereka kuphunziraBaibulo ndi anthu amene amakonda choonadi. Komatu ife aMboniza Yehova sikuti tangokhala gulu basi. Ndife banja ndipo Atate wathundi wachikondi. Ndife abale ndi alongo amene timakondanandi kusamalirana. (2 Atesalonika 1:3) Popeza anthu a Ye-hova ndi gulu limene limachita zinthu zokondweretsaMulungu ndiponso limathandiza ena, iwo apanga ba-nja losangalala kwambiri padziko lonse. D Were-ngani Salimo 33:12; Machitidwe 20:35.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 19 m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

1. Kodi mungapindule bwanji mukapitiriza kuphunzira Baibulo?

Pofika pano mwaphunzira mfundo zambiri za m’Baibulo ndipomosakayikira, zakuthandizani kuti muyambe kukonda kwambiri Yeho-va. Koma nthawi zonse muyenera kuchita zinthu zothandiza kuti chi-kondicho chizikula. (1 Petulo 2:2) Kuti mudzapeze moyo wosatha zi-kudalira kuti mupitirize kuyandikira Mulungu mwa kuphunzira Mawuake. D Werengani Yohane 17:3; Yuda 21.

Pamene mukupitiriza kudziwa zambiri zokhudza Mulungu, chikhu-lupiriro chanu chidzalimba kwambiri. Ndiyeno chikhulupirirocho chi-dzakuthandizani kuti muzichita zinthu zokondweretsa Mulungu. (Ahe-beri 11:1, 6) Komanso chikhulupiriro chidzakuthandizani kuti mulapen’kusintha moyo wanu. D Werengani Machitidwe 3:19.

2. Kodi mungatani kuti zimene mukudziwa zokhudza Mulunguzithandizenso anthu ena?

Mwachibadwa, mudzafuna kuuza anthu ena zimene mwaphunzira,ndipotu tonsefe timasangalala tikamauza anthu ena uthenga wabwi-no. Pamene mukupitiriza kuphunzira Baibulo, mudzadziwa mmenemungagwiritsire ntchito Baibulo pofotokoza zimene mumakhulupirirazokhudza Yehova ndiponso zokhudza uthenga wabwino. D Were-ngani Aroma 10:13-14.

Anthu ambiri akamayamba kuuza ena uthenga wabwino, amaya-mba ndi kuuza achibale awo kapena anzawo. Koma m’pofunika ku-chita zinthu mwanzeru. M’malo mowauza kuti chipembedzo chawon’cholakwika, auzeni zimene Mulungu walonjeza. Komanso muziku-mbukira kuti kawirikawiri anthu amakopeka kwambiri ndi khalidwelanu la kukoma mtima osati ndi zimene mumalankhula. D Were-ngani 2 Timoteyo 2:24, 25.

3. Kodi mungakhale pa ubwenzi wotani ndi Mulungu?

Kuphunzira Mawu a Mulungu kudzakuthandizani kuti mukulemwauzimu. M’kupita kwa nthawi, mungakhale pa ubwenzi wapaderakwambiri ndi Yehova, ndipo mungafike pokhala m’gulu lake, lomwe lilingati banja. D Werengani 2 Akorinto 6:18.

15N’chifukwa Chiyani MuyeneraKupitiriza Kuphunzira zaYehova?

Mungakhale pa ubwenziwapadera kwambiri ndiYehova

Zimene BaibuloLimaphunzitsa

31

4. Kodi mungatani kuti muphunzire zambiri zokhudza Mulungu?Mukapitiriza kuphunzira Mawu aMulungu, mungakule kwambiri

mwauzimu. (Aheberi 5:13,14) Choncho, pemphani munthu aliyensewaMboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo pogwiritsa ntchitobuku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.Mukamaphunzira kwambiriMawu aMulungu, mudzaona kuti zinthu zizikuyenderani bwino kwa-mbiri pa moyo wanu. D Werengani Salimo 1:1-3; 73:27, 28.

Uthenga wabwino ukuchokera kwa Yehova, yemwe ndi Mulunguwachimwemwe. Mungamuyandikire Mulungu ameneyu ngati munga-yesetse kugwirizana ndi anthu ake. (Aheberi 10:24, 25)Mukamayese-tsa kuchita zonse zimene mungathe kuti musangalatse Yehova, ndiyekuti mukuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kudzapeza moyo we-niweni, womwe ndi moyo wosatha. Choncho, chinthu chabwino zedichomwemungachite n’kuyandikira Mulungu. D Werengani 1 Ti-moteyo 1:11; 6:19.

Bukuli lili m’zinenerozambirimbiri ndipo liku-pezekanso pa Intaneti paadiresi iyi: www.jw.org

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 18, m’buku lakuti,Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

fg-C

N1

80

21

3

KODI NDINKHANI ITI IMENE

IMAKUSANGALATSANIKWAMBIRI?

1 2 3

4 5 6 7

8 9 10 11

12 13 14

Kodi uthengawabwino n’chiyani?

Kodi Mulungundani?

Kodi uthengawabwino ndiwochokeradikwaMulungu?

Kodi Yesu Khristundani?

Kodi Mulungu alindi cholinga chotanichokhudza dzikolapansili?

Kodi palichiyembekezo chotanichokhudza anthuamene anamwalira?

Kodi UfumuwaMulungun’chiyani?

N’chifukwa chiyaniMulungu walolazinthu zoipa komansokuti anthu azivutika?

Kodi mungatanikuti banja lanulikhale losangalala?

Kodi chipembedzochoona mungachidziwebwanji?

Kodi mfundoza M’Baibulozimatithandizabwanji?

Kodi mungatanikuti muyandikireMulungu?

Kodi pali uthengawabwinowotaniwokhudzazipembedzo?

N’chifukwa chiyaniMulungu ali ndigulu?

s