mbiri ya kasindikizidwe ka bukhuli banja la … ndi kuwonetsera chikondi kwa wina ndi mzake. zolinga...

199
> Mbiri ya kasindikizidwe ka Bukhuli Mbiri ya Kasindikizidwe ka Bukhuli Banja La Chisangalalo, lalembedwa ndi ukadaulo wochokera ku Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs ndi chithandizo chochokera ku United States Agency For International Development (USAID). Losindikizidwa ndi: Johns Hopkins University Bloomberg School of Public Health Center for Communication Programs, 2012. Chilolezo Bukhuli likhoza kusindikizidwa popanda chilolezo. Chofunika ndi chakuti bukhu losindikizidwalo ligawidwe kwa anthu mwaulele komanso osindikizawo anene kuti achita izi molumikizana ndi a Johns Hopkins University Bloomberg School of Public Health For Communication Programs. Ndemanga Ndemanga zochokera kwa owerenga bukhuli kapena amene agwiritsako ntchito bukhuli zikhoza kutumizidwa kwa. Glory Mkandawire John Hopkins University Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs BRIDGE II Project P.O. Box 30782 Lilongwe, Malawi Tel: (265) 01 750 733 / 553 Fax: (265) 01 750 496 Email: [email protected] Onse amayiko ena ofuna kupempha chilolezo chokhudzana ndi bukhuli kuti agwiritse ntchito, akhonza kulembera kwa: Director, Strategic Communication Unit Johns Hopkins University Bloomberg School of Public Health Center for Communication Programs 111 Market Place, Suite 310 Baltimore, Maryland 21202 USA Tel: (410) 659 6300 Fax (410) 659 6266 Email: [email protected] Website:http://www.jhuccp.org i

Upload: lylien

Post on 26-Mar-2018

494 views

Category:

Documents


18 download

TRANSCRIPT

> Mbiri ya kasindikizidwe ka Bukhuli

Mbiri ya Kasindikizidwe ka Bukhuli Banja La Chisangalalo, lalembedwa ndi ukadaulo wochokera ku Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health Centre for Communication Programs ndi chithandizo chochokera ku United States Agency For International Development (USAID).

Losindikizidwa ndi: Johns Hopkins University Bloomberg School of Public Health Center for Communication Programs, 2012.

Chilolezo Bukhuli likhoza kusindikizidwa popanda chilolezo. Chofunika ndi chakuti bukhu losindikizidwalo ligawidwe kwa anthu mwaulele komanso osindikizawo anene kuti achita izi molumikizana ndi a Johns Hopkins University Bloomberg School of Public Health For Communication Programs.

Ndemanga Ndemanga zochokera kwa owerenga bukhuli kapena amene agwiritsako ntchito bukhuli zikhoza kutumizidwa kwa.Glory MkandawireJohn Hopkins UniversityBloomberg School of Public Health Centre for Communication ProgramsBRIDGE II ProjectP.O. Box 30782Lilongwe, MalawiTel: (265) 01 750 733 / 553Fax: (265) 01 750 496 Email: [email protected]

Onse amayiko ena ofuna kupempha chilolezo chokhudzana ndi bukhuli kuti agwiritse ntchito, akhonza kulembera kwa:

Director, Strategic Communication Unit Johns Hopkins University Bloomberg School of Public HealthCenter for Communication Programs 111 Market Place, Suite 310 Baltimore, Maryland 21202 USA Tel: (410) 659 6300 Fax (410) 659 6266 Email: [email protected]:http://www.jhuccp.org

i

> 2 Banja la chisangalalo> Mbiri ya kasindikizidwe ka Bukhuli

Mau othokoza

Banja La Chisangalalo, lidalembedwa ndi a Assana Magombo, Jane Brown, Leanne Wolff ndi Glory Mkandawire. Zowonjezela zina za mbukhuli zidalembedwa, ndi mabungwe ena achipembedzo monga: Jessy Puwapuwa (Blantyre Synod Health and Development Commission), Godfrey Mkandawire (Malawi Council of Churches), Ellen Molosi (Evangelical Association of Malawi) Emily Kaimba (Chikwawa Diocese), Mary Ganiza (Arch Diocese), Idah Yusufu (Quadria Muslim Aassociation of Malawi), Shekh Matola (Muslim Aassociation of Malawi), Patrick Kaudzu (Student Christian Organisation of Malawi), Ps. Anderson Mataka (Assemblies of God), Ps. Constance Kadango (Seventh Day Adventist), Ps. Peterson Kamanga(Seventh Day Adventist ), Sheikh Kangomba (Muslim Aassociation of Malawi ), Salome Ziwaya and Dean Alick Msuku (Evangelical Lutheran Development Services), Zione Chimalizeni (Zomba Diocese), ndi Malawi Interfaith Aids Association (MIAA).

Bukhu la Banja La Chisangalalo, linawunikiridwa mu mwezi wa April 2011 ndi cholinga chopereka mwayi kwa achipembedzo osiyanasiyana omwe atchulidwa pamwambapa kuti apereke ndemanga zawo pa bukhuli. Akulu akulu ochokera mu zipembedzo zonsezi nawonso anatengapo mbali powunikila bukhuli. Tikufuna kuthokoza Abusa a Patrick Semphere, omwe anathandiza kulikonza bukhuli ndi kulitanthauzila mu chichewa.

Kuwunika bukhuli komaliza kunachitika ndi a BRIDGE II. Zolembedwa zina zomwe zili m’bukhuli zidatengedwa ku mabukhu otsatirawa; The Total Marriage: A guide to a successful marriage, Jeffrey and Pattiejean Brown (2001), Answers for your Marriage, Bruce and Carol Britten (1995), Happiness for Husbands and Wives, Shyrock H (1970), Planting Our Tree of Hope: A Toolkit on Positive Prevention for People Living with HIV, Basalla, L. and Deutsch B. et al. (2008), Heart to Heart Communication, Vanpelt N. (2008), Communication for Couples, By Nancy Van Pelt (2008). Hand in hand Bible studies to transform our response to HIV, Isabel Carter and Maggie Sandilands- Tearfund (2010), Keys to a Healthy Relationship; A Guide to Reduce HIV Transmission and Strengthen Long-Term Committed Relationships (2007), A Theological Call to Action; A Statement by The International HIV/AIDS Faith Advisory Board of The Balm In Gilead.

Zomwe zalembedwa mbukhuli zidatheka chifukwa cha chithandizo chomwe chidachoka kwa anthu aku America podzela ku bungwe la USAID. Komabe zonse zimene zalembedwa m’bukhuli zinakonzedwa ndi a BRIDGE II Project ndipo sizikuwonetsa maganizo a USAID kapena boma la America.

ii

> Mbiri ya kasindikizidwe ka Bukhuli

> Za mkatimu

Mau othokoza ............................................................................................................... i

Gawo 1: Mau oyambilira ............................................................................................ 1

Gawo 2 – Kagwiritsidwe ntchito ka bukhuli .............................................................. 3

Gawo 3 a: Kuunika uphungu ...................................................................................... 7

Gawo 3 b: Kuunika zofunika ...................................................................................... 7

Gawo 3 c: Kupitiriza uphungu .................................................................................. 13

Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanaga nalo banja ...................................................1

Phunziro 2: Banja - Mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah ...................................2

Phunziro 3: Kulankhulana: Gwero la chisangalalo ......................................................3

Phunziro 4: Kugonana m’banja - Mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah ...............4

Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja.......................................................................5

Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-Kuteteza mwana ku HIV

......................................................................................................................................6

Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana .................................................................................7

Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja .........................................................................8

Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi ...................................9

Kuomba mkota pa bukhuli .........................................................................................12

Zolemba zofotokozera ................................................................................................12

Kodi HIV imafala bwanji? .........................................................................................16

Tanthauzo la kangaude wa zibwenzi ..........................................................................17

Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV..........................................................18

HIV ndi kutenga pathupi ............................................................................................20

Maluso a moyo ...........................................................................................................24

iii

> Banja la chisangalalo 1

> Gawo 1: Mau oyambilira

Takulandirani ku Banja La chisangalalo-bukhu lothandizira a Phungu ndi Atsogoleri a Zipembedzo omwe akugwira ntchito ndi maaanja a Chikhristu komanso a Chisilamu m’madera a m’dziko la Malawi.

Bukhuli lakonzedwa kuti lithandize atsogoleri a zipembedzo omwe apatsidwa udindo wopereka uphungu ku mipingo/mizikiti yawo. Bukhuli ndilothandiza anthu amene ali pa banja ndi iwo amene akuyembekeza kulowa m’banja, kamanga maziko olimba achiyanjano chawo ndi kuonetsetsa kuti HIV isalowe m’nyumba mwao. Mbukhuli mulinso maphunziro othandiza kupereka uphungu kwa maanja omwe m’modzi mwa iwo ali ndi HIV poonetsetsa kuti ali ndi banja la moyo wamphamvu ndi wachikondi.

Mdziko la Malawi, azipembedzo akhala akuchitapo kanthu komanso kutenga gawo lofunika pa ntchito yothandiza kupewa HIV komanso kuthandiza amene ali kale ndi HIV kukhala moyo wabwino. Kupereka uphungu kwa anthu omwe ali pa banja ndi mbali imodzi ya ntchitoyi ndipo mabungwe azipembedzo ali ndi mbali yapadera yopereka uphunguwu. Anthu azipembembedzo ali ndi mwai wokumana pafupipafupi m’mipingo/mizikiti yawo ndi m’magulu ena sabata iliyonse. Misonkhano imeneyi imapereka mwai wopereka ndi kulandira uphungu, anthu amagawana zomwe akukumana nazo pamoyo wawo ndi kulimbikitsana. Atsogoleri a zipembedzo amalemekezedwa kwambiri ndi anthu awo amene amadza kwa iwo kudzalandira malangizo, chitsogozo ndi uphungu pamene asowa kapena kuthedwa nzeru.

Dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko amene ali ndi chiwerengero chachikulu cha anthu amene ali ndi HIV kumwera kwa Africa. Kawirikawiri matendawa amafala m’banja pamene m’modzi kapena onse awiri alowa mbanja popanda kudziwa mmene mthupi mwawo muliri, kapena atuluka mnyumbamo kukapanga zibwenzi kunja. Anthu amatuluka mbanja kukapanga zibwenzi kunja pamene kulumikizana kwasokonekera, chikondi chatha kapena malonjezano omwe anapanga kwa wina ndi mnzake ayiwalika. Cholinga cha bukhuli ndi kuthandiza maanja kulimbitsa maanja awo powakumbutsa kudzipereka kwao kwa Mulungu/Allah ndi kwa wina ndi mnzake ndiponso powapatsa zitsanzo zochitika za momwe angakhalire ndi luso lakulankhulana bwino ndi kuwonetsera chikondi kwa wina ndi mzake.

Zolinga za Bukhuli

Cholinga chachikulu cha bukhuli ndi kupititsa patsogolo ntchito yolimbana ndi HIV yomwe achipembedzo akugwira powapatsa alangizi/aphungu zitsanzo zakupereka uphungu ndi mau a Mulungu kuti athandize anthu a pabanja ndi achinyamata kumanga maanja olimba kuti potero apewe kutenga HIV, kupatsila bwenzi lawo yemwe ali bwino komanso kutenga HIV ya mtundu wina. Zolinga Zina:

• Kupereka chikhulupiriro ndi chilimbikitso kwa anthu amene akukonzekera kulowa m’banja powathandiza kuonetsetsa kuti asankha bwenzi loyenera.

• Kupititsa patsogolo kulumikizana ndi kulimbitsa chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi amene ali pabanja.

> 2 Banja la chisangalalo

• Kutsimikiziraanthuapabanjandiameneakuyembekezakulowam’banjakutichikondi cha Ambuye ndi malamulo Ake, ndi njira imodzi yopewera HIV kulowa mnyumba mwawo.

• Kuthandizaabambondiamayikuganizirandikuchitapokanthupazomweakuyenera kuchita kuti akhale pa banja losangalala.

• KuthandizakulimbitsamaanjamchikhulupilirochaomwaMulungu/Allah(1Yohane 3:1-3; Masalmo. 128:1; Korani 66: 6) kuti akhale olimba, odalirika ndi anthu okhulupirika mchipembedzo chao ndiponso nzika zabwino za dziko lawo.

• KuwasonyezamaanjamomweangatumikireMulungu/Allahmongaanthuapabanja.

• Kuwasonyezamaanjanjirazosiyasiyanazogonjetserakusamvanandikuphunziranjira zothetsera mavuto mwauzimu. (Korani 2:228; Rute 1:15-17; Mateyu. 19.9).

Amene Bukhuli lakonzedweraBukhuli lakonzedwera aphungu ophunzitsidwa kale amene akugwira ntchito mogwirizana ndi zipembedzo pothandiza anthu amene ali pabanja ndi iwo amene akukonzekera kulowa m’banja. Ngakhale bukhuli likuunika mfundo zokhazikika za uphungu, silinakonzedwere kusula aphungu amene sanaphunzitsidwepo pa ntchitoyi.

> Banja la chisangalalo 3

> Gawo 2 – Kagwiritsidwe ntchito ka bukhuli

A. Kugwira Ntchito ndi Maanja ndi magulu

Bukhuli lakonzedwa kuti ligwiritsidwe ntchito pagulu ngakhalenso ndi maanja angapo kapena banja lirilonse palokha palokha. Pogwiratsa ntchito bukhuli ndi banja limodzi palokha, mafunso okambiranawo angathe kusithidwa kuti athandize banjalo kusinkhasinkha mokhudza banja lawo. Pogwira ntchitoyi mwapagulu, mwayi wosinkhasinkha mwamtunduwu ungakhalepo kudzera mumafunso apadera pamapeto a zochitikazi.

Phunziro lirilonse la bukhuli likuwonjezera pa phunziro la pambuyo pake kotero kuti maphunzirowa akuyenera kutsatidwa mundondomeko yomwe yalembedwera; komabe aphungu angathe kusankha maphunziro kapena ntchito malinga ndi momwe akuonera, kugwirizana kwa maphunzirowo ndi anthu amene akulandira uphunguwu. Bukhu lonseli lingathe kugwiritsidwa ntchito mosiyanasiyana – mwachitsanzo, Phunziro lirilonse lingathe kuphunzitsidwa kwa theka la ola limodzi, patsiku kapena kamodzi pa sabata kwa sabata zisanu ndi zinai, kapenanso mulimonse momwe phungu akuonera.

Pogwira ntchitoyi m’magulu, ndibwino kwambiri kupanga magulu ang’ono bwino kuti aliyense akhale ndi mwayi wotenga nawo mbali. Makamaka maguluwa akhale ndi anthu osapitilira 24 (maanja 12) komanso akhoza kukhala anayi (maanja awiri).

Bukhuli ndi lofunika kwambiri panthawi yokambirana ndi anthu omwe akhala zaka zosiyanasiyana mbanja, kuphatikizapo omwe ali pa chitomelo, angolowa kumene m’banja, kapena amene akhala limodzi kwa zaka zambiri. Lingathe kugwiritsidwa ntchito popereka uphungu kwa maanja amene akukumana ndi mavuto, amene akufuna kulimbitsa ubale wawo, kapena akufuna kukhala chifupi ndi Mulungu/Allah.

B. Ndondomeko ya Zokambirana

Pali mitu isanu ndi inai m’bukhuli Maphunziro onse ali mu mndandanda wotsatirawu:• Mutuwaphunzilo• Phunzilomwachidule• Ntchitoyotsogoleraphunziro• Ntchitozamuphunziro• Kumalizandikutsekazokambirana• Ntchitoyakunyumba• Malemba

C. Njira ZophunziliraBukhuli likugwiritsa ntchito njira zosiyansiyana zimene zimapereka mpata kwa maanja kunena zakukhosi kwao. Njirazi zikuphatikizapo zokambirana za m’magulu, kufufuza njira, kuchita timwasewero, zokambirana za m’magulu ang’onoang’ono, masewero ndi nthano. ake. “Ndiuzeni momwe zokambiranazi zakukhudzirani?” ndi funso lina lofuna kufotokozera.

> 4 Banja la chisangalalo

Phindu lolimbikitsa kutenga mbali ndi iri: 1. Zimalimbikitsa luso loganiza modekha; 2. Ophunzira amatha kukumbukira ndi kugawana zinthu zachilendo; 3. Zimaonjezera chilimbikitso; 4. Zimaonjezera luntha lokambirana.

Njira Zakutenga Mbali

Kuchangamutsana: Alangizi angathe kuwatsogolera maanja mu zochitika zomwe zingathe kuwachangamutsa kapena kuwadzutsa. Izi zingathandize kuti maanja asangalale, amasuke, komanso apatsane moni/adziwane. Zochitikazi zingathe kukhala korasi, nyimbo ya mbukhu kapena kuchokera kwa gulu loyimba. Mlangizi akuyeneranso kuwafunsa maanja ngati ali ndi njira zina zochangamutsila kapena kudzutsila gulu kapena angathe kungowawuza maanja kuti ayendeyende apatsane moni wina ndi mzake.

Kukambirana mwakuya: Uku ndi kufufuza mfundo zofunikila ndipo ndi njira yothandizila kuyambitsa zokambirana. Nthawi yomwe anthu akukambilana mwakuya, sipafunika kuti wina aweruze kapena kunyoza yankho lomwe wina wapereka. Kukambilana mwakuyaku kumathandiza anthu kuganiza kwambiri zokhuza mfundo zosiyanasiyana ndi kuliwona phunzilo mu njira ina.

Kukambirana kwa Magulu: kukambirana kwa magulu kumadzetsa mayankho kuchokera kwa aliyense pa mutu wokambidwawo ndipo kumapereka mpata kwa phungu wodziwa zambiri kapena kukonza zimene anthu anamva molakwika. Kukambilana mmagulu kumathandizanso kuti anthu okambiranawo athe kuwona momwe iwo amaganizila. Kukambirana kwa magulu kumathandiza amene amachita manyazi kulankhula pagulu lalikulu kuti athe kulankhulapo pa zokambiranazo. Ubwino wa kukambirana kwa magulu wagona pakugwiritsa ntchito mafunso amene amafuna kuti munthu afotokoze osati kungoti ‘’Eeh’’ kapena ‘’Ayi’’. Mafunso oterewa amathandiza kutulutsa zakukhosi kapena maganizo ena okhudza mutu wokambirana kapena zochitika.

Chitsanzo:1. “Mwaphunzirapo chiyani pa zomwe tachitazi?” ndi funso lofuna kufotokoza chifukwa likufunsa munthu kuti agawane ndi anzake maganizo ake. “Ndiuzeni momwe zokambiranazi zakukhudzirani?” ndi funso lina lofuna kufotokozera.2. “Mwaphunzirapo kalikonse?” si funso lofuna kufotokozera, chifukwa munthu angathe kungoyankha ‘’eeh’’ kapena ‘’ayi’’. “Zikumveka bwinobwino?” ilinso si funso lofuna kufotokozera. Njira ina yotsimikizira ubwino wa kukambira m’magulu ndi kuonetsetsa kuti aliyense amve kuti maganizo ake akuvomerezedwa ndi gululo. Anthu angathe kukambapo ngati akudziwa kuti saweruzidwa kapena kudzudzulidwa kamba kolankhula zakukhosi kwao kapena ngati aona kuti ena akuganiza monga momwe iwo akuganizira. Iwo amene akutsogolera maguluwa aonetsetse kuti sakulankhula kwambiri koposa ena onse pazokambirana koma kuti aliyense alimbikitsidwe kutenga nawo mbali.

Magulu ang’onoang’ono okambirana: Awa ndi magulu a anthu ochepa; anthu awiri kapena nayi pagulu lilonse. Nthawi imeneyi anthu amakambirana pa mutuwo mwa kanthawi kochepa ndipo amafunsidwa kupereka mayankho awiri kufikira asanu,m’malo mopereka zonse zomwe akambirana.

> Banja la chisangalalo 5

Masewero:iyi ndi njira ya pamwamba yoyesera kugwiritsa ntchito nzeru mothandizidwa. Popeza kuti kuyerekeza kutenga mbali kumatha kukhumudwitsa maganizo athu, nkofunika kuti Phungu alimbikitse anthu kuzindikira kuti ndizongoyerekeza chabe. Nkofunika kuti Phungu alimbikitse anthu kuyerekeza zimene zimachitika pa moyo weniweni osati nthano chabe. Kuyerekeza kutenga mbali kumapereka mwayi wakumva za moyo weniweni popanda kukumana ndi zovuta za moyo weniweniwo.

Ngati athu akukayikira kutenga mbali yoyerekeza, aphungu angathe kupanga iwo eni mothandizidwa ndi m’modzi kapena awiri ena odzipereka ndipo awafunse anthu enawo kuti apereke nzeru za zimene ayenera kuchita panthawi ya sewerolo. Nkofunika kutsindika kuti kutenga mbali yoyerekeza ndi mwai kwa anthuwo woyeserera nzeru zawo pamalo otetezedwa asanakayesere kunja kwa iwo okha.

D. Kugwiritsa ntchito ndime za mu Korani kapena Baibulo Mau kapena ziphunzitso za m’Baibulo ndi Korani zayikidwa mkati mwa bukhu lonse. Izi zithandiza Phungu kuwonetsetsa kuti maphunzilo onse akhazikika mu mau a Mulungu. Mau osankhidwawa ndi ongotsogolera chabe koma mulangizi ali ndi ufulu opeza mavesi ena owonjezera.

E. Zipangizo zofunika1. Baibulo/Korani2. Bukhu lina lirilonse limene lingathandize pa dongosolo la uphungu.3. Zolembera ndi mapepala akuluakulu kapena choko ndi bolodi ndi zofunika pa mitu ina. Ngati zinthu zimenezi palibe, Phungu ayendetse dongosolo lonse pogwiritsa ntchito zipangizo zomwe zapezeka.4. Kugawa mapepala olembedwa kale kungafunike pa mitu ina. Ngati simungathe kukonza mapepala okwanira anthu onse, yesetsani kupeza pang’ono pokha kuti anthuwo athe kuonera limodzi. Ngati ena sangathe kuwerenga, aphungu angathe kufotokozera zimene zalembedwa papepalapo ndiponso kuwagawira ndi kuwapempha kuti akagawane ndi achibale awo amene angathe kuwawerengera. 5. Asanayambe dongosololi, Phungu ayenera kudziwa za kumene anthu angakapeze chithandizo cha mavuto ena omwe angakhale nawo. Malowa ndi monga malo komwe: • Aperekauphungundikuyezamagazi. • Amaperekauphunguwakutetezamwanakutiasatengekachirombo ka HIV kuchokera kwa mai wake (PMTCT). • AmapangaMdulidwewaamuna • Maloothandiziraanthuameneachitiridwankhanza • Zipatalazoperekamakhwalaothandizakuchepetsakuchulukana kwa HIV.

F. Phungu akumbukile izi: • Werenganibukhulonselimusanayambedongosololoyamba;onetsetsanimau ofunikira pa mutu uliwonse. • Dziwanibwinolomwezimenezilipamutuuliwonsemusanayambekuphunzitsa koyamba; onetsetsani kuti mwakonza zipangizo zonse nthawi yabwino. • Longosolanizochitandizokambiranam’magulukutidongosolo

> 6 Banja la chisangalalo

• Longosolanizochitandizokambiranam’magulukutidongosololonselikhale logwirizana ndi chipembedzo, msinkhu, ndi kuzindikira kwa gulu lanu ngati nkofunika.

• Ganiziranimomwemungathaniranendikusiyanamaganizopazokambirana zimene zingakhumudwitse anthu ena.

• Perekanizitsanzozimenezikukhudzamiyoyoyaanthuwopoyang’aniramoyo watsiku ndi tsiku.

• Mukhalendinthawiyodziwabwinoanthuamenemukuwapatsauphungu.• Onetsetsanikutimaloamenemukuperekerauphungundiwoyenera.• Dziwanibwinozamauam’baibulokapenaKoraniamenemugwiritsentchito

pa mutu uliwonse ndipo mukhale ndi nthawi yopeza mau ena amene angathandize kutsindika mfundo zikuluzikulu.• Werenganimabukhuenakapenafunsaniaphunguenaameneangathekudziwa

bwino makamaka za mfundo zina zimene inu simukuzidziwa bwino. • Onetsetsanikutimwapezanjirayoyankhiramafunsokapenandemangazimene anthu angapereke koma zosagwirizana ndi mfundo zimene mukukambirana – afotokozereni kuti maganizo awo ndiofunika ndipo muwaunikanso kanthawi

kena; mungathenso kulemba papepala lapadera kuti muthe kukumbukira ndi kukumbutsa gulu lonse.• Konzanimauotsekulirandizochitazochangamutsagulu.Izizimathandiza

kwambiri pamene mukusintha kuchoka ku mutu wina kupita ku mutu wina komanso zimadzutsa gululo pamene likuoneka kuti lafooka.• Tsatiranialiyensekutimuonetsetsekutiakutengapombalindipomuonetsetsenso kuti simukulankhula nokha kwambiri. Limbikitsani aliyense kuyankha mafunso a

wina ndi mnzake. Mwachitsanzo, ngati wina afunsa funso, apatseni mpata enawo kuti ayankhe powafunsa kuti, “alipo amene ali ndi yankho ku funso limeneli?”

• Onetsetsanikutimukumalizabwinozokambiranazo,aliyenseapitendiuthenga womveka bwino. Pakafunika, sonyezani bwino lomwe zoyenera kuchita kutsogolo

kapena njira zothetsera mavuto. • Sangalalani!Zokambiranazizikhalezosangalatsandipozopatsampataaliyense.

Ngati inu muli ndi chidwi, enanso adzakhala ndi chidwi.

> Banja la chisangalalo 7

Uphungu ndi Chiyani?

Uphungu ndikuthandiza munthu, banja, kapena gulu la anthu: kuona mavuto omwe alipo ndi amene angadzakumane nawo m’moyo wawo, kuwaunika mavutowo moyenerera ndi mokhuzidwa ndi kuthandiza kupeza njira yogonjetsera mavutowo kuti munthu akhale ndi moyo wabwino ndi okwanitsidwa. Kufufuza ndi kupeza njira yothanilana ndi mavutowo ndi udindo wa awiriwo omwe akukumana ndi mavutowo. Ntchito ya Phungu ndi kungounikirapo pa mavuto amene alipo kapena amene angadze ndi kuthandiza munthuyo kapena banjalo kumvetsa momwe angawagonjetsere.

Uphungu wauzimu ndi wapadera chifukwa umagwiritsa ntchito zipangizo zauzimu ndi kumvetsa maganizo amunthu ndi moyo wabwino. Ungathe kuperekedwa ndi atsogoleri a chipembedzo, atumiki wamba, Atumiki osankhidwa, kapena ogwira ntchito ena amene anachita maphunziro aza umoyo, zachitukuko ndi za Mau a Mulungu.

Kodi Uphungu ndiwofunika bwanji?

• Umathandiza anthu kapena maanja kukhala ozindikira ndi kupanga ziganizomozindikira chimene akuchita.

• Umathandiza anthu ndi maanja kuunikanso ziganizo za moyo wawo ndikudzifunsanso modekha ndi khala cholinga chakuti apangenso ziganizo zabwino zothandiza kumanga banja lokondwa ndi la thanzi.

• Umapatsaanthumwaiounikazinthuzamoyowawozimenezimawapangitsaiwokapena okondedwa awo kumva zowawa ndi kupeza njira yabwino yothetsera mavutowo.

• Umathandizaanthukupirirapazovutazamoyowawondikudzilimbitsapounikirazovuta zina zimene zingadze kutsogolo.

• Ungathetsenkhawa,mathandimalingaliroamenemunthuangathekukhalanawo okhudza chibwenzi kapena moyo wa banja.

• Ungathandizeanthukupangazisankhozabwinokutiadzitetezeokhandikuteteza okondedwa awo ku HIV ndi EDZI.

Kukhala Phungu wokhudzidwa ndi wodalirika:

• Onetsenanikutianthuakumasukakutiathekugawananawozimeneakumvandikuganiza.

• Mvetseranibwinozimeneanthuakunenandipomusawadule,ngatiakuvutikakutambasula maganizo awo, afunseni mafunso amene angathandize kufotokozera zimene ziri mumtima mwawo.

• Musaweruzemayankhoawokomaathandizenikuzindikiramomwezisankhozawo zingadzetsere zowawa pa moyo wawo kapena wa anzawo.

• Mvetseranimomwethupilanulikudzionetserapothandizakuperekauthengaumene inu mukulankhula – mwachitsanzo, kodi mwaima mosonyeza kuti mukumvetsera zimene akunena kapena mwapinda manja anu, kapena mukuyang’ana moweruza? ‘’Mukumvetsera’’ – kuvomereza ndi mutu nthawi zina, kumwetulira kapena kuoneka okhudzidwa pamene pafunika kutero? Kapena mukuoneka obalalika ndi kumayang’ana kwina?

> Gawo 3 a – Kuunika uphungu

> 8 Banja la chisangalalo

• Atengenianthuamenemukuwapatsauphungungatianthuozindikiraomwealindi uthenga ndi luso loti nkugawana nanu, osati ofuna kudzangophuzira kwa inu.

• Kumbukiranikutiudindowanundikutsogoleradongosolopameneanthu,maanja kapena magulu angathe kuunika mavuto ndi kutha kuchita zisankho zotukula miyoyo yawo.

• Pezanimayankhoangapooyenerapavutokapenafunsoosatiyankholimodzilokha lolondola.

• Phungukapenamlangiziwabwinoakuyenerakukhalaosungachinsinsi.Ngatiphungu wopanda chinsinsi anthu samamukhulupilira ndipo samamasuka kumuwuza nkhawa zawo.

> Banja la chisangalalo 9

> Gawo 3 b: Kuunika zofunikaUdindo umene mipingo yatenga polimbikitsa kupewa HIV, chisamaliro ndi chithandizo ukuchokera pa maziko a chikondi ndi kukhudzidwa kwa aliyense pa zolengedwa za Mulungu/Allah. Anthu ambiri achipembedzo akhala akuvutika ndi momwe angatengere nkhani za HIV, akhala akuchiona chinthu chovuta kusiyanitsa pakati pa kuweruza khalidwe ndi kuweruza munthu. Anthu ena akhala okhudzidwa pamene ena akhala akukolezera moyo ndi makhalidwe ozipatula ndi osankhana mosayang’anira zovuta zimene zingadze kamba ka mchitidwewu.

Tonsefe timaumbidwa ndi maganizidwe athu ndi zikhulupiliro zathu pa nkhani za HIV, kawirikawiri mosazindikira. Kwa anthu ambiri, izi zikusintha kamba kophunzira zambiri za momwe matendawa amayambira ndi zotsatira zake poona maanja, anzawo ndi okondedwa awo akudwala kapenanso kukhudziwa ndi HIV.

Mchitidwe oweruzana ungabweretse chikhalidwe chobisa matenda ndi kusalana zomwe zingapangitse omwe ali ndi HIV kapena edzi kulephera kutenga nawo mbali momasuka. Zingapangitsenso munthuyo kusiya kupemphera. Kuonjezerapo, chikhalidwe chobisa matenda ndi kusalanachi chingasokoneze kupewa kwa HIV ndi kulepheretsa anthu kupita kukalandila chithandizo ndi chisamaliro choyenera. Kuti mukhale Phungu wabwino, ndi kofunika kuunika mwachilungamo maganizidwe anu, makonda anu ndi mfundo zofunika za HIV. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni inu kuti muunike bwino ndi kuti mumvetse momwe mungapangire kuti anthu khale omasuka kudzalandila uphungu.

> 10 Banja la chisangalalo

> Ntchito: Kudzifufuza nokha

Mphindi: 30

Zida zofunikira• Mfundozothandizakuzifufuzandikufotokozerakwake.

Kukonzekera mwapadera kwa Mlangizi• Ngatimulimphunzitsiyemwemukuphunzitsazomwezilim’bukhuli,izi zikhonza kuchitika pagulu. • Ngatimulimulangizimukugwiritsantchitobukhuli,onanimfundozindi kufotokoza kwake panokha.

Zokambilana mwachiduleMlangizi ayang’anitsitsa maganizo ndi zikhulupiliro zake zokhuza HIV, ndikuzindikila kuti ena mwa maganizo ndi zikhulupiliro zake zingathe kusokoneza ntchito yake yopereka malangizo omwe ali omupanga munthu kukhala omasuka komanso abwino.

ZolingaCholinga cha ntchitoyi ndikuthandiza mlangizi kuonanso maganizo ndi zikhulupiliro zolakwika zomwe zingalepheretse ulangizi omwe ungalipange banja kumva kulandiridwa ndi kuthandizidwa.

Ndondomeko

Khwerero 1: Werengani mfundo zomwe zili mmusimu. Ganizilani za mayankho anu. Mungathe kuwalemba mayankho anu musanawone mayankho omwe ali mbukhumu. Nenani chilungamo cha zomwe mumakhulupilira

Mfundo zothandizira kuwunikila zikhulupiliro:

Mfundo 1: EDZI ndi chilango/temberero lochokera kwa Mulungu/Allah?

Mfundo 2: Amai ndi Abambo apabanja amene ali okhulupirika kwa wina ndi mnzake sangatenge Edzi.

Mfundo 3: Makondomu amalimbikitsa khalidwe loipa ndipo tisamawakambe

Mfundo 4: Munthu woopa Mulungu/Allah sangatenge Edzi

Mfundo 5: Amene ali pabanja apite limodzi kukayezetsa kachirombo ka HIV.

Mfundo 6: Mtsogoleri wa mpingo amene watenga kachirombo ka HIV asaloledwe kupitiliza kulalika.

Mfundo 7: Ngati wina apita kokayezetsa HIV, zikutanthauza kuti wakhala akuchita khalidwe lochimwa

Mfundo 8: Mai amene ali ndi kachirombo sayenera kubereka

> Banja la chisangalalo 11

Mfundo 9: Banja limene m’modzi ali ndi kachirombo pamene wina alibe likhozanso kukhala banja lokhathamira

Mfundo 10: Akazi sayenera kuyambitsa zogonana kapenanso kuuza mwamuna wake kuti amusangalatse motani

Khwerero 2: Mukamaliza mfundo zonse, unikani mayankho anu. Onani mayankho omwe ali pa tsamba lotsatila ndipo muwayerekeze ndi anu. • Mwaonachodabwitsandiyankholirilonse?• ZikukuuzanichiyanipazomweinumumakhulupilirazokhuzaHIV?• NangazikukuwuzanichanipazaHIVndianthuapabanja?• Kodimukudzimvakutimwakonzekakuperekauphungukwaena?• Ngatimukuonakutimukuyenerakulimbanabendizovutazamaganizidweanu,

pemphaniuphungukwaenamusanayambentchitoyoperekauphungu.

Khwerero 3:Ngatimukumvakutimungathekulangizaena,yambanindikutsatiraphunziro1kwaomwesalimbanjakomaakonzekerakulowambanjakapenaphunziro2mpaka9kwaomwealimbanja.

> 12 Banja la chisangalalo

KUFOTOKOZA MFUNDO ZAKAUNI-UNI

Mfundo 1: EDZI ndi chilango/temberero lochokera kwa Mulungu/Allah

Kufotokoza: Edzi ndi nthenda yomwe imakhuza chitetezero cha mthupi la munthu ndiku-mupangitsa munthuyo kulephera kulimbana ndi matenda ena. Wina aliyense angathe kutenga HIV, kachilombo koyambitsa Edzi.

M’Malawi muno muli anthu okwana zana limodzi omwe ali ndi HIV. Mwa anthu zana limodzi-wa, ana alipo okwana zikwi 120 ndipo ana ena oposa theka la zana ndi amasiye. Anthu omwe ali ndi HIV ndi anthu akenso a Mulungu/Allah monga momwe ena aliri.

Mulungu/Allah amationa tonse ngati ana ake amtengo wapatali -osati osauka ndi olemera, osati mfulu ndi akapolo, osati a HIV ndi opanda. Tikuyenera kuti ifenso tiziwawona choncho anthu onse ndikukondana wina ndi mzake mofanana. Mipingo ndi mabungwe ambiri, amasiyana maganizo pankhani yokhudza Edzi. Ena amati ndi chilango chochokera kwa Mulungu/Allah. Mtsutsanowu, sitingathe kuwuthetsa mbukhu iri. Komabe, tilangize anthu achipembedzo kuti sibwino kusala munthu chifukwa cha matenda a edzi, ngakhale atakhala kuti adachimwa kuti atenge matendawo.

Mfundo 2: Amai ndi Abambo apabanja amene ali okhulupirika kwa wina ndi mnzake sangatenge Edzi.

Kufotokoza: HIV imafala ngati magazi kapena madzi ena a mthupi (mkaka, umuna kapena ukazi) kuchokera kwa munthu yemwe ali ndi HIV zilowa mthupi mwa yemwe alibe: • Nthawiyomweanthuakugonana(njirayotchukakwambiri) • Nthawiyomwemayialindimimba,poberekandipoyamwitsa. • Popatsanamagazi(ngatialiosayedzetsa) • Kugwiritsantchitosinganokapenazinthuzomwezimachekazomweziri ndi HIV.

NgatimwamunandimkazianalibeHIVnthawiyomweamakwatilanandipoakhalaokhulu-pilikakwawinandimzakenthawiimenealim’banja,mpataotengaHIVumakhalaochepa.Komabe ngati mmodzi kapena onse awiri sanayezetse HIV asanakwatilane, angathe kumupat-silaokondedwawawomosadziwa,ngakhaleangakhaleokhulupilikambanjamwawo.

Mfundo 3: Makondomu amalimbikitsa khalidwe loipa ndipo tisamawakambe

Kufotokoza:Ndikofunikakuonakayengatikulikoyenerakukambazamakondomundianthuomwealipabanja.NjirayabwinoyopewerekutengaHIVndikudziletsa,kapenakwaomwealipabanjakukhalaokhulupilikakwawinandimzake.Ndizoonansokutikugwiritsantchitokon-domu nthawi zonse komanso moyenerera kungathandize kuchepetsa kufala kwa HIV. KugwiritsantchitokondomukwamaanjaomwemmodzialindiHIVndikovomerezekandicholinga chomuteteza yemwe alibe HIV kuti asatenge.

> Banja la chisangalalo 13

Mfundo 4: Munthu woopa Mulungu/Allah sangatenge Edzi

Kufotokoza: Anthu omwe ali oopa ndi okonda Mulungu nawonso ndi anthu ndipo nthawi zina amalakwitsa kapena kupezeka pa malo omwe amawayika pa chiopsezo chotenga HIV. Ena angathe kutenga HIV mosadziwa kuchokera kwa okondedwa wawo yemwe ali osakhulupirika. Komanso ngati samadziwa za momwe okondedwa wawo analiri asanakwatilane. HIV imafalanso kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana kapena kupyolera mukulandila magazi omwe ali ndi HIV.

Zikhulupiliro zathu zingapangitse mipingo/mizikiti kukhala malo omwe anthu omwe ali ndi HIV sangamve kutetezeka kapena kulandiridwa monga momwe Mulungu/Allah amafunila. Kotero ndikofunika kuti tisaweruze omwe ali ndi HIV, koma khalani achifundo ndikumuthandiza iye kukhala moyo wabwino ndi wokwanitsidwa.

Mfundo 5: Amene ali pabanja apite limodzi kukayezetsa HIV.

Kufotokoza: Maanja alimbikitsidwe kupita kukayezetsa limodzi. Kukayezetsa limodzi kumawapatsa mwayi maanja wodziwa ngati mzawo ali ndi HIV kapena ayi. Izi zimabweretsa zotsatila poyera, ndikuchotsa nkhawa yakuti ndikamuuza bwanji mzanga popanda thandizo la akuchipatala.

Kuonjezerapo amalandila uphungu wa momwe angakhalire ndi HIV mbanja mwawo makamaka wina akakhala kuti alibe HIV.

Ndi zotheka mbanja mmodzi kukhala ndi HIV wina alibe. Izi zimachitika mu njira zosiyasiya. (Onani kumapeto kwa bukhuli mfundo zowonjezera)

Mfundo 6: Mtsogoleri wa chipembedzo amene watenga HIV asaloledwe kupitiliza kulalika.

Kufotokoza: Mtsogoleri wa mpingi akuyenera kuloredwa kupitiliza kularikila. Ngakhale anthu ena sangasangalatsidwe nazo, pali a kulu ampingo ambiri omwe ali ndi HIV omwe akupitiliza kutsogolera ndikuphunzitsa. Mu mpingo ndi mu mzikiti ndi malo olandila onse ndipo akuyenera kuyimila chikondi, chifundo ngakhale kwa atsogoleri.

Monga tafotokozera pamtundapa , atsogoleri achipembedzo amatha kulakwitsa kapena kupezeka pa malo omwe amawapangitsa kukhala pa chiopsezo ku HIV. Ena angathe kutenga HIV mosadziwa kuchokera kwa okondedwa wawo yemwe ali osakhulupilika. Komanso ngati samadziwa za momwe okondedwa wawo analiri asanakwatilane. HIV imafalanso kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana kapena kupyolera mukulandila magazi omwe ali HIV.

Mfundo 7: Ngati wina apita kokayezetsa HIV, zikutanthauza kuti wakhala akuchita khalidwe lochimwa

Kufotokoza: Tonse tiyenera kupita kukayezetsa ndi kulandila uphungu, chifukwa pali njira zambiri za momwe mungatengere HIV. Ndi pokhapokha ngati wina akudziwa mmene aliri, pamene angathe kulandila malangizo akuchipatala kapena chitsogozo cha uzimu pofuna kuonetsetsa kuti akukhala bwino-ndipo ngati kuli kofinikakulandilamaARV.

> 14 Banja la chisangalalo

Mfundo 8: Mai amene ali ndi HIV sayenera kubereka

Kufotokoza: Mayi yemwe ali ndi HIV angathe kukhala ndi ana. Amayi ambiri omwe ali ndi HIV amatha kukhala ndi ana omwe alibe HIV,kamba ka malangizo ndi mankhawala a ma ARV omwe amaperekedwa kwa mayi ndi achipatala mwana asanabadwe, ndi kwa mwana atangobadwa. Dziko la Malawi layam,ba kutsatila njira ya makono kwa mayi woyembekezera omwe ali ndi HIV yomwe yakhazikitsidwa ndi bungwe loona za umoyo pa dziko lonse lapansi. Amayo onse omwe ali ndi HIV akumapatsidwa mankhwala amphamvu zitatu ngati njira yodalirika yochepetsera kufala kwa HIV kuchoka kwa mwana kupita kwa mayi ndi kuteteza moyo wa onse awiri. Mankhwalawa ndi omwa moyo onse ndipo akuperekedwa kwa amayi onse oyembekezera omwe ali ndi HIV mosayang’anila kuchuluka kwa chitetezo cha mthupi mwawo.

Maanja akuyenera kulangizidwa ndi achipatala odziwa bwino pa zoopsa zomwe zingakhalepo ndi cholinga chakuti anthuwa apange ganizo labwino. Ndikofunika kuti banja litsatile ndondomeko yonse yokhuza kupewa kufala kwa HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana.

Mfundo 9: Banja limene m’modzi ali ndi HIV pamene wina alibe likhozanso kukhala banja lokondwa

Kufotokoza: Ndikotheka kwa banja lomwe wina ali ndi HIV kukhala ndi banja lokondwa lomwe muli chikondi. Banja lingathe kudziwa kuti wina ali ndi HIV akayezetsa. Pali zovuta zambiri zomwe banja lingakumane nazo ndipo akuyenera kulangizidwa kuti athe kuthandizana ndikusungabe malonjezo awo kwa wina ndi mzake mu nthawi yovuta ngati iyi.

Ngati anthu awiri okondana wina atapeze ali ndi HIV wina alibe, angathe kukwatilana kapena ngati ali okwatilana kale angathe kupiliza kugonana akudziwa momwe mthupi mwawo muliri. Potengera ndi chipembedzo, awiriwo ayenera kulangizidwa pa zoopsa zomwe zingakhalepo kuti apange chisankho chabwino. Njira yokhayo yowonetsetsa kuti winayo asatenge HIV ndi kudziletsa kapena kugwiritsa ntchito kondomu.

Mfundo 10: Akazi sayenera kuyambitsa zogonana kapenanso kuuza mwamuna wake kuti amusangalatse motani

Kufotokoza: Kugonana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu yomwe inapangidwa kuti ithandize kupanga banja labwino lomwe liri losangalala. Mayi ndi bambo wonse akuyenera kusangalatsidwa akamagonana.

Chikhalidwe chathu chimaphunzitsa kuti amayi sakuyenera kuyambitsa zogonana. Akayambitsa, abambo amawawona ngati ichi sicholoredwa ndipo amaona kuopsezedwa. Chikondi pakati pa mamuna ndi mkazi chamangika pa kukhulupilirana, kulankhulana ndi kukondana.

Ndikofunika kwa banja –amayi ndi abambo-kukambilana zomwe zimawasangalatsa ndi cholinga chakuti onse azikwanitsidwa mbanja. Izi zikhonza kukhala zovuta chifukwa cha miyambo ina yoletsa kukambilana zogonana makamaka kwa azimayi, koma akuyenera kulimbikitsidwa kupyolera mu ulangizi.

> Banja la chisangalalo 15

Gawo 3 c: Kupitiriza uphungu

Kukonzekera banja kumakhazikika kwambiri pa zokonzekera za mwambo waukwati ndipo timachita zochepa zokonzekera moyo umene ulipo likapita tsiku la mwambo waukwati. Popeza kuti banja ndi ubale wa nthawi yaitali, uphungu uyenera kuganizira izi pozindikira kuti banja likhoza kutha ngakhale awiriwo atakalamba. Ndi kwabwino kuti ifeyo tiganizire ndondomeko yopitiliza uphungu pa zifukwa izi:-• Maanjaenasakhalitsakambakotiolowam’banjawosanakonzekeremokwanira

moyo wa m’banja. • Achinyamataomwealowakumenem’banjaamadzidzimukandizimene

amakumana nazo m’banjamo pamene azindikira kuti zimene amayembekezera nthawi imene anali pachibwenzi sakuzipeza.

• Maanjaakufunikakukhalandinjirazopezerachumakutiathekukhalandibanjalabwino lopanda mavuto ambiri azachuma.

Ndondomeko yoperekera uphungu kwa maanja atsopano:-• Aphunguayenerakukonzekerakuwayenderakutiamvemomwebanja

latsopanolo likukhazikikira m’banja ndi kuwalimbikitsa kumanga banja lawo(e.g. moyo wauzimu; kulumikizana; kusamala chuma; kuthetsa mikangano; kukonza dzibale; moyo wogonana).

• Asonyezenikumisonkhanoyamaanjaatsopanomumpingomo.• Phunzitsaniaphunguamumpingokutiapitilirekuperekauphungumasikuonse

a banja lawo. Komanso maanja atsopano ayenera kupatsidwa mwai wokumana ndi aphungu a kumtima kwao.

• Limbikitsanibanjalatsopanolikutiliyambekufikiraenaameneakufunakulowam’banja.

• Pakutimavutoazachumandigwerolalikululakupasukakwamaanja,dongosolo lapadera liyenera kukonzedwa kuti alangize banjali za kagwiritsidwe ntchito ka chuma.

• Mwapadera,tiyenerakuganizirakuperekauphungupankhanizakulera,kubereka ndi kulera ana.

• Ayenerakuthandizidwakutiamvetseudindowakuleraanakutindiwamakoloonse awiri.

• Afunikakuunikiridwapamaderaofunikakutumikirandikutengapombalipazochitika mumpingo.

• Nkofunikakutitiyambitsemaguluothandizanamumpingopofunakuonetsetsakuti pali kulumikizana ndi anzawo.

• Aphunguamaanjandiofunikamaphunziloamomweangaperekereuphungu,zipangizo (mabukhu auphungu) maphunziro owakumbutsa momwe akuyenera kugwilira ntchito yawo yopereka uphungu.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:1

Mu phunziro iri tiona zinthu zofunikira zomwe achinyamata ayenera kuziganizira akamasankha bwenzi lodzamanga nalo banja. Chinthu chimodzi chofunikira posankha bwenzi lodzamanga nalo banja chikukhudza HIV/EDZI.

Phunziroli lifotokoza za nthawi ya ubwenzi yomwe ndi nthawi yoyenera kumvetsetsa bwino kuti bwenzi lanu ndi lotani nanga inuyo ndinu ndani kwa bwenzi lanulo.

Mu phunziroli muli zochitika zolimbikitsa aliyense kutengapo mbali zomwe cholinga chake ndikuthandiza anthu onse kumvetsetsa bwino nkhani zomwe zikukambidwa.Mulinso tinkhani tomwe tiwathandize achinyamata kumvetsetsa za makhalidwe omwe akuyenera kuyang’ana mwa munthu wozamanga naye banja.

Phunziro 1

Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

> 1:2 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

> Phunziro mwachidule

Omwe akuyenera kuphunziraAnthu omwe akuyenera kukhalapo pa phunziro limeneli ndi amene akukonzekera kulowa mbanja.

Ndondomeko ya phunziro• MutuwaGawo• Mauotsogoleraphunziro• Kutseguliraphunziro1• Miyamboyamakolo• Kusankhabwenzilomanganalobanja• UbwenziwowopaMulungu• Malusoamoyo-kuthanandizikakamizo• Kupangachiganizochosakhalilalimodzitisanalowem’mbanja• Ziganizozabodza• Ubwinowakudziletsandizotsatilazakusadziletsa• KukambiranamwapaderazaHIVndimatendaopatsiranapogonana• Kuombamkota• Ntchitoyakunyumba

Nthawi yofunikaMaola asanu

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Pepala ndi cholembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani dongosolo lonse nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za mu Baibulo/Korani zokhudzana ndi mutuwo ndi zolembedwa zina.3. Ganizirani zowerenga zina zimene zingafunike pa dongosololi.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:3

> Kutsegulira phunziro 1

Nthawi: Mphindi 20

Phunziro MwachiduleAchinyamata amene ali paubwenzi ndi chiyembekezo cholowa m’banja akambirana za kusankha bwenzi lomanga nalo banja. Akambirana za momwe angapangire chisankho cha nzeru cha bwenzi lodzamanga nalo banja; nkhani za kugonana asanalowe m’banja ndi kudziletsa ali paubwenzi.

Zolinga• Kumvetsetsabwinozakufunikakosankhabwinobwenzilodzamanganalobanja

ndikuti zikutanthauza chiyani.• KudziwamokwanirazaHIVndikuopsakogonanamosadzitetezatisanalowe

mbanja.• Kufotokozazomwetikuyembekezerandikupangamalamuloagulu.

Ndondomeko

Khwerero 1: Alandireni achinyamata onse. Afotokozereni kuti akhala ndi mwayi ophunzira zokhuza iwo komanso bwenzi lawo.

Khwerero 2: Fotokozani za phunziro la kusankha bwenzi lomanga nalo banja kwa achinyamata:

• Kusankhabwenzindichimodzimwaziganizozofunikirakwambirizimenemunthu angapange muchipembedzo.

• Nthawizambirianthuamasankhabwenzipotsatilazomweakumvamthupikomanso maonekedwe akunja koma chofunikila kwambiri posankha bwenzi lomanga nalo banja ndi khalidwe kapena mtima wa munthu.

• Chiganizochichikuyenerakutengedwamwakuyamongaganizolinalilonsemmoyo wa munthu-mpofunika kupemphera, kufufuza mokwanira komanso kupempha abale kuti athandizepo.

Khwerero 3: Awuzeni achinyamata kuti:

• Achinyamataakuyenerakutengapogawomwachidwipazochitikazonse.• Achinyamataakambiranamomweakuganizira,zikhulupirirozawondimomwe

amawonera pa nkhani zokambidwazo.• Achinyamataayeseramalusoenaothandizakulimbikitsaubwenziwawo.• Kugonanamusanalowem’banjakumathandizakutiawirinumudziwane

musanalowe m’banja ndikuona ngati mukuyenerana.

> 1:4 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleAchinyamata ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zomwe zimalimbikitsa achinyamata kuyamba zogonana asanalowe mbanja. Achinyamatawa akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupezazikhulupilirokapenazoyankhulidwazosiyanasiyanazomwe

zimalimbikitsa achinyamata kuyamba zogonana asanalowe mbanja. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizeachinyamatakukhala

oziletsa mpaka azalowe mbanja.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni achinyamata kuti akambirana za zikhulupiliro ndi zoyankhulidwa zokhuza kugonana. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni achinyamata kuti atchulepo ina mwa miyambo ya makolo ndi nkhamba kwamwa zokhudza kugonana asanalowe m’banja. Pokambirana zimenezi tifuna kulekanitsa mfundo zoona ndi nkhambakamwa.

Khwerero 3: Ina mwa miyambo ndi nkhamba kamwa zomwe achinyamata angatchule ndi yomwe iri mmusiyi. Werengani zomwe achinyamatawa sanatchule.

• Anyamataamenesachitachiwerewereasanakwatireamatchulidwakutisiamunaenieni.

• Amauzidwakutiadzimvakuwawamsanakwambiri,ndipoadzakhalaosabereka.• Atsikanaamauzidwakutiadzimvakuwawakwambirinthawiyosamba,adzimva

kuwawa msana ndipo mawere awo sadzakula.• Kugonanaasanalowem’banjakumaonekangatinjirayosonyezachikondi.• Amalimbikitsidwakuchitachiwerewerepoopakutichibwenzichitha.• Akachitamwambowachinkhoswe,amauzidwandiachibalekutiangathekuyamba

kugonana.• Akavinidwaachinyamataamauzidwandianankungwikutiakachotsefumbingati

satero azituwa.• Palinsomauotchukaakuti-“kuyeserakumamupangitsamunthukukhalakatswiri”.• Mnyamataakadziletsa,amatiziwalozakendizofokandizasathantchito(hafu-

sikisi). Mtsikana samakhala ndi thupi loumbika bwino, amakhala ndi thupi lotuwa.• Popandakugonana,umasowaVitaminiK.• Kugonana musanalowe m’banja kumathandiza kuti awirinu mudziwane

musanalowe m’banja ndikuona ngati mukuyenerana.

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:5

Khwerero 4: Ombani mkota pa ndimeyi potsindika nfundo izi:-

• Alimbikitseniachinyamatazakudziletsaasanalowem’banjapopezakugonanaasanalowe m’banja ndi chimo pamaso pa Mulungu.

• Anthuameneamagonanaasanalowem’banja,sizimavutakutichibwenzichawochithe asanalowe mbanja.

• Mavitaminiomweatchulidwaamathakupezekansomuzakudyazinandipopalibe umboni wakuti mavitaminiwa amapezeka mukagonana.

• Sikusowekakutiuyeserakugonanakutiukathekugonanapopandavutom’banjakomanso kuyeserelaku kungathe kumupangitsa wachinyamata kutenga HIV.

• NgatibwenziwakoamakukondadindipoamawopaMulungu/Allah,adzalolerakudikira, osagonana nthawi yake isanakwane. Sadzakakamira kuti mugonane ngati umboni wa chikondi.

ZopemphereraPempherani kuti Mulungu/Allah akuthandizeni: • MuthekuvomerachifunirochaMulungu/Allahchokhuzachiyanjanochanundi

kuchitsatilaMuthandizane kuti mukhale oziletsa mpaka muzalowe mbanja.• Kumuthandizandikumumvetsetsabwenzilanukutimusagonanemusanalowe

mbanja.

Malemba OwerengaKorani 24: 2Koranio 17:321 Akorinto 6:15-20

> 1:6 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Khwerero 4: Ombani mkota pa ndimeyi potsindika nfundo izi:

• Alimbikitseniachinyamatazakudziletsaasanalowem’banjapopezakugonanaasanalowe m’banja ndi chimo pamaso pa Mulungu.

• Anthuameneamagonanaasanalowem’banja,sizimavutakutichibwenzichawochithe asanalowe mbanja.

• Mavitaminiomweatchulidwaamathakupezekansomuzakudyazinandipopalibe umboni wakuti mavitaminiwa amapezeka mukagonana.

• Sikusowekakutiuyeserakugonanakutiukathekugonanapopandavutom’banjakomanso kuyeserelaku kungathe kumupangitsa wachinyamata kutenga HIV.

• NgatibwenziwakoamakukondadindipoamawopaMulungu/Allah,adzalolerakudikira, osagonana nthawi yake isanakwane. Sadzakakamira kuti mugonane ngati umboni wa chikondi.

ZopemphereraPempherani kuti Mulungu/Allah akuthandizeni: • MuthekuvomerachifunirochaMulungu/Allahchokhuzachiyanjanochanundi

kuchitsatilaMuthandizane kuti mukhale oziletsa mpaka muzalowe mbanja• Kumuthandizandikumumvetsetsabwenzilanukutimusagonanemusanalowe

mbanja.

Malemba OwerengaKorani 24: 2Korani 17:321 Akorinto 6:15-20

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:7

> Ntchito 2: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Nthawi: Mphindi 45

Zokambirana MwachiduleAchinyamata akambirana za makhalidwe omwe akuyenera kuonetsa kwa mzawo womanga naye banja, komanso makhalidwe omwe iwo akuyembekezera kwa bwenzi lawo. Mu gawo ili akambirananso kuti ndi chifukwa chani makhalidwe amenewa ali ofunikira komanso ngati anyamata ndi atsikana amayembekezera zosiyana mbanja mwawo

Zolinga• Kukambilanamakhalidweomwemunthuangafunekuchokerakwabwenzilake• Kukambiranazakusiyamuzinthuzambirikomwekumakhalapopakatipaamuna

ndi akazi. • KukambiranamomwemakhalidweabwinoangathandizilekupewaHIV/Edzi

mbanja

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani kwa gulu lonse. Tsopano ayamba kuganizira pa mutu wakuti kupeza bwenzi lozamanga nalo banja.

Khwerero 2: Agaweni achinyamatawa mumagulu. Anyamata ndi atsikana a funseni kuti:

• Akambirane makhalidwe atatu omwe angawawonetsere kwa bwenzi lozamanga nalo banja yemwe amamukonda.

- Makhalidwe atatu omwe angawayembekezere kuchokera kwa bwenzi lozamanga nalo banja,

- Zizndikiro za munthu yemwe angakonde kumanga naye banja yemwe ali wa chikondi.

• Lembani makhalidwe oyenera omwe mwakambilana.• Sankhani munthu m’modzi yemwe adzapereke mayankho kuimira gulu lirilonse

Khwerero 3: Gulu lirilonse ligawane ndi gulu lonse zimene akambirana m’magulu mwao. Lembani mndandanda wa makhalidwe onse omwe anthu akambirana.

Khwerero 4: Ngati gulu lonse, gwirizanani za makhalidwe enieni abwino omwe munthu angawayembekezere kuchokera kwa bwenzi lake. Onjezerani makhalidwe ena omwe mukuwawona kuti ndi abwino.

> 1:8 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Khwerero 5: Onani mndandanda wa makhalidwe uja ndipo kambirana pamodzi mafunso awa:

• Chifukwa chiyani nkofunika kuti bwenzi lomanga nalo banja likhale ndimakhalidwe awa?

• Pali kusiyana pakati pa zomwe anyamata alemba ndi zomwe atsikanaalemba? Alimbikitseni kuti afotokoze kuti ndi chifukwa chani pali kusiyana. Mwachidziwikile mayankho awo akhuza kusiyana komwe kuli pakati pa amayi

ndi abambo (genda). Muwalimbikitse kuti akambilane.• MungadziwebwanjikutibwenzilanualindimakhalidweawaMwachitsanzo;ndi

wachikondi, amakuthandiza kuti mukhale ozidalira.• Kuyankhulanakapenakulumikizanandikofunikamuchiyanjanochilichonse.Kodi

pakati pa anthu awiri omwe ali pa chibwenzi pakuyenera kukhala kuyankhulana kotani?

• MakhalidweomweakambidwawaangathandizebwanjikupewaHIVkutiisalowemnyumba?

• Funsaningatipalizoonjezera.

Khwerero 6: Ombani mkota pa mfundo zikuluzikulu izi:

• Kusankha bwenzi lomanga nalo banja ndi chimodzi mwa ziganizo zofunikira kwambiri zimene munthu angapange.• Nthawi ya ubwenzi ndi nthawi yoyenera kumvetsetsa bwino kuti bwenzi lanu ndi lotani. Kodi ndiwokhulupirika muchipembedzo chake. Nanga ali ndi mphamvu kapena zofooka zanji pa Khalidwe Lake? Ndi wachilungamo kapena ali ndi khalidwe lonama?• Palibe lamulo lilonse lokamba za kutalika kwa nthawi yomwe anthu akuyenera

kukhala pa chibwenzi. Kutalika kwa nthawiyi kukhonza kukhala kosiyana kwa anthunso osiyana. Ena atha kukhala pa chibwenzi kwa miyezi isanu ndi umodzi mpaka chaka chimodzi, kapena kupitilira apa.

• Nthawi ya ubwenzi ndi nthawi imene muyenera kufuna chitsogozo cha Mulungu/Allah ndi chitsimikizo chake kuti mwasankha bwenzi labwino ndi kuti mwakonzeka kulowa mbanja.

• Bwenzi lomanga nalo banja liyenera kukhala lokonda, lothandizira ndipo lofuna kutulutsa zabwino kuchokera mwa bwenzi lake.

• Kuyankhulana kwa bwino pakati pa anthu awiri okondana kuyenera kulimbikitsidwa anthuwa akadali pa chibwenzi. Anthu omwe ali pa chibwenzi akuyenera kumayankhulana momasuka, kuwuzana zomwe amaopa, zomwe amayembekezera, zokhumba zawo, zomwe amakonda ndi zomwe amadana nazo. Izi zizathandiza kuti azizatha kuyankhula momasuka akazakwatilana.

• Monga mwa chikhalidwe chathu amayi samalimbikitsidwa kuyankhula koma kumangomvetsera amuna akamayankhula. Izi siziyenera kukhala choncho;akazi ayenera kulimbikitsidwa kumayankhula momasuka ndi okondedwa awo. Amuna ayenera kulimbikitsa akazi awo kuti aziyankhula.

• Kuyankhulana kwabwino kukutanthauza kuti onse awiri ndi omasuka kulankhula zakukhosi kwawo mwachikondi ndipo mzawo akuwamvetsera.

• Kukhala ndi bwenzi lokonda ndi lothandiza, ndi kuyankhulana momasuka kungathandize kuonetsetsa kuti HIV sikulowa mnyumbamo. Pakakhala kuti kuyankhulana palibe ndipo awiriwo sakuthandizana, mmodzi kapena onse awiri angathe kupeza chibwenzi china chimene chingamakwaniritse zomwe okondedwa wakeyo akulephera.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:9

ZopempheleraPempherani kuti Mulungu/Allah akuthandizeni: • Kuthandizanawinandimzakekutimukhalebwenzilopambana,kukwanilitsazofunazanu

komanso za bwenzi lanu.• KuvomeraChikonzero chaMulungu/Allah kuti akunetsereni ngatimwasankha bwenzi

loyenera

Malembo OwerengaKorani 24:3, 32Korani 4:3Korani 40:441 Samueli 16:7Yeremiaya 29:11

> 1:10 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

> Ntchito 3: Maluso a moyo - Kuthana ndi vuto lokakamizidwa kuchita zomwe sukufuna

Nthawi: Mphindi 50

Zokambirana MwachiduleAchinyamata akambilana zikakamizo zomwe amakumana nazo mu ubwenzi komanso kunja kwaubwenzi wawo monga kuchokera kwa anzawo, makolo, abale komanso mmudzi/dera lomwe amakhala. Awonanso maluso omwe akuyenera kukhala nawo kuti athane ndi zikakamizo zimenezi ndi kukhala ndi ubwenzi opambana.

Zolinga• Kukambilanazikakamizozomweachinyamataamakumananazomuchibwenzi kapena kuchokera kunja kwa ubwenzi wawo.

• Kuphunzilamalusoomweangawathandizekuthanandizikakamizozi.

Ndondomeko

Khwelero 1: Awuzeni onse kuti:

• Palimalusoambiriamoyoomweachinyamataakuyenerakukhalanawokuti agonjetse mavuto kapena zikakamizo zosiyana siyana zomwe amakumana nazo mmoyo wawo.• Zikakamizozimenezizikhonzakuwalepheretsakukwaniritsamasomphenya omwe ali nawo. Zina mwa zikakamizo ndi monga kukakamizidwa kuchita zomwe sakufuna kuchokora kwa okondedwa wawo, kuchokera kwa anzawo, makolo, abale komanso dera lomwe amakhala. • Ngatisanachitebwinondizikakamizozi,ubwenziwawoukhonzakusokonekera.• Zinamwazikakamizozi.

Khwerero 2: Werengani nkhani ya Tambula yomwe ili kumapeto a ntchitoyi. Afunseni onse kuti akambilane mafunso awa ali limodzi:

• KodiTambulaanalindimasomphenyaotani?• Tambulaamayenerakukhalandimalusoamoyokutiamuthandizekukwaniritsa masomphenya omwe anali nawo. Ndi maluso anji omwe amayenera kukhala nawo kuti akwaniritse masomphenya akewo?• Ndimalusoanjienaomwealioyeneram’moyo?

Khwerero 3: Ombani mkota pa zokambilanazi potsindika mfundo yomwe ili mmusiyi.

• Palimalusoosiyanasiyanaomweachinyamataakuyenerakukhalanawondi cholinga chakuti akwaniritse masomphenya amoyo wawo. Ena mwa malusowa ndi monga awa; kupanga zisankha zabwino, kuzidalira wekha, kuyankhula ndi kukhala bwino ndi anthu.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:11

• Palinsomalusoenamongalusolokanakapenalokambilanakutizakozikuyenderendi luso lothetsa mikangano.

Khwerero 4: Funsani anthu awiri omwe ali pa ubwenzi kapena wina aliyense kuti afotokoze zina mwa zikakamizo zomwe anakumanapo nazo ndi momwe anachitila ndi zikakamizozi. Izi zikhonza kukhala zikakamizo kuchokera mkati kapena kunja kwa ubwenzi wawo.

• Ngati saliomasukakukambankhanizawo,angathekugawanandigulunkhaniya ubwenzi wina kapena munthu wina yemwe akumudziwa. Sakuyenera kuti awatchule mayina.

• Mungathensokupereka zitsanzo za zikakamizo zomwe anthu amalandila ngatisapemphera limodzi.

Khwerero 5: Akamaliza kugawana ndi gulu lonse nkhani zawo, funsani gulu lonse kuti akambilane mafunso awa:

• Ndizikakamizozinazitizimeneachinyamataamakumananazokuchokerakwaanzawo, makolo, abale ndi anthu ena am’mudzi?

• Achinyamataamachitabwanjindizikakamizozi?• Njirayolondolandiitiyothanilanandizikakamizozi?• Ndimalusoatiomweachinyamataakuyenerakukhalanawokutiathanendi

zikakamizozi?

Khwerero 6: Ombani mkota pa zokambilanazi pofotokoza mfundo izi:

• Palizikakamizozosiyasiyanazomweachinyamataamakumananazokuchokerakwa bwenzi alwo, makolo, abale ndi anthu a mdera lawo.

• Zikakamizo zomwe zimakhalapo mu ubwenzi ndi monga kukakamizidwakuchita zogonana, mamuna kukakamizidwa kumupatsa bwenzi lake zosowa zake komanso kukakamizidwa kuti akwatilane msanga ndi zina zotero.

• Nthawi zambiri zikakamizo zochokera kwa ena zimabwera ngati awiriwoamapemphera mipingo yosiyana, ndi osiyana zikhalidwe/miyambo, komanso ngati wina ali ochokera ku banja lopeza bwino.

• Zikakamizo zikhonzansokubwerangati awiriwo analeledwamosiyana,winaali ophunzira kwambiri makama akakhala kuti mkazi ndi amene ali ophunzira kwambiri.

• Achinyamata akuyenera kudziwa kuti kugonjera ku zokakamizazi kungathekusokoneza ubwenzi wawo komanso tsogolo lawo.

• Nthawizinamakoloakhonzakukhalandimaganizoolakwikapabwenzilamwanawawo popanda chifukwa chenicheni ndipo akhonza kumuuza mwana wawoyo kuti athetse chibwenzi chake.

• Mwana wawoyo ayenera kukhala pansi ndi kukambilana ndi makolo ake.Sakuyenera kuthetsa chibwenzi chifukwa makolo ake atero.

• Komabenthawizinamakolokapenaabaleamakhalandizifukwazomvekazomwezingawapangitse kudana ndi munthu yemwe mwana wawo akufuna kukwatirana naye. Ngati zili choncho ndikofunika kuti mnyamata kapena mtsikanayo amvere zomwe makolo kapena abale akewo akunena.

> 1:12 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:Mulungu akuthandizeni kugonjetsa zikakamizo zomwe mumakumana nazo muubwenzi wanu komanso kuchokera kwa anthu ena.

MalembaAfilipi4:13Masalmo 1:1

> 1:13 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

> Nkhani ya TambulaTambula anali mwana yekhayo wamamuna wa mai ndi bambo Galasi. Anali ndi achemwali ake awiri. Makolo awo anamwalira iwo ali ana ang’ono. Makolo awo atamwalira anayamba kukhala ndi amalume awo omwe amkapanga bizinesi. Ndalama zomwe amkapeza sizinali zokwanila kulipirila sukulu ana awo, Tambula ndi achemwali ake. Izi zinapangitsa Tambula kuyamba kugwira ntchito kwa anthu. Masomphenya a Tambula ndi akuti apite ku sukulu ya ukachenjede ndikuzakhala dotolo, azakhale ndi nyumba yayikulu ndi kuzakwatila mkazi wabwino. Masomphenya ena aTambula ndi akuti azawatumize achemwali ake ku sukulu yabwino komwe kuli maphunzilo apa mwamba.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:14

> Ntchito 4: Ubwenzi wolemekeza Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 45

Malangizo Apadera Kwa Mulangizi• Achinyamata akuyenera kulangizidwa mokwanira pofuna kutsimikiza kuti

ndiwokhulupilika kwa Mulungu asanaganize zokhala ndi bwenzi lozamanga nalo banja.

• Akuyenera kulimbikitsidwanso kuti ayetsetse kukhala pa ubwenzi kwa nthawiyokwanila ndi cholinga chakuti adzachite chiganizo akuzindikira.

Zokambirana MwachiduleAchinyamata awona nkhani zinayi ndi kuyamba kukambirana ngati nkhanizo zikuonetsera ubwenzi okondana ndi olemekezana, komanso ngati ubwenziwo uli woopa Mulungu/Allah. M’magulu ang’ono ang’ono apezanso mayankho kwa maubwenzi omwe ali munkhaniyo a momwe angalimbikitsire ubwenzi wawo. NKhani za HIV/EDZI zikambidwanso.

Zolinga• Kupezatanthauzolaubwenziwokondana.• Kukambiranazomwezingachitikepofunakulimbikitsaubwenzi.

Ndondomeko

Khwerero 1: Agaweni achinyamata mumagulu anayi.Angathe kukhala ndi bwenzi lawo gulu limodzi kapena ayi. Awuzeni ndondomeko izi:

• Nonsemupatsidwankhaniimodziimodzi.Nkhanizindizosiyana.• Sankhanimunthummodzipagulupokutiawerengenkhaniyokwaanzakeonse.• Ngatigulukambirananiizi: - Kodi uwu ndi ubwenzi wokondana ndi wolemekeza Mulungu/Allah?

Chifukwa chiyani? - Ndi chiyani chimene awiriwa angachite kuti alimbitse ubwenzi wawo? • Sankhanimmodziyemweazafotokozezomwemwakambiranamukamaliza.

Khwerero 2: Awuzeni abwerere mmalo mwawo. Gulu lirilonse liwerenge nkhani yawo ndi kupereka mayankho awo. Ngati anthu akulephera kumvetsetsa nkhanizi, mungathe kugawana nawo mfundo izi zokhuzana ndi nkhani iliyonse:

Nkhani ya Rajab ndi Rachel• Ndiabwenziokondana.• Rajab ndi Rachel anakhala okhulupilika kwa wina ndi mzake, amayenderana,

amachitirana zinthu zabwino, amauzana mavuto ndi masomphenya awo ndipo amathandizana.

• AwiriwaamakondaMulungu/Allah.

> 1:15 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

• Pofunakulimbikitsaubwenziwawo,RachelatengerechitsanzochaRajabchomachita zina zake kapena kugula mphatso pofuna kumuonetsa bwenzi lake kuti ndiwoyamika komanso amamukonda bwenzi lakeyo. Izi zikuyenera kupitilira ngakhale mbanja.

• RajabndiRachelakuyenerakumayamikilana.

Nkhani ya Yankho and Yasimin• UwusiubwenziwoopaMulungu.• Samalemekezanakomansokuyamikilana.• Yankhondiameneakuonekakutiamayetsetsakutiubwenziwawouziyenda

bwino.• Yasimminsadziwakufunikakomalumikizana.• PofunakulimbikitsaubwenziwawoakuyenerakulolaMulungukukhalamu

ubwenzi wawo.• YankhondiYasiminakuyenerakuwonetsetsakutiakulumikizanakomanso

akumvetsetsana.

Nkhani ya Jacob and Amina• Inde,unaliubwenziwachikondi.• JacobndiAminaamakondanakwambirindipoalindinzeruzokhwima.• Palikulumikizanakwabwinopakatipawo.• Amalimbikitsanakutiakhalemunthuwabwino.• Palibechinyengo.• NdiowopaMulungundipokhalidwelawolikuwonetseraizi.

Nkhani ya Atikonda and Lonjezo• Inde,unaliubwenziwokondana.• NgakhaleLonjezoakuonekawachikondi,mwamunayuakufunikakusintha

chifukwa izi zingapangitse mkazi kumusiya. Zikhonzanso kuzakhala zovuta akaziwa mbanja. Mwachitsanzo,Atikonda akhonza kuzayamba kumamumenya Lonjezo.

• Pofunakukonzaubwenziwawopafunikakukumbutsidwaziphunzitsozachipembedzo chawo.

• AtikondandiLonjezoakuyenerakuwonetsetsakutiakulumikizanabe.

Khwerero 3: Funsani gulu:

• Ndinjirazinazitizimeneanthuwiriamenealipachikondiangaonetseranechikondi kwa wina ndi mzake. Perekani nthawi kuti aakambilane.

Khwerero 4: Magulu onse akagawana ndi amzawo zomwe anakambilana, funsani gulu lonse kuti awonenso nkhani ya Lonjezo ndi Atikonda. Funsani munthu modzi kuti awerenge ndipo kambilani mafunso awa:

• Ndinkhanzazamtunduwanjizomwezikuchitikamuchibwenzichimenechi?• Ndinkhanzazinazitizomwezimachitikaanthuakakhalapachibwenzi?• Kodianthuawiriokondanaangapewebwanjikutinkhanzazisachitikemu

chibwenzi chawo? Nanga ngati nkhanzazo zikuchitika angazithetse bwanji?

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:16

Khwerero 5: Ombani mkota pa zokambiranazi potsindika mfundo izi:

• UbwenziwokondanaumeneumalemekezaMulungu/Allahndiumenebwenzilakolo limaika patsogolo zokonda zako.

• Ngatibwenzilanusilikusonyezakudziperekapaubwenziwokondanandiwolemekeza Mulungu/Allah musanalowe m’banja, nkovuta kuti angadzasinthe mutalowa m’banja.

• KumbukilanikuyankhulanandikofunikakwambirimuubwenziwoopaMulungu/allah. Ngati kyankhulana kapena kulumikizana palibe kapena ngati kuyankhulanaku kuli kochepa mu ubwenzi ndi chizindikilo chakuti zinthu sizili bwino. Awiriwo ayenera kuthana ndi vutoli koma akapanda kutero vutoli likhonza kuzapitilira mpaka mbanja zomwe zingazakhale zoopsa.

• Palimitunduyosiyanasiyanayankhanzazomwezimachitikapachibwenzi.Achinyamata ayenera kupewa kuti nkhanza zimenezi zisawachitikile.

• Achinyamataomwealipachibwenziayenerakudziwakutikusemphanakapena mikangano ingathe kuchitika ngakhale mu ubwenzi oopa Mulungu/Allah. Mmene angachitile ndi kusemphana naku kapena mikanganoyi zingathe kuthandiza kulimbikitsa ubwenzi wawo kapena kuuononga. Ena amachitila nkhanza okondedwa wawo akakhala kuti asemphana mu ubwenzi wawo.

• Achinyamataomwealipachikondiwaakuyenerakukambilanamomasukangati mu ubwenzi wawo mukuchitika za nkhanza komanso angathe kupita kwa alangizi kuti akawathandize. Ngati nkhanza zikupitililabe , wochitilidwa nkhanzayo angathe kuthetsa chibwenzicho.

ZopemphereraNgati abwenzi Pemphererani:• ChitsogozondichitetezochaMulungukutimusankhebwenzindichitsogozocha

Mulungu ndikuti ubwenzi wanu ukhale olimba• ChikondichaMulungu/Allahmuchiyanjanochanu.

Malemba Owerenga1 Akorinto 13:5, 15:33Aefeso 4:26Miyambo 18:22Korani 40:42Korani 42:43Koran 3: 134Korani 7:199

Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale kwa iye) anati: Mulungu wa mwambamwamba ndi wachifundo ndipo amakonda kuchitirana chifundo komanso amalipira zabwino, kulolerana koma sadzamupatsa madalitso ochitila zoipa kapena china chilichonse chofananila ndi icho.

> 1:17 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

NKHANI ZA NTCHITO 4:

Nkhani yoyamba: Rajab amakhalamdera lotchuka kwambiri kumene amagwira ntchito. RajabanafunsirabanjakwaRachelyemweamakhalamdera linakutalindikumenekumakhalaRajab.Analipaubwenziwokhazikikandipomakoloawoankazidziwa.NgakhalekutiRajabamakhaladeralina, wakhala wokhulupirika kwa Rachel. Amamuyendera ndi kumamuguliramphatso. Nthawiyokumbukira kubadwa kwake, amamudzidzimutsa ndi mphatso ndipo nthawi zina amamukonzera maphwando. Atsikana ambiri akhala akumuyesa kuti amusokoneze pachikondi chake kwa Rachel koma zakanika. Rachel nayenso wakhala wokhulupirika kwa iye. M’modzi mwa mabwana a pa kampani imene iye amagwira ntchito wakhala akumufunsa kuti agone naye kuti amukweze pa ntchito. Koma iye yankho lake nthawi zonse ndi ‘’toto’’, chifukwa anapanga kale chiganizo chokhala ndiRajab.AmamukondaRajabkwambiri;amakhalaakumuimbirafoni,kungofunakumudziwitsakutiamamukonda.Amauzanamavutoawondipoamathandizanakupezanjirazowathetsera.Onsendi okhulupirika ku chipembedzo chawo.

Nkhani yachiwiri: Yankho ndi Yasimin onse ali ku sukulu ya ukachenjede. Ali pa ubwenzi wokhazikika ndipo alonjezana kuti adzamanga banja. Yasimin ali ndi mavuto pa kulumikizana kwao. Sakonda kugawana zofuna zake ndi bwenzi lakelo. Pamene Yasimin akufuna kuchita kanthu kapena kupita kwina kwake, amangodzipangira yekha osauza bwenzi lakelo. Tsiku lina Yasimin anapita ku South Africa kukagula katundu wa geni. Yankho anayesera kumuimbira foni, koma foni yake siimapezeka. Atabwerako sanasamare kuti amuimbire foni kumudziwitsa kuti wabwerako mpaka pamene Yankho anaganiza zomuyendera. Pamene Yankho anamufunsa chifukwa chiyani amachita zimenezi, yankho lake linali losavuta, “kodi ukuyenera kumadziwa kulikonse kumene ndikupita ndi zimene ndikuchita? Ndili ndi ufulu wochita zimene ndikufuna, kupita kulikonse kumene ndikufuna popanda kukuuza.”

Nkhani yachitatu: Yakobo ndi Amina ali pa ubwenzi wokhazikika ndipo amakondana kwambiri. Ubwenzi wawo wakula mwaphamvu kotero kuti agwirizana kuti amange banja. Yakobo ndi Amina amadziwa kuti nthawi ya ubwenzi ndi nthawi yodziwa mphamvu ndi zofooka za wina ndi mnzake. Nthawi zonse pamene Yakobo waona cholakwika mwa Amina, onse amakhala pansi ndi kukambirana. Amina alibe vuto lirilonse ndi Yakobo kuti amamudzudzula pa zofooka zake. Nayenso amachita chimodzimodzi ndipo Yakobo nayenso alibe nazo vuto. Yakobo ndi Amina amanyadirana ndi kulimbikitsana pamene m’modzi wachita chabwino. Onse amalimbikira kupemphera.

Nkhani yachinayi: Atikonda ndi Lonjezo onse ndi okhulupilira ndipo amapita mpingo umodzi. Analonjezana kuti adzamanga banja akamaliza sukulu. Nthawi zonse Lonjezo akalakwitsa kanthu, Atikonda amalephera kuugwira mtima wake. Amakonda kulandira nkhaniyi molakwika monga kukwiya ndi kugwiritsa ntchito mau olakwika, kutukwana mkaziyo ndipo nthawi zina kumuopseza kuti amumenya. Pambuyo pa izi amakhala kanthawi osalankhulana kwa masiku oposa awiri. Mkwiyo wake ukazizira, amapitanso kwa mkaziyo ndipo ubwenzi wawo umapitilira. Lonjezo wakhala akudandaula ndi zimenezi koma sizinaphule kanthu.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:18

>Nthawi: Mphindi 40

Kukonzekera Kwa Padera Kwa Mlangizi

• Mugwiritsa ntchito ziganizo “zabodza” zomwe ziri kumapeto kwa ntchitoyi.Fufutani zomwe ndi zosayenera ndipo owonjezerani zomwe mukudziwa kuti ndi zofunikira ndi zatanthauzo.

• Mbali inayabolodi, lembani“ndikugwirizananazo”ndipombali ina lembani“sindikugwirizana nazo”

Zokambirana MwachiduleAchinyamata akambirana mfundo zokhuza zifukwa zimene anthu amayambira zogonana asanalowe mbanja kapena zifukwa zimene amaziletsela mpaka azalowe mbanja.

Zolinga• Kuwapatsambalionsekuganizilamwakuyazamaganizoawokapenamaganizoa

anthu ena okhuza kugonana ndi kuwalimbikitsa maganizowo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Afotokozereni zomwe achite: • Lero mukambirana zina mwa zifukwa zimene zimapangitsa anthu kugonana

kapena kuziletsa. • Palizinthuzambirizomwezimawapangitsaanthukuganizazogonana.Nthawizina

anthu amakanika kuti aganize bwinobwino. Izi zikambidwa mu ndime zotsatila.

Khwerero 2: Adziwenso izi:

• Pofunakukambiranamwakuyapankhaniyi,ndiwerengamfundozingapo.Izindimfundo zokhuza zikhulupiliro za anthu, palibe yankho loona kapena lolakwa ku mfundozi.

• Pa mfundo ili yonse, ngati mukugwirizana nayo, mukayime mbali imeneyalembedwa “ndikugwirizana nazo, ngati simukugwirizana nazo chimodzimozi.

• Mudzikakamizekusankhambaliosatikukhalapakati,ngakhalemaganizoanualia pakatikati. Anthu ochepa angathe kugawana maganizo awo ndi gulu lonse.

Khwerero 3: Werengani mfundo iliyonse.

• Mukawerenga,perekaninthawikutiachinyamataasankhembali.Lolanindemangaziwiri kuchokera ku mbali zonse.

• Kenako pitani pa mfundo ina ngakhale zokambirana zisanafike pamapeto.Werengani mfundo zambiri malingana ndi nthawi.

Ntchito 5: Kupanga chiganizo chodziletsa mpaka kudzalowa mbanja

> 1:19 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Khwerero 4: Mukamaliza kuchita izi, afunseni mafunso awa:

• Achinyamataamakhalandizifukwazosiyasiyanaakamasankhakuti azigonana kapena asamagonane. Ndi chifukwa chiyani kuli kofunika kwa

wachinyamata kuganiza bwino za zifukwa zake zomwe zinamupangitsa kusankha kuti asamagonane kapena azigonana?

Zopempherera:Pempherani ngati banja, kuti:• Mulungu/Allahakuthandizenikugonjetsamayeseroofunakugonana

musanalowe mbanja• Mulungu/Allahakukhululukireiwoameneanayambakalezogonana

asanalowe mbanja ndikupatsa mphamvu yoyambilanso mwatsopano.

Malemba:1 Akorinto 7:8-9 Genesis 39:5-20 Eksodo 20:14Korani 7:32Korani 24:33

Komanso Mtumiki wa Mulungu mtendere ndi madalitso zipite kwa Iye anati:Ee inu achinyamata amene akuona kuti angathe kukwatira,atero chifukwa kukwatira kumathandiza kupewa zinthu za dama koma kwa amene sangathe ayenera kumasala chifukwa kusalako zidzakhala ngati chishango kwa iwo.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:20

> Ntchito 5: Ziganizo

1. Ngati mtsikana amamukonda bwenzi Lake, akuyenera kuonetsera pogonana naye mnyamatayo.

2. Ndikuganiza kuti achinyamata onse amakhala ndi maganizo osakhazikika okhuzana nkhani za kugonana, amafuna kuchita zogonana komanso nthawi yomwe amakhala asakufuna.

3. Ndikuganiza kuti palibe vuto kumupatsa munthu ndalama kapena mphatso kuti ugonane naye.

4. Ndikuganiza kuti palibe vuto kuvomera kulandila ndalama ukagonana ndi munthu ngati ndalamazo ukuzifuna.

5. Ndikuganiza kuti mwamuna weniweni amakhala ndi akazi ambiri ogonana nawo.

6. Zithunzi zolaula za kanema komanso mumagazini zimapangitsa achinyamata kufuna kuchita zogonana.

7. Kumukakamiza wina kuti achite zogonana iye asakufuna, ngakhale usakumukakamiza pomugwira ndi chimodzimodzi kumugwiririla.

8. Ndi chabwino mtsikana kuchita chibwenzi ndi a bambo kuti azilandirako ndalama zogulira zomwe akufuna.

9. Ngati uli ndi chilakolako chogonana, ndibwino kupeza woti ugonane naye kuti uzimitse chilakolakocho.

10. Atsikana ambiri omwe ndimawadziwa amagonana chifukwa amamva kuti akuyenera kutero.

11. Achinyamata ambiri samafuna zogonana. Maganizo awowa samakhuzana ndi nkhani ya Edzi kapena mimba kapena zomwe akulu akulu amawawuza. Iwo samafuna zogonana ngakhale atakhala ndi chibwenzi.

12. Si cholakwa kugonana musanakwatiwe ngati ukufuna kukhalabe mu gulu limodzi ndi anzako.

13. Ambiri omwe amapezeka kuti agonana, amamva chisoni ndi zomwe anachita.14. Ambiri omwe amapezeka kuti agonana, samamva chisoni ndi zomwe anachita.15. Achinyamata ambiri asanagonane amakambilana kaye ndi okondedwa

wawo ngati onse ali omasuka ndipo akufuna kugonana komanso momwe angazitetezere ku HIV, matenda opatsilana pogonana ndi mimba.

> 1:21 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

>Nthawi: mphindi 30

Zokambirana MwachiduleAchinyamata apitiliza kukambirana nkhani zokhuza kugonana asanalowe mbanja, maka pokhudzana ndi matenda a Edzi. Achinyamata afunsidwa kunena ubwino wakudziletsa, komanso zotsatila zakugonana asanalowe mbanja.

Zolinga• Kumvetsetsaubwinowakuziletsaachinyamataasanalowembanja.• Kukambiranazotsatilazakugonanaasanalowembanja.• Kupezanjirazomweachinyamataangatsatekutiasagonaneasanalowembanja.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni achinyamata kuti:

• Lerotipitilizakukambilanazakugonanaachinyamataasanalowembanja,kuyang’ana ubwino wa kuziletsa ndi zotsatila zakugonana asanalowe mbanja.

• Ndiwerengankhaniyaachinyamataenaomweamasinkhasinkhakutiazigonanakapena ayi.

Khwerero 2: Agaweni achinyamatawa mu magulu anthu apakati pa 3 kapena 4.

Khwerero 3: Werengani mokweza nkhani ya Nagama ndi Balani kwa anthu onse.

Khwerero 4: Mutawerenga nkhaniyo, awuzeni kuti akambirane mafunso ali m’musiwa. Mungathe kuwagawa mafunsowa mofanana mumagulu onse malingana ndi nthawi.

• Mukuganiza kuti chinamupangitsa Nagama ndi Balani kugonana asanalowem’banja ndi chiyani?

• Mukuganizakutizotsatirazaganizolizinalizotani?Ndizotsatirazinazitizimeneachinyamata angakumane nazo ngati agonana asanalowe m’banja?

• Achinyamataangatanikutiapewekugwamuvutoli?• Mungawalangizemotaniabwenziameneayambakugonanaasanalowem’banja

ndipo akufuna kusiya mchitidwewu?• Paliubwinowotanipakudziletsakufikirakulowam’banja?• Ndizovutazitizomwezingapezekepakudziletsa?

Ntchito 6: Ubwino wodziletsa ndi zotsatira za kugonana musanalowe m’banja

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:22

Khwerero 5: Gulu lirilonse lipereke ku gulu lonse zimene akambirana.

(chidziwitso kwa mlangizi: ngati maguluwo atchula HIV ngati chimodzi mwa zotsatira kapena zovuta, auzeni kuti pakhala nthawi yapadera yokambirana za HIV patsogolo pa zimenezi. Ngati satchula, fufuzani kuti pa zochitika zakutsogolo zidzatsindike mfundoyi.)

Khwerero 6: Malizani zochita ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Mulungu anapereka lamulo lakuti achinyamata asagonane asanalowe mbanjachifukwa chachikondi chomwe ali nacho pa ife.

• Mukagonanamusanalowembanjamumatayamphatsoyamtengowapataliyomwemukanazamupatsa bwenzi lanu-unamwali.

• Kugonanamusanalowem’banjanditchimopamasopaMulungu.• Kugonana musanalowe m’banja kungabweretse mavuto monga kukhala ndi

pathupi posakonzekera, matenda opatsirana kudzera mchiwerewere kuphatikizapo HIV, kukhumudwa, kukayikirana, kudzida, kunyozeka, kudzimvera chisoni ndi manyazi. Zingabweretsenso manyazi ndi mnyozo kwa makolo, abale ndi chipembezo.

• Kukhala ndi chilakolako cha kugonana sikutanthauza kuti muyenera kuchitachiwerewere. Palibe choipa chimene chingakuchitikireni ngati simugonana. Kudziletsa mpakana muzalowe mbanja ndi njira imodzi yosunga malamulo a Mulungu/Allah komanso kulemekezana wina ndi mzake.

• Mulungu/Allahanatilonjezakutipamayeseroaliwonseamatipatsanjirayothawirakotero kuti kupambana ndikotheka nthawi zonse. Ndi chithandizo cha Mulungu/Allah abwenzi angathe kugonjetsa mayesero ofuna kugonana asanalowe m’banja.

• Kukamizidwandianzawokapenakuwerengandikuoneramawailesiakanema zimabweretsanso mavuto kwa achinyamata. Koma kuyamba zogonana ndi ganizo limene aliyense amapanga payekha ndipo mutha kupeza anthu amene angakulimbikitseni pa chisankho chanu, osati kukukakamizani kuyamba zogonana. Kuonjezerapo masewero olimbitsa thupi monga mpira, wa miyendo, wamanja kapena kuyenda, kuwerenga kapena kuganizila zinthu zina zingathandize kugonjetsa zilakolako.

• Amenealipachibwenzichodziwikangatianayambakugonana,angathekusiyandi kuyamba kudziletsa mpaka atalowa m’banja.

ZopemphereraPempherani ngati abwenzi kuti:• Inuyondibwenzilanumuzithakukambiranazinthumomasukakutimungathe

kudikila mosangalala osagonana pomvera mawu a Mulungu.• Mulunguakuthandizenikuthanandizilakolakozofunakugonanampaka

muzalowe mbanja.

Malemba OwerengaKoran 12Korani 6: 153Korani 5:2Luka 1:27-282 Samueli 131 Akorinto 15:33

> 1:23 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

> Nkhani ya Balani Ndi Nagama

Nagama anabadwa m’banja la ana asanu, atsikana atatu ndi anyamata awiri. Iye anali wachiwiri kubadwa ndipo anali wolimbikira ku sukulu. Ichi chinakondweretsa makolo ake kwambiri. Masomphenya ake anafuna kudzakhala dotolo. Nagama atasankhidwa kupita ku sukulu ya sekondale, anagwa mchikondi ndi mnyamata wina wotchedwa Balani. Awiriwa, Nagama ndi Balani ankadziwa kuti kugonana asanalowe m’banja linali tchimo pamaso pa Mulungu/Allah ndipo anagwirizana kuti sadzachita zimenezi. Posachedwapa Balani wakhala akukopedwa ndi anzake kuti ayese kugonana ndi Nagama. Amamuuza kuti sangakhale ‘’mwamuna weniweni’’ pokhapokha atachita zimenezi. Ngakhale poyamba analimbikira kudziletsa, pang’onopang’ono zolankhula za anzake aja zinamugonjetsa. Nayenso anayamba kumulimbikitsa Nagama. Poopa kutaya mwamunayo Nagama anavomera kugona naye asanalowe m’banja.

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:24

> Ntchito 7: Kukambirana mwapadera za HIV ndi matenda opatsirana pogonana

Nthawi: Mphindi 30

Kukonzekera Mwapadera Kwa mlangiziAchinyamata angathe kukhala ndi mafunso ambiri okhuza HIV/Edzi. Pali mfundo zoonjezera kumapeto kwa bukhuli zomwe zingakuthandizeni kuyankha mafunsowo. Mungathenso kufunsa kapena kuyitana wachipatala ophunzira bwino kuti azayankhe mafunso omwe angakhale ovuta.

Zokambirana MwachiduleAchinyamata awona za HIV ndi matenda opatsirana kudzera pogonana monga zotsatila za kugonana mosaziteteza. Achinyamata alimbikitsidwa kuyezetsa magazi kuti awone ngati ali ndi HIV asanalowe mbanja ndi kukhala okhulupilika ndi cholinga choti akhale otetezeka komanso ateteza okondedwa wawo.

Zolinga• Kukambiranazaubwinoowoyezetsamagazindimatendaopatsilanakudzeramu

kugonana asanalowe mbanja.• Kukambiranaubwinoodziwammenemthupimwakomulirindikuwululangati

uli ndi kachilombo ka HIV.

Ndondomeko

Khwerero 1: Afotokozereni achinyamata kuti:

• Chimodzimwazotsatirazamchitidwewogonanamusanalowem’banja,ndiyekutenga HIV ndi matenda ena opatsirana kudzera pogonana.

• HIVimafalakwambirikudzeramukugonana.

Khwerero 2: Afunseni anthu awiri (abwenzi). Awuzeni omwe adzipereka kuchita sewero kuti:

• Akukonzekerakumangabanja.• Sanagonanepochikhalire.• AganizazokayezetsaHIVasanalowem’banja.• Zotsatirazikusonyezakutim’modzimwaiwoalindikachirombokaHIV.• Amenealibwinoyoawonekaokhuzidwakomaapangachisankhochopitilizabe

chibwenzi.

Khwerero 3: Akamaliza kuonetsa sewerero afunseni onse mafunso awa:

• Funsanianthuwoafotokozechimenechinachitikakutim’modzimwaawiriwaapezeke ndi kachirombo ka HIV.

• Kodimukuganizakutikunalikofunikakutiayezetseasanalowem’banja?

> 1:25 Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja

Khwerero 4: Ombani mkota potsindika mfundo izi:

• Ndikofunikakutiabwenzialimbikitsidwekupitakokayezetsamagazindi kulandira uphungu moyenera asanalowe m’banja limodzi, ngakhale asanakhalilepo limodzi:

o zikhonza kutheka kuti m’modzi mwa abwenzi apezeke ndi HIV ngakhale kuti awiriwo amadziletsa. Akhonza kukhala kuti anabadwa nayo HIV kapena anagwiriridwa.

o zikhonza kutheka munthu kukhala wokhulupirika kwa bwenzi lake koma ndi kumakagonana ndi anthu ena.

o Komanso zikhonza kutheka kuti m’modziyo anakatenga kachiromboka asanakumane ndi mnzakeyu ndipo samadziwa.

• Kusankhakupitirizakukonzekerakumangabanjapamenem’modziwapezekandi HIV kumakhala m’manja mwa awiriwa.

• NgatimmodziwaanthuomwealipachibwenzialindiHIVndikofunikakuululamomwe m’thupi mwake muliri kwa bwenzi lake.

• Kuululamoyowakowakalekuyenerakuphatikizapozinazimenemukuonakutiwokondedwa wanu akuyenera kudziwa monga; ngati muli ndi mwana, kapena ngati munatengapo matenda opatsirana pogonana kapena ngati munakwatiwapo.

• Abwenziwaakuyenerakuzindikirakutindikofunikakukayezetsamatendaopatsirana pogonana. Ngati munthu ali ndi matendawa m’magazi mwake zingathe kudzetsa mavuto kwa mwana amene akuyembekezeka kubadwa, kusabereka ndi mavuto ena.

• NjirayokhayoyodzitetezerakuHIVndimatendaenaopatsiranapogonanandikudziletsa basi.

• Akalowam’banja,njirayabwinokwambiriyopeweraHIVkulowamnyumbamwanu ndiye kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake.

ZopemphereraPempherani ngati abwenzi kuti:• Mulungu/AllahawapatsechiyembekezoachinyamataamenealindiHIV.• Mulungu/Allahaperekechilimbikitsochokanamakhalidweomweangayikeiwo

ndi okondedwa wawo pa chiopsezo.

Malemba Yesaya 1:181 Yohane 1:9Korani 39:9Korani 16:43

> Phunziro 1: Kusankha bwenzi lomanga nalo banja 1:26

> Kuomba mkota phunziro 1Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni achinyamata kuti: kusankha bwenzi lomanga nalo banja ndi chiganizo chofunika kuikapo mtima kwambiri.

Khwerero 2: Ombani mkota pa gawoli pofotokoza mfundo zomwe zakambidwa mu phunzilori zomwe ndi:

• KupempherandimtimaonsekutiMulungu/Allahawatsogolerepopangachisankho chimenechi ndi kutsogolera ubwenzi wawo.

• Kudziletsakumchitidwewogonanaasanalowem’banjakutialemekezemalamulo a Mulungu/Allah. Kudziletsa kuli ndi phindu lalikulu kuphatikizapo kupewa HIV.

• Kufufuzamakhalidweabwinoabwenzilomanganalobanja.• Ngakhalezingakhalezovutakuchita,panganiganizolothetsachibwenzingati

ngati mukuona kuti munthu yemwe muli naye pa ubwenzi simunthu wabwino.• TatsindikankhanizamatendaopatsiranapogonanandiHIV/Edzikomanso

ubwino womasukirana.

Ntchito ya Kunyumba: Auzeni achinyamata kuti apitirize kukambirana mitu iyi kunyumba kwao. Muwalimbikitsenso pa izi:-

• KufufuzandimezinazamuBaibulo/Koranizomwezikuperekamalangizoakasankhidwe ka bwenzi la banja.

• Kudziperekansopokhalaodziletsa.• Kukambiranamomweangapatsiraneulemupaubwenziwaondimomwe

ubwenziwu ungapitilire kukula mwa chikondi.• Kufunauphunguwinandichitsogozozomwezimaperekamwayiwokambirana

ndi kugwirizana.

Malemba OwonjezeraKorani 2:27, 221-228 Koran 8:30Korani 3:36Korani 2:2211 Samueli 16:71 Akorinto 5:1, 6:13-18, 10:81 Atesalonika 4:3Mateyu 7:7-8Genesis 24:1-67

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:1

Banja ndi mphatso yochokera kwa

MulunguBanja ndi kudzipereka kwa moyo wonse. Sitimalowa m’banja mongoyesera ayi. Pa chifukwa ichi, sibwino kulowa m’banja mwaphuma (Mateyu 19:6/Korani 30:21). Mulungu/Allah adalenga munthu ndi chilakolako choti azifuna kugonana.

Mu phunzilori anthu akumbutsidwa kuti banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah ndipo ndiloyenera kulilemekeza.

Pali zochitika zosiyana siyana zomwe ziri mu gawoli zomwe anthu alimbekitsidwe kutengapo mbali ndi cholinga chakuti amvetsetse zomwe zikukambidwa. Mu zochitika zina maanja afunsidwa kupanga timasewero, pomwe muzochitika zina akhala magulu kukambirana kuti amvetsetse bwino kuti banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah. Pamapeto pa gawoli maanja amvetsetsa za kufunika kokondana.

Phunziro 2

> 2:2 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

> Phunziro mwachiduleAnthu ofunika kuwafikilaZochitika za mu phunzilori ndi za omwe ali mbanja kale

Ndondomeko ya phunziro 1. Mutu 2. Phunziro mwachidule3. Kutsegulira phunziro 24. Miyambo ya makolo5. Banja ndi chani?6. Ntchito zomwe Amayi ndi Abambo amagwira7. Kudzipereka mmoyo wa mbanja8. Kukondana ndi wokondedwa wanu9. Kuomba mkota pa gawo10. Ntchito ya kunyumba11. Malembo

Nthawi yofunikaMa ola awiri ndi mphindi 55

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera3. Zolembedwa zina pa za malumbiro a ukwati

Zokonzekera za mlangizi1. Werengani mndandanda wa zokambirana nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zogwirizana ndi mutu komanso

zolembedwa zoonjezera.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:3

> Kutsegulira phunziro 2

Nthawi: Mphindi 20

Malangizo apadera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati mudakumana ponso kale , akumbutseni maanja kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Phunziro lonse mwachiduleMaanja afotokozeredwa za phunziro la banja-Mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah. Awunikirana za ntchito zomwe amayi ndi abambo amagwira mbanja, ndikukumbutsidwa za malumbiro a ukwati ndi momwe angawonetserane chikondi kwa wina ndi mzake. Akambirananso za HIV ndi EDZI.

Zolinga zaphunziro• Kumvetsetsabwinozakufunikakwabanjalomwendimphatsoyochokerakwa

Mulungu/Allah.• KumvetsetsazomweBaibulo/Koranizimanenapazabanja.• Kumvetsetsazantchitozomweamayindiamamboamagwiram’banjandi

momwe angaonetserane chikondi.

Ndondomeko

Khwerero 1: Alandireni anthu onse ku zokambirana. Afotokozereni kuti akhala ndi mwayi ophunzira zokhuza banja.

Khwerero 2: Fotokozani za phunziro la banja-mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah pofotokoza mfundo izi: • Banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah Kulengedwa kwa banja

kunalembedwa mu Baibulo ndi mu Korani. banja silinayambitsidwe ndi munthu, Mulungu/Allah ndiye analikhazikitsa.

• Mulungu/Allah analenga mwamuna kenaka anapanga mkazi womuthangatira.Malinga ndi chikonzero cha Mulungu/Allah, mwamuna ndi mkazi pamodzi amapanga thupi limodzi. Mwamuna kapena mkazi payekha payekha ndi gawo limodzi la thupili.

• PaChisilamu,ukwatiwamwamunandimkazisichikonzerochandalamakapenakungofuna kukhala limodzi koma mgwirizano woyeretsedwa, mphatso ya Mulungu/Allah, kutsogolera mtundu wosangalala, moyo wokondwa ndi kupitiriza mtunduwo. Mgwirizano woyeretsedwawu ndi pangano lolimba (mithaqun Ghalithun). Cholinga chachikulu cha banja pachisilamu ndi kuzindikira bata ndi kukhudzidwa PAKATI PA mwamuna ndi mkazi

• PaChikhristuukwatindiubaleofunikaumeneufanizidwandiubaleumeneulipakati pa Khristu ndi mpingo. Mwamuna ndi mkazi ali ndi udindo wawo pabanja. Mwamuna akuyenera kukonda mkazi wake monga momwe Khristu amakondera mpingo wake ndi kuufera. Chimodzimodzinso, mkazi ayenera kumvera mwamuna wake. Cholinga chachikulu cha ukwati wa chikhristu ndi kuti awiriwa alemekeze Mulungu pa banja lawo.

> 2:4 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

Khwerero 3: Awuzeni maanja kuti:

• Atenganawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizakutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse.

• Akhalandimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momweamaonera zinthu komanso mfundo zina zofunkira.

• Maanjaaphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo

Khwerero 4: Afunseni maanja:

• Kodiakuyembekezakupindulachiyanikuchokeramkukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

Khwerero 5: Afunseni onse kuti:

• Ndimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakutipalibeyemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi dzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza banja. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupeza/kuunikazikhulupiliromiyamboyosiyanasiyanandizinazomweanthu

samazimvetsetsa zokhuza banja. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizemaanjakukhala

okondwa.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja akambirana za zikhulupiliro ndi zoyankhulidwa zokhuza banja. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti afotokozepo miyambo ina yamakolo kapena nkhambakamwa zokhudzana ndi banja. Apatseni nthawi yokambirana.

Khwerero 3: Mfundo zina zomwe anthu angatchule zingathe kukhala ngati zomwe ziri mumsimu. Werengani zomwe sizinatchulidwe.

• Akazindiameneayenerakugwirapafupifupintchitozonsezapakhomo.

• Akaziayenerakukhalaongomvera,sayenerakukhalandimphamvuzofananandi

amuna.

• Akazindiwopandapake/apansindipoamunandiapamwamba/ofunikila

kwambiri.

• Banjacholingachakendikuberekaana.

• Mamunasakuyenerakumasamalaanaake.

• Kumenyanandimankhawalaabanjaomweamalipangabanjakukhalalomba.

• Zambanjazisakakambidwekunjangakhaleukuzunzidwa.

• Mkaziwakokapenamamunawakosimbalewako.

• Chiyanjanochabanjachingathekuchithetsanthawiinailiyonseyomwewina

wafuna.

> 2:6 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilanazi pofotokoza mfundo izi:

• Mulungu/Allahanalengamwamunandimkazichimodzimodzi,palibeamenealiwapamwamba kuposa mzake.

• Anthu akuyenela kudziwa kuti banja ndi chiyanjano cha moyo wonse ndiposakuyenera kulitenga mwamasewera ndikuthamangila kukwatiwa/kukwatila.

• Amayi ndi abambo ayenera kuthandizana kugwira ntchito pakhomo. Baibulolimanena kuti Mulungu analenga mkazi ngati wothangatila osati ochita zonse yekha.

• AnandimdalitsoochokerakwaMulungu,choteroamayiasamatengedwengatimakina opanga ana. Thanzi la mayi limakhala pa chiopsezo ngati abereka ana ambiri.

• Mulungu akuyembekezeramwamuna ndimkazi kukhala okondanamonga iyeamatikondera ndipo amaleza nafe mtima. Chotero kumenyana sikungakhalepo ngati anthuwo akukondana ndipo kumenyana sikukuyenera kutengedwa ngati mankhwala omanga banja koma chida chopasula.

• Zinthuzinazambanjazikuyenerakunenedwakwaenakutiaperekepomalangizo.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulungu/Allah akuthandizeni kutsutsana ndi miyambo, nkhambakamwa ndi

zoyankhulidwa zomwe zili zotsutsana ndi mau a Mulungu komanso zomwe zingabweretse mavuto mbanja.

Malembo OwerengaGenesis 1:27Mateyu 19:5-6Korani 49:13

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: mukufuna ndikuzeni za paradizo? Kumeneko munthu wina aliyense amene ali wofooka ndi wodzichepetsa: akapanga lumbilo kwa Mulungu, Mulungu adzakwaniritsa lumbilo lake.

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:7

> Nthito 2: Kodi banja ndi chiyani?Nthawi: mphindi 20

Zokambirana MwachiduleMaanja akhala ndi mwayi okambirana kutanthauza kwa banja ndi momwe iwo amamvetsera mau a Mulungu/Allah.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakutibanjandichani.

Ndondomeko

Khwerero 1: Afotokezereni maanja: Tsopano tiyamba kuyang’ana pa mawu akuti banja ndi kufufuza kuti akutanthauza chani kwa ife tonse.

Khwerero 2: Agaweni onse mumagulu ang’onoang’ono a anthu anayi (magulu okwana maanja awiriawiri)

Khwerero 3: Funsani anthu kuti ayerekeze kuti akukumana ndi alendo kuchokera ku dziko linalake amene sanamvepo za ukwati.

• Awuzeniafotokozekutiukwatiumatanthauzachiyanikwaiwo.• Akonzekerekuzafotokozakugululonse.

Khwerero 4: Uzani gulu lirilonse kuti lipereke zimene lakambilana.

Khwerero 5: Kambiranani mpaka gulu lonse ligwirizane chimene chimapanga banja. Magulu onse akafotokoza zomwe anakambirana, kambiranani mafunso awa:

• Kodianthuamatibanjandichani?• Chasiidwandichani?Palinsochinachimenesichirigawolabanja?

Khwerero 6: Konzani zonse zomwe zingazetse mavuto m’banja ndi kuwonjezerapo mfundo izi ngati sizinakambidwe kale:

• Banjandichiyanjanochaanthuawiri.• Anthuomwealimbanjaakuyenerakulemekezana,kugawanachimwemwe,ndikukhala

omasukilana ndi cholinga chakuti athe kukwanilitsa zilakolako za wina ndi mzake.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• MukhalendiBanjalokondweretsaMulungu.• Muzigwirirantchitolimodzikutimulemekezane,kugawanachimwemwe.ndikukhala

omasukilana kuti muthe kukwanilitsa zilakolako za wina ndi mzake.

MalembaKorani 9:71-72; Korani 2:228; Mateyu 19:5-6

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: mukufuna ndikuzeni za paradizo? Kumeneko munthu wina aliyense amene ali wofooka ndi wodzichepetsa: akapanga lumbilo kwa Mulungu, Mulungu adzakwaniritsa lumbilo lake.

> 2:8 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

>Nthawi: Mphindi 35

Kukonzekera Mwapadera Kwa Mlangizi

• Papepalalimodzilembanintchitozosiyanasiyanazapakhomo.Panganimapepalaambiri malingana ndi kuchuluka kwa magulu.

• Dziwanintchitozomwemderalanuamatindizaamayikapenaabambo

Zokambirana MwachiduleMaanja akambirana za ntchito za amayi ndi abambo mbanja. Mothandizidwa ndi mau a Mulungu maanja awona momwe angathandizilane wina ndi mzake mbanja mwawo. Akambirananso momwe nkhaniyi ikukhudzilana ndi HIV/Edzi.

Zolinga• Kukambilanazantchitozomweamayindiabamboamagwirambanja.• Kuthandizamaanjakuonamomweamayindi abamboangathandizilanentchito

mbanja mwawo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni onse kuti:

• Tsopanotikambiranazantchitozomweamayindiabamboamagwiram’banja.• Ntchitozozimamvetsetsekamosiyanandimaderaathukomansobaibulo/korani.

Koma zokambirana zi zithandiza kuti tonse tigwirizane chimodzi.

Khwerero 2: Agaweni onse mumagulu a amuna ndi akazi ndipo gulu lirilonse likhale ndi anthu osapitilira asanu ndi m’modzi.

Khwerero 3: Apatseni anthu onse mapepala omwe mwalembapo ntchito za amayi ndi abambo. Funsani gulu lirilonse kuyankha mafunso awa:

• Ndintchitozitizomwezimatengedwakutindizamkazim’banja?• Ndintchitozitizomwezimatengedwakutindizaabambom’banja?• Kodintchitozizinagawidwamofananakwaamunandiakazi?Alindizambirindi

ndani? • Amunandiakaziangathandizanebwanjikugwirantchitozi?

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulungu/Allah akuthandizeni kuti muzithandizana wina ndi mzake kugwira

ntchito zosiyanasiyana pakhomo.• Mulungu/Allah awapatse azibambomtimawodzichepetsa komanso kuti amayi

akhale ndi mtima othokoza pa zomwe amuna awo akuchita.

Ntchito 3: Ntchito zomwe Amayi ndi Abambo amagwira

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:9

MalembaKorani 30:211 Timoteo 3:2-72 Atesalonika 3:10Aefeso 5:25-29

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: Wina aliyense wa inu ndi mbusa,Ndipo wina aliyense wa inu ali ndi udindo pa anthu omwe ali pansi pa ulamulilo wake. (Bukhar)

> 2:10 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

Ntchito Amuna Akazi

Kulima kumunda/dimba

Kuchapa

Kuphika

Kuyamwitsa

Kulera ana

Kupita kuchigayo

Kupita kusikero ndi mwana

Kukhala pa ntchito

Kukonza mnyumba

Kusamalira matenda

Kukonza kuchipinda

Kulipirafiziyaana

Kuyambitsa zogonana

Kugula katundu wa myumba monga (mipando,

matebulo, wayilesi, wayilesi ya kanema dni zina)

Kugula ziwiya zakukhitchiti ndi zakudya (pots,

plates, shuga, Mchere, mapoto,ndiwo, Chimanga, etc)

Kusita

Kusamala pakhomo

Kugula zovala za ana

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:11

>Nthawi: mphindi 30

Kukonzekera Kwapadera Kwa Mlangizi• Konzanimapepalaolembedwamalumbiroaukwati

Zokambirarna MwachiduleMaanja awunikanso malumbiro aukwati ndi kuthandizana kuwamvetsetsa bwino. Akambirananso momwe kusunga malumbiro kungatetezere banja lawo ku HIV kapena kuwathandiza kukhala moyo wa chiyembekezo ngati atapezeka ndi HIV.

Zolinga• Kuwakumbutsamaanjazakupatulikakwamalumbiroaukwatindimomwe

angawagwiritsile ntchito.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti: Athandizana kuonanso malumbiro aukwati.

Khwerero 2: Gawani anthu mumagulu a anthu osaposera asanu ndi m’modzi (maanja akhale limodzi) Awuzeni magulu kuti akumbutsane malimbilo aukwati omwe anthu amapanga ndipo afunseni maguluwo kuti achite izi:

• Aunikemalumbilowondikukambirana.• Gululirilonselisankheanthuodzipereka(maanjaawiri)kutiapangesewero.• Banjalimodzilisonyezemomwelikusungiramalonjezoameneanapangapatsiku

laukwati wawo ndipo lina lisonyeze kulephera kusunga malonjezo. Apatseni mpata woyesera pambali.

Khwerero 3: Akatha kuyesera pambali abwere pamodzi ndi kudzasonyeza gulu lonse masewero awo.

Khwerero 4: Magulu onse akamaliza kuonetsa masewero awo, funsani anthu kuti akambirane m’magulu mwao zimene aona m’masewerowa:

• Maanjawoanasonyezabwanjikutiakusungamalonjezoawo?• Nangaamasonyezabwanjikutiakulepherakusungamalonjezoawo?• Ndichifukwachanianthuamakanikakusungamalumbiloaukwati?• Nangaakuyenerakuchitachiyanikutiasungemalonjezoameneanapangapatsiku

la ukwati wawo?• Ena mwa malumbilo a ukwati amanena kuti ndidzakhala okhulupilika,

ndidzakusamalila ndikukonda nthawi zonse. Kodi kusunga malonjezo amenewa kungathandize bwanji kupewa HIV kuti isalowe mnyumba mwawo?

Ntchito 4: Malumbilo a ukwati

> 2:12 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

Khwerero 5: Kumaliza ntchito ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Malonjezoaukwatindioyeretsedwandipoayenerakumvetsetsedwabwino,kulemekezedwa, kumbukiridwa ndi kukwaniritsidwa mmoyo wonse wa banja.

• Kukhalaokhulupilikakwawinandimzake,kukondanandikukangamilakwaokondedwa wathu kungathandize kuti HIV isalowe mnyumba.

• Mulunguanatilengatonsechimodzimodzi;palibeamenealiwapamwambakuposa mzake. Amayi ndi abambo akuyenera kuonana wina ndi mzake monga chifaniziro cha Mulungu.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguakupatsenimphamvundichitsogozokutimukwaniritsemalonjezoanu.

MalembaMateyu 19:6Rute 1:16Korani 4:25Korani 2:27

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:13

>Nthawi: mphindi 30

Zokambirana MwachiduleMaanja akambirana njira zomwe abambo ndi amayi angawonetserane chikondi ndi kuyamikilana wina ndi mzake ndi momwe angadzitetezere ku HIV kapena kukhala ndi chiyembekezo ngati atapezeka ndi HIV.

Zolinga• Kuthandizakulimbikitsachikondim’maanjandikupezanjirazamomwe

angawotserane chikondi kwa wina ndi mzake.

Ndondomeko Khwerero 1: Awuzeni zomwe achite. Afotokozereni kufunika kowonetsa chikondi ndi kuyamikila okondedwa wawo.

Khwerero 2: Agaweni anthu m’magulu a amuna ndi akazi osaposera anthu asanu ndi m’modzi pa gulu lirilonse. Afotokozereni kuti akambirana njira zosiyanasiyana za momwe angawonetserane chikondi kwa wina ndi mzake.

Khwerero 3: Funsani gulu lirilonse kukambirana: • Ndinjirazitizimenemungamusonyezerewokondedwawanukuti

mumamukonda?

Khwerero 4: Afunseni onse kuti abwere pamodzi ndi kufotokoza zomwe akambirana.

Khwerero 5: Onse akafotokoza zomwe anakambirana, funsani gulu lonse kuti likambirane izi:

• Kodipanalikusiyanapamomweabambondiamaianayankhira?• Ndinjirazitizimeneamaindiabamboangasonyezerechikondikwawinandi

mnzake?

Khwerero 6: Malizani ntchito ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Palinjirazambirizimenemwamunandimkaziangagwiritsentchitopofunakusonyeza chikondi kwa wina ndi mnzake kuphatikizapo: kukonzerana chakudya chabwino, kukhala limodzi kuchita zimene amakonda, kuyamikirana maonekedwe, kupatsana mphatso ndi kuuzana kuti ndimakukonda.

• Musaiwalekupangatizinthutimenetimakupangitsaninosekusekererandikumva kukondedwa.

• Onetsetsanikutimzanuyoakudziwabwinokutiinumumakondwerandi

Ntchito 5: Kukondana ndi wokondedwa wanu

> 2:14 Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu

• Onetsetsanikutimzanuyoakudziwabwinokutiinumumakondwerandizazing’onozimene amakuchitirani, monga kuchapa kapena kukonza pogona.

• Ngatimukuonakutinzanuakuonekaosasangalalandiokhumudwa,pezaninthawiyomukumbatira bwenzi lanu ndi kumufunsa chimene chavuta, mwina nthawi imeneyo amakhala akufuna chikondi chanu kwambiri. Ugwiritseni bwino ntchito mpata umenewu.

• Pakakhalakusamvanam’banjamo,mwamunandimkaziakambirane.Mwamunawopembedza amaika mkazi ndi banja lake lonse pamaso pa Mulungu/Allah mwini. Mkazi wopembedza amaika mwamuna ndi banja lake lonse pamaso pa Mulungu/Allah mwini. Amayenera kuika zofuna za banja lake pamwamba pa zofuna zake.

• MtumikiMuhamadi(Mtendereukhalekwaiye)anati,aliyensewainundim’busandipo aliyense ali ndi udindo pa zonse zimene zili pansi pa utsogoleri wake. Mtsogoleri ndi m’busa, mwamuna ndi m’busa pa banja lake ndipo mkazi ndi m’busa wa mwamuna wake, nyumba ndi ana

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulungu/Allahndichikondindipoakuyembekezeramabanjakukhalaokondana.

Chotero kondani ndi kusamalira okondedwa wanu kuti mukwaniritse zimene Mulungu amayembekezera.

• Mulunguakuthandizenikukhalandichikondichangwirokwaokondedwawanu• Mulunguathandizemaanjakukhalaamoyowopemphera.

Malemba1 Akorinto 13:1-13Aefeso 5:25-29Korani 30:21

Mtumiki wa Mulungu mtendere ukhale pa iye anafunsidwa kuti ndi zinthu ziti zimene zingamupangitse munthu kuti akalowe ku paradizo, ndipo anayankha, ‘ kuopa Mulungu ndi khalidwe labwino’ Anafunsanso kuti ndi zinthu ziti zomwe zingamupangitse munthu kukalowa ku jehena, ndipo anati; Pakamwa (ndi zoyankhula zake zoipa) ndi maliseche pamene achita chiwerewere (Al Trimidhii)

> Phunziro 2: Banja ndi Mphatso yochokera kwa Mulungu 2:15

> Kuomba mkota wa phunziro 2Nthawi: mphindi 20

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti:

• KuliwonabanjangatimphatsoyochokerakwaMulungu/Allahzimathandizakulimbikitsa chikondi ndi kulemekezana m’banja.

Khwerero 2: Ombani mkota pa gawoli.

• Fotokozanikutitawonamakhwereroenaomwealiofunikakuwaganizilapokonzanso chiyanjano chawo wina ndi mzake komanso ndi Mulungu/Allah. Taona kuti:

• UkwatindimphatsoyochokakwaMulunguimeneiyenerakulemekezedwandialiyense.

• Palintchitozambirizaamunandiakazindipondikofunikakuthandizanantchitoz.

• Malonjezoameneanapangapatsikulaukwatiwawoayenerakutsatidwammoyowonse wa banja.

• Ndikofunikakuonetsachikondikwawinandimzake,kuyamikilanandikusamalana.

Ntchito ya Kunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana phunziro iri kunyumba. Alimbikitseni:

• Kukambutsanazamalonjezoameneanapangatsikulaukwatiwawo.Kodimukuwasungabe?

• Kambilananimomwemungayambirensokuwasunga.

MalembaKorani 4:1, 19,21Korani 4:34Korani 3:36Aefeso 5:22-29Genesis 1:26-28, 2:18, 23-25Masalmo 127:1Aheberi 13:4

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:1

Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

Kulankhula ndikugawana nzeru, maganizo, zolinga/kapena zokhumba pakati pa anthu awiri. Zimatanthauza kutumiza, kupereka, kapena kulandila uthenga. Kwa omwe ali pa banja , zikutanthauza kulankhulana pa zokonda ndi zodana nazo, zofuna ndi maganizo. Zikutanthauzanso kugawana zomwe wina akudziwa zokhuza umoyo.

Kulankhulana ndi kofunika mbanja. Mu phunzilo iri tiona za kulankhulana ndikuthandiza maanja, kumvetsetsa kufunika kwa kulankhulana mbanja.

Pali zochita zosiyanasiyana zolimbikitsa onse kutengapo mbali zomwe zithandize maanja kukambilana kufunika kwa kulankhulana, kuipa kwa kusayankhulana bwino, ndi ubwino wakulankhulana bwino mbanja. Zochitazi zithandiza maanja kuphunzira momwe angapititsile patsogolo kulankhulana kwawo mbanja.

Phunziro 3

> 3:2 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

> Phunziro mwachiduleOmwe akuyenera kuphunzira phunziro iri:Anthu omwe ali m’mbanja

Ndondomeko ya phunziro1. Mutu2. Phunziro mwachidule3. Kutsegulira phunziro 34. Miyambo ya makolo5. Moyo wokondwa wa mbanja6. Ntchito ya kulumikizana/kulankhulana mbanja7. Kulankhulana koyenera mbanja8. Chimachitika ndi chani ngati mbanja sakulankhulana9. Kukonzanso mmene timayankhulilana: mbali yoyamba10. Kukonzanso mmene timayankhulilana: mbali yachiwiri: kumvetselana11. Kuomba mkota12. Nthcito ya kunyumba13. Malemba

Nthawi Yofunika Maola atatu ndi theka

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani ndondomeko ya zokambirana nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zokhudzana ndi mutuwu komanso

zolembedwa zina.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:3

> Ntchito yotsogolera phunziro 3Nthawi: Mphindi 20

Malangizo apadera kwa Mlangizi Tsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati mudakumanapo kale , akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Phunziro lonse mwachiduleAlandileni maanja ku zokambilana ndikuwafotokozera kuti aphunzira za kulankhulana: makiyi achimwemwe mbanja. Maanja awona momwe kuyankhulana kwabwino kungalimbikitsile chiyanjano chawo ndi momwe kuyankhulana koyipa kungasokonezere chiyanjano chawo.Akambiolananso momwe izi zikukhuzilana ndi HIV/edzi.

Zolinga za phunziro 3• Kumvetsetsabwinozakufunikakwakulankhulanambanjandimomwemaanja

angalimbikitsile kulankhulana kwabwino m’banja.• Kuwapatsamaanjamalusoamomweangayankhulilanebwinondiokondedwa

awo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro la kulankhulana-gwero la chimwemwe mbanja- pofotokoza mfundo izi:

• Pafupifupibanjalirilonselimayambandichikondwelerochachikulu.Pamodzindi achibale awo, banja lirilonse limakhala ndi chiyembekezo ndi masomphenya a moyo wawo wosangalala kutsogoloko. Koma kukhala ndi banja losangalala sichinthu chophweka ayi. Chimwemwe cha mbanja ndi chofunika kwambiri.

• ChikonzerochaMulungu/Allahndichakutiawiriameneasandukathupilimodziakhale osangalala. Pakhomo pawo pakhale paradizo wamng’ono pansi pano.

• Pamutuunotionamfundozinazofunikakutsatangatitifunakukhalandibanjalosangalala ndi ntchito imene kuyankhulana kwabwino kumagwira polimbikitsa kusangalala. Awonanso momwe kuyankhulana kukhuzilana ndi HIV/edzi.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Atenganawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizakutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse.

• Akhalandimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momweamaonera zinthu komanso mfundo zina zofunkira.

• Aphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo.

> 3:4 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti: • Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku. Khwerero 4: Afunseno maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi dzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Ntchito: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kulankhulana mbanja. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupezazikhulupiriromiyamboyosiyanasiyanandizinazomweanthu

samazimvetsetsa zokhuza kulankhulana m’banja. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizekulankhulana

momasuka mbanja mwawo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiriro ndi zoyankhulidwa zokhuza banja. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti atchule zina mwa zikhulupiriro ndi miyambo zokhudza kulumikizana m’banja. Tikuyenera kusiyanitsa pakati pa mfundo ndi nkhambakamwa.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu.

• Amaiamalimbikitsidwakukhalachetendikumvetseraamunaawo.• Nkhanizabanjandizachinsinsi,osakauzawinangakhaleukuchitilidwankhanza

Khwerero 4: Ombani mkota pozakambilana zokhuza zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kulankhulana mbanja pofotokoza mfundo izi:

• Kulankhulanakulindimbaliziwiri,zomwezikutanthauzakutionseamayindiabambo ali ndi ufulu oyankhula za kukhosi kwawo.

• Onseakuyenerakulimbikitsidwakulankhulazakukhosikwawokutiakhalendibanja lokondwa.

• Nkhanizabanjazingathekukambidwandimunthuwinakapenawachibalewokhulupilika ngati banjalo likufuna malangizo apadela.

> 3:6 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Abamboazikondaakaziawondikuwapatsamwayiwoyankhulazakukhosi

kwawo.• Mulunguathandizemaanjakusiyamiyambo,nkhambakamwandizoyankhula

zomwe akhala akukhulupilira zomwe zili zosemphana ndi mawu a Mulungu.

Malemba Mateyu 19:5-6Genesis 1:27Korani 2:228Korani 30:21Korani 39:6

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: Dziko lapansi ndilosangalatsa koma chosangalatsa kwambiri ndi mkazi woopa Mulungu,’ kuonjezera apo Mtumiki mtendere ukhale pa iye anati “ yemwe wapatsidwa mkazi woopa Mulungu (mkazi wabwino), Mulungu wa mphamvu yonse wamuthandiza kukwaniritsa theka la chipembedzo chake; ndipo. Iye akuyenera kukwanilitsa mbali yotsalayo.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:7

> Ntchito 2: Moyo wachisangalalo m’banja

Nthawi: mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja akambirana mfundo zina zomwe zingathandize banja kukhala lokondwa. Mu ntchitoyi ayamba kukambilana za kulumikizana/kuyankhulana chomwe ndi chinthu chofunikila kwambiri kuti banja likhale losangalatsa .

Zolinga• Kuthandizamaanjakukhalaokondwapozindikirachinsinsichabanjalokondwa.

Ndondomeko

Khwerero 1: Afotokozereni maanja kuti:

• Abambondiamaiakuyenerakugwirantchitolimodziyokhazikitsabanjalachikondi ndi lokhalitsa.

• BanjalachikondindilaulemulingathekutetezaHIVkulowamnyumba.

Khwerero 2: Werengani mokweza nkhani ya banja lina limene linakondwelera kuti latha zaka makumi asanu liri m’banja:

Munthu wina ndi mkazi wake anakhala pabanja zaka makumi asanu. Momwe tsiku lokondwelera limayandikira, anakonza phwando. Akukonzekera mwambowu, anakhala pansi ndi kusinkhasinkha za zimene akumana nazo pa nthawi ya ukwati wawo zomwe zathandiza kuti akhale limodzi mpaka tsiku ili.

Khwerero 3: Kambiranani mafunso awa ndi gulu lonse:

• Ndizinthuzitizomweanakambilanapameneamakumbukilakutiathazaka50ali mbanja.?

• Mukuganizakutindizinthuzitizimenezinathandizilakutibanjaliakhalekwazaka 50 ali limodzi?

• Kodimukuganizakutizomweanakambilanakutindizomwezinawathandizakuti akhale mbanja zaka 50 zingathandize bwanji kupewa HIV kubwera m’nyumba?

Khwerero 4: Ombani mkota pa ntchito iyi pogawana ndi anthu onse mfundo angatsate pofuna kuti akhale ndi banja lokondwa ndikukhala limodzi kwa nthawi yayitali. Izi ndi zinthu monga:

• Kupemphera ndi kuwerenga mau a Mulungu/Allah pamodzi. Banja limenelimapemphera pamodzi limakhala pamodzi.

> 3:8 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

• Pezaninthawiyopitakoyendandikukhalalimodzipauwiripanu.Perekaninthawiyofanana ku ntchito ndi ku banja lanu. Onetsetsani kuti banja lanu likuyenda bwino. Nthawi zina, mungathe kupezeka kuti mukupereka nthawi yambiri ku ntchito ndi kuiwala banja lanu. Yesetsani kuti izi zisakuchitikireni.

• Kumvetsetsa kuti amuna ndi akazi ali ndi njira zosiyana za kulumikizana,maganizidwe osiyana, ndi makhalidwe osiyana kungathandize kukonza mavuto a m’banja lanu.

• Dziwanibwenzilanubwinolomwe.Ngatimudziwazimenemnzanusakondweranazo, mudzatha kupewa kuchita zimene zingamukhumudwitse mnzanuyo. Izi zidzamutsimikizira mnzanuyo kuti mumamuganizira, chinthu chofunika kwambiri pofuna kukwaniritsa banja lokoma.

• Lemekezanimaganizoawinandimnzakendipongatinkothekapanganiziganizolimodzi.

• Muuzenimoonakuti‘’ndimakukonda’’mwinakamodzikokhapatsiku.• Musaululezinsinsizam’banjamwanukapenakuzigwiritsantchitopamikangano

yanu.• Dabwitsananinditimphatsonditinatosonyezakuyamika.Izizimapangitsabanja

kukhala chinthu cha mtengo wapatali. Mphatso zimafunika zikhale zapamwamba ndiponso zodula kwambiri.

• Kumbukirani kuti muzonse ndinu mzimu umodzi, matupi awiri, kotero kutikumupweteka mnzanu ndiye kuti mwadzipweteka nokha.

• Khalaniodekhakwawinandimnzake.• Ngatititatsatiramfundozimenezi,nkobvutakutiHIVilowem’banjamwathu.

ZopemphereraPempherani kuti ngati banja:• Mulunguathandizemaanjakukhalaokondanakutiakhalendibanjalokondwa• Pempheranikutimaanjaachitepokanthukutiadziwanendikupewakuchitazinthu

zimene wina sagwirizana nazo.

MalembaMiyambo 15:1Aefeso 4:25Korani 2:228Korani 49:11, 13

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: Dziko lapansi ndilosangalatsa koma chosangalatsa kwambiri ndi mkazi woopa Mulungu,’ kuonjezera apo Mtumiki mtendere ukhale pa iye anati “ yemwe wapatsidwa mkazi woopa Mulungu (mkazi wabwino), Mulungu wa mphamvu yonse wamuthandiza kukwaniritsa theka la chipembedzo chake; ndipo. Iye akuyenera kukwanilitsa mbali yotsalayo.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:9

> Ntchito 3: Njira zinai zolankhulirana-kusalankhula, kulankhula mwamamvumvu, kusalankhula ndi kulankhula mwamamvumvu ndi kulankhula modekha

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja apitiriza kukambilana za ubwino wakulankhulana bwino mbanja ndi momwe izi zikukhuzilana ndi HIV/Edzi. Awonanso njira zinayi zolankhulilana ndikuwona kuti ndi njira iti yomwe iri yabwino ndi yothandiza.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakutiazilankhulamomasuka.• Kuwathandizamaanjakusankhakutindinjiraitiyabwinoyolankhulilanapakati

pa njira zitatu zomwe aphunzile.

Nndondomeko:

Khwerero 1: Fotokozani za zochitika: • Akambirananjirazinayizoyankhulirana.• Fotokozanikutimomweamalankhulirandiwokondedwawawozingathandize

kumanga banja lawo.

Khwerero 2: Fotokozerani za njira zinayi zolankhulirana:

• Anthu omwe sayankhula, ongoyankhula pang’ono kapena amangokhala chete. Panthawi yamkangano, amakonda Kukhala chete. Mwina amangosiya kulankhula, kuvomereza kuti alakwa ndiwo pofuna kuti nkhaniyo ingotha. Olankhula mwamphwayiwa amamvetsera koma osalankhulapo ayi. Amagonjera zonena za ena—amayembekezera kuti mwina ziwayendera popanda kunena kanthu. Amasiyira ena kuwapangira chisankho.

• Olankhula mwa mavuvu: Amayesetsa kuteteza kuti wina asawaloze chala. Salabadira kuti winayo akumva bwanji ndipo samvetsera bwino. Amakonda kupsa mtima ndikupondereza anzawo ndi malankhulidwe awo. Amafuna aliyense adziwe maganizo awo kupyolera mumayankhulidwe awo ndi ntchito zawo.

• Olankhula mwa mphwayi ndi mwamavuvu: Amalankhula mwamphwayi ndi mwa mavuvu momwe. Mwamaonekedwe amakhala ngati amphwayi koma machitidwe awo amakhala amavuvu. Akhoza kukana kulankhula ndi wokondedwa wawo kapena kuchita zinthu zina zokhumudwitsa wokondedwa wawo powonetsa ngati ali ndi chifundo. Ngakhale saonetsera mkwiyo, komabe ntchito zawo zimaonetsa kuti ndiwokwiya.

> 3:10 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

• Olankhula modekha: Awa amadziwa chimene akufuna kunena ndipo amachilankhula momveka bwino. Amafotokoza zomwe akumva ndikufuna. Amalankhula mosaonjeza, ndi mosachepetsa. Akamalankhula, saoneka moopseza.

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti alingalire pa njira zinayi tafotokozazi. Apatseni aliyense pepala:

• Afunsenikutialembekutindinjiraitiyomweamagwiritsantchito.Asalembedzina lawo, koma alembepo ngati ali amuna kapena akazi.

• Landiranimapepalawondikugawanazotsatirazondigulu.• Funsanigulukutiakambilane:

- Kodi azibambo akuoneka kuti amagwiritsa ntchito kwambiri njira yakuyankhulilana imodzimodzi yomweyo kuposa amayi?

- Kodi amayi akuoneka kuti amagwiritsa ntchito kwambiri njira yakuyankhulilana imodzimodzi yomweyo kuposa abambo?

- Ndi mavuto anji omwe angakhalepo mbanja ngati awiriwo akugwiritsa nthcito njira zoyankhulilana zosiyana? Mavuto amenewa angathetsedwe bwanji?

- Kodi maanja angagwiritse bwanji ntchito njira ya kuyankhulana modekha?

Khwerero 4: Ombani mkota pa ntchito iyi pofotokoza mfundo izi:

• Anthuomweamayankhulamodekhandiomwealiabwino.Amanenamaganizoawo ndikunena zinthu zomwe akufuna mopanda kumuweruza munthu winayo.

• Njirayabwinoyolankhulilanandiyolankhulamodekha.Chitsanzochakendikugwiritsa ntchito mawu akuti “Ineyo”

• Kulankhulanabwinokungalimbikitsekukhulipirikambanjachifukwakumawapatsa mpata anthu omwe ali mbanjawo kuthetsa mikangano yawo ndi kukambilana zofuna zawo-kotero mmodzi wa iwo kapena onse awiri sangatuluke kunja kukafuna wina yemwe angawoneke ngati akuwamvetsetsa bwino.

• Kulankhulabwinokumalimbikitsachikondikwawinandimzake-yankhulalanizowona mchikondi.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguathandizemaanjakukhalaodekhandizofookazawinandimzake.• Maanjaaphunzirekulankhulanawinandimzakemwachikondindi

molemekezana.

MalembaMiyambo 15:1Aefeso 4:25Korani 42:43Korani 3:159Korani 2:263

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: amene ali wabwino pakati panu ndi amene ali wamsangala ndi ololerana ku banja lake ndipo ine ndine wabwino ndi wamsangala kwambiri pakati pa inu ndi anthu akubanja langa.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:11

Zina zokhudza ntchito 3

Kulankhula koyamba ndi mau akuti “Iweyo”-Mamuna kwa mkazi wake:“Ndiwe wa ulesi, sumasesa mnyumba, umaphika chakudya changa mochedwa komansoana mangolira ali osasamba. Sindikudziwa kuti ndi chifukwa chani ndinakwatila iweyo. Ukuyenera kuyamba kulimbikila kugwira ntchito kuyambira lero

Kulankhula koyamba ndi mau akuti “Iweyo”- Mkazi kwa Mamuna wake:

“Umakonda kubwera pakhomo mochedwa. Sumasiya ndalama zogulira chakudya. Sumandithandiza kusamala ana. Sindikudziwa kuti ndi chifukwa chani ndimakhalabe ndi iwe. Ukuyenera kusintha khalidwe lako kuyambira lero.”

Kulankhula koyamba ndi mau akuti “Ineyo”-Mwamuna kwa mkazi wake:

“Ndikafika pakhomo ndimakhumudwa chakudya chikakhala kuti sichinaphikidwe,mnyumba ndimosasesa, ana akungolira komanso ndi osasamba.Ndikufuna tikambilanemmene tingakonzere zinthu kuti chakudya chiziphikidwa nthawi yabwino komanso ana akhale osangalala. Mmene zilirimu sizili bwino.”

Kulankhula koyamba ndi mau akuti “Ineyo”- Mkazi kwa Mamuna wake:

“Mukabwera kunyumba mochedwa usiku, ndimakhumudwa chifukwa ndimafuna ndizikuonani,komansondikufunandalamazachakudyachaana.Ndikufuna tikambiranemmene tingakonzere zinthu kuti zonse zizikhala bwino.”

> 3:12 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

> Ntchito 5: Zotsatira zakulephera kuyankhulana

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana zimachitika mbanja ngati sakulankhulana/kulumikizana komanso momwe kulumikizana kukukhuzilana ndi HIV/Edzi. Akambilananso mmene kusayankhulana kungaonongere chikondi chawo komanso kukhulupirilana.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakumvetsetsavutolakusayankhulana.• Kulimbikitsakulankhulanamomasukambanja.

Ndondomeko

Khwerero 1: Yambani zokambila pofotokoza kuti:

• Kulankhulana/kulumikizanandikofunikakwambiri.• Mongamomwekulumikizanakungathandizekutibanjalikhalelosangalala,

kusayankhulana kapena kusayankhulana bwino kungathe kubweretsa mavuto mbanja.

Khwerero 2: Afunseni anthu onse kuti akambilane mafunso awa. (Perekani nthawi yokwanila yokambilana ndipo limbikitsani maanja ambiri kutengapo mbali.)

• Chingachitikendichaningatipalibekulumikizanakwenikwenipakatipaawiriomwe ali pa banja. Awuzeni kuti apereke zitsanzo zomwe akudziwa.

• Kusayankhulanakapenakulankhulanakoyipa,kungakhudzebwanjichikondi,kukhulupilirana kapena kukula kwa chiyanjano kapena kubweretsa HIV m’banjamo?

Khwerero 3: Ombani mkota ndi kutsendera pogwiritsa ntchito mfundo zikuluzikulu izi:

• Kuvutakwakulumikizanakumasokonezachilichonsem’banja.Kumaonongamaziko aubalewu munjira zosiyanasiyana, kusokoneza zimene awiriwo akanatha kuchitira limodzi.

• Kuyankhulanakukasokonekera,kumakhalakovutakudziwazomweokondedwawako akufuna. Izi zimapangitsa onse kapena mmodzi kukhala osakondwa komanso kuganiza zokapanga chibwenzi zomwe zingapangitse kuti HIV ilowe mnyumbamo.

• Kulumikizanakumathandizaubalekutiupitepatsogolondipokumafunikakusintha pamene anthu akusintha m’banjamo.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:13

• Mmusimumulizinamwazomwezimachitikamukakhalakutimbanjamulikusayankhulana:

- Kusakhulupilirana: popanda kuyankhulana kwenikweni, mwamuna ndi mkazi sangathe kulimbitsana mitima ndipo izi zimaonjezera vuto la kusakhulupilirana.

- Chinsinsi: kusowa kwa kulumikizana kutanthauza kuti ndi mavuto ochepa amene amakambidwa ndipo amayamba kubisirana mavuto ambiri.

- Kukhulupilirana: kusalankhula kumasonyeza kusakhulupilirana, pakuti aliyense sakufuna kumumasukira mnzake pa zimene akuganiza.

- Kutalikirana: mwamuna ndi mkazi amene sakulankhulana amakhala akutalikirana. Amatalikirana kotero kuti chikoka chimatha ndipo banja limagwedezeka kwambiri. Modzi kapena onse awiri amapeza wina amene angathe kumumasukira. Izi zimachulukitsa chiopsezo chobweretsa HIV mnyumba.

- Kutayilira: popanda kulumikizana, banjali silitukuka. Kutayilira kumalowelerapo, zotsatira zake ndikuti banja silitukuka.

ZopemphereraPempherani ngati banja: • Kutipakhalekusinthapamomweamayankhulilanandicholingachotibanjalo

likhale lolimba.

MalembaMiyambo 15:1Aefeso 4:25Korani 42:43

> 3:14 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

>Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja awona zinthu zomwe akuyenera kuziganizila akamayankhulana ndi okondedwa wawo, monga nthawi yoyankhulirana. Awonanso kulankhulana posagwiritsa ntchito mawu ndi momwe angaonetsele chikondi kwa wina ndi mzake poyankhula osagwiritsa ntchito mawu. Apitiliza kuwona momwe kuyankhulana kumalumikizilana ndi HIV/Edzi.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakumvetsetsazakufunikakoyankhulananthawiyabwino

ndi malonso abwino.• Kuwathandizamaanjakumvetsetsazammenekulankhulakosagwiritsantchito

mau kungalimbikitsile chikondi kwa wina ndi mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti:

• Tipitilizakukambilanapaphunzilolakulankhulana.• Awonamomwekuyankhulanamosagwiritsantchitomawukungalimbikitsile

amayankhulilana pogwiritsa ntchito mau komanso posagwiritsa ntchiyo mau.

Khwerero 2: Awuzeni kuti tsopano apanga sewero. Fotokozani ndondomeko yake ya sewero.

• Anthuodziperekaasankhidwakuchokeramugululo.Odziperekawaakhalemaanja.

• Banjalirilonselifunsidwakupangaseweropogwiritsantchitomfundozomweapatsidwe limene adzaonetse ku gulu.

• Apatsenimphindikhumindizisanu.Anthuenaotsalawoangathekumaimbanyimbo kapena kupanga zinthu zina. Asadziwe masewero amene enawo akufuna kuonetsa.

Khwerero 3: Funsani anthu odzipereka (maanja) kuchokera mgulumo omwe apange sewero lomwe ligwiritsidwe ntchito pazokambilana za ntchitoyi. Apatseni nkhani izi maanjawo:

1. Funsani mwamuna kapena mkazi kuti auze mnzakeyo sakukondwera ndi momwe mnzakeyo wavalira. Anene izi mwachikondi, nthawi yoyenera ndi malo oyenera ncholinga chakuti zisamukwiyitse winayo.

2. Funsani banja linalo kuti achite izi mosiyana ndi enawo kuti akhumudwitsane. Mwamuna kapena mkaziyo akhale okwiya ndipo alankhule mokalipa komanso pa nthawi ndi malo osayenera.

Ntchito 6: Kupititsa patsogolo kulumikizana- Gawo I

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:15

Khwerero 4: Afunseni maanjawo kuti awonetse masewero awo kwa gulu lonse. Akaonetsa funsani gulu kukambilana izi:

• Mwaonapochiyanipakulankhulanakwamaanjawo?• Kodiyemweamayankhulidwayoanamvazomwemzakeyoamanena?• Kodichinapangitsakutienawoalyankulanebwinondichiyani?Nanga

chinalepheretsa enawo kuyankhulana bwino ndi chiyani? • Chimeneanayenerakuchitandichiyanikutiamvanebwinopopanda

kukhumudwitsana? • KumbukiranikutikulankhulanakoyenerakungatitetezekumatendaaHIV/Edzi.

Khwerero 5: Kumaliza zokambirana ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Tonse tikuyenera kuona momwe timayankhulira ndi wokondedwa athu ndipotiyetsetse kukonza momwe timayankhulira.

• Ngati tikufuna kungomenyana, nthawi iliyonse ilibwino. Koma ngati tikufunakukonza zinthu, nthawi ndi mau ake ndi zofunika kusankha mosamala. Kuyankhulana kwa maanja kumayamba ndi kumvana tokhatokha.

• Vutolimodzilalikululimakhalapopamenemwamunandimkazialiotanganidwakotero kuti samapeza nthawi yokambirana. Onetsetsani kuti mukupeza nthawi yoyenera youzana kalikonse kamene mukufuna kuuzana ndi wokondedwa wanu. Mwachitsanzo, ngati anali otanganidwa nthawi yaitali ku ntchito, mungakonde kudikira mpakana kumapeto kwa sabata kuti munene zakukhosi kwanu. Ngati ali wotopa kapena sakufuna kukamba nkhani, mudikire mpaka mtima ukhale pansi.

• Polankhulanandiwokondendwawanu,sankhanimalankhulidweabwinomongakuyankhula modekha, motsitsa ndi mosathamanga. Izi zingakope kapenanso kuthamangitsa wokondedwa wanu. Konzani nthawi yokambirana.

• Kukwera kwa mau, kuchuluka kwa mau, mmene ukuyankhulila, kuyankhulamofulumila, kuchita chibwibwi, ndi zina zonse zimapereka tanthauzo ku zomwe ukuyankhula kuposa mau omwe wagwiritsa ntchito. Anthu awiri akhonza kuyankhula mau omwewo koma mawuwo akhonza kuyankhulidwa kapena kulandilidwa mosiya chifukwa cha mmene mauwo atulutsidwira/ayankhulidwila.

• Kukwerakwamaukungathekukhalakwabwinokapenansokosautsa.Zindikiranikuti mau amatha kupereka uthenga woipa, womasula kapena wosamala, wachikondi ndi wansangala.

• Kumbukilani kuti kuyankhula kwa bwino kungathandize kuti HIV isabweremnyumba.

Khwerero 6: Gawanani ndi maanja onse mbali ina ya kulumikizana/kulankhulana yomwe ndi kulankhulana kosagwiritsa ntchito mawu. Maanja onse adziwe kuti:

• Kulankhulamosagwiritsantchitomaukumatanthauzazambirikoposamauotulukapakamwa panu. Zitsanzo za kulankhulana kosagwiritsa ntchito mau ndi izi: kugwirana, kuyang’anana m’maso, ndi zina. Kuyankhulana kungathe kuchitika pogwira, kuseweretsa kapena kugunditsa pakamwa dzanja la okondedwa athu.

• Njira zina zolumikizirana mosalankhulana ndi monga; kugwirana chanza,kukumbatirana, kukunga chibakera, kumenyetsa chitseko, kutaya zinthu, kulozetsa chala kumwamba, kumenya pamsana mwachikondi, kuwusa moyo, misozi yotsikira m’masaya, kuseka ndi zina.

• Mungathekugwiritsantchitonkhopengatichidachakuyankhulanandipomasondi gawo limene limapereka uthenga kwambiri pankhope, kuyenda kwawo, kuchepetsa zikope, kukulitsa zikope, kuwazungulitsa, ndinso momwe ukuphethilira

> 3:16 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

zimasonyeza momwe maganizo ako aliri.• Kulankhulandithupikumathandizakuperekabwinouthengapopandakutulutsa

mau.• Makhalidweonseathupiamavomerezakapenansokutsutsauthengawapakamwa.

Kutalikirana pakati pa anthu pamene akulumikizana kungatathauze chikondi kapenanso ayi.

• Kuyankhulanakosalankhulanakumachokeramumtima.Munthuangathekubisamaganizo ake koma sangabise zimene thupi lake likuchita.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaazithakuwonetseranachikondipolumikizanaosagwiritsantchitomau.• Maanjaazithakuwuzanankhawandizokondazawomosavuta.

Malemba1 Samueli 3:9Korani 49:12Korani 104:1

Mtumiki Muhamad (MUPI) anati; mukuyenera kukhala ndi chiyembekezo chokhazikikandichamuyayamwaMulungu/Allahkufikiranthawiyakufaitayandikila.

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:17

> Ntchito 7: Kupititsa patsogolo kulumikizana- Gawo II - Kumvetsera

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana kufunika komvetserana wina akamayankhula ndi momwe kungalimbikitsile kulankhulana momasuka mbanja. Awonanso tanthauza lakuya lakumvetsera ndi kuphunzila momwe angamuonetsere wokondedwa wawo kuti akumvetsera zomwe akulankhula.

Zolinga• Kuthandizamaanjakumvetsetsamauakutikumvetserandikuyamikilakufunika

komvetsera wina akamayankhula.• Kuwalimbikitsamaanjakutiazimvetserawokondedwawawoakamayankhulana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Yambani ndi kuwafotokozera maanja onse kuti:

• Kumvetserandimbaliimodziyakulumikizanakwabwino.Choncho,mwamunandi mkazi ayenera kuphunzira kukhala odziwa kumvetsera.

• Kumvetseramzakoakamayankhulasikophwekakomandikhalidwelofunikakuliphunzira.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti akhale awiri awiri. Awuzeni ndondomeko iyi:

• M’modziafotokozezinthuzimeneanakumananazopamoyowakewam’banjazomwe zinamusangalatsa.

• Winaayambendikumvetserakomakenakaasiyiletukumvetsera.• Kenakaasinthane.• Maguluwaakambiranezotsatirazi:- - Anamva bwanji ataona kuti wokondedwa wawo wasiya kumvetsera

zimene akunena? - Anamva bwanji ataona kuti wokondedwa wao akumvetsera zimene iwo

akunena? - Chimene akanachita ndi chiyani kuti adzimvetserana mwachikondi?

Khwerero 3: Magulu abwerere kuti adzakambirane zimene aphunzira.

Khwerero 4: Kumaliza zokambirana ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Kumvetserakumapitirirakungomvandimakutu.Kumafunansokuonetsetsazimene olankhula akuchita, kuonetsa kukhuzidwa, kuyang’anana m’ maso, kufunsa mafunso oyenera, kupereka mayankho abwino komanso kukhala chete.

• Ndikofunikakumvetselazomweokondedwawanuakunena,inuyonsomukuyenera kunena momwe mukumvera. Mukuyenera nonse kukhala achilungamo chodzadza kwa wina ndi mzake.

> 3:18 Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja

• Kumvetserakwathunthukumakhudzathupilonse,gawolirilonselathupi liyenera kutengapo mbali; - Pitirizani kuyang’anana maso ndi maso- Zimitsani kanema, ikani pansi

nyuzipepala. Pamene wina akukuyang’anani m’maso, zimapereka chilimbikitso ndipo zimamanga kukhulupilirana mu chiyanjano chanu.

- Khalani momvetsera-kwa mphindi zochepa chitani ngati kuti palibe chirichonse padziko lapansi chimene muli nacho chidwi koposa kumvetsera wokondedwa wanu akulankhula. Pewani zosokoneza zonse za mumtima mwanu. Sunthirani kutsogolo pa mpando wanu kuti mumvetsere liu lirilonse.

- Sonyezani kusangalatsidwa ndi zomwe mukuyembekezera kumva, tsitsani nsidze zanu, gwedezani mutu movomereza, mwetulirani kapena kuseka pakafunika.

- Funsani mafunso abwino amene akusonyeza chidwi chanu ndipo perekani chilimbikitso.

- Musadule ngati mukuona kuti mwamaliza kumvetsera, mvetseranibe pang’ono.

• Mvesteranimosamalakoposamomwemuyenera–musanafikepoyambakukambilana, onetsetsani kuti mwamumvetsetsa bwino okondedwa wanu.

• Nthawizambirivutolalikulupakulumikizanam’banjalimadzakambakoonakuti mnzako sakukumvetsera.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaamvetsetsekutikumvetserakapenakuonetsachidwipameneokondedwa

wawo akulankhula ndi chinthu chofunika kwambiri• Maanjaaphunzirelusolakumvetseranawinaakamayankhula.

MalembaKorani 3:103-105Yakobo 1:19

> Phunziro 3: Kuyankhulana ndi kiyi wa chimwemwe m’banja 3:19

Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti:

• Kumvetsetsakufunikakwakulankhulanakungathandizekupititsapatsogolokulankhulana momasuka m’maanja awo.

Khwerero 2: Ombani mkota pofotokoza kuti:

• Taonamfundozikuluzikuluzomwezikuyenerakuganiziridwapofunakulimbikitsa kulankhulana mbanja, monga izi:

• Kuyakhulanakwabwinondimomasukandikofunikambanjandipokungathandize banja kukhala lokondwa ndi lokhalitsa.

• Kulankhulanabwinokukutanthauzakusankhanthawiyabwinoyoyankhulana,kugwiritsa ntchito mau oyenerera komanso kusankha nthawi yabwino. Kusayankhulana mbanja kumabweretsa mavuto ambiri. Kumaononga maziko abanja ndikulepheretsa maanja kuchitila zinthu limodzi.

• Kulankhulanakosagwiritsantchitomaukumamvekakwambirikuposamauoyankhulidwa. Kungathe kugwiritsidwa ntchito poyankhulana ndi kuonetserana chikondi. Koma ngati sikunagwiritsidwe ntchito bwino kungathe kuononga chiyanjano cha banja.

• Kumvetserapomwewokondedwawakoakulankhulakumathandizakumuuzawokondedwa wakoyo kuti uli ndi chidwi ndi zomwe akulankhula.

• Pamenepalibekuyankhulana/kukambilanakwabwinombanja,mmodzikapenaonse awiri angathe kupeza wina yemwe akuona kuti angathe kumayankhulana naye. Izi zikhonza kuyambitsa kupanga chibwenzi kunja ndi kuchulukitsa chiopsezo cha HIV kulowa mnyumba.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli. Alimbikitseni maanja:• kukakambilanammeneakhalaakuyankhulilana• Akuganizakutiakonzabwanjikutikulankhulanakwawokukhalekwabwinondi

kothandiza kwambiri.

Malemba owonjezeraMiyambo. 15:2; 15:28; 16:23; Mateyu. 12:34-37, Mateyu.6:6,Akolose 4:6, Yakobo 1:19, 1 Atesalonika 5:17, Korani 16:90 Korani 4:129, Korani 30:21

> Ntchito 7: Kuomba mkota wa phunziro 3

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:1

Kugonana m’banja ndi Mphatso yochoka kwa

Mulungu/AllahKugonana ndi mphatso ya ukwati yochoka kwa Mulungu/Allah kwa banja lirilonse ndipo ndipofunika kuti aliyense mbanja akhutitsidwe. Kukhutitsidwa ndikugonana m’banja kumadza pamene musonyezana chikondi wina ndi mnzake, ndipo palibe lamulo la mmene mukuyenela kuchitila. Mwamuna ndi mkazi onse ayenera kuphunzila momwe angasangalatsilane chifukwa aliyense amafuna kukwanitsidwa. Kukwanitsana pogonana ndi udindo wa onse osati mayi yekha.

Kugonana mbanja ndi njila yina yolumikizana mwakuya . Mu gawo ili tiyang’ana kwambiri momwe maanja angapangire moyo wawo wogonana kukhala osangalatsa.Pali ntchito zosiyana siyana zomwe maanja apangire limodzi kuti amvetsetse kuti kugonana ndi mphatso yomwe Mulungu anayipereka ku banja , kufunika kwa kulankhulana pa nkhani zogonana.

Phunziro 4

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:2

Omwe akuyenera kuphunzira phunziro iri:Anthu omwe ali m’banja

Ndondomeko ya phunzilo1- Mutu wa phunzilo2- Phunzilo mwachidule3- Kutsegulira phunziro 4 4- Miyambo ya makolo5- Kugonana mbanja-mphatso yochokera kwa mulungu6- Kuyankhulana ndi kugonana7- Mmene mungakupangile kugonana kukhala kosangalatsa8- Kuomba mkota9- Ntchito ya kunyumba10- Malemba

Nthawi yofunika: Ola limodzi ndi Mphindi 55

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi Zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zokambirana nthawi isanakwan.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zolingana ndi mutuwu komanso zolembedwa zina.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa phunziroli.

> Phunziro mwachidule

> 4:3 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 20

Malangizo a padera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati munakumanapo kale, akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Phunziro lonse mwachiduleAlandileni maanja kuzokambilana ndikuwawuza kuti akhala ndi mwayi wokambilana pa mutu wakuti; kugonana mbanja-Mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah. Aphunzira kufunikila kolankhulana pa nkhani ya kugonana ndi momwe angakhalire ndi moyo wogonana wokwanitsana. Akambilananso mmene kusayankhulana pa nkhani zokhuza kugonana ndi kusakwanitsidwa ndi moyo wogonana mbanja kungabweretsere HIV/EDZI pakhomo.

Zolinga za phunziro 4• Kumvetsetsaubwinowakutikugonanambanjandimphatsoyochokerakwa

Mulungu/Allah.• Kuwathandizamaanjakukhalaomasukakuyankhulankhanizakugonanandi

okondedwa awo mbanja.• Kuwathandizamaanjakukhalaodziperekakukwanilitsazosowazamzawopa

nkhani yogonana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro la kugonana-mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah- pofotokoza mfundo izi:

• KugonanandimphatsoyaukwatiyochokakwaMulungu/Allahkwabanjandipondi mphatso yabwino.

• Kugonanambanjandinjirayolumikizilanamwakuya• Kugonanambanjandichinthucholemekezekandipondichinthuchopatulika.Pa

chifukwa ichi kuyenera kuchitika molemekezana ndi mwachikondi• Kwamzimayikutiakhutitsidwe,akuyenelakumvakukhalawofunikilandi

wokondedwa.

Khwerero 2: Awuzeni mfundo izi:

• Maanjaatenganawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizakutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse.

• Maanjaakhalandimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momwe amaonera zinthu komanso mfundo zina zofunikira.

• Maanjaaphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo.

> Kutsegulira phunziro 4

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:4

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti:

• Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

Khwerero 4: Afunseno maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi kudzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> 4:5 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kugonana mbanja yomwe ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupeza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu

samazimvetsetsa zokhuza kugonana mbanja. • Kuwafotokozela mfundo zoona zomwe zingawathandize maanja kukhala ndi

moyo wogonana wokondwa.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiliro ndi zoyankhulidwa zokhuza kugonana m’banja. Pokambirana mwakuya, tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti afotokoze miyambo ndi zikhalidwe zina zomwe zimakhudzana ndi kugonana m’banja.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu.

• Akaziayenerakuonetsetsakutiakukwaniritsazofunazaamunaawopakugonana.• Akazi ayerenera kungovomera kwa mwamuna wawo ngakhale atakhala ndi

zifukwa zokwanira zokanira kugonana ndi mwamuna wawo.• Akazi ayenera kumangochita zofuna za amuna awo, asamayambitse zogonana

kapenanso kuyambitsa mchitidwe wachilendo pakugonana.• Mzimayi aziyikamikanda yofira kapena kansalu kofila pa bedi akakhala kuti

akusamba.• Amunasakuyenerakuchitapokanthukutiamusangalatsemkaziwawopogonana

chifukwa amakhulupilira kuti iwo ndi oziwa zonse.• Amunaomwendiodulidwa, akaziomwealindi zokoka,kapenaamayiomwe

amavala mikanda ukagona nawo umakwanitsidwa kwambiri kusiyana ndi omwe alibe.

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilana zokhuza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu samazimvetsetsa ndi mfundo izi:

• KugonanambanjandimphatsoyochokerakwaMulunguyomweanayiperekakwa anthu okwatiwa ndipo onse awiri ayenere kusangalala nayo. Mayi kapena bambo angathe kuyambitsa zogonana osati bambo yekha.

• Kumva kukoma pogonana kumadalila pamaganizo amunthu.Ngatimaganizosanazazidwe ndi zinthu zina koma onse ali pa zomwe mukuchita, mungathe

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:6

kukwanitsidwa kwambiri. Ngati mmodzi akumukondadi okondedwa wake ndikuyesesa kumusangalatsa okondedwa wawo, nawonso angathe kukhala okwanitsidwa ndi kugonana nako.Sizoona kuti abambo omwe ndi odulidwa, amayi omwe ali ndi zokoka/ maleveni ndi omwe amavala mikanda mchiuno ali bwino kuposa omwe alibe. Komabe kudulidwa kumathandiza pa nkhani ya ukhondo.

• Amayi ndi abambo azikambilana zomwe amafuna akamagonana kutiazikwanitsidwa mokwanila kusiyana ndi kupita kunja. Izi zithandiza kuteteza banja lawo ku HIV/Edzi.

ZopemphereraNgati banja:• PempheranikutiMulunguathandizemaanjakusiyamiyambo,nkhambakamwa

ndi zoyankhula zomwe akhala akukhulupilira zomwe zili zosemphana ndi mawu a Mulungu makamaka zomwe zimapangitsa amayi kukhala osakwanitsidwa ndi osakondwa.

• Mukhaleomasukilanapankhanizakugonanakutimuzithakukwanilitsana.

MalembaKorani 16:4Korani 7:89Korani 2:228Genesis 2:25

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale pa iye anati: okhulupilira weniweni ndi amene ali ndi makhalidwe abwino, ndipo wopambana pa inu nonse, ndi omwe ali ndi makhalidwe abwino kwa akazi awo.

> 4:7 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

> Ntchito 2: Kugonana m’banja ndi mphatso yochoka kwa Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 20

Kukonzekera kwa padera kwa ophunzitsa• Phunzilorindilowumitsapakamwandipoizizingachititseanthuenakumangika

kutengapo mbali. • Ganizilani phunzilo lisayambe mmene mungachitile kuti anthu onse atengepo

mbali.• Mungathenso kukambilana ndi gulu pa mawu omwe mungagwiritse ntchito

potchula zinthu zina zolaula.

Zida zofunikira1. Tambula ya galasi/botolo lowonekela mkati2. Madzi

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kukambilana za kugonana komwe kuli mphatso ya anthu omwe ali mbanja. Agwiritsa ntchito nthanokukambilana za momwe angayilemekezele mphatsoyi yomwe Mulungu/Allah anayipereka. Zokambilanazi zifukulanso za HIV/Edzi.

Zolinga• Kuwathandiza maanja kumvetsetsa kuti Mulungu akuyembekezela kuti

ayilemekeze mphatso yakugonana yomwe anawapatsa pokhala okhulupilika kwa wina ndi mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Yambani ntchitoyi powafotokozera maanja kuti ugonana mbanja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu yomwe ndiyofunika kuyilemekeza.

Khwerero 2: Dzazani makapu kapena mabotolo atatu ndi madzi ndi kufotokoza nkhani iyi:

Ndabweretsa makapu (kapena mabotolo) atatu amadzi. Kapu imodzi yamadzi yatungidwa mu chitsime mmudzi momwe muli Korela. Makapu awiri enawo ali ndi madzi omwe ali abwino opanda korela. Monga mukudziwa kuti ukamwa madzi omwe ali ndi kolera pakapita masiku pang’ono umayamba kudwala kolera. Komano tiyerekeze kuti muli ndi luzu kwambiri. Kunja kukutentha ndipo mukufuna mutamwa madzi. Koma ndinu okhuzidwa kwambiri ndi nkhani ya kolera ndipo simukufuna kudwala kolera. Simukudziwa kuti ndi kapu iti yomwe ili ndi kolera chifukwa simungathe kudziwa pongoyang’ana makapuwa. Koma mukadalibe ndi ludzu.

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:8

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti ndi chisankho chiti chimene chiri chabwino?

• Osamwamadzimpakautapitakunyumbandikukamwamadziamchisimechako,omwe ukudziwa kuti ndi aukhondo.

• Kudikilakanthawipang’onondikumwakuchokelamutambulaimodzi• Kumwakopang’onokuchokelamutambulailiyonse.

Khwerero 4: Afunseni maanja kuti akambilane:

• Tingaphunzilechanikuchokeramunkhaniyi?• NdiubwinowanjiwomwemunthuangaupezepolemekezamphatsoyaMulungu/

Allah?

Khwerero 5: Malizani zochitika ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Chisankhochoyambachija(kumwapachitsimekochako)ndichomwechingakupatseni chitsimikizo chodzaza kuti simungatenge kolera. Chisankho chachiwiri (kuonjezela bwenzi lina logonana nalo) ndi chisankho chachitatu (kukhala ndi abwenzi ambiri ogonana nawo) kuli ndi chiopsezo chokupangitsani kutenga matenda.

• Kukhalaokhulupilikakwawokondedwawanundinjiraimodziyolemekezelamphatso ya kugonana yomwe Mulungu/Allah anayipereka kwa anthu okwatiwa. Kukhulipirika ndi chisankho chokhacho chomwe chimapereka chitetezo chodzadza ku HIV. Monga momwe tingapangire zisankho zabwino zokhuzana ndi madzi omwe tikumwa, tikuyeneranso kupanga zisankho zabwino zokhuza kugonana. Imwani kuchokera mu chitsime chanu.

• Kugonanandinjirayabwinoyomweanthuomwealimbanjaamaonetselanachikondi.

• AmayindiabamboomweamalemekezamphatsoyaMulunguyiamakhalandibanja lokhalitsa ndi lathanzi.

• NgatiwinasakukwanitsidwandimphatsoyaMulungu/Allah,mbanjamumakhala kusagwilizana ndipo mmodzi wa iwo akhonza kuganiza zokapeza bwenzi lina logonana nalo. Izi zingabweretse HIV mnyumbamo.

ZopemphereraPempherani nati banja kuti:• AbamboangathekutsatilachitsanzochaMulungu/Allahkukondanawinandi

mzake ndi kuphwanya zikhulupililo zozunza mayi. Apatseni kulimba mtima kuti akhale mosiyana ndi anthu ena ndikuonetsera chikondi cha Mulungu/Allah kwa akazi awo.

• MaanjaamvetsetsekutikugonanandimphatsoyaanthuokwatiwayochokakwaMulungu. Pempherani kuti akhale omasukilana ndi opanda manyazi.

• Mukhalendimphamvuzogonjetsamayeserondikumwamuchitsimechanuchokha.

MalembaNyimbo ya Solomo 4:9-16, Miyambo 5:15-21,Rute 3:3;Korani 16:4, Korani 7:89

> 4:9 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 35

Kukonzekera mwapadera kwa ophunzitsa• Werenganinsogawolakufunikakwakulumikizanambanja.• Phunzilorindilowumitsapakamwandipoizizingachititseanthuenakumangika

kutengapo mbali. • Ganizilani phunzilo lisayambemmenemungachitile kuti anthu onse atengepo

mbali.• Mungathenso kukambilana ndi gulu pa mawu omwe mungagwiritse ntchito

potchula zinthu zina zolaula.

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana momwe angauzilane zomwe amafuna akamagonana ndi wokondedwa wawo ndi momwe izi zingathandizile iwo kukhala ndi moyo wogonana wokwanitsidwa. Awonanso momwe kusakambilana pa nkhani za kugonana kungabweretsele kusakhulupilika ndi kubweretsa HIV m’banja.

Zolinga• Kuwalimbikitsa maanja kuti azikambilana momasuka zomwe amafuna

akamagonana ndi okondedwa awo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni anthu mwachidule za zokambirana za mmbuyomu zokhudza kufunika kulumikizana m’banja. Auzeni kuti kulumikizana ndi kofunikanso pamoyo wogonana:

• Awuzenikutikulankhulanazokhuzakugonanandikofunikakutiakhalendimoyo wogonana wabwino.

• AkumbutseninsokutikugonanambanjandimphatsoyochokerakwaMulungu/Allah ndipo onse akuyenera kukwanitsidwa. Amayi ndi abambo akuyenera kuphunzila mmene angamasangalatsilane pogonana.

Kwerero 2: Funsani anthu kuti aganizire momwe amalumikizanirana ndi wokondedwa awo pa nkhani yogonana. Aganizire ndipo alembe mayankho awo ndikuwapereka kwa mlangizi ndipo asalembepo mayina awo koma alembe ngati ali amuna kapena akazi. Mungathe kuwakambilana mayankhowo popanda gulu kudziwa kuti analemba ndani.

• Kodimumamasukakukambiranankhanizogonanandiwokondedwawanu?• Kodindinuomasukakuuzawokondedwawanumomwemukufunirakuti

wokondedwa wanu akuchitireni panthawi yogonana?• Kodimumamasukakufunsawokondedwawanukutimugonanekapena

mumadikira kuti iye aziyambitsa?• Kodimumauzanabwanjipamenemukufunakutimuyesenjirayinakapena

machitidwe ena pamene mukugonana?

> Ntchito 3: Kuyankhulana ndi kugonana

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:10

• Kodimumathakuuzawokondedwawanungatisimunakhutitsidwemutagonana?

Khwerero 3: Akuganizila za mafunsowa, afunseni kuti akambilane ngati gulu mafunso awa:

• Ndi chifukwa chiyani nthawi zina kumakhala kovuta kukambirana za kugonana ndi wokondedwa wathu?

• Ndi chiyani chimene amuna ndi akazi angachite kuti azitha kulumikana bwino pa nkhani zogonana mbanja mwawo?

Khwerero 4: Kumaliza ntchito ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Kuuzanazofunikapakugonanandikofunikakwambiri.Kafukufukuakusonyezakuti kuwuzana zomwe timafuna pankhani ya kugonana ndi gwero lamphamvu la moyo wogonana wokoma.

• Mwamunandimkaziayenerakukambiranazimeneakufunakutiasangalarendimoyo wawo pakugonana. Kupanda kuuzana, wokondedwa wanu sangadziwe zimene zimakusangalatsani komanso ngati mumakhutitsidwa.

• Kulumikizanapankhaniyakugonanakungakhalekovutakwaonseawiri-winaangathe kuchita manyazi ndi nkhaniyi kapena angathe kuopa kuti mnzakeyo ayilandira bwanji nkhaniyo, wina angaganizenso kuti mwina akumudzudzula ndipo sangakhale ndi chidwi chomvetsera.

• Chikondichenichenichikuyenerakuyambirakunjamusanafikenthawiyogonana. Kukhutitsidwa pa kugonana kumadza kamba ka kumvana pa zinthu za m’banjamo. Ngati pali mavuto pakati pa awiriwo zimaoneka pa nthawi yakugonana.

• Mongandikuyankhulanakonsekwabwino,onetsetsanikutimwapezanthawiyoyenera kulankhula zimene mukufuna kunena. Fotokozani zimene mukuganiza, monga “ndikadakonda ukana…” m’malo mwakuti “chifukwa chiyani suna….” Musamuseke kapena kumudzudzula wokondedwa wanu kamba kokamba nkhani zakuchipinda.

• Ngatimulipaubalewokhulupilirana,mudzathakulumikizanandiwokondwedwa wanu pa chilichonse.

• Kusalumikizanapankhanizogonanandichifukwachimodzichimeneamunandiakazi amafuna kugonana ndi ena amene sali nawo pa banja, zimene zimadzetsa HIV mnyumba.

• Zingakhalezovutakugonanamwachikondipamene: - Kunja kwa chipinda chogona awiriwa sakukondana; - Akulephera kuuzana zimene zikuwasangalatsa; - Sakufuna kuyesa njira zachilendo. • Kukhutirapakugonanandikwaonsemwamunandimkazi.Sikwamkaziyekha

kuti akwaniritse zofuna za mwamuna. Izi ndi zofunika kusunga mumtima kamba koti pachikhalidwe timangomva mkazi yekha akulangizidwa asanalowe m’banja za momwe angakwaniritse zofuna za mwamuna wake pamene zochepa zimauzidwa kwa mwamuna kuti ayenera kuchita.

> 4:11 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguathandizemaanjakukhalaomasukilanandikukambilanazomwe

amafuna akamagonana popanda mantha ndi manyazi.• Mukhalaolimbamtimakukhalandikukambilanakomasukandikwachilungamo

ndikumanga ubwenzi watanthauzo.

MalembaNyimbo ya Solomo 7:1-91 Akorinto 7:4-5Genesis 2:25Korani 53:45-46Korani 7:89

Mtumiki Muhamad (MUPI) anati; Chifukwa chani mkazi wamasiye, bola ukanakwatila namwali amene ukanamasewera naye ndi kuti iye azisewera ndi iwe

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:12

> Ntchito 4: Mungatani kuti kugonana kukhale kwa chikondi ndi kosangalatsa

Nthawi: Mphindi 20

Kukonzekera mwapadera kwa ophunzitsa• Phunzilorindilowumitsapakamwandipoizizingachititseanthuenakumangika

kutengapo mbali. • Ganizilaniphunzilolisayambemmenemungachitilekutianthuonseatengepo

mbali.• Mungathensokukambilanandigulupamawuomwemungagwiritsentchito

potchula zinthu zina zolaula.• Nthawiyazokambiranazi,anthuangathekuperekazitsanzozazikhulupilirozina

zimene zimaletsa kugonana m’banja nthawi zina pa zifukwa zosiyanasiyana. Sikoyenera pa gawo lino kuti tikambirane ngati izi ziri zoyenera kapena ayi. Mfundo yaikulu ndi yakuti ganizo lirilonse lopewa kugonana m’banja libvomerezeke ndi onse, mwamuna ndi mkazi.

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana mmene angapangile moyo wawo wogonana kukhala osangalatsa ndi zinthu zomwe zingawalepheretse kusangalalaku.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakutiaphunziremmeneangakhalirendimoyowogonana

wokondana ndi wokondweretsa.• Kuwapatsamwayimaanjakukambilanazinthuzomweakuyenerakuzipewa

zomwe zingawalepheletse kukondwera akamagonana ndi momwe angapewere zinthu zimenezo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Yambani ntchitoyi powafotokozera maanja kuti tikambilana za momwe tingapangire kugonana kuti kukhale kwachikondi ndi kokoma powonetsetsa kuti mmbanja muli kulankhulana momasuka ndi mwachilungamo.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti akhale mumagulu amayi ndi abambo ndipo akambilane mafunso awa:

• Ndizinthuzitizomwezimapangitsaife(amayi/abambo)kutitisamvebwinotikamagonana? Nanga tingazipewe bwanji?

• Nangatimafunaamuna/akaziathuazitanikutitikondwerendikugonanakwathu?• Ndiziwalozitipathupipathuzomwezimapangitsakutitimvebwino

tikagwiridwa?

> 4:13 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

Khwerero 3: Magulu onse afotokoze zimene akambirana kwa gulu lonse.

Khwerero 4: Ombani mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Kugonanandichinthuchosangalatsakwambiringatipalichikondindikukhulupilirana m’banja.

• Kambirananimomasukandiwokondedwawanumomweangakuthandizirenipanthawi yogonana. Kumasukirana ndi gwero la kukhutira ndi kusangalala pa kugonana.

• Onetsetsanikutimukusinthasinthamachitidwepakugonanandipomusaopekapena kuona ngati cholakwika kuyesa njira zina zachilendo. Anthu ambiri amene ali pa banja amadandaula kuti zimatopetsa kumagonana mnjira imodzimodzi, ndipo izi zimapangitsa kuti chidwi chithe. Izi zingapangitse kuti mmodzi kapena onse awiri akapeze kukwanitsidwaku kunja kwa banja zomwe zingachulukitse mwayi wobweretsa HIV. Mwamuna ndi mkazi alimbikitsidwe kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pogonana.

• Amunandiakaziakhalendinthawiyokwanirakukonzekeretsanampakaonseatakonzeka kugonana. Akuyenera kudziwa kuti amuna ndi akazi amadzuka munthawi zosiyana ndinso munjira zosiyana. Nthawi zambiri mkazi amatenga nthawi yayitali kuti adzuke. Khalani tcheru ndi zofuna za mnzanu. Amuna aphunzire kudzigwira ndi kudikira mpaka mkazi wawo atakonzeka kumulowa. Izi zidzathandiza onse kumva kukoma.

• Pamenemwamunandimkaziakukonzekerakapenaakugonana,mtimawawousasokonekere pakuganiza zina monga mavuto awo a m’banja, kapenanso za kuntchito. Mtima umafuna kukhazikika pa kugonanako kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto, kupanda kutero simungamalize bwino kapenanso simungamalize kumene. Ngati mtima wasokonezedwa, umayamba kuganiza zina. Mapeto ake , thupi limazizira ndipo chilakolako chimatha .

Khwerero 5: Awuzeninso maanja mfundo izi zofunikila kuziziwa zokhuza kugonana:

• Kugwiritsantchitokugonanangatinjirayothetserakusamvanakuyenerakupewedwa. Musanagonane, mwamuna ndi mkazi ayenera kuchotseratu mkwiyo wawo. Kukana kugonana kungathe kukhala njira imodzi yomulangila wokondedwa wanu kapena kusonyeza kukwiya. Kusungira mkwiyo, kumalepheretsa munthu kukhala ndi chilakolako.

• Nkofunikakulemekezazilakolakozawokondedwawanu.Komabenthawizina, wokondedwa wanu angathe kukhala ndi zifukwa zokwanira zosafuna kugonana – mwina sakumva bwino m’thupi. Winayo akuyenera kumvetsa ndipo asamuumirize mnzakeyo kuti agonane.

• Komangatikugonanakwalepherekakangapom’banja,zingasonyezemavutoam’banjamo ndipo zingadzetse chikayiko cha kusakhulupirika kwa m’modzi.

• Chidwichakugonanachimasinthandinthawikapenamalinganandinyengo.Mwachitsanzo;mkaziamenewafikanyengoyosiyakuberekasangakhalendichidwi kwenikweni chogonana kapena mwamuna amene watopa kwambiri ku ntchito sangathe kupuma mokwanira kuti amve kukoma pakugonana. Khalani tcheru ndi zofuna za mnzanu ndipo kumbukirani kukambirana momwe mukumvera mthupi mwanu.

• Banjalirilonselirindimwayiwogwirizanamomweangamachitirepogonana.Kutengera za zithunzi kapena kanema wolaula kuyenera kupewedwa pakuti zimenezi zimachotsa chidwi pa wokondedwa wanu ndikuika pa anthu a pa zithunzipo.

> Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah 4:14

• PaChisilamu,ukwatisichiyanjanochauzimuchokhapakatipamwamunandi mkazi, komanso sichofuna kungobereka ana ayi. Dzina la ukwati paChisilamu ndi, “Nikah” kutanthauza kuti kugonana. Chisilamu chimamvetsa kuti chilakolako cha kugonana chikhale chopanda malire. Zilakolako zingayanjanitsidwe chikhalidwe cha umunthu pa moyo uno ndi wakutsogolo. Pamene banja liphunzira tanthauzo la chikondi chenicheni ndipo iwo eni akulemekezana, kukhulupilirana, ndiye kuti ayembekezere moyo wokhutira pa kugonana.

• Muchisilamundizoletsedwakotheratukukonzekerakugonanakugwiritsantchito njira yotulukila chimbuzi kapena mkamwa, kapenanso kupsopsonana ku maliseche. Kugonana kuchitike kudzera mu njira ya amayi basi.Kupyolera mu njira iyi mungathe kugwiritsa ntchito luso lina liri lonse pogonana.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaapezekugonanandiokondedwaawokukhalakosangalatsandikuti sakanizana monga momwe baibulo/korani imanenela• Mukhalaolimbamtimakukhalandikukambilanakomasukandikwachilungamo ndikumanga ubwenzi watanthauzo.

Malemba1 Akorinto 7:4-5Genesis 2:25, 26:5Korani 7:89Korani 2:223

> 4:15 Phunziro 4: Kugonana m’banja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah

Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti kugonana mbanja ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo ndi udindo wa onse kulemekeza mphatsoyi.

Khwerero 2: Ombani mkota pofotokoza kuti:

• Taonamfundo zikuluzikulu zomwemaanja akuyenera kuchita kuti akhale ndimoyo wogonana wokwanitsidwa.

• Maanja akuyenera kukambilana momwe akufunila kuti wokondedwa wawoaziwachitila akamagonana. Kukambilana momasuka ndi njira imodzi yokhalila ndi moyo wogonana wokwanitsidwa.

• Chikondichenichenichikuyenerakuyambirakunjakwachipindachogonanthawiyogonanaiasafike.Kukhutitsidwapakugonanakumadzakambakakumvanapazinthu za m’banjamo. Ngati pali mavuto pakati pa awiriwo zimaoneka pa nthawi yakugonana.

• Ngatimaanjaangakhaleokwanitsidwandimoyowawowogonanasangapezekeakutuluka kukachita chigololo poteropo angapewe HIV kubwera mnyumba.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli. Alimbikitseni maanja kukakambilana ngati:

• Amakhutitsidwandiwinandimzake?• Ngatindiindeakalimbikitsaizibwanji?• Ngati ayi, akambilane mmene angapangire kuti kugonana kwawo kukhale

kosangalatsa ndipo azikwanitsidwa.

Malemba owonjezeraDeutronomo 5:18Nyimbo ya Solomo 4:16Aroma 12:10Miyambo 5:19Korani 77:20-23Korani 23:12-14

Komanso Mtumiki Muhammad (mtendere ndi madalitso zipite kwa iye) anati: Kuchita banja (kugonana) kuli ndi malipiro (kwa Mulungu tikapeza mphoto).

> Kuomba mkota pa phunzilo 4

>

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:1

Kukhala ndi zibwenzi zina zogonana nazo kunja kwa banja ndi limodzi mwa mavuto omwe maanja akukumana nawo. Phunziroli lithandiza maanja kumvetsetsa zomwe zimayambitsa khalidwe iri ndizotsatila zake.

Ntchito za mu phunzilori zomwe wina aliyense atenge nawo mbali zithandiza maanja kukambilana ndi kupanga masewero akuyipa kwa kukhala ndi zibwenzi kunja kwa banja ndi kuopsa kokhala mukangaude wa chiwerewere. Maanja akambilananso momwe angagonjetsere vuto limeneli ndikukhala okhulupilika kwa wina ndi mzake.

Phunziro 5

Kugonana kunja kwa banja-chigololo

> 5:2 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

> Phunziro mwachidule

Omwe akuyenera kuphunzira phunziro ili:Anthu omwe ali m’mbanja

Ndondomeko ya phunziro1. Mutu2. Gawo mwachidule3. Kutsegulira phunziro 54. Miyambo ya makolo5. Kukhulupilika kukutanthauza chani?6. Kukhala ndi zibwenzi: Chimayambitsa ndi chani?7. Kukhala ndi zibwenzi: Zotsatila zake8. Ntchito yapadera yokamba za HIV/EDZI ndi kangaude wa chiwerewere9. Kapewedwe ka kangaude wa zibwenzi10. Kuomba mkota11. Ntchito ya kunyumba12. Malemba

Nthawi yofunikaMaola atatu ndi Mphindi 25

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi Zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zochitika nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zolingana ndi mutuwu komanso

zolembedwa zina.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:3

> Kutsegulira phunziro 5

Nthawi: Mphindi 20

Malangizo apadera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati munakumanapo kale, akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Zokambirana mwachiduleAlandileni maanja kuguluri ndi kuwawuza kuti akhala ndi mwayi wokambilana za mutu woti kugonana kunja kwa mbanja-chigololo maka pa m’mene zikukhudzirana ndi HIV/Edzi. Awona zomwe zimayambitsa, zotsatila zake ndi momwe angakhalire okhulupirika kwa wina ndi mzake.

Zolinga• Kumvetsetsabwinozomwezimachititsandikuopsakogonanakunjakwabanja.• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakuopsakokhalamukangaudewa

chiwerewere.• Kuwathandizamaanjakupangansolumbilolakukhalaokhulupilikakwawinandi

mzake.

Ndondomeko

Khwelero 1: Akumbutseni za phunziro latha momwe timaphunzila za kugonana ngati mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah:

• Kulankhulanakwabwino,chikondindikukhulupililanakumatsimikizakutimaanja likuyilemekeza mphatso ya kugonana imene Mulungu/Allah anapereka ku banja.

• Nthawizina,komabebanjalimakumanandizovutapamenemodziwaawiriwowayesedwa kutuluka mbanja kukachita zogonana kunja.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Atenganawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizakutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse

• Akhalandimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momweamaonera zinthu komanso mfundo zina zofunkira.

• Aaphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti:

• Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

> 5:4 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

Khwerero 4: Afunseno maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi dzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kugonana kunja kwa banja ndi momwe zikukhudzirana ndi HIV/Edzi. Iwo akambirana ngati zimenezi ziri zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupezazikhulupiliromiyamboyosiyanasiyanandizinazomweanthu

samazimvetsetsa zokhuza kugonana kunja kwa banja. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizemaanjakukhala

okhulupilika kwa wina ndi mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiliro ndi zoyankhulidwa zokhuza kogonana kunja kwa banja. Pokambirana mwakuya asiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti akambirane miyambo ndi zikhulupiriro zina zokudzana ndi kugonana kunja kwa banja zomwe amadziziwa.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu.

• Kutimwamunaakhalemwamunaweniweniakhalendizibwenzizingapo.• Ndichosadabwitsakutimwamunaakhalendizibwenzi.Palimiyambindi

zining’a zotchuka zimene zimalimbikitsa amuna kuchita zimenezi. Monga mwamuna ndi mwana; mwamuna azinyenga; mwamuna ndi galu.

• Mkaziakagwidwachigololoimakhalankhanikomaakakhalamwamunatimatindi momwe zimakhalira.

• Akaziokwatiwaamenealindimwamunaosakhulupirikaamalimbikitsidwakuti asamusiye mwamuna wawo ponena kuti palibe mwamuna wokhulupirika (mwamuna osanyenga ukampeza kuti?).

• Akaziamakhulupilirakutipamakhalamwinimwamunaenawosiokhalitsa.(Iwende mwini wake wa banja enawo ndi atidyenawo chabe).

• Palizinthuzinazomweamayikapenaabamboangachitekutiakhaleokomakugonana nawo monga kudulidwa, azimayi kukhala ndi zokoka kapena kuvala mikanda.

• Ngatiulimwamunasungadyendiwozomwezomwezotsikunditsiku,ukuyenerakusintha.

• Chigololondimwinithako.

> 5:6 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilana zokhuza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu samazimvetsetsa potsindika mfundo izi:

• Maanjaalimbikitsidwekumauzanazomweiwoamafunaakamagonanakutiazithakukwanitsidwa.

• Amunaalimbikitsidwekukhalaokhulupilikakwaakaziawongakhalemiyamboina ingakhale kuti imakuwalimbikitsa kutuluka kunja. Kugonana kunja kwa banja ndi tchimo pamaso pa Mulungu. Kuti titetezeke ku HIV tikuyenera kukhala okhulupilika kwa okondedwa wathu ndikukhala ndi ubale wabwino ndi Mulungu/Allah.

• Kusinthasintha abwenziogonananawokumaonjezera chiopsezo chotengaHIVchotero anthu ogonana nawo sakuyenera kasinthasintha ngati chakudya. Ziwirizi ndi zosiyana.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguatithandizekuonansomiyambo,nkhambakamwandizoyankhulazomwe

takula nazo zomwe timazikhulupilira kwambiri. Izi ndi zomwe zimapangitsa maanja kukhala osakhulupilika kwa wina ndi mzake.

MalembaAefeso 5:25-29Korani 17:32Korani2:27

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:7

Nthawi: Mphindi 30

ZofunikiraMapepala, zolembela

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana mwakuya kutanthauza kwa mau akuti kukhulupirika mbanja.Akambilananso zabwino zimene zimabwera maanja akakhala okhulupirika kwa wina ndi mzake ndi za HIV/Edzi.

Zolinga• Kulimbikitsamaanjakukhalaokhulupirikakwawinandimzake.• Kuthandizamaanjakumvetsetsazaubwinowakukhalaokhulupirikakwawinandi

mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti:

• KukhalaokhulupirikambanjandilamulolaMulungundipoliyenerakulemekezedwa.

• Mauakutikukhulupirikaalindimatanthauzoosiyasiyanakwaanthunsoosiyanasiyana.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti akambilana pa mawu akuti ‘kukhulupirika’:

• Afunsenimaanjakutianenekutimawuakutikukhulupirikaamatanthauzachani.• Mukafunsadikilanikutianthuayankhe.• Ngatindimunthummodzikapenaawiriayankha,funsaninsofunsolomosiyana.

Mwachitsanzo, zikutanthauza chani kukhala bwenzi lokhulupirika? Kapena mayi okhulupirika? Limbikitsani kukambilana.

• Afunsenikutinangakukhulupirikam’banja?

Mayankho omwe mungawayembekezere akhonza kukhala ngati awa: Kukhala odzipereka kwa munthuyo. Kukhala okhazikika osisasinthasintha kuzipereka kwako pakakhala pa mavuto. Munthu amene ali okhulupirika ndi odalirika.

Khwerero 3: Ombani mkota pa nkhaniyi:

• Kukhulupirikambanjanthawizambirikumakhuzankhaniyogonana.kukhalaokhulupilika zikutanthauza kuti uzigonana ndi mzako wa banja yekha. Zikutanthauza kuti ukusankha kusakhala ndi abwenzi ena ogonana nawo, kapena kuchita zogonana zina zilizonse kunja kwa banja.

• NgatimaanjaakhalaokhulupilikakwawinandimzakendipongationsealibeHIV, amapanga mpanda wa chitetezo kuzungulira banja lawo.

> Ntchito 2: Kukhulupirika kumatanthauza chiani?

> 5:8 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

• Ndi chithu chofunikila kuti tiganizile momwe zomwe timachita kapenazikhulupirilo zathu zimakhuzila moyo wathu wogonana mbanja ndi momwe izi zikhuzilana ndikutenga kachilombo ka HIV. Nthawi zina pamakhala zinthu zina za kunja kwa banja lathu zomwe zimatikanikitsa kukhala okhulupilika. Koma tikakhala okhulupirika kwa wina ndi mzake ndi kwa Mulungu, tingathe kugonjetsa zonsezi.

Khwerero 4: Agaweni anthu onse mumagulu anayi ndikulipatsa gulu lilonse mapepala ndi zolembela. Lipatseni gulu lirilonse chimodzi mwa zochita izi:

• Gulu loyamba: Ngati maanja ali okhulupirika kwa wina ndi mzake moyo wawo ungakhale otani? Zotsatila za kukhala okhulupilikako ndi chani? Jambulani chithunzi cha banja lokhulupirika kufotokoza yankho lanu.

• Gulu lachiwiri: Ngati maanja ali osakhulupilika kwa wina ndi mzake moyo wawo ungakhale otani? Zotsatila za kukhala osakhulupilika ndi chani? Jambulani chithunzi cha banja lomwe ndilosakhulupilika kufotokoza yankho lanu.

• Gulu lachitatu: Jambulani chithunzi cha thalitchi/mzikiti womwe uli ndi maanja okhulupirika kwa wina ndi mzake. Ngati maanja ali okhulupirika mmipingo/mizikiti, zosatila zake zingakhale zotani kwa mpingo/mzikiti? Chingachitike ndi chani kwa mpingo/mzikiti?

• Gulu lachitatu: Jambulani chithunzi cha thalitchi/mzikiti womwe uli ndi maanja osakhulupirika kwa wina ndi mzake. Ngati maanja ali osakhulupirika mmipingo/mizikiti, zosatila zake zingakhale zotani kwa mpingo/mzikiti? Chingachitike ndi chani kwa mpingo/mzikiti?

Afunseni kuganizila izi pamene akujambula zithunzi zawo:

• Kodikuchitachigololokapenakhalidwelachiwerewerelimasokonezabwanjiumodzi kapena kugwirizana wa anthu mmudzi?

• Nangandizovutazanjizomweana,anaamasiye,ogwirantchitozachipatala,angakumane nazo, nanga mabweredwe akutchalitchi/mzikiti angakhuzidwe bwanji, nanga chuma cha dziko?

• NdimugululitimmenemungapezeanthuambiriomwealindiHIV.Izizikhuzabwanji zithunzi zanu?

Khwerero 5: Itanani magulu onse kuti abwere pamodzi:

• Sankhanimunthummodzipagululirironsekutiawonetsechithunzichomweajambula ndi kufotokoza kuti chikutanthauza chani? Akhonza kukhala ndi zithunzi zokamba zabwino kapena zoipa. Chofunikila ndi chakuti athe kufotokoza momwe amavera za mau akuti kukhulupirika ndi zotsatila zake.

• Afunsenimaguluenakutiafotokozengatiakugwirizananazokapenaayi.• Ombanimkotapamfundozonsezomwezakambidwapagululirilonse.

Khwerero 6: Ombani mkota pa nkhani iyi ndi mfundo izi:

• Kukhulupirikakungakutetezeinundiwokondedwawanukumatendaopatsilanapogonana ndi HIV.

• KukhulupilikakungakutetezeanaanuamtsogolokutiasazabadwendiHIV(ngati mayi yemwe ali oyembekezera alibe HIV).

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:9

• Kukhulupirika ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zipembedzo zambirizimalimbikitsa. Achipembedzo chotero akhonza kukhala osangalatsidwa ndi ganizo lokhala okhululupirika ndipo atha kukulimbikitsani.

• Kukhulupilika kumabweretsa mtendere mbanja -pamakhala kukhulupilana ndichilungamo.

• Ukakhalaokhulupirikasumakhalandimanthaogwidwandiwinaaliyense.• Maanjaomwealiokhulupilikasakanganankhanizokhuzanakusakhulupilika.• Maanjaokhulupililanaamakhalandinthawiyokwanilayochezandibanjalawo,• Maanja okhulupililana ndi athanzi mmaganizo ndi kuthupi ndipo amapanga

mpingo/mzikiti ndi mudzi olimba.• Midziyokhalandianthuokhulupilikaimakhalayotukukaanthuamakhalaathanzi

ndipo amatha kugwira ntchito ndi kukhala ndi katundu wambiri.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulungu/Allahathandizemaanjakukhalaokhulupilikakwawinandimzake.

Kukhulupilika ndi kovuta makamaka kwa abambo, Mulungu/Allah angathe kutisintha tikazichepetse pamaso pake.

MalembaAefeso 5:28-29Miyambo 5:18-20Korani 4:34Korani 23:4 -10Korani 70:27Korani 16:91Korani 37:2-3

> 5:10 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kukambilana zomwe zimayambitsa kusakhulupirika m’banja. Maanja akumbutsana za malonjezo omwe anapangapo omwe anakwanitsa kuwasunga ndi momwe angaphunzilire kuchokera ku malonjezo amenewa kusunga lonjezo lakukhala okhulupilika kwa wokondedwa wawo. Pokambilana za nkhani zochitika, maanja akambilana momwe angapewere kukhala ndi zibwenzi kunja kwa banja.

Zolinga • Kuthandizamaanjakudziwazomwezimayambitsakusakhulupirika• Kuthandizamaanjakumvetsetsakutiangathekukhalaokhulupilikakwawinandi

mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani zokambilana powadziwitsa maanja kuti:

• Tikhala tikukambilana za kusankhulupirika, kupeza kuti chimayambitsa ndichani.

• Kudziwa zomwe zimayambitsa kusakhulupirika, maanja akambilana mmeneangapewere vutoli.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti akumbukile za malonjezano omwe anapangapo kalekale, zaka zapita mbuyomo ndipo anakwaniritsa kuwasunga. Apempheni angapo kuti afotokozepo za malonjezano awo.

Khwerero 3: Afunseni maanja ngati akuganiza kuti ndi zovuta kusunga lonjezo lakukhala okhulupirika kusiyana ndi malonjezo ena, nanga ndi chifukwa chani?

Khwerero 4: Ombani mkota ndi kufotokoza mfundo izi:

• Kusungalonjezolakukhalaokhulupilikandikovutakwaanthuenachifukwachazilakolako zawo koma angathe kuphunzira ku malonjezo ena omwe anasungapo.

• Nkhanizathuzokhuzamalonjezoamenetinakwanitsakuwasungazingatiphunzitseife mmene tingakwanitsile kusunga malonjezo ovuta (kukhulupilika).

• Kuchokeramu zomwe takambilana, tingathe kuona kuti tonse tinakwanitsapokusunga malonjezo athu.

• Komabe,nthawizinaanthuamapangazinthuzimenezimawapangitsakulepherakusunga lonjezo lakukhala okhulupilika. Mwina ndi anzathu omwe timacheza nawo. Mwina ndi mowa kapena timakhala nthawi yambiri tikuganiza za mkazi kapena mwamuna wina osati mwamuna kapena mkazi wathu. Nthawi zina timaziuza kuti palibe vuto kupeza chibwenzi ngati tapita kukagwila ntchito kutali.

• Maganizoathuamatipangitsaifekulepherakuziletsa.

> Ntchito 3: Zomwe zimayambitsa kugonana kunja kwa banja

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:11

Khwerero 5: Agawane maanja mumagulu anayi a anthu anayi kapena asanu pa gulu lirilonse. (amayi ndi abambo mosiyana). Afunseni maguluwo kuti akambilane mafunso awa:

Abambo• Ndizinthuzitizomwemukuganizakutindizimenezimapangitsaamunakuzembera

akazi awo?• Ganizilani zinthu zinayi zomwe abambo amdela lanu kapena mpingo/mzikiti

amachita kapena kuganiza zimene zimawapangitsa kulephera kukhala okhulupirika.

Amayi • Ndizinthuzitizomwemukuganizakutindizimenezimapangitsaamayikuzembera

amuna awo.• Ganizilani zinthu zinayi zomwe amayi amdela lanu kapena mpingo/mzikiti

amachita kapena kuganiza zimene zimawapangitsa kulephera kukhala okhulupirika.

Khwerero 6: Onse akakonzeka:

• Afunsenionsekutiagawanezomweakambilanandigululonse• Funsani gululo kuti awone ngati zifukwa zomwe amayi apereka ndi zomwe

abambo apereka ziri zofanana.

Khwerero 7: Ombani mkota ndi kupereka mfundo izi: Kupanga zibwenzi uli mbanja kumachitika pa zifukwa zambiri monga:

• Mavuto okhalitsa a M’banja: ngati banjalo lasokonekera kapena ubale pakati pa awiriwo sukuyenda bwino.

• Kusaka chikondi: ena amayamba zibwenzi chifukwa sakuona kuti akukondedwa ndi mwamuna kapena mkazi wawo. Monga zinthu zina pa munthu, chikondinso chimasintha ndi nthawi. Chikondi chikafa pakati pa awiriwo, mapeto ake amakasaka chikondi kwina.

• Kusakhutitsidwa pa kugonana: kugonana ndi chimodzi mwa zifukwa zimene zimayambitsa maphokoso m’banja, ndipo m’modzi amakayang’ana kwina. Awiriwa akuyenera kukambirana ndi kupititsa patsogolo moyo wawo wakugonana kuti choncho usawatopetse ndipo chilakolako chisathe.

• Kuyembekezera zinthu zosatheka: anthu ambiri amalowa m’banja ndi ziyembekezo za zinthu zimene sizingatheke kuchokera kwa wokondedwa wawo. Amaganiza kuti zikhala ngati mmene zinaliri ali pachibwenzi kapena kuti munthuyo asintha makhalidwe ake oipa. Akakhumudwa ndi okondedwa awawo chifukwa zomwe amayembekezera sizikukwaniritsidwa amayamba kuganiza zoyamba kupanga zibwenzi.

• Banja limafuna kulimbikira kuti zonse zidziyenda bwino. Anthu ena amasankha kusiya kulimbikira za banja lawo, kumaona ngati bola kupeza wina wachilendo. Chikondi chimasinthanso monga momwe chiyanjano chanu chimasinthila. Ngati m’modzi mwa iwo sanakhwime kokwanira kuti angakwanitse moyo umenewo amayamba zibwenzi.

• Kusowa wocheza naye ndi kuiwalidwa: anthu amaona ngati wokondedwa wawo

> 5:12 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

sakuwakondanso kapena wasiya kuwasamala ndipo amakayang’ana izi kwina. • Zikhulupiliro zakusiyana pakati pa amai ndi abambo: anthu ena amakhulupilira

kuti mwamuna sangathe kudzigwira akafuna kugona ndi mkazi ndipo ayenera kukhala ndi akazi ambiri kuti asangalale; akazi amaona kuti adzingovomera panthawi yogonana ndipo amalephera kulankhula nkhani ya kugonana kapena kuyesa njira zina.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjasasankhakukhalaosakhulupilikangatinjirayotheselamavutoawo

mbanja.Apatseni kulimba mtima kuti athane ndi mavuto awo mwamtendere ndikufikamogwirizana.

• Mukhalandikusungachikondichenichenipakatipainundiokondedwawanupomayankhulana bwino, kuthetsa mavuto limodzi, ndikukhala okhulupilika kwa wina ndi mzake.

MalembaKorani 17:32Korani 22:1-6Korani 2:27Korani 49:121 Akorinto 7:3-5Aefeso 5:22-33

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:13

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja aganizila mwakuya ndi kukambilana zotsatila za kukhala ndi zibwenzi kunja kwa banja zomwe ndi kuphatikizapo kubweretsa HIV mnyumba.

Zolinga• Kuthandizamaanjakumvetsetsakutikusakhulupirikakulindizotsatilazoipa

ndipo kuyenera kupewedwa.

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja za ntchito yapambuyo pa iyi pomwe amaona tanthauzo la kukhala okhulupirika ndi zomwe zimayambitsa kusakhulupirika. Fotokozani kuti ngati gulu, tipitiliza kukambilana mwa kuya za nkhani yakusakhulupilika poyang’ana zotsatila zakusakhulupilika.

Khwerero 1: Funsani anthu kukambilana mafunso awa:

• Kuchitazibwenzikungadzetsemavutoanjimbanja?• Afunseningatialindizitsanzozamakomoomweanakhuzidwapondikhalidwe

lokhala ndi zibwenzi kunja kwa banja. Awuzeni kuti simukusoweka kudziwa mayina awo.

• Lolanikutianthuakambilane.

Khwerero 2: Omba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Chibwenzi chimasokoneza maanja munjira zosiyanasiyana. Chotsatira choipakwambiri ndi kupupusisidwa kumene winayo amakumva akamva za chibwenzi cha mnzakeyo. Ndikovuta kuti uyambenso kumkhulupilira mzako yemwe anakachita chibwenzi kunja kwa banja.

• Winaakakhalandichibwenzikunjakwabanja,angathekubweretsaHIVmnyumbandikumupatsila mzake. Kafukfuku akusonyeza kuti anthu amene ali mbanja ali pa chiopsezo chachikulu chotenga kachilombo ka HIV chifukwa chakuchuluka kwa chiwerengelo cha maanja omwe mmodzi amakhala ndi zibwenzi zina. Pokhala okhulupilika kwa mzanu wa banja mumachepetsa chiopsezo chofalitsa kachilombo ka HIV kwa ena, banja lanu komanso mudzi onse.

• Zibwenzizimayambitsamavutoosatikwamwamunandimkaziokha,komansopa kakhalidwe ka pakhomopo. Ngakhale winayo atakhala kuti sanadziwe za chibwenzicho, koma zotsatira zake zimayamba kupweteka. Wozembayo sakhalapo kawirikawiri ndipo amabwera mochedwa ndipo chidwi chake chimachepa pa banjalo. Nkhani za chuma zingatuluke ngati m’modzi wosakhulupirikayo akuononga ndalama pa mphatso za chibwenzi. Zotsatira za zibwenzi zimakhudza gawo lirilonse la banjalo.

• Zibwenzi zimatha kudzetsa mavuto pa ana. Ana ena amasokonezeka akaona

> Ntchito 4: Zotsatira za kuchita zibwenzi

> 5:14 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

zowawa zimene makolo awo akukumana nazo. Anawo angathe kukhudzidwa kwambiri kamba kakusapezekapezeka pakhomo kwa kholo limodzi. Ena angathe kutengera khalidwe la makolo awo ndikuzachita zomwezo mu zibwenzi zawo.

• Mwamuna ndi mkazi angathe kukonza banja lawo ngati kukhulupiliranakwasokonekera koma zimavuta ndipo zimatenga nthawi. Zibwenzi zimathetsa banja, ndipo izi zimakhudza banja lonse – makamaka ana. Amayamba kuona chitetezo cha kholo losiyidwalo ndipo amadana ndi kholo linalo.

• Khalidwelochitazibwenzilimatanthauzakutimukuphwanyachipanganochanundi Mulungu/Allah.

ZopemphereraNgati banja:• Pempheranikutimulunguamangensomaanjaosweka.Pempherelanianaomwe

amavutika pakakhala kuti palibe mtendere pakati pa makolo• Mukhalendimphamvuzakukhalaokhulupirikakwaokondedwawanukuti

mumuteteze.• Pempherelaniiwoomweakuvutikachifukwachakusakhulupilikakwa

wokondedwa awo.

MalembaKorani 17:32Korani 24:2-3Korani 5:5Miyambo 6:26-29, 32-34

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:15

>Nthawi: Mphindi 30

Zida zofunikiraMapepala, mapentopeni, ulusi, mapepala olembapo akulu akulu.

Kukonzekera mwapadera kwa Mlangizi• Werengani mfundo zofunikila zokhuza kangaude wa chiwerewere zomwe zili

kumapeto abukhuli.• Mumvetsetsemgwirizanoomweulipopakatipakangaudewachiwerewerendi

HIV/Edzi.

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana zotsatila zokhala ndi zibwenzi kunja kwa banja makamaka kuopsa kopezeka mu chipwirikiti cha chiwerewere. Nthano zomwe ziri mu gawoli zithandiza maanja kumvetsetsa momwe HIV imafalira msanga mu kangaude wa chiwerewere.

Zolinga• Kuthandizamaanjakumvetsetsazamgwirizanoomweulipopakatipachipwirikiti

cha chiwerewere ndi HIV/Edzi.• Kuwathandiza maanja kumvetsetsa zakuopsa kopezeka mu kangaude wa

chiwerewere.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani zokambilana powawuza maanja kuti:

• Tiwonakuopsakokhalandiabwenziambiriogonanawonthawiimodzi.• Fotokozanikutichipwirikitichachiwerewerendichiyani.(Onanikumapetokwa

bukhuli). • Akumbutseni kuti kudziwa za momwe mthupi mwawo muliri ndi kukhala

okhulupirika kwa wina ndi mzake ndi imodzi mwa njira zopewera kubweretsa HIV mnyumba.

Khwerero 2: Awuzeni anthu kuti akambilana kuopsa kwa kugonana ndi anthu ambiri kudzera mu sewero losonyeza momwe kangaude wa zibwenzi amakhalira:

• Pezani anthu odzipereka okwana khumi kuchokera mu gulu (Amai asanu ndiabambo asanu ngati nkotheka). Fotokozani kuti odziperekawo atenga mbali mu kasewero kakang’ono kokhudza kangaude wa chiwerewere.

• Nkhaniilimmusiyindiyongothandizila,mungathekusinthamayinawondikuyikamoena. Mungathenso kuwafunsa anthu ena mgulu kuti athandize kufotokoza za zibwenzi zomwe zimachitika, kumpatsa aliyense dzina, chiwerengero cha zibwenzi, ndi zifukwa zimene akukhalira mu kangaude wa zibwenzi. Ndikofunika

Ntchito 5: Kukambirana kwapadera za HIV/Edzi ndi mchitidwe wokhala ndi abwenzi ambiri ogonana nawo

> 5:16 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

kuti muonjezere zibwenzi zina zambiri, ndipo owonjezeredwawo ayime pafupi ndi omwe analipo kale aja.

• Ngati mukufunamungathe kusankha anthu ozipereka kuti agwire kumapeto ampila wa ulusi ndipo mu udutsitse kuti wina aliyense agwireko mbali imodzi kuti muonetse momwe anthu amalumikizilana mu kangaude wa zibwenzi. Ulusiwo uziyenda pakati pa anthuwo kumafotokoza za zibwenzi zomwe zingachitike. (Mwachitsanzo: Mussa agwira ulusi omwe umulumikize ndi Maria, keneko ubwerela kwa Mussa mkupita kwa Joice, kenakonso kwa Mussa mkupita kwa Sara.....)

Khwerero 3: Pogwiritsa ntchito nthano yomwe iri kumapeto kwa ntchitoyi, awuzeni amayi ndi abambo omwe azipereka aja kuti ayimilire kuti awonetse ubwenzi omwe uli pakati pawo.

Khwerero 4: Mu chisoti kapena kabokosi:

• Ikanizidutswazamapepalaokwanakhumi.• Mapepalaawiri akhalendi chizikirochophatikiza (+)asanundiatatuotsalawo

akhale ndi chizindikilo chochotsera (-)• Mapepalawoasakanizidwe.• Funsani anthuwo kuti atenge kapepala kamodzikamodzi, komamuwauze kuti

asamasule mpakana atauzidwa.

Khwerero 5: Onse akamaliza kutola, auzeni kuti amasule mapepala awo.

Funsani anthu kuti aimike manja:

• Ndiatiamenealindichindikirochophatikiza?• Ndiatiamenealindichizindikirochochotsera?

Khwerero 6: Kambiranani zotsatira ndi gulu:

• MunthuyemwealindikachirombokaHIVpakatipaanthuamenewaakukhudzabwanji anthu enawo?

• Sonyezanigulukutingatim’modziyekhaalindiHIVpagululimeneli,aliyenseamene akugona naye pagululi ali pa chiopsezo. Pamene kugonana kuli kowilikiza, chiopsezonso chimakula.

Khwerero 7: Gawanani ndi gulu lonse mfundo izi:

• Ambirimwa ife sitidziwakuti tirimuchipwirikiti chachiwerewere,makamakangati tiri ndi anthu ambiri amene tikugonana nawo.

• AnthuapabanjandiamenealipachiopsezochachikuluchaHIVchifukwachakukula kwa mchitidwe wa chisembwere.

• Kukhalandizibwenzizambirindiponsokukhakamuchipwirikitichachiwerewerechimakuikani inu ndi wokondedwa wanu mu chiopsezo cha HIV.

• Ngatimukukhalandimavutom’banjamwanundipomukuyesedwakukhalandichibwenzi, funani uphungu kuti mukonze mavutowo. Musayese kupeza njira pofuna kukagonana ndi ena.

• Imfa ya makolo yodza kamba ka HIV/Edzi ikukuonjezera chiwerengero chaana amasiye pa dziko lapansi. Kodi mukufuna kuti ana anu adzakhale amasiye?

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:17

Ganizani musanagwe mumchitidwewu.• Ngatimunakhalapondichibwenzikunjakwabanjalanu,mungathekupezekandi

HIV ndipo munaapatsire mnzanu wabanja. Njira yokhayo yodziwila ndikupita kukayezetsa HIV; maanja ayenera kupita kukayezetsa limodzi.

• Kukhalamukangaudewachiwerewere/zibwenzindikoopsakwambirikwaanthuamene ali kale ndi kachilombo ka HIV chifukwa chakuti amakhala pa chiopsezo chotenga tizilombo ta mtundu wina ta HIV komanso amakhala pa chiopsezo cha matenda opatsilana kudzela mukugonana.

ZopemphereraPempherani ngati banja, kuti:• Iwoomwealimukangaudewachiwerewere/zibwenzikutiMulunguawathandize

kutulukamo.• Pempherelani iwo omwe mitima yawo ndi yosweka chifukwa chodziwa kuti

wokondedwa wawo amawazembera.• Iwoamenealindizibwenzikunjakwabanjaapezemphamvuyogonjetsamayesero

ndi kukhalanso okhulupilika kwa wokondedwa wawo.

MalembaMarko 11:25-26Miyambo 5:15, 18-20Korani 23:1-6Korani 24:30-31Korani 25:68Korani 16:90Korani 4:29

> 5:18 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

 • Maria ndi Mussa ali pa banja (mwamuna ndi mkazi aima pakati).

• Mussa amakonda mkazi wake kwambiri, koma wakhala akuyenda ndi Mariya

kwa zaka ziwiri (Mariya aima pafupi ndi Mussa).

• Mwapatalipatali amayenda ndi Sara, yemwe amagwira ntchito mu bala mdera

la mumzinda womwe amakachita geni (Sara aimanso pafupi).

• Mariya, ngakhale amamukonda Mussa kwambiri, sakhutitsidwa ndi

ubwenziwo. Ali ndi John m’moyo wake, amene amakumana naye mwa apo

ndi apo. Amamuthandiza pamavuto ena a zachuma ndipo amasangalala naye

nthawi zambiri. (John aima pafupi ndi Mariya).

• Sara, ali ndi chibwenzi, Mavuto, amenenso amamuthandiza. Koma,

ndiosadalirika ndipo nthawi zina amagona ndi amuna ena kuti azidzimva

kufunika, azimugulira mphatso ndi kumupatsa ndalama.

• Mateyu amakumana naye pafupipafupi ndipo nthawi zonse amakhala naye

limodzi akamapita ku boma kwao kumene amagwira ntchito. (Mavuto ndi

Mateyu aima pafupi ndi Sara).

• Mavuto ali ndi mkazi dzina lake Elube yemwe amakhala naye. (Elube aima

pafupi ndi Mavuto)

• Mateyu ali ndi mkazi dzina lake Naphiri ndi chibwenzi chakalekale dzina lake

Monika. (Naphiri ndi Monika aima pafupi ndi Mateyu) Zingathe

kumangopitilira.….

Nkhani yotsogolera zokambilana za Ntchito 5

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:19

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana mmene angapewere kukhala mu kangaude wa chiwerewere powakumbutsa zomwe zinakambidwa mu ndime zina za mbuyomu zokhuza kukambilana momasuka ndi kukambilana nkhani zokhuza kugonana mbanja.

Zolinga• Kulimbikitsamaanjakutiakhaleokhulupirikakwawinandimzake.• Kupezanjirazamomwemaanjaangapeweremayesero.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani phunziro powadziwitsa maanja kuti tikhala tikuonanso maphunziro ndi ntchito zina za mbuyomu.

Kwerero 2: Werengani phunziro 4, Ntchito 4 ndi 5; Phunziro 5, Ntchito 3.

Akumbutseni maanja za mfundo izi zomwe zinakambidwa mu phunziro awa:-

• Kukambirana za nkhani zogonana nkofunika kwambiri. Kafukufuku wambiriwaonetsa kuti kutha kukamba zakukhosi pa nkhani zogonana kupapititsa mtsogolo moyo wogonana.

• Maanjaamayenerakukambiranamomasukankhanizogonanangatiafunakukhalandi kugonana kosangalatsa. Popanda kukambirana, mwamuna kapena mkazi wako sangadziwe chomwe chimakukomera.

• Popanda kukambirana kwabwino, amuna kapena akazi amayamba kugonanakunja kwa banja zomwe zingabweretse HIV m’banja.

• Kugonanakumakomapakakhalachikondindikukhulupiriranam’banja.• Onetsetsanikutimukusinthasinthamachitidwepakugonanandipomusaopekapena

kuona ngati cholakwika kuyesa njira zina zachilendo. Anthu ambiri amene ali pa banja amadandaula kuti zimatopetsa kumagonana mnjira imodzimodzi, ndipo izi zimapangitsa kuti chidwi chithe. Mwamuna ndi mkazi alimbikitsidwe kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pogonana.

• Amuna ndi akazi akhale ndi nthawi yokwanira kukonzekeretsanampaka onseatakonzeka kugonana. Akuyenera kudziwa kuti amuna ndi akazi amadzuka munthawi zosiyana ndinso munjira zosiyana. Nthawi zambiri mkazi amatenga nthawi yayitali kuti adzuke. Khalani tcheru ndi zofuna za mnzanu. Amuna aphunzire kudzigwira ndi kudikira mpaka mkazi wawo atakonzeka kumulowa. Izi zidzathandiza onse kumva kukoma.

> Ntchito 6: Kupewa chipwirikiti cha chiwerewere

> 5:20 Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti mfundo ziri mmusizi zingathandize bwanji bwanji kupewa kukhala ndi zibwenzi zambiri zogonana nazo:

• Kulankhulanamomasukandimwachilungamo?• Kukwanitsidwapogonanandikulankhulanapankhanizakuchipinda?• KuziperekakwawinandimzakendikwaMulungu?

Khwerero 4: Afunseni ngati ali ndi zina zowonjezera za zomwe maanja akuyenera kuchita kuti apewe kukhala mu chipwirikiti cha chiwerewere kuti achepetse chiopsezo chawo ku HIV ndi matenda ena opatsilana pogonana.

ZopemphereraPempherani ngati banja:• Kutimuthakukhalaokhulupirikakwawinandimzake.Mulunguyekhandiamene

angatithandize kugonjetsa mayesero ofuna kukhala osakhulupilika kwa wina ndi mzake.

• Pempherani kutiMulungu atithandize kuti tizitha kukambilanamomasuka ndiwokondedwa athu nkhani zokhuza kugonana kuti tisakhalenso ndi zifukwa zotulukila mbanja ndikupita kunja kukafuna kukwanitsidwa.

MalembaKorani 23:1-6Korani 24:30-31Korani 17:34Miyambo 5:18-19Aefeso 5:26-29

Komanso Mtumiki Muhammad madalitso ndi mtendere zipite kwa iye anati:’Ngati m`modzi wa inu aona mkazi (ndipo akumusirira),Iye ayenera kuthamangira kwa mkazi wake kuti akathandizike(kukagonana naye)chifukwa kutero kudzampeputsira iye kuchimwa potsatira chilakolako chake.

> Phunziro 5: Kugonana kunja kwa banja - Chigololo 5:21

Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti ndizotheka kukhala okhulupirika kwa wina ndi mzake ndipo ayenera kuyesesa kolimba kupewa zinthu zomwe zingawalepheretse iwo kukhala okhulupilika.

Khwerero 2: Ombani mkota pofotokoza kuti :

• Taona mfundo zikuluzikulu zokhuza kugonana kunja kwa banja, zina mwamfundozi ndi monga izi:

- Pali zinthu zambiri zimene zimapangitsa anthu kukhala osakhulupilika kwa okondedwa awo zomwe ndi mavuto a mbanja, kufuna chikondi,

kusakwanitsidwa ndi moyo wawo wogonana, kumva kusalidwa ndi zina. - Zotsatila za kusakhulupilika zimakhuza mbali zosiyasiyana za moyo

wabanja. Zimakhuza mzako wa banja and ana ndi banja lonse. - Mmalawi muno HIV ikufala kwambiri kudzera mu mchitidwe wokhala ndi abwenzi ambiri ogona nawo nthawi imodzi. Kukhala ndi mabwenzi ambiri ogona nawo kumayika moyo wanu ndi wawokondedwa wanu pa chiopsezo chotenga HIV ndipo izi zili ndi zotsatila zoopsa kwambiri ku banja lanu. Khalani ndi mkazi/mwamuna wogonana naye mmodzi yekha ndi kuchepetsa chiopsezo chotenga HIV ndikupatsila okondedwa wanu.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli. Alimbikitseni maanja kukakambilana za m’mene angakhalire okhulupirika kwa wina ndi mzake.

Malemba owonjezeraMasalmo 128:1-3Levitiko 15:19; 1 Akorinto 7:3-5, Eksodo 20:14Korani 30:21Korani 23:4- 6Korani 24:1-6

> Kuomba mkota wa phunziro 5

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:1

Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- Kuteteza mwana

ku HIV Kupezeka kwa banja lomwe mmodzi ali ndi HIV wina alibe ndi nkhani yomwe anthu ambiri samayimvetsa ndipo imabweretsa mavuto ambiri mbanja.

Mu phunziro iri tikambirana momwe banja lomwe wina ali ndi HIV wina alibe angakhalire mu banja lawo ndi zomwe akuyenera kudziwa ngati akufuna kukhala ndi mwana.

Ntchito zomwe zirimbikitse aliyense kutengapo mbali zithandiza kukambilana zikhululupiliro zokhuza kukhala ndi banja lomwe wina ali ndi HIV wina alibe, kufukula mwakuya ubwino wokayezetsa HIV ngati banja ndikufotokoza kuti zimatheka bwanji kukhala ndi banja momwe wina ali ndi HIV wina ayi komanso nkhani ya momwe amayi omwe ndi HIV angapewere kupasila mwana wawo HIV.

Phunziro 6

> 6:2 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

> Phunziro mwachidule

Omwe akuyenera kuphunzira phunziro iriAnthu omwe ali m’banja

Ntchito 1. Mutu2. Phunziro mwachidule3. Kutsegulira phunziro 64. Miyambo ya makolo5. Mfundo zokhuza HIV/Edzi6. Banja lomwe wina ali ndi HIV wina alibe7. Kuyezetsa HIV ngati banja8. Mmene tingachitile ndi zotsatila za kuyezetsa9. Kupewa kufala kwa HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana10. Kukhala moyo wachiyembekezo ndi HIV11. Kuomba mkota12. Ntchito ya kunyumba13. Malemba

Nthawi yofunikaMaola atatu ndi mphindi 20

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zokambirani nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zolingana ndi mutuwu komanso

zolembedwa zina.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:3

> Kutsegulira phunziro 6

Nthawi: 20 Mphindi

Malangizi apadera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati munakumanapo kale, akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Zokambirana mwachiduleAlandileni maanja kuzokambilana ndikuwawuza kuti akhala akukambilana pa mutu wakuti kukhala mbanja lomwe mmodzi ali ndi HIV-Kuteteza mwana ku HIV. Maanja akambirana zomwe zimachitika kuti mmodzi mbanja akhale ndi HIV wina alibe, ubwino woyezetsa HIV limodzi ngati banja ndi momwe mayi woyembekezera yemwe ali ndi HIV angapewere kumupatsila mwana wake.

Zolinga• KumvetsetsabwinokutimunthummodzikukhalandiHIVmbanja

kumatanthauza chani?• Kuthandizamaanjakumvetsetsakufunikakothandizanazikawawonekerazotere.• Kulimbikitsakuyezetsamagazilimodzingatibanja.• KumvetsetsazambirizamomweHIVimafalirakuchokakwamayikupitakwa

mwana ndi kudziwa kuti ndi njira ina imene HIV imafalira ndi momwe maanja angathandizilane pofuna kuteteza mwana ku HIV.

Ndondomeko

Khwerero 1: Afotokozereni maanja mfundo izi:

• Kwaanthuawiriomwealim’banja,winaakhonzakukhalandiHIVwina osakhala nayo. Wina akapezeka ndi HIV sizikuthandauza kuti anali osakhulupilika. Ndi chifukwa chake kuli kofunika kuyezetsa musanalowe mbanja.

• NjirayayikuluyachiwiriyamomweHIVimafalirandikuchokerakwamayikupita kwa mwana.

• MbanjamomweonseawirialindiHIVkapenammodzialinayowinaalibe,akhonza kupanga chiganizo chokhala ndi ana kapena ayi atalandila uphungu wabwino.

• AnthuamenealindiHIVangathekukhalandimaanjaathanzindiokondanandikukhala moyo wawutali wotukuka.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Maanjaatengenawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizekutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse.

• Maanjaakhalendimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momwe amaonera zinthu komanso mfundo zina zofunikira.

> 6:4 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

• Maanjaaphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo.

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti:

• Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

Khwerero 4: Afunseni maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi kudzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kukhala mbanja lomwe mmodzi ali ndi HIV, kuyezetsa magazi ngati banja ndi Kuteteza mwana ku HIV. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupezazikhulupiliromiyamboyosiyanasiyanandizinazomweanthu samazimvetsetsa zokhuza kukhala mbanja lomwe mmodzi ali ndi kachilombo ka HIV, kuyezetsa magazi ngati banja ndi Kuteteza mwana ku HIV. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizemaanjakumvetsetsa za kukhala mbanja lomwe mmodzi ali ndi HIV, kuyezetsa magazi ngati banja ndi Kuteteza mwana ku HIV.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti:

Akambirana za zikhulupiriro ndi zoyankhulidwa zokhuza kukhala mbanja lomwe mmodzi ali ndi HIV, kuyezetsa magazi ngati banja ndi Kuteteza mwana ku HIV. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti atchulepo miyambo ndi zonenedwa zina zokhudza mutu umenewu. Perekani nthawi yoti akambirane.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu:

• Amenealibekachiromboamatengedwakutindiyeamapatsiraenandipoiyesadwala.

• Omwemagaziawondiagulu‘O’samatengaHIVkomamangopatsilaena.• AmenealindiHIVanaliwosakhulupirika.• Mayiakakhalakutindiamenealindikachilombo,Banjalikuyenerakuthakoma

akakhala kuti ndi mamuna amene ali ndi kachilombo, banja likhalepobe.• MbanjamomwemmodzialindiHIVwinaalibeasakhalendiana.• Sizothekakutim’mbanjawinaakhalendiHIVpomwewinaalibe.

> 6:6 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilanazi potsindika mfundo izi:

• HIVingathekubwerambanjandibambokapenamayi,choterobanjalikuyenerakupitilira ndipo akuyenera kukhala achifundo kwa wina ndi mzake ndi kuthandizana.

• Pokhapokhangationseanayezetsaasanalowembanja,ndizosathekakunenakutiwina anali osakhulupirika. Mayi kapena bambo akhonza kulowa mbanja ali kale ndi HIV koma osaziwa kuti ali ndi HIV.

• MaanjaomwealindiHIVangathekukhalandianaomwealibeHIV.Chofunikilandi kupita kukalandila malangizo kuchipatala.

• NdizothekammodziwaanthuawiriomwealimbanjakukhalandiHIVngakhaleakhala akukhalila limodzi mosaziteteza.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaasiyemiyambondinkhambakamwazomwezimalimbikitsakufalakwa

HIV.• Mulunguathandizemaanjakuonansomiyambo,nkhambakamwandizoyankhula

zomwe takula nazo zomwe timazikhulupilira koma zili zotsutsana ndi mawu.

MalembaMateyu 9:35-361 Yohane 1:9Korani 30:21Korani 66:6

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:7

> Ntchito 2: HIV ndi EDZI

Nthawi: Mphindi 20

Kukonzekera mwapadera kwa MlangiziWerengani Mfundo zokhuza HIV kumapeto kwa Bukhuli.

Zokambirana mwachiduleMaanja akumbutsidwa mwapatali patali nkhani zokhuza HIV ndi Edzi. Apatsidwa mpata wofunsa pamene samamvetsetsa nkhani zokhuza HIVndi Edzi.

Zolinga• KuwadziwitsaanthuzambirizokhuzaHIVndiEdzi.• KuwathandizamaanjakumvetsetsazinazokhuzaHIVndiEdzi.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani phunziro powadziwitsa maanja kuti:

• TikhalatikuphunzilazokhuzaHIV/Edzi.• HIV/Edziikhonzakukhuzachiyanjanochathundibanjalathulonse.• TikuyenerakudziwazambirizaHIV/Edzindikuonetsetsakutitikuzitetezatokha

komanso banja lathu.

Khwerero 2: Kumbutsani anthu mfundo zokhazikika zokhuza momwe HIV imafalira pogawana nawo izi. Ngati musowa mau owonjezera, onani kumapeto kwa bukhuli:

• HIVndikachirombokamenekamaonongachitetezochamthupilamunthuHumanimmunodeficiencyvirus).Kachirombokandikamenekamayambitsamatenda a Edzi.

• HIVmunom’Malawiimafalakwambirikudzeramukugonanakosadzitetezandimunthu amene ali ndi kachiromboka. Kusadziteteza kutanthauza kuti awiriwo sanagwiritse ntchito kondomu.

• HIVingafalensokupyoleramumadziomweamakhlamthupimwamunthumonga, magazi, umuna ukazi,mkaka ndi ena.

• HIVimafalansokuchokakwamaikupitakwamwananthawiimenemaiyoaliwoyembekezera, nthawi yobereka, kapenanso nthawi yoyamwitsa mwanayo atabadwa.

• HIVimafoolachitetezochamthupi.Chitetezochamthupindichimenechimathandiza kumenyana ndi matenda. Chitetezo cha mthupi chikafooka sichingamenyanenso ndi matenda, munthuyo amati akudwala matenda a Edzi.

• PalimankhwalaotchedwamaARVameneamathandizamunthuyemwealindiHIV kukhala moyo wautali, wamphamvu ndi wosangalala.

> 6:8 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

• AnthuamenealindiHIVangathensokukhalandimaanjaachikondi,osangalatsandi amphamvu.

• KulibemankhwalaochizaedzikomanjirayokhayoyodziwirangatiulindiHIVndi kupita kukayezetsa.

Khwereo 3: Funsani gulu ngati liri ndi mafunso ena. Yankhani amene muli womasuka kuyankha.

• Kwa mafunso omwe simukudziwa yankho lake, kapena sindinu omasukakuyankha , alembeni penapake ndipo muwauze kuti mudzawapatsa mayankho mukakumananso.

ZopemphereraPempherani ngati banja:• KutiomwealindindiHIVkapenaomwealindiabalekapenamakoloomwealindi

HIV, Mulungu/Allah awalimbikitse kupanga zisankho zomwe zingawathandize kukhala moyo wawutali ndi wathanzi.

• Omweakugwirantchitozachipatalamdelalathu,kutiawonetserekutiamayidziwantchitoyawo,chifundo,nzerundikusakonderapofikilazosowazaomweakufunathandizo lawo. Tipemphere kuti mzipatala mukhale makhwala ndi zida zofunikila zokwanila.

• Chikondi chenicheni chifukwa chikondi chenicheni chimathamangitsa manthaangakhale mantha omwe amabwera chifukwa chokhala ndi HIV mbanja mwathu.

MalembaEzekieli 37:1-141 Yohane 3:16Aefeso 5:26-29Korani 39:9Korani 16:43

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:9

> Ntchito 3: M’banja momwe wina ali ndi HIV wina alibe

Nthawi: Mphindi 30

Kukonzekeramwapadera kwa Mlangizi• Phunziroirindilokhuzazachipatalachoterondikofunikakuyitanawachipatala

kuti azathandize kuyankha mafunso omwe anthu angakhale nawo kapena kuwatumiza anthu kuchipatala kuti akayankhidwe mafunsowa.

• Palimfundozinazowonjezerakumapetokwabukhulizomwezingakhalezothandiza kuyankha mafunso ena omwe angafunsidwe.

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuwona imodzi mwa nkhani zovuta zokhuza HIV ndi Edzi-banja lomwe mmodzi ali ndi HIV. Aphunzira kuti izi zimatheka bwanji, zovuta zomwe anthu amenawa amakumana nazo. Aphunziranso kuti kodi ngati banja anathandizane bwanji izi zitawachitikila.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakutizimathekabwanjikutimbanjammodzi

akhale ndi HIV pamene wina alibe.• Kuperekachiyembekezokwamaanjaomwendiokhuzidwandikuwathandiza

momwe angachitile ndi vuto ngati limeneli.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani phunziro powadziwitsa maanja kuti:

• TikhalatikukambilanazokhuzabanjalomwemmodzialindiHIVpamenemzakewa banja alibe.

• AkumbutsenimaanjakutimunthummodzimbanjaangathekukhalandiHIVpamene mzake wa banja alibe.

• Anthuambiriamasokonezekakutizingathekebwanjiwinakugonandimnzakeamene ali ndi HIV koma osakatenga.

• IzizimachitikamakamakangatimunthualinditizilombotaHIVtochepamthupi mwake. Anthu amakhala ndi HIV yochepa pamene asilikali a mthupi aononga tizilombo tambirita HIV tomwe tinali mthupi. HIV imachepanso mthupi pamene munthu akumwa ma ARV. Ma ARV amalepheretsa tiziromboto kuti tisaberekane.

Khwerero 2: Afotokozereni onse kuti:

• Palinjirazitatuzomwezingapangitsekutimbanjammodziakhalendikachilombo pamene wina alibe.

- M’modzi akhoza kukhala kuti anatenga kachiromboka asanalowe m’banja- mwina anagonanako ndi munthu m’buyomo. Ngati sanakayezetse sangadziwe ngati ali ndi HIV kapena ayi.

> 6:10 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

- Mmodzi wa iwo anabadwa ndi HIV koma sanauzidwe kuti ali ndi kachilombo.

- Njira ina ndi yakuti m’modzi kapena onsewo anakachita chiwerewere kwina ndipo anatenga HIV.

Khwerero 3: Afunseni kuti maanja aganizire za:

• Anthuomwealimbanjawinaalindikachilombowinaalibe(awuzenikutisimukufuna kudziwa mayina awo, pokhapokha ngati ali omasuka kutchula mayinawo).

• Amakumanandimavutoanji?• NgatisakudziwabanjalinalirilonselomwewinaalindiHIVwinaalibe,

afunseni kuti akuganiza kuti banja lotereli lingakumane ndi mavuto anji?

Khwerero 4: Gwanani ndi maanja onse mfundo izi:

• Maanjaomwemmodzialindikachilombopamenewinaalibeangathekukumanandi mavuto awa:

- Kusakhulupirilana. Yemwe alibe HIV angathe kuganiza kuti mzakeyo amamuzembera.

- Kuwulula kwa abale ndi anthu ena za momwe aliri zomwe zingathe kubweretsa kusankhidwa ndi kusalidwa.

- Kunyozedwa ndi anzawo, abale ngakhale mwamuna/mkazi wawo atatha kuwulula kuti ali ndi HIV.

- Yemwe alibe HIV akhonza kumakana kukhalira limodzi ndi bwenzi lakeyo poopa kuti angathe kutenga HIV komanso ngakhale atakhalira limodzi angathe osakwanitsidwa kwenikweni.

- Akhonza kukhala ndi nkhawa pankhani yokhuzana ndi kukhala ndi ana - Ntchito yosamalira yemwe akudwala. • AkumbutsenikutinjirayokhayoyoziwirakutiulindiHIVkapenaulibendi

kuyezetsa.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• KwamaanjaomwemmodzialindiHIVMulunguawapatsechilimbikitso

chovomereza zotsatila za kuyezetsa kwawo ndi kutsatila zomwe analangizidwa kuti akhale moyo wabwino.

• KutiMulunguathandizeyemwealibeHIVkukhululukilamzakeyongativutolinabwera chifukwa cha kusakhulupilika.

• Ngatimpingo/mzikititikuyenerakupemphererandikuwalimbikitsaiwoameneali ndi HIV.

• Kwaiwoomweamazisankhaokhandipoamamvakutianthuonseakuwasala.• Chikhululukilopamawuathu,zochitazathundizinazomwe

zimawakhumudzitsa kapena kuwasala ena. Malemba1 Atesalonika 5:15Mateyu 5:23Korani 4:35, 135Korani 2:195

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:11

> Ntchito 4: Kuyezetsa limodzi ngati banja

Ntchito: Mphindi 30

ZokambiranaMaanja ayamba kukambilana za ubwino opita kukayezetsa magazi limodzi ngati banja ndipo momwe angawalimbikitsile ena kuti nawonso apite akayezetse. Ntchitoyi ithandiza maanja kupita kukayezetsa limodzi ndi njira yabwino yochitila ndi zotsatila. Zolinga• Kulimbikitsamaanjakupitakukayezetsalimodzi.• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakufunikirakopitakukayezetsalimodzi.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani zokambilana pofotokoza kuyezetsa ngati banja kuti:

• Kukutanthauzakupitakukayezetsangatibanja,kulandilazotsatilandikukonzekera moyo wawo wa mtsogolo.

Khwerero 2: Werengani nkhani yomwe ili kumapeto kwa ntchitoyi.

Khwerero 3: Mukawerenga nkhaniyo, kambilanani ndi maanja mafunso awa:

• Tikuphunzilapochanikuchokerakunthanoiyi?• NdichifukwachiyanikulikofunikakukalandirauphungundikuyezetsaHIV

limodzi ngati banja?• AngamvebwanjiwokondedwawawoatawapemphakutiapitekukayezetsaHIV

limodzi?• AngataniwokondedwawawoatapenenakutiapitekukayezetsaHIVlimodzi?• Angalimbikitsebwanjimaanjaenakupitakukayezetsa?

Khwerero 4: Akumbutseni mfundo zofunikila zotsatilazi:

• Maanjaayenerakukayezetsalimodzikutiathekukambiranapazotsatirazakendikukonzekera moyo wakutsogolo.

• Zotsatilazakuyezetsazingathekuwathandizamaanjakupangachiganizochokhuza kulera kapena kubereka.

• Maanjaangathekuthandizanakukhalamoyowodalirikangatim’modzimwaiwokapena onse ali ndi HIV.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Omweakugwirantchitozachipatalamdelalathu,kutiawonetserekuti

amayidziwantchitoyawo,chifundo,nzerundikusakonderapofikilazosowazaomwe akufuna thandizo lawo, komanso kuti mzipatala mukhale makhwala ndi zida zofunikila.

• MaanjakutiMulunguawapatsechilimbikitsochopitakukayezetsamagazindikuvomera zotsatila zake bwinobwino.

MalembaMateyu 19:5-6; Korani 39:9

> 6:12 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

Nkhani ya ntchito 4

  Abambo ena ake anadwala ndikumwalira atadwala kwa nthawi yayitali. Mkazi wake anali wokhuzidwa kwambiri ndi imfa ya mamuna wake. Atayika maliro, akuntchito kwa abambowo anamupempha kuti akatenge zinthu zomwe mwamuna wake anasiya kuntchito. Mmene amatenga zinthuzo, anapeza botolo loyera, lomwe linali ndi mapilitsi mkati mwake. Anatenga botolo ndikukamufunsa mzake yemwe anali namwino kuti mankhwalawo ndi achani. Anadzidzimuka mmene mzakeyo anamuuza kuti mankhawalawo ndi ma ARV. Kenako anazindikila kuti mwamuna wake anamwalira chifukwa cha Edzi. Anapita kukayezetsa ndipo nayenso anapezeka ndi HIV.

 

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:13

> Ntchito 5: Kulandira zotsatira za kuyezetsa

Nthawi: Mphindi 30

Kukonzekera mwapadera kwa MlangiziPhunziro ili ndi lokhudza za chipatala chotero ndikofunika kuyitana wa chipatala kuti azathandize kuyankha mafunso omwe anthu angakhale nawo kapena kuwatumiza anthu kuchipatala kuti akayankhidwe mafunso awo.Mungathe nso kuwerenga mfundo zina zowonjezera kumapeto kwa bukhuli. Kumbukilani kupanga nthano zimene anthu agwiritse ntchito pokambilana.

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana nkhani zosiyana siyana zokhuza banja limene mmodzi ali ndi HIV pamene wina alibe. Mumagulu ang’onoang’ono ayamba kumvetsetsa kuti izi zingathe kuchitika mosiyana maanja osiyanasiyananso.

Zolinga• Kuzamitsachidziwitsochamaanjapankhanizokhuzabanjamomwemodziali

ndi HIV wina alibe.• KuwapatsachiyembekezomaanjaomwemmodzialindiHIVwinaalibendi

kuwathandiza kuti angachite bwanji ndi moyo wawo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani phunziro.

• Akumbutsenimaanjazantchitoyambuyomumomwetimaonazabanjalomwemmodzi ali ndi HIV wina alibe.

• Musanapitirizeonetsetsanikutimaanjaakudziwazaphunzilolokhuzabanjalomwe mmodzi ali ndi HIV wina alibe, ndipo funsani ngati ali ndi mafunso.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti akhale mumagulu ang’onoang’ono a anthu atatu.

Khwerero 3: Perekani nkhani kwa gulu liri lonse (gulu lirilonse likhale ndi nkhani imodzi) Awuzeni kuti akambirana nkhani zokhuza banja momwe mmodzi ali ndi HIV, wina alibe zomwe apatsidwa.

Khwerero 4: Afunseni kuti agawane ndi gulu lonse zimene akambirana.

Khwerero 5: Afotokozereni onse mfundo izi zowonjezera:

Nkhani ya Jane ndi Richard• NdizothekakutiJaneanatengaHIVasanakwatiranendiRichardndipoonse

awiri sanayezetse asanakwatilane. • NdizothekakutinthawiyomweamakwatilanachiwerengerochaHIVmthupi

mwa Jane chinali chochepa kotero kuti chiopsezo chakuti atha kumupatsila mwamuna wake chinali chochepa kwambiri. Choncho Mwamuna wake sanatenge HIV.

> 6:14 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

Nkhani ya Maria ndi Yusufu• NdizothekakutinthawiyomweamapitakukayezetsaanalimunthawiyomweHIV

inali isanayambe kupezeka mmagazi mwake (window period). • AchipembedzoamalolakutibanjalomwemmodzialindiHIVwinaalibeangathe

kumagwiritsa ntchito makondomu. Kotero ndikofunika kuti Maria ndi Yusufu azigwiritsa ntchito makondomu chifukwa Maria nayenso akhonza nthawi yina kudzatenga HIV.

• Ndizofunikiransokwambirikutianthuapabanjaakhaleomasukilana,asabisilanengati wina ali ndi HIV.

Nkhani ya Magreti ndi Filipi• Nthawi imene Filipo amakwatila nkotheka kuti anali atayamba kale kumwa

mankhwala a ma ARV koma sanamuuze mkazi wake. Mankhwala a ma ARVs amachulukitsa chitetezo cha mthupi komanso amachepetsa chiwerengero cha HIV mumagazi. Izi zinapangitsa kuti chiopsezo chopatsila mkazi wake HIV chikhale chochepa.

• AchipembedzoamalolakutibanjalomwemmodzialindiHIVwinaalibeangathekumagwiritsa ntchito makondomu. Kotero ndikofunika kuti Filipo ndi Magreti azigwiritsa ntchito makondomu chifukwa Magreti nayenso akhonza nthawi yina kudzatenga HIV.

• Ndizofunikiransokwambirikutianthuapabanjaakhaleomasukilana,asabisilanengati wina ali ndi HIV.

Nkhani ya Sofiya ndi Matini• NdizothekakutiSofiyaanalindiHIVyochepamthupimwakechifukwachitetezo

chake chinali chitakwera mmene amakwatilana ndi Matini. Izi zinapangitsa kuti chiopsezo chomupatsira mwamuna wake HIV chikhale chochepa.

• Sofiya ndi Matini alangizidwe kuti ngakhale mmodzi ali ndi HIV sichifukwachakuti banja lithe.

• SofiyandiMatiniakuyenerakutsatilandondomekoyatsopanoyamomwemayiangapewere kumupatsila mwana wake HIV.

• Atsogoleri afotokozereni maanja mfundo zomwe zikupezeka pa tsamba 176mpaka 177 komanso zolemba zowonjezera pa tsamba 265 mpaka 268.

• SofiyandiMatiniakuyeneransokuyambakugwiritsantchitomakondomu.

Khwerero 6: Malizani ntchito ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluziku:

• Ndizothekam’modzikukhalandiHIVndipowokondedwawakekukhalawopandaHIV ngakhale atakhala limodzi kwa nthawi yaitali.

• Ngati muli ndi HIV, ndipo mukugonana osaziteteza ndiye kuti mukumuyikapachiopsezo yemwe mukugonana nayeyo. Inunso mukuziyika pa chiopsezo chotenga mitundi yina ya HIV yomwe thupi lanu likuyenera kulimbana nayo. Nkofunika kwambiri kuti mwamuna ndi mkazi onse adziwe momwe mthupi mwawo muliri kuti adziteteze, komanso kutetezana wina ndi mnzake ku HIV, makamaka ngati m’modzi ali ndi HIV pamene wina alibe.

• Ndizothekambanjam’modzikukhalandiHIVwinaalibe.Ndikofunikakutianthuawiri omwe ali mbanja lotere akhale othandizana pofuna kuonetsetsa kuti banja likupitilira kuyenda bwino.

• AnthuomwealimbanjalomwewinaalindiHIVwinaalibeakuyenerakumagwiritsantchito makondomu nthawi zonse pofuna kuteteza yemwe alibe HIV yo.

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:15

• Ngatimulim’banjalomwewinaalindiHIVwinaalibe,tengeranipomwayiwofikiramaanjaenaamenealinsochonchokomaakusowamtendere.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti: • Mulungu/Allahatithandizekukhululukilamongamomweiyeamatikhululukila

ife tikalakwa. Ndi Mulungu/Allah palibe chosatheka.• Mulunguatithandizekukondanandichikondichenicheningakhaleiwoameneali

ndi HIV.• PemphereranimaanjaomweanayezetsandipommodzianapezekandiHIVkuti

athe kusamalana ndi kukondana.

MalembaKorani 2:227-229Korani 5:2Mateyu 6:14-15; 18:21-35Aefeso 5:26-29

> 6:16 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

1. Nkhani 1: Sadayezetse asanamange ukwati; m’modzi mwa iwo adadzapezeka kuti ali ndi HIV:

Jeni ndi Richadi anamanga ukwati asanayezetse HIV. Patapita nthawi ali m’banja, Jeni anapezeka ndi HIV pamene Richadi analibe. Mukanakhala inu mukanatani? Fotokozani kuti zinatheka bwanji kuti zinthu zikhale chonchi.

2. Nkhani 2: Anayezetsa asanamange ukwati koma kenaka, m’modzi apezeka ndi HIV.Mariya ndi Yusufu anakayezetsa HIV asanamange ukwati ndipo sanapezeke nayo ndi HIV. Onse anali okhulupirika kwa wina ndi mnzake. Patapita nthawi, m’modzi mwa iwo anapezeka ndi HIV. Fotokozani kuti izi zinatheka bwanji? Mukanakhala inu mukukanatani pamenepa?

3. Nkhani 3: Mwamuna anabadwa ndi HIV koma sakupatsira mkazi wake. Magireti ndi Filipo anamanga ukwati chaka chatha. Filipo sanaululire Magireti kuti anabadwa ndi HIV. Patapita nthawi ali m’banja, Magireti anatenga mimba ndipo analimbikitsidwa kupita kukayezetsa HIV ndi mwamuna wake Filipo. Monyinyirika, Filipo anapita kukayezetsa ndipo anapezeka ndi HIV pamene Magireti analibe. Zimenezi zinatheka bwanji, nanga mukanakhala inu pamenepa mukanatani?

4. Nkhani 4: Atapezeka ndi HIV bambo anakwiya Sofi ndi Matini anamanga ukwati asanakayezetse. Patapita nthawialim’banja, Sofi anaima ndipo atapita ku sikelo ya amayi anapezekandi HIV. Matini sanapezeke ndi HIV. Mwatsoka Martin, analandira zotsatirazi mokwiya ndipo waganiza zothetsa banja poopa kutenga HIV. Mungalithandize bwanji banja limeneli?

Nkhani yotsogolera zokambilana za ntchito 5

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:17

>Nthawi: Mphindi 30

Kukonzekera mwapadera kwa MlangiziWerengani nkhani zokhuza Kapewa kufala kwa HIV kuchoka kwa mai kupita kwa mwana kumapeto kwa bukhuli.

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuwona za mmene makolo omwe ali ndi HIV angakhalire ndi mwana wathanzi yemwe alibe HIV. Maanja akambilananso mmene abambo angawathandizile akazi awo kupewa kupatsila mwana wawo kachilombo.

Zolinga• Kuwonjezera mzeru za maanja pa nkhani zokhuza kupewa kufala kwa HIV

kuchoka kwa mai kupita kwa mwana ndi kuwalimbikitsa kupita kukalandila nthandizo pa nkhaniyi.

• Kuwathandizabambokumvetsetsaubwinowowathandizaakaziawopankhaniya kupewa kufala kwa HIV kuchoka kwa mai kupita kwa mwana ndi kuvomera kuwathandiza akazi awo.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani phunziro: Adziwitseni maanja kuti tikhala tikukambilana za kupewa kufala kwa HIV kuchoka kwa mayi kupita kwa mwana.

Khwerero 2: Akumbutseni maanja kuti:

• KufalakwaHIVkuchokakwamaikupitakwamwanandinjirayachiwiriimeneikufalitsa kwambiri HIV muno m’Malawi.

• Popanda kuchitapo kanthu, ana 27 kapena 30 pa ana 100 aliwonse ameneabadwa kwa amai omwe ali ndi HIV angatenge kachiromboka. Mwa ana 100 otenga kachiromboka, 65 amakatenga pa nthawi yobadwa, zimenezi zingathe kuchepetsedwa potsata njira zopewera.

• Ngatinjirazopewerazatsatidwabwino,mayiangathekutetezamwanawakekuHIV .

• Pali ndondomeko yatsopano ya kapewedwe ka kufala kwaHIV kuchoka kwamayi kupita kwa mwana ndipo ndikofunika kukapeza malangizo ngati inu kapena akazi anu ali ndi mimba.

Khwerero 3: Awuzeni maanja kuti tsopano apanga sewero lothandiza kuti amvetsetse nkhani zokhuza kufala kwa HIV kuchoka kwa mai kupita kwa mwana:

• AwuzenikutiawerengenkhanizokhuzakufalakwaHIVkuchokakwamaikupitakwa mwana. Afunseni kuti aziyima ngati akugwirizana nazo, kapena akhalebe pansi ngati sakugwirizana ndi chiganizo chomwe chawerengedwa.

Ntchito 6 – Kupewa kufala kwa HIV kuchoka kwa mai kupita kwa mwana (PMTCT)

> 6:18 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

• Pachiganizochirichonse,mmodziafunsegulu: - Mukuganiza kuti ndi chifukwa chani ziri zoona (kwa omwe ayima) - Ndi chifukwa chani mukutsutsana nazo (kwa omwe akhala)

Khwerero 4: Konzani maganizo onse olakwika powerenga nkhani zomwe zili kumapeto abukhuli. Mungathenso kuwonjezera mfundo izi:

• MwamunandimkaziamenealindiHIVkapenam’modzimwaiwoalindiHIVangathe kukhala ndi mwana wopanda HIV. Zofunikila kuti mukhale ndi mwana amene alibe HIV ndi izi:

- Kudziwa momwe mthupi mwanu muliri musanakhale ndi pakati - Mukasankha kukhala ndi mimba onetsetsani kuti muli ndi thanzi labwino. - Pitani ku sikelo ndipo kambiranani za kupewa kupatsira HIV kuchoka

kwa mai kupita kwa mwana (PMTCT) ndi anamwino; tsatani malangizo amene akupatseni• Bungwe lowonazaumoyopadziko lonse lakhazikitsandondomekoyatsopano

yopewera kufala kwa HIV kuchoka kwa mayi kupita kwa mwana. Amayi oyembekezera omwe ali ndi HIV azayimbilatu kumwa mankhwala otalikitsa moyo ama ARV ngakhale chitetezo chawo chitakhala kuti chili bwino.

• Ndi ndondomeko ya makono yi, amayi akulangizidwa kuyamwitsa ana awomomwe akufunila osati miyezi isanu ndi umodzi okha momwe zinaliri poyamba.

• Banjalirilonselikuyenerakukambilanandiadotolozokhuzaganizolawolofunakukhala ndi mwana, mavuto omwe angakhalepo, ndi njira zochepetsera mavutowa.

• Ndikofunika kupewa kufalitsa HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwanapowonetsetsa kuti amai omwe ali pa msinkhu wobereka asatenge HIV. A Khristu/Achisilamu amakhulupilira kuti kudziletsa kwa anthu omwe salipabanja ndi njira yopambana yopewera. Kwa amene ali pa banja, kukhulupirika kwenikweni ndiye kofunika.

• KwaamenealikalendiHIV,chofunikakwambirindikuwatumizakwaazaumoyo/achipatala kuti akalandile uphungu

• Komabe,kwaamaiamenealindipathupindipoalindiHIV,paliumboniwokwanirakuti atamwa makhwala owonjezera chitetezo mokhulupilika ndikutsatila malangizo akuchipatala angathe kupewa kupatsira mwanayo HIV.

• Abamboakuyenerakuwalimbikitsaakaziawokutsatilanjirayatsopanoyotetezeramwana ku HIV.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti: • MaanjaomwealindiHIVndiomwemodziyekhandiamenealindiHIV

koma akufuna kukhala ndi ana kuti Mulungu awathandize kuvomera zovuta zimenezingabwere chifukwa cha momwe aliri ngati atafuna kukhala ndi

ana. • Pempheranikutiomwealipamankhwalaamwemakhwalamokhulupilika

ndi kutsatila malangizo ena omwe angapatsidwe ndikuti athe kukhala ndi ana opanda HIV ngati ali ndi mwayi wokhala ndi ana. • Pempheranikutikuweruzanamumpingo/mzikitikusinthekutianthuomwe ali ndi HIV apeze chikondi ndi chithandizo ndi kugawana mphatso zawo

ndi mpingo.

MalembaAhebri 13:4Aefeso 5:26-29Korani 66:6

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:19

ZIGANIZO ZA NTCHITO 7

• Mayi wina aliyense yemwe ali ndi HIV azakhala ndi mwanayemwe ali ndi HIV (zabodza)

• Palizambirizomwetingachitepofunakumutetezamwanawathukuti asatenge HIV kuchokera kwa mayi. (Zoona)

• HIV ingafale kupita kwa mwana nthawi yomwe mayi ali ndimimba yokha. (zabodza)

• Kugwiritsa ntchito makondomu nthawi zonse ndikofunikilanthawi imene mayi ali ndi mimba komanso akuyamwitsa. (Zoona)

• Ukuyenerakukhalandianthuothandizapofunakuonetsetsakutimwana akudyetsedwa bwino. (Zoona)

• SimungayamwitsemwanawanungatimulindiHIV.(Zabodza)• Moyo wa mayi umakhala pa mpanipani ngati ali ndi mimba

komanso HIV. (Zoona)• AmayionseomwealindiHIVakuyenerakukachilirakuchipatala

(Zoona)• KupewakufalakwaHIVkuchokakwamayikupitakwamwana

ndi udindo wa mayi yekha, bambo sizikuwakhudza. (Zabodza)

> 6:20 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

>Nthawi: Mphindi 30

Ntchito mwachiduleMaanja akambilana momwe munthu yemwe ali ndi HIV angakhalire moyo wokondwa ngakhale ali ndi HIV. Awonanso zinthu zomwe munthu yemwe ali ndi HIV akuyenera kuzipewa ndi zomwe akuyenera kumachita. Zolinga• KuwathandizaomwealindiHIVkutiakhalendimoyowachiyembekezondi

HIV.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti:

• MunthuakadziwakutialindiHIV,maganizoakeamasokonezeka;amakhalandi mantha, kuwawidwa mtima, kukhumudwa, kukanika kuvomereza, mkwiyo komanso kusowa mtendere.

• KupezakandiHIVsizitanthauzamatheroamoyo,chiyembekezochilipo.Ngakhale edzi ilibe mankhwala, pari njira zambiri za momwe ungakhalire moyo wabwino uli ndi HIV.

• MunthuangathekukhalandiHIVkomandikukhalabewathanzi,okwanitsidwandikukhalanso ndi banja losangalala.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti akambilane pamodzi.Perekani nthawi kuti anthu

akambilane.

• NdizinthuzitizomwemunthuyemwealindiHIVakuyenerakuzipewa?• MunthuangakhalebwanjimoyowabwinoalindiHIV?Ndizinthuzitizimene

akuyenea kumachita?

Khwerero 3: Ombani mkota wazokambilanazi potsindika mfundo zili mmusizi zomwe ndi zina mwa zinthu zomwe munthu yemwe ali ndi HIV akuyenera kuzichita.

• Mugawane ndi ena za vuto lanu - Munthu angathe kukhala moyo wabwino ngakhale akudwala ngati anthu

akumukonda ndi kumuvomera monga momwe aliri. Chotero ndi chofunika kuyankhula ndi munthu yemwe angakuthandizeni. Mungathe kuyankhula ndi mzanu, mbale wanu, mlangizi, adotolo/a chipatala, abusa/ashehe, kapena munthu yemwe amapempherela anthu ndi kuchira.

- Kukhala ndi anthu okuthandiza omwe akumvetsetsa za vuto lanu ndikofunika. Anthu ambiri omwe ali ndi HIV amanena kuti izi zimapangitsa moyo wawo kukhala watanthauzo. Zimalimbikitsa moyo wathanzi.

• Mukuyenera kudya bwino - Mukuyenera kuphunzila momwe mungazisamalire komanso kudya

bwino kuti thupi lanu lithe kuthana ndi matenda osiyanasiyana. Chakudya

Ntchito 7: Kukhala ndi chiyembekezo muli ndi HIV

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:21

sichingachilitse edzi koma chikhonza kuthandiza kuti mukhale ndi chitetezo cha mthupi cha mphamvu.

- Idyani zakudya monga zipatso ndi masamba tsiku lirilonse. Zakudya izi zimathandiza kulimbana ndi matenda.

- Idyani nyemba zambiri, mphodza, soya ndi nsomba za mchitini, ngati mungathe gulani nyama ndi nkhuku. Zakudya izi zimathandiza kamanga thupi ndikukuthandizani kuti mukhale ndi mphamvu.

- Idyani mpunga wosapuntha kwambiri, nsima ya mgayiwa, buledi wa bulawuni, mbatata, chinangwa. Zakudya izi zimapatsa mphamvu.

- Muwonjezereponso mafuta, mkaka, chiponde ndi mtedza kuchakudya chanu. Izi zikuthandizani kukhala ndi mphamvu komanso kuti

musawonde. - Imwani makapu osachepera asanu ndi atatu amadzi pa tsiku. - Mukuyenera kusiya kusuta, kumwa mowa ndi kudya zakumwa zomwe

zilindikhafinimongatiyi,zakudyazopandapakendimakhwala ozunguza bongo chifukwa izi zingachepetse chiteteze cha m’thupi lanu.

• Muzipanga masewero olimbitsa thupi - Pangani masewero olimbitsa thupi pafupifupi kanayi pa mulungu.

Chitsanzo chabwino cha masewerawa ndi kuyenda. - Mungathe kufotokoza za momwe mukumvera kupyolera mu nyimbo,

maluso osiyanasiyana ndi kuvina. • Imwani mankhwala owonjezera chitetezo - Palibe makhwala a edzi komabe pali mnkhwala omwe angathandize

kuwonjezera chitetezo cha mthupi. Mankhwalawa amalipatsa thupi lanu mwayi wokhala ndimphamvu zolimbana ndi matenda.

- Kambilanani ndi aza umoyo kuti akuuzeni kuti mukuyenera kuyamba liti kumwa makhwala. Makhwalawa amayenereka kumwedwa kwa moyo wako onse.

- Ngati mukuganiza zakumwa mankhwala ena azitsamba monga alovera, galiki, mukuyenera kufunsa achipatala chifukwa ena mwa mankhwalawa sagwirizana ndi mankhwala otalikitsa moyo a ma ARV.

• Mukhale ndi maganizo abwino okhuza moyo wanu - Muphunzire kukhala ndi maganizo abwino- kukhala okondwa ndi

kuganiza zabwino kumathandiza kuwonjezera chitetezo cha mthupi. - Tengani nawo mbali muzochitika za ku chipembedzo chanu komanso

mmudzi mwanu. - Phunzilani kuyankhula bwino ndi anthu ena-mukatero anthu enanso

azakuyankhulani bwino, ubale wanu ndi anthuwo uzakhala wabwino. Komanso izi zizapangitsa kuti mukhale ndi maganizo abwino a moyo wanu

ndikuchepetsa kukhumudwa. • Kuwonjezera apa - Gwiritsani ntchito kondomu nthawi zonse ndi moyenerera pamene

mukugonana ndi okondedwa wanu ngakhale atakhala kuti ali ndi HIV kapena ayi.

- Muzikhala ndi nthawi yokwanila yopuma ndi kugona. - Ngati muli oyembekezera ganizilani za momwe mungamutetezere

mwana wanu kuti azabadwe opanda HIV. - Lowani nawo mumagulu omwe cholinga chake ndi kulimbikitsana wina

ndi mzake – Kafukufuku akusonyeza kuti kukhala mumagulu amenewa ndi kukhala ndi maganizo abwino amoyo wanu kumathandiza

kuwonjezera chitetezo cha mthupi ndi kutalikitsa moyo.

> 6:22 Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV- kuteteza mwana ku HIV

- Pewani kukhala wankhawa ndipo khalani okondwa nthawi zonse. - Khalani ndi nthawi yoganiza ndi kuyankhula zina osati zokhuza HIV ndi

edzi.

ZopemphereraNgata banja, pempherani kuti:Mulungu awathandize anthu omwe ali ndi HIV kuti akhale ndi makhawlidwe abwino omwe angawathandize kukhala moyo wokondwa ndi wathanzi.

MalembaMasalmo 55:22Mateyu 28:20Yeremia 33:2-3

> Phunziro 6: Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV-kuteteza mwana ku HIV 6:23

>Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti:

• NdizothekambanjammodzikukhalandiHIVkomawinaalibe.• KomansondizothekakutimayiamenealindiHIVkukhalandimwanawopanda

HIV.

Khwerero 2: Ombani mkota wa phunziro lonse:

• Fotokozakutitaonazomwezimapangitsakutim’mbanjammodziakakhalendiHIV wina alibe komanso kuti njira ina imene HIV imafalira ndi kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana. Nkhani zina zomwe zakambidwa ndi monga izi:

• HIVkuMalawikunoikufalakwambirikudzeramukugonanakosazitetezandimunthu amene ali ndi HIV. Tikati osaziteteza tikutanthauza opanda kondomu.

• HIVimafoolachitetezochamthupi.Chitetezochamthupindichimenechimathandiza kumenyana ndi matenda. Chitetezo cha mthupi chikafooka ndikokuti sichingamenyanenso ndi matenda, munthuyo amati akudwala matenda a Edzi.

• Palinjirazambirizomwezimapangitsakutim’banjammodziakhalendiHIVwina ayi. Anthu omwe ali mbanja momwe mmodzi ali ndi HIV wina ayi angathe kukhala moyo wokondwa limodzi.

• Maanjaoterewaamakumanandizovutazambirichoteroakusowekakulimbikitsidwa.

• Maanjaakuyenerakuyezetsalimodzikutiathekukambilanazatsogololawolimodzi.

• KupewakufalakwaHIVkuchokerakwamayikupitakwamwanandiudindowamayi ndi bambo onse limodzi.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli.

Malemba owonjezeraKorani 2:179Korani 23: 6Korani 4:35Korani 42:30Korani 104:1Luka 15:11-24Yesaya 1:18

Kuomba mkota wa phunziro 6

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:1

Kuthetsa kusamvanaAnthu awiri omwe amakhala limodzi amakhala ndi nthawi zomwe amasemphana. Banja losangalala silitanthauza banja lomwe mulibe kusamvana koma banja lomwe liri ndi luso lothetsera kusamvanako.

Phunzilo iri lithandiza maanja kudziwa kuti kusamvana mbanja sichinthu chachilendo komanso liwathandiza kuphunzila mmene angathetsere mavuto awo moyenera.

Pali zochita zosiyanasiyana zomwe ziri mu phunzilori zomwe zithandize maanja kudziwa zomwe zimayambitsa kusamvana mbanja nthawi zambiri, zomwe zimachitika kusamvana kukapanda kutha bwino ndi momwe angathetsere kusamvana kwawo kuti kusafikekunkhanzakapenakuthakwabanja.

Phunziro 7

> 7:2 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

> Phunziro mwachidule

Omwe ayenera kuphunziraAnthu omwe ali m’banja

Ndondomeko ya phunziro1. Mutu wa phunziro2. Phunziro mwachidule3. Kutsegulira phunziro 7 4. Miyambo ya makolo5. Kumvetsetsa kuti kusamvana ndi chani6. Kukambilana mwapadera nkhani za ndalama 7. Zotsatila za kusamvana8. Kuthetsa mikangano9. Nkhanza:kukambilana kukakanika-kukonza ndondomeko yopewera11. Kuomba mkota wa phunzilo lonse12. Ntchito ya kunyumba13. Malemba

Nthawi yofunikaMaola awiri

Zofunika 1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zokambirana nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za mu Baibulo/Korani zolingana ndi mutuwo komanso

zolembedwa zina.3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:3

>Nthawi: Mphindi 20

Malangizo a padera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati munakumanapo kale, akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Zokambirana mwachiduleAlandileni maanja kuzokambilanazi ndipo awuzeni kuti akhala akukambilana pa mutu wokhuza kuthetsa kusamvana mbanja ndi momwe mutuwu ukukhuzilana ndi nkhani za HIV/Edzi. Maanja akambirana momwe angachitile pakati pawo pakakhala kusamvana ndi kupewa kuchitilana nkhanza.

Zolinga• Kuthandizamaanjakumvetsetsakutikukanganakungathekuchitikaangakhale

mbanja momwe muli chikondi.• Kuwathandizamaanjakuzindikilakutingatisanakambilanebwino

zakusemphana kwawo, banja lawo lingathe kusokonekera.• Kupangazomweakuyembekezelandimalamuloagulu.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro la kuthetsa kusamvana mbanja: • Maanjaambiriamayembekezerazinthuzosathekamongakutimkwiyondi

kusamvana siziyenera kukhalapo m’banja la chikondi. • Maanjaakuyenerakukhalandimalusooyenereraomweangawathandize

kugwiritsa ntchito mkangano kubweretsa chikondi pakati pawo. • Ngatibanjasilinakambilanebwinozakusamvanakwawo,kusamvanako

kukhoza kukhala chida chowononga banja lawo chifukwa cha mkwiyo omwe ungakhalepobe mbanjamo.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Atenganawombalimuzochitikazonse,osatikungomvetsera.Athandizakutsogolera zokambirana popereka ndemanga ndi kutenga nawo mbali mu zochitika zonse.

• Akhalandimwayiwokambiranamomweakumvera,zikhulupilirozawo,momweamaonera zinthu komanso mfundo zina zofunikira.

• Aphunziramalusoowathandizakulimbikitsaubwenziwawo.

Kutsegulira phunziro 7

> 7:4 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti:

• Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

Khwerero 4: Afunseni maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi kudzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:5

>Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiriro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kuthetsa kusamvana mbanja ndi momwe zikukhudzirana ndi HIV. Iwo akambirana ngati zimenezi ziri zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupeza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu

samazimvetsetsa zokhuza kuthetsa kusamvana mbanja. • Kuwafotokozela mfundo zoona zomwe zingawathandize maanja kuthetsa

mkangano yawo moyenerera.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiriro ndi zoyankhulidwa zokhuza kuthetsa kusamvana mbanja. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti atchulepo miyambo ndi zikhulupiriro zina zokhudzana ndi kuthetsa kusamvana. Perekani nthawi yokambirana.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu:

• Akazi amalimbikitsidwa kukhala pakhomo limene akukumanapo ndi nkhanza(Banja ndi kupilira).

• Kumenyanambanjandimankhwalaabanja.• Amunaakafotokozakutiakaziawoamawazunzaenaamawaseka.• Mwamunandimutuwabanjandipoamayenerakumumveranthawizonse.

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilana zokhuza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu samazimvetsetsa potsindika mfundo izi:

• Maanjaalimbikitsidwekukondanandichikondichenicheni.Mbanjamukakhalachikondi cheni cheni, sipangakhale kumenyana ndipo izi zidzathandiza kupereka chitetezo ku HIV.

• Maanjaalimbikitsidwekukapezathandizokunjakwabanjangatiawiriwoakanikakukambilana paokha.

• Amunaaziwawonaakazimongansoanthundipoazikhalanawobwinomongaalichifanizilo cha Mulungu.

Ntchito 1: Miyambo ya makolo

> 7:6 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguathandizemaanjakuonansomiyambo,nkhambakamwandizoyankhula

zomwe takula nazo zomwe timazikhulupilira zomwe zili zotsutsana ndi mawu.

MalembaGenesis 2:22-24Yohane 15:13-14Korani 49:13Korani 7:28

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale ndi iye anati “ndingakuuzeni za munthu yemwe ali oletsedwa kukalowa kumoto, kapena amene moto uli oletsedwa kwa iye kuti akalowe?Motondiwokanizidwakwawinaaliyenseyemwendiofikilika,wosavutakukhala naye, woleza ndi wozichepetsa” (Al-Trimidhii).

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:7

>Nthawi: Mphindi 20

Zida zofunikiraMapepala akuluakulu olembapo/mapepala ang’onoang’ono olembapo, zolembela/mapento maka.

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana mwakuya ndi kumvetsetsa tanthauzo la mau akuti kusamvana. Maanja akambilananso zomwe zimayambitsa kusamvana mbanja ndi momwe mikangano yomwe sinathetsedwe ingapangitsile mmodzi wa iwo kukachita zibwenzi zomwe zingabweretse HIV m’banja.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakutiakambilanemmeneamamverazamauakuti

kusamvana mbanja.• Kukambilanazomwezimayambitsakusamvanambanja.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani phunziro iri powafotokozera maanja kuti:

• Tikambilanankhanizosiyasiyanazokhuzakusamvanambanjandikufukulazinamwa zomwe zimayambitsa kusamvana mmbanja.

• Kusamvanakungathekuyambandinkhaniyaying’onompakakukafikapochitilana nkhanza ndipo ngati kukambilana sikungayende bwino, kusamvana kukhonza kuononga chiyanjano cha banja.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Akhalandinthawiyoganizamwakuyakutiamvetsetsekutikusamvanambanjandi chani ndi momwe anthu osiyanasiyana mgulumo amamvetsetsela za nkhaniyi.

Khwerero 3: Afunseni maanja mau akuti:

• Kusamvanaamatanthauzachanikwaiwo.Lolanikutipakhalemwayiwokambilana ndipo lembani mayankho onse pa pepala lalikulu ngati liripo.

Khwerero 4: Lembani pa mapepala akulu akulu aja zomwe zimakonda kuyambitsa kusamvana mbanja: Kusayankhulana moyenerera, nkhani zokhuza ndalama, abale, ana, kugonana ndi kukhulupililana.

Ntchito 2: Kumvetsa nkhani zokhudza kusamvana

> 7:8 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

1. Zimateni pakhoma mu malo osiyanasiyana.2. Afunseni kuti onse ayendere momwe mwamatidwa mapepalamo ndi kuwapatsa

mavutowo manambala apakati pa 1 ndi 5. Vuto lomwe akuliona kuti ndi nambala wani poyambitsa kusamvana alilemba 1, kenako apitiliza kuperekanso manambala kumavuto enawo.

Khwerero 5: Akamaliza kupereka manambala kwa mavutowa awuzeni kuti onse abwerere mmalo mwawo kuti akambilane:

Funsani gulu lonse ngati akugwirizana ndi momwe manambala aperekedwera kwa mavuto a mbanjawa.

• Funsanianthuangapokutiafotokozekutindichifukwachaniaperekamanambalachoncho kwa mavutowo?

• Kodiamayindiabamboaperekamanambalamosiyana?• Kodi mavutowa amakhuza kwambiri amayi kapena abambo? Nanga izi

zimabweretsa mavuto anji mu banja lawolo?

Khwerero 6: kumaliza ntchito ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu:

• Kusamvanakumatanthauzakusagwirizanakapenakutsutsana.• Anthutonsendifeosiyanawinandimzake,tilindizofunazosiyana,zosowandi

masomphenya osiyananso. Timakonda anthu chifukwa chakusiyana uku komwe kumakhalapo, koma kusiyanaku kumabweretsanso kukhumudwa pamene tikufuna kukhala ndi kugwira ntchito limodzi.

• Sizachilendokutianthuawiriomwealimbanjaasagwirizane.Komatikuyenerakuphunzira maluso amomwe tingathetsere kusamvana kwathu moyenerera.

• Palizinthuzambirizomwezimayambitsamikanganombanja,ndipozomwezilizoziwika bwino ndi monga zomwe takambilanazi. Izi zimakhuza mayi ndi abambo mosiyana.

• Amayi ndi abambo amaperekanso manambala mosiyana kwa zoyambitsakukanganazi. Zomwe zikutanthauza kuti chomwe chiri choyambitsa mikangano chachikulu kwa amayi ndi chosiyana ndi cha abambo.

• Chofunikilandichakutizonsezomwetakambazizingathekuyambitsamikanganombanja ndipo amayi ndi abambo akuyenera kukambilana momasuka za zithu izi.

• Maanja akuyeneranso kudziwa kuti kusamvana kungathe kufulumizam’modzimmodzi m’banjamo kukafuna chibwenzi zomwe zingabweretse HIV/Edzi m’banja.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguathandizemaanjakuthetsamikanganoyawomoyenerera.• Maanjaakhaleolezamtimandiwinandimzakepodziwakuti tonse timalakwa

munjira zosiyanasiyana.

Malemba1 Petro 5:7-9Yakobo 1:19Korani 3:133, 154

Mtumiki Muhammad (MUPI) anati Aliyense wa inu ndi mbusa ndipo aliyense wa inu ali ndi udindo pa zomwe zili pansi pa ulamuliro wake.

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:9

>Nthawi: Mphindi 40

Zokambirana mwachiduleMaanja awona momwe ndalama zingakhalire choyambitsa mikangano mbanja ndi momwe izi zingabweretsere HIV mnyumba. Maanja aphunzira ubwino wowuzana za ndalama zimene aliyense ali nazo kwa mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro:

• Awuzeni maanja kuti tikambilana nkhani zosiyanasiyana zokhuza kusamvanamakamaka chifukwa cha ndalama/chuma.

• Ndalama/chumandichinthuchinachomwechimayambitsakusamvanambanja.Kupezeka kapena kusowa kwa ndalama pakhomo kungapangitse wina kukayamba kuyenda mnjira za mtseli zomwe zingawayike pachiopsezo ku HIV.

Khwerero 2: Afunseni maanja mafunso awa pa gulu. Awuzeni kuti akhale omasuka kugawana ndi gulu lonse mayankho awo. Ngati sali omasuka kutero: • Mungathe kuwapatsa mapepala ang’onoang’ono kuti alembe mayankho awo

koma asalembe mayina.• Landilanaimapepalawo ndikuwerengamapepala ochulukamalinga ndi nthawi

yomwe muli nayo.• Perekaninthawikutimaguluakambilane.

- Mumadziwa za ndalama zomwe amuna/akazi anu amalandila kuntchito pa mwezi kapena amapanga kuchokera ku bizinesi yawo?

- Kodi mumawawuza akazi/amuna anu mukafuna kugula chinthu kapena kamanga nyumba kapena kutumiza ndalama kwa bale anu?

- Mumapanga dongosolo la ndalama kapena momwe mugwiritsile ntchito ndalama limodzi?

- Ndi mikangano yanji yomwe imakhalapo mbanja mwanu chifukwa cha nkhani za ndalama?

Khwerero 3: Maanja akatha kukambilana mayankho awo, werengani nthano iyi kwa gulu lonse:

Nkhani iyi ndi ya banja la bambo ndi mayi Landilani omwe anali ndi ana atatu, mtsikana mmodzi ndi anyamata awiri. Bambo Landilani amapanga bizinesi ndipo akazi awo amangokhala pakhomo. Bambo Landilani samawawuza akazi awo ndalama zomwe amapeza kuchokera ku geni yawo. Nthawi zonse akamapita ku geni yawo, amawasiyila akazi awo ndalama zogulira zinthu pakhomo. Ndalama zomwe amasiya sizimakwanila pachifukwa ichi mayi Landilani napeza chibwenzi cha mseri. Chibwenzicho chimakumana ndi mayi Landilani nthawi ndi nthawi ndipo

Ntchito 4: Kukambirana mwapadera nkhani za ndalama ndi banja

> 7:10 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

amawapatsa mayi Landilani ndalama zomwe amagulira zinthu zina zowonjezera za pakhomo. Mwana wawo wa mkazi nayenso anali ndi chibwenzi ndi abambo akulu omwe amamupatsa ndalama zogulira zomwe akufuna.

Khwerero 4: Awuzeni maanja kuti apite mumagulu akakambilane mafunso awa;

• Ndi mavuto ati omwe tikuwawona mu banja la bambo ndi mayi Landilani? • Mukuganiza kuti ndi chifukwa chani bambo Landilani sasiya ndalama zokwanira

pakhomo?• Ndi mavuto anji omwe angabwere pakhomopo chifukwa cha khalidwe la bambo

Landilani, mayi Landilani ndi mwana wawo?• Ndi malangizo anji omwe mungapereke ku banja ili?

Khwerero 5: Ombani mkota potsindika mfundo izi:

• Chimodzimwazinthuzomwezimapangitsaanthukuyambanambanjandinkhaniza ndalama/chuma, makamaka ngati ndalamazo palibe zokwanira kulipilira zinthu zosinasiyana ngati madzi, magetsi, kugula chakudya chokwanira ndi zinthu zina zofunika ndikukhalako ndi ndalama zina zosunga. Mayi wosunga/kusamala ndalama akhonza kukwatiwa ndi mamuna yemwe samatha kusunga/kusamala ndalama.

• Mbanjamulibe‘ndalamazaine’kapena‘ndalamazako’.Mulubenso‘ngongolezanga’ ndi ‘ngongole zako’. Koma muli ’ndalama zathu’ ndi ‘ngongore zathu’. Anthu awiri mbanja sangakhale thupi limodzi ngati ali yense ali ndi ndalama zake pa yekha.

• Bambo ndi mayi akuyenera kukonza ndondomeko (bajeti) ya ndalama zawolimodzi kapena ngati ndondomekoyo (bajeti) wakonza ndi mmodzi winayo agwirizane nayo. China chilichonse nchofunika kuchikambilana, kuchipempherera ndi kuchigwirizana. Chofunikila kwambiri ndikukhala ndi ndondomeko yabwino yomwe ingathandize kuti banjalo lisamawononge ndalama zawo.

• Mbanja,mayindibambondiabwenziomwealiodalirana.Zikudaliraanthuawiriwakulipanga banja lawo kukhala lopambana. Zikudaliranso awiriwa kugwirizana za momwe angamayendetsere ndalama/chuma chawo.

• Malamulo a Mulungu akupereka malangizo amomwe ndalama zikuyenerakugwiritsidwila ntchito zomwe ndi zothandiza kulimbikitsa chiyanjano mbanja. Maanja akawerenga malangizo amenewa, kuwaphunzira ndi kuwagwiritsa ntchito m’maanja awo, ndikupitilizabe kuwatsatila, maanjawo akhonza kukhala olimba ndi a bwino.

• Nkhani za ndalama zikafika povutambanja, ndibwino kupemphera.Yankho laMulungu ndi lodalirika.

ZopemphereraNgati banja, pempherani kuti:• Mulunguathandizemaanjakukhalaomasukilanangakhalepankhaniyachuma/

ndalama.

MalembaGenesis 3:17-19, 2 Atesalonika 3:10Tito 2: 4-5, Aefeso 5: 28-29, Korani 65: 6-7

Mtumiki Muhammad (MUPI) anati aliyense wa inu ndi mbusa ndipo aliyense wa inu ali ndi udindo pa zomwe zili pansi pa ulamuliro wake.

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:11

>Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana zabwino ndi zoipa zimene kusamvana kumabweretsa. Pokambilana za nkhani ziwiri zimene zili mu ntchito iyi, maanja amvetsetsa za zotsatila za kusamvana mbanja.

Cholinga• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakutikusamvanakulindiubwinokomanso

kuipa kwake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani ntchito:

• Akumbutsenizinthuzomwezimakondakuyambitsakusamvanambanjazomweakambilana mu ntchito 1.

• Awuzenimaanjakutitsopanoakambilanazotsatilazakusamvanambanja.Izizikhonza kukhala zabwino komanso zoipa.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti tichita masewero awiri, ndipo tifuna anthu ozipereka. Funsani anthu ozipereka kuti apange masewero awiri osiyana.

• Sankhanianthuasanuoziperekakutiapangesewero.Enaasaziwekutimasewerowa akukamba za chani.

• Apatseninthawiyokakonzekerapomweenaakuyimba.• Onetsetsaningatimulangizikutiakukambazomwezikuyenerakukambidwa.

Sewero loyambaAnthu atatu oyambilira apanga sewero momwe mwamuna ndi mkazi wake akangana kwambiri ndipo akanika kugwirizana.Omwe akupanga sewero aganize za nkhani yomwe akufuna kukangana, mwachitsanzo, amayi sanakonze kuchipinda kapenaabamboanayiwalakuperekafiziyamwanawawowamkazi.Akakanikakugwirizana, abambo achoke pakhomo apite koyenda. Ali koyenda akumane ndi mzimayi yemwe awakope abambowa kuti agonane naye.

Sewero la chiwiriSewero la chiwiri likhale lokhuza banja lomwe akangane kwambiri koma kumapeto kwake agwirizane bwinobwino. Kumapeto kwake onse aphunzire china chake chokhuza wina ndi mzake.

Ntchito 5: Zotsatira za kusamvana

> 7:12 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

Khwerero 3: Akamaliza kukonzekera masewero afunseni kuti awonetse masewero kwa gulu lonse.

Khwerero 4: Afunseni onse kuti apite mumagulu akakambilane mafunso otsatilawa. Gulu lina likambilane za sewero loyamba, lina lachiwiri:

• Tikuphunzirachanikuchokeramumaseweroamenewa?• Gululoyamba:Afunsenizovutazomwezingabwerengatibanjalakanika

kukambilana za kusamvana kwawo?• Gululachiwiri:Kusamvanakungakhalekwabwinomunjirayanji?

Khwerero 5: Akamaliza zokambilana mmagulu awuzeni kuti afotokozere gulu lonse zomwe anakambilana. Funsani ngati pali zoonjezera. Khwerero 6: Ombani mkota ndi kumalizitsa zokambilanazi pofotokoza mfundo izi:

• Kusamvanakungathekukhalakwaphinduchifukwakudzeramukukambilanamwamuna ndi mkazi angakule ndikuzamitsa kumvana ndi chikondi pa wina ndi mnzake. Kukambilanaku kungabweretse kukwanitsidwa mbanja.

• Popandakusamvana,makhalidwe,machitidwendiubaleumangokhalawosasintha.

• Ngatikusamvanasikuthetsedwa,mwamunandimkazisangathekutulukamukukhumudwa ndi kupitilira kukula mu banja lawo.

• Kusamvanangatisikuthetsedwakumapangitsam’modzikuyambakuyang’anachibwenzi kunja, amene akuona kuti angamumvetse bwino – kukhala ndi zibwenzi ndi kumene kumaonjezera chiopsezo cha HIV kulowa mnyumba.

ZopemphereraNgati banja:• PempheranikutiMulunguabweretsemtendere,chikondindikukhazikika

mmaanja momwe muli kusamvana.

MalembaMiyambo 12:16Yakobo 1:191 Petro 3:7Korani 51:8- 11Korani 2:195

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:13

>Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana tanthauzo lakuti kukambilana ndi cholinga chothetsa kusamvana, ndipo agwiritsa ntchito masewero kukambilana ndi kugawana maganizo a momwe angathetsera kusamvana kwawo moyenerera.

Cholinga• Kuwapatsamaanjamalusoabwinoothetserakusamvanakwawo

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani zokambilana. Akumbutseni anthu kuti ngakhale kusamvana kumakhala ndi phindu, phindulo limakhalapo ngati kusamvanako kwatha bwino.

Khwerero 2: Perekani tanthauzo la kuthetsa kusamvana:

Kuthetsa kusamvana kumatanthauza ndondomeko yothetsera kusagwirizana kapena mkangano, popereka zomwe mbali zonse ziwiri zikusowa ndi kuunika zofuna zawo kuti onsewo akhutitsidwe ndi zotsatira zake.

Khwerero 3: Funsani gulu ngati likuvomereza kapena ngati ali ndi zoonjezera.

Khwerero 4: Gawani anthu m’magulu ang’onoang’ono.

• Awuzenikutiapangamaseweroankhanizosiyanasiyana.• Gululirilonselipangesewerolokhuzakusamvanandipoakambilaneza

momwe kusamvanaku kunathetsedwera. Apatseni mphindi zokwana zisanu kuti akonzekere.

Nkhani zake ndi izi:• Mkaziakufunakugulachovalachatsopanokomapalibendalama.• Mwamunaakufunakupitakoyendakomamkaziwakhalamasousikuonsendi

mwana wodwala ndipo akufuna kukhala pakhomo.• M’modziakufunamnzakeyoamuperekezekopempherakomawinayosakufuna• Achibaleamnzakeyoabweramodzidzimutsa.• Mkaziakufunaapezentchitokapenakuyambagenikomamwamunawake

sakuvomereza. • Mwamunaakufunamwanachakachomwechokomamkaziakufunakuti

adikirebe.• Abamboakufunakutiagonanekomaamayiatopa.

Ntchito 5: Njira zothetsera kusamvana

> 7:14 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

Khwerero 5: Funsani gulu lirilonse kuti liwonetse kasewero kawo. Akamaonetsa sewerolo afunseni enawo kuti aziwonetsetsa zomwe zikuchitika.

• Kodikusamvanakunatha?• Anagwiritsantchitonjirayanjiyothetserakusamvanakwawo?• Kodionseanakhutitsidwa?• Akanayenerakuchitachiyanichosiyanakutikusamvanakuthebwino?

Khwerero 6: Fotokozerani gulu zofunikira pa kuthetsa kusamvana. Maanja akuyenera kuganizila mfundo izi zomwe ndi zofunika pofuna kuthetsa kusamvana:

• “Kodi nkhani iyi ndi yoyenera kuti tikambilane?” Ndi nkhani yofunikila kwambiri? Kodi vutoli likukhumudwitsa okondedwa wanga kapena ine? Ngati silikumukhumudwitsa aliyense ndipo sivuto lalikulu, chofunikila ndi kuliyiwala vutolo ndipo musavutike kukambilana. Koma ngati china chake chachitika mobwereza , mwachitsanzo , mzanu wa banja sanakulemekezeni ma ulendo angapo poyankhula nkhani zochititsa manyazi pagulu. Zikhonza kukhala bwino kupeza nthawi yabwino ndikukambilana ndi wokondedwa wanu. Kambilanani vuto lanu, zikhonza kutheka kuti wokondedwa wanu sakudziwa kuti amakukhumudwitsani.

• Fukulani za vutolo - Vuto kwenikweni ndi chani? Ngati pali vuto mpofunika kuyang’anitsitsa

chomwe chiri vuto kwenikweni. - Mwachitsanzo wokondedwa wanu amakwiya kwambiri mukapita kukacheza ndi woyandikana nawo nyumba. Ndipo iye akupemphani kuti

musiye kupitakoso. Chomwe chikubweretsa kukwiyaku ndi chani? Kapena akufuna muzikhala ndi nthawi yocheza limozi yambiri? Kapena akuchita nsanje ndi kucheza kwanu? Fukulani kuti vuto kwenikweni ndi chani?• Pepesani ngati mwalakwa ndipo phunzirani kukhululuka. - Kambiranani zimene simukugwirizana/vuto mtima uli pansi limodzi. Mupepeseni wokondedwa wanu ngati munalakwa. Nenani kuti pepani ndipo tchulani chimene munalakwitsacho ndikupempha kuti akukhululukireni. Kupempha kukhululukidwa ndi gawo lofunika kwambiri pofuna kuthetsa vuto. Kulakwitsa ndi mbali imodzi ya umunthu. Tonse timalakwitsa. Ndiye tiphunzire kunena ‘’pepani’’ kwa wokondedwa wathu. - Mukhale ndi mtima ovomera kulakwa kwanu ngati mwalakwitsa osati kuziyikila kumbuyo nthawi zonse. Kumbukilani kukhala ndi chidwi ndi kumvetsera bwino okondedwa wanu akamayankhula. - Khalani ndi mtima wogonjerana kwa wina ndi mnzake. Simungakhale opambana nthawi zonse. • Thanani ndi vuto lirilonse palokha - Kambiranani za mavuto anu lirilonse palokha palokha, kungobweretsa mavuto onse nthawi imodzi nkovuta kuti mungakonze vuto ngakhale limodzi. - Mukamakambilana nkhani yatsopano, pewani kukumbutsa wokondedwa wanu za zolakwa zomwe anachita m’mbuyo.• Khalani omasukilana - Khalani omasuka kwa wokondedwa wanu pa zonse zimene mukuchita ndi zimene mukuyembekezera.• Sankhani nthawi ndi malo abwino - Mukuyenere kupeza nthawi yokambilana yina. Kuthana ndi vuto nthawi yabwino ndi kwabwino koma onetsetsani kuti nonse ndinu okonzeka

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:15

kukambilana. Ndi zosathandiza kukambilana pamene nonse mulu okwiya.

- Sibwino kukambila nkhani zanu pa malo pamene pali anthu ena kapena achibale. Onetsetsani kuti muli panokha ndipo anthu ena sakulowerela mu zokambilana zanu. - Sibwino kuyakhula pamene mzanu wangobwera kumene kuchokera ku ntchito kapena komwe anapita. Ndi bwino kumufunsa nthawi imene wapuma ndipo ali omasuka kuti mukambilane, osati atangolowa pakhomo. Mawu a Mulungu amatiphunzitsa kuti chiri chonse chiri ndi nthawi, nthawi yakulankhula ndi yakukhala chete. Tiwonetsetse kuti tikulankhulana ndi wokondedwa wathu pa nthawi yomwe ndi yoyenerera kwa tonse. - Sankhani malo abwino. Akadaulo ena amavomereza kupita ku malo ena kutali ndi kunyumba kwanu kumene mukapeze malo abwino opanda

zosokoneza• Gwiritsani ntchito mau oyenerera - Pewani kukamba zakuthetsa banja, musakambe zoipa zokhudza achibale a wokondedwa wanu, osatchulana maina kapena kunyoza mnzanu, osanyoza maonekedwe ake, osamenyana/kutsinana, osamudula mzanu akamayankhula, osatukwanana kapena kugwiritsa ntchito mau opweteka. - Yesetsani kugwirizana pa mfundo imodzi musanamalize kukambirana. Musachoke mkangano uli pakati, ndipo gwiritsani ntchito chilankhulo chovomerezeka ndi aliyense wa inu. - Cholinga chothetsera kusamvana chikhale kuonetsetsa kuti onse awiri akhutitsidwa ndi zotsatira. - Kusamvana kungathe pakukambirana, kulemekeza zonena za wina ndi mnzake ndi kukambirana mwachikondi.• Onetsani kumvetsetsa - Gwiritsani ntchito ziganizo zoyamba ndi mau akuti “Ine”. Onetsetsani kuti mukumvetsetsa zomwe wokondedwa wanu akulankhula ndi kuvomereza. Musanyoze maganizo awo, kapena kuwayimba mlandu, kapena kuziyikila nokha kumbuyo. Ingomvetserani. - Kumuyimba mlandu kapena kumunyoza wokondedwa wanu sikukuthandizani kuthetsa kusamvana kwanu. Tigwiritse ntchito mau athu kuthandizila ena. - Gwiritsani ntchito mau anu kuthetsela kusamvana osati kuyambitsa mkangano wina.• Funani chitsogozo cha Mulungu - Pa nthawi ina Mtumiki Muhamadi (mtendere ukhale pa Iye) ananena kuti aliyense amene athamangitsa mkwiyo ndi kukhululuka, Allah adzaza mimba yake ndi chikhulupiliro ndi chitetezo. Ndime za mu korani zimene tikukambirana zilumikizitsa ife, ndi kutibweza mkwiyo, komanso kukhulukira ife. - Ikani Mulungu/Allah poyamba mu ndondomeko yanu yonse yokonza mavuto anu kuti Iye akutsogolereni. - Baibulo limanena kuti, “Chiyambi cha nzeru ndi kuopa Mulungu’’ Yesu

anauza omutsatira kuti adzithetsa kusamvana asanapereke nsembe.

> 7:16 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

Khwerero 7: Afunseni maanja kuganizila mfundozi. Afunseni kuti akambilane:

• Potengerandimfundozothetserakusamvanazomwezakambidwazi,palichinachake chomwe mukanachita mosiyana mu sewero lanu lija? Chifukwa chani?

Khwerero 8: Ombani mkota ndi kutsendera ntchitoyi powunikanso mfundo zoyenera kutsata pothetsa mikangano zija ndi zina zomwe anthu azinena mmene mumakambilana maka pokhudza HIV/Edzi.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaaphunzirekukhalaodekhamtimandikuchitilanawinandimzakezabwino

monga momwe Mulungu amachitila nafe tikalakwitsa. • Pempherani kuti tikhale osamalitsa pa mawu amene akugwiritsa ntchito ndi

momwe akuchitila ndi okondedwa awo.• MongamaanjaMulunguatithandizekukhalaodzichepetsa.

MalembaKorani 4:134; Korani 42:40-43Korani 4:59Mateyu 5:23-24; 2 Akorinto 2:71 Petro 3:7Miyambo 9:10; 19:11Luka 17:3Yakobo 1:19Aefeso 4:29

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:17

>Nthawi: Mphindi 60

Mfundo yofunikira kwa Mlangizi• Ntchitoiyindiyayitalindipoingathekugawidwamuzigawoziwiri

Zokambirana mwachiduleMaanja awona nkhani zokhuza nkhanza zomwe ndi zotsatila za kukanika kumvana pa kakhala kusamvana. Maanja awonanso kuipa kwa nkhanza ndipo akonza njira ya momwe angakhalire okonzeka pa nkhani za nkhanza.

Zolinga• Kuwafotokozera maanja za komwe angakapeze thandizo akamachitilidwa

nkhanza.• Kuthandiza azipembezo kukhazikitsama gulu omwe azikhalapo nthawi zonse

othandiza ochita nkhanza ndi ochitilidwa nkhanza.• Kuthandiza maanja kudziwa za kuipa kwa nkhanza ndi momwe angapewere

kuzunzana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti:

• Tikambilanankhaniyovutakwambirindiyachinsinsiyomwesikondakukambidwakunja kwa banja. Awuzeni kuti:

• Ngakhalekukanganakulindimbaliyakembanja,nthawizinakungathekubweretsaukali ndi kunzunzana.

• MayikapenaBambosakuyenerakuvomerakuchitiridwankhanzam’banja.• Nkhanza zimachitika pamene wina akufuna kukhala ndi mphamvu/

kumamupondereza mzake ndipo zonse cholinga chake ndi kuononga osati kamanga.

• Nkhanza zimapereka mabala mumtima mwa munthu ndipo kawirikawirizimasintha maganizidwe ndi mwayi okhala moyo wodzadza.

• Nkhaza ndi nkhani yomwe amayi ndi abambo akuyenera kukhala okhuzidwanayo.

Khwerero 2: Funsani anthu kuti akambirane mitundu ya nkhanza yosiyana siyana zomwe zimachitika m’banja. Lembani mayankho awo pa pepala lalikulu.

Khwerero 3: Akamaliza, unikani mfundo zotsatirazi zokhudza nkhanza:

• Nkhanza ndi chinthu choipa chimene wina aliyense angagwiritse ntchito pamzake.

• Palizitsanzozosiyanasiyanazankhanzakomazonsecholingachakendikuonongaosati kumanga.Nkhanza zomwe zatchulidwa pa mwambapa zingathe kugawidwa mumagulu awa:

Ntchito 6: Nkhanza - Pamene kusamvana sikukukonzeka

> 7:18 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

- Nkhanza zapathupi: izi zikuphatikizapo kumenya ndi njira iliyonse yozunza thupi la munthu wina. - Nkhanza zokhudzana ndi kugonana: izi zikuphatikizapo kuumirizana kugonana m’banja, kugwiriridwa mbanja kapena kunja kwa banja,

chigololo, kugonana pachibale, kumukanira wokondedwa wako kugonana naye.

- Nkhanza pa zolankhula: izi zikuphatikiza kulankhula zinthu zokhumudwitsa mnzanu m’maganizo kapena zinthu zolankhula kuti mugonjetse mphamvu

ya kulankhula mwa mnzanuyo. - Nkhanza za Uzimu: izi zikuphatikiza kumukaniza mnzanu kupita kopemphera, kunyoza chipembedzo cha mnzanu. - Nkhanza pa Chuma: kulephera kupereka zofunika za pakhomo monga chakudya, nyumba ndi zina, kumulepheretsa mnzanu kuchita kanthu

kopezera ndalama monga geni kapena kupeza ntchito.

Khwerero 4: Awuzeni maanja kuti: • Banja lirilonse lipanga ndondomeko yomwe ingapereke chitsogozo kwamayi

kapena bambo. Afotokozereni kuti ndondomeko imeneyi:• Ikhala pangano kwa wina ndi mzake lothandiza kupewa kuchitilana nkhanza

mbanja.• Ifotokozazamakhwereroomwebanjalizitsatapakachitikankhanza.• Kufufuza zinthu ndi anthu omwe alimbanjamo,mdela ndimumpingo/mzikiti

omwe angathandize ngati kuli kofunika kutero.

Khwerero 5: Awuzeni maanja kuti akhale awiri awiri. Onetsetsani kuti mwafotokoza za ndondomekoyi:

• Ikhalandimbaliziwiri: - Mbali ya zochitika mwazizizi, yomwe ikhale ndi mfundo za zomwe angachite nkhanza ikachitika. - Mbali ya kapewedwe, yomwe ikufotokoza za zomwe zikuyenera kuchitika pofuna kupewa nkhanza mbanja.• Ipangidwakutiitetezeochitilidwankhanza.

Khwerero 6: Afunseni maanja kuti ayankhe mafunso awa limodzi:

Ndondomeko ya Dzidzidzi• Mungadziwebwanjikutinkhanzazikuchitikambanjamwanu?• mungachitechiyaningatiakukuchitiraninkhanza?Mungapite kuti mdera lanu ngati:• Mukuchitilidwa nkhanza?• Mukuchitila nkhanza wokondedwa wanu?• Ganizilani za malo omwe mukuona kuti mukhonza kukhala otetezedwa

monga mtchalitchi/mzikiti, polisi ndi kuchipatala.Mungakadandaule kwa ndani ngati:• Mukuchitilidwa nkhanza?• Mukuchitila nkhanza wokondedwa wanu?

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:19

• Ganizilani za anthu omwe mukugaiza kuti angathe kukutetezani kapena kukuthandizani kusiya nkhanza. Awa atha kukhala anthu amumpingo/ mzikiti, apabanja panu, abwenzi, anthu ena ammudzi, apolisi, ndi azaumoyo.Ndondomeko ya kapewedwe:• Ndinjirazitizimenemungatsatepofunakutinkhanzazisachitikemnyumba

mwanu? Izi zitha kukhala zinthu monga izi:• Chokani mchipinda kapena pakhomopo ngati mwakwiya kwambiri. Mtima ukakhala pansi bwererani mukakambilane zomwe zinachitika.• Muzikhala ndi nthawi yokambilana mavuto omwe mukuwawona mbanjamo. Kambilanani izi nkhanzazo zisanachitike.• Gwirizanani kuti muzimvetserana wina akamayankhula.• Musanyozere za momwe mzanu akumvera.• Fufuzani komwe mungakalandile uphungu ngati mukuona kuti simungathe kuzigwira mukakwiya ndipo simuchedwa kumupanga

nkhanza wokondedwa wanu.• Pewani kuchita zinthu zomwe zimamukwiyitsa wokondedwa.

Khwerero 7: Banja lirilonse likapanga ndondomeko yawo, awuzeni kuti onse asayinile kuti azitsatila zimenezi nkhanza zikamachitika mnyumba mwawo.

Khwerero 8: Awuzeni kuti onse abwerenso pamodzi ndipo awuzeni kuti agawane ndi gulu lonse ndondomeko yawo.

Khwerero 9: Onse akagawana ndi gulu lonse ndondomeko zawo, unikilani mfundo izi zofunika:

• Ngatimungatsatilendondomekoyomwemwapangandiokondedwawanu,ithandiza kupewa nkhanza mbanja lanu, komanso kupereka chitsogozo nkhanza ikachitika.

• Zikuonekakutiubaleweniwenipakatipamwamunandimkaziwagonapachikondi ndi chifundoso.

• NkhanzazimayikamoyowaokondedwawanupachiopsezomakakubweretsaHIV/Edzi mnyumba.

• Maanjaonseamathakusemphanakanthawikena.Banjalimatithandizakuzindikira kuti penapake tiyenera kusintha. Koma mkangano usakulitsidwe.

• Nkhanzazapakhomozipewedwem’banjamwanu.Ulemu,chikondindichisamaliro pa wina ndi mnzake ndiye zofunika.

• Konzani kusamvana kulikonse mwabata ndipo moyo upitilire. Khululukanipa zoipa zonse zimene wokondedwa wanu wachita pozindikira kuti tonsefe timalakwitsa.

• Kukhululukasikukutanthauzakubwererakubanjakomweumazunzidwakokomakuti muziteteze kaye nokha kenako mumukhululukire yemwe amakunzunzani uku mukuziteteza.

• Polimbanandinkhanizankhanza,nkofunikakuyang’anankhaniyombalizonseziwiri osangoweruza munthu m’modzi mwachangu. Nthawi zambiri, mkazi amadzudzulidwa chifukwa cha nkhanza posayang’ana zimene zinayambitsa kusamvanako.

• Ngatinkhanzazikuchitikambanja,ayenerakukapezathandizolimodzi.• Si chifunirochaMulungu/Allahkutimnyumbamuzikhalamavuto,kuchitirana

nkhanza kapena kumenyana. Ndi satana amene amabweretsa izi ndipo tisamulole kuti pakutero tilandire uphungu wa Mulungu/Allah pa khomo pathu.

> 7:20 Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana

Zopempherera:Pempherani ngati banja kuti:• Zipembezdo zitenge mbali kulimbana ndi nkhanza za amayi ndipo akhale

okonzeka kuthandiza iwo amene achitiridwa nkhanza.• Machiritsokwaiwoameneanachitilidwankhanzandiwokondedwaawo.• Ngatimulimuchiyanjanomomwemukuchitilidwakapenamukuchitankhanza,

mupeze chirimbikitso ndi thandizo kuti muthetse nkhanza.

MalembaKorani 30:20-21Korani 3:104Korani 42:10-12Genesis 2:23Mateyu 6:14-15Mateyu 7:121 petro 3:7

Zoyenera kudziwa mlangizi:• Ngatimukuonakutiwinamugulumoakuchitiridwankhanza,kapenawinaabwera

kwa inu kudzakamba nanu za nkhanza zimene akukumana nazo, konzani nthawi kuti mukumane nawo zitatha zokambirana kuti muwapatse uphungu woonjezera.

• Ngatiwinawabwerakudzakuuzanikutiakuchitilidwankhanza,ndizothekakutiakhala akuzunzidwa kwa nthawi yayitali ndipo tsopano akuopa.

• Mungathenso kuwatumiza kumene amathandiza anthu ochitiridwa nkhanza kupolisi kuti akawathandize.

• Muthandizekupezakomweonse-ozunzandiozunzidwa-angakalandilemalangizo.• Musanamuuzemunthuyemweakuzunzidwakutiabwererekubanjalake,dziwani

kuti mukhonza kukhala mukuyika moyo wake pa chiopsezo.

> Phunziro 7: Kuthetsa kusamvana 7:21

Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti ndi zotheka kuti pakhale kusamvana mbanja momwe amakonda komanso onse ndi oopa Mulungu/Allah.

Khwerero 2: Ombani mkota:

• Fotokozanikutitaonamfundozingapozofunikilazokhuzakusamvanambanjandipo zina mwa izo ndi monga:

• Anthuawiriameneamakhalalimodzitsikunditsikuangathekusemphanapenapake.

• Ngatimaanjasangakambilanebwinozakusamvanakwawo,kusamvanakokukhonza kubweretsa mavuto popangitsa kuti mbanjamo mukhale kukwiyilana. Nthawizina kusamvana kungabweretse ukali ndi nkhanza.

• Ngatimaanjasanakambilanezakusamvanakwawo,banjalolikhonzakukhalabelosamasuka ndipo izi zingapangitse banjalo kuti lisakule.

• Mikanganoyosathetsedwandiyomweimapangitsawinambanjamokukapezachibwenzi cha mseri chomwe akuganiza kuti chiziwamvetsetsa bwino. Kukhala ndi chibwenzi cha mseri kumachulukitsa chiopsezo chobweretsa kachilombo ka HIV mbanja.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli. Alimbikitseni kuti:

• Akaganizilemomweamathetselamikanganoyawondikukambilanammeneangamachitile bwino ndikugwiritsa ntchito zomwe aphunzira:

MalembaMasalmo. 128:1-3.Rute 1:15-17 Mateyu. 19:9Korani 2: 224-237Korani 4:35Korani 30:21Korani 3:36, 133,134Korani 42:30. Korani 65:1

> Kuomba mkota wa phunziro 7

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:1

Ana ndi madalitso a banja

Phunziro 8

Ana ndi mdalitso ochokera kwa Mulungu/Allah, koma izi sizikutanthauza kuti ngati ana palibe banjalo ndilosadalitsidwa. Phunziro iri lithandiza maanja kuphunzira mmene angakhalirebe banja lokondwa mbanja mwawo muli ana kapena mulibe.

Muphinzilori muli zochita zomwe zithandize maanja kukambilana mavuto omwe angabwere ngati mbanja mulibe ana ndi momwe angachitile ndi mavutowo. Zochitazi zithandizanso maanja kukambilana kusintha komwe kumabwera ana akayamba kubwera mbanja ndipo momwe izi zimakhuzila chikondi chawo kwa wina ndi mzake.

> 8:2 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

> Phunziro mwachiduleOmwe akuyenera kuphunziraAnthu omwe ali m’banja.

Ndondomeko ya phunziro• Mutuwaphunziro• Phunziromwachidule• Kutseguliraphunziro8• Miyamboyamakolo• Kusinthakomwekumakhalapongatianaayambakubwerambanja• Kuyanjanitsachikondikwamwanandiwokondedwa• Ngatimbanjamulibeana• Kuombamkotapaphunziro• Ntchitoyakunyumba• Malembaowonjezera

Nthawi yofunika Maola awiri ndi Mphindi 50

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zokambirana nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zolingana ndi mutu uno. 3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:3

> Kutsegulira phunziro 8

Nthawi: Mphindi 20

Malangizo apadera kwa MlangiziTsatilani khwerero 2, 3, ndi 4 ngati mukukumana koyamba. Ngati munakumanapo kale, akumbutseni kuti akuyenera kutenga nawo mbali momasuka. Akumbutseninso za malamulo omwe munapanga.

Zokambirana mwachiduleAlandileni maanja ndikuwawuza kuti ayamba kukambilana pa mutu wakuti banja ndi madalitso a ana. Maanja akambirana nkhani zokhuza kulephera kukhala ndi ana ndi momwe angalimbikitsile chikondi chawo kwa wina ndi mzake ana akayamba kubadwa mbanja.

Zolinga• Kumvetsetsabwinokutitikatianandimadalitsoochokerakumwamba

tikutanthauza chani?• Kuzindikirakutingakhaleopandaana,banjalikhozakukhalalokwanira.• Kumvetsakusinthakomwekumachitikaanaakabadwamnyumba.• Kuphunziramomweangaphatikizirechikondichamzakowabanjandimwana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro la banja ndi madalitso a ana:

• AnandimdalitsoochokerakwaMulungundipokupezekakwawokapenakusapezeka kwawo mbanja kusasokoneze chiyanjano chomwe chiripo pakati pa mayi ndi bambo mbanja.

• Masalmo127:3-5,Korani42:49amanenamomvekabwinokutianandimadalitso ochokera kwa Mulungu/Allah ndipo mwamuna ndi mkazi asangalale pakubwera kwa ana.

• Komabe,maanjaambiriamaonachovutakuphatikizachikondichawokondedwawawo ndi cha mwana. Kupanda kuonetsetsa bwino zimenezi, zingathe kusokoneza ndipo kuti wina ayambe kuchita zibwenzi kapena banja kutha kumene.

• Kuonjezeraapo,maanjaenaamenealibeanaamapezekamukusagwirizanakumene mathero ake kumakhala kutha kwa banja kapena kuyamba zibwenzi. Zibwenzi zimabweretsa HIV mnyumba.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Maanjaakuyenerakutenganawogawopamaphunzirowa,osangomvetsera.Akuyenera kuthandiza pazokambiranazi pakupereka mfumdo ndi kuchita nawo zomwe zakonzedwa.

> 8:4 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

• MaanjaAkuyenerakukambiranamomweakumverandimaganizoawondizinazomwe akuphunzira.

• Maanjaayeserakugwiritsantchitomalusoomweaphunziraomweangawathandize kulimbikitsa ubwenzi wawo ndi wokondedwa wawo.

Khwerero 3: Afunseni maanja kuti:

• Akuyembekezelakupindulachanikuchokeramukukhalanawopagululi.• Lembanimayankhoawondipofotokozaningatimukuwonakutizinazomwe

akuyembekeza sizikwanitsidwa kupyolera mukukambilanaku.

Khwerero 4: Afunseni maanja kuti:

• Akuganizakutindimalamuloatiomweayenerakutsatidwapofunakuonetsetsakuti palibe yemwe akumva kunyozedwa.

• Onjezeranienaomwemukuonakutindiofunikirandipomusayiwalelamulolokhuza kusunga chinsinsi.

Khwerero 5: Tsenderani ntchitoyi pokambirana pa mfundo izi:

• Kufunsamafunsondinjiraimodziyofunikirapotengapombali.• Palibeyankhololondolakapenalolakwa;komakudziwakwanu,kukambirana

ndi kudzipereka kwa Mulungu/Allah zithandiza kupeza mayankho abwino.

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiliro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza banja ndi madalitso a ana. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupeza zikhulupiliro miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu

samazimvetsetsa zokhuza kukhala ndi kukhala opanda ana. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizemaanjakumvetsetsakuti

ana ndi madalitso ochokera kumwamba.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiliro ndi zoyankhulidwa zokhuza banja ndi madalitso a ana. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti atchule miyambo ndi zikhulupiriro zomwe amaziziwa zokhuza nkhani yakuti ana ndi mdalitso wochoka kwa Mulungu. Perekani nthawi yokwanira yokambirana.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu:

• Mwamunandimkaziasiyekugonanapamenemkaziyoalindipakatipamiyeziisanu ndi umodzi ndipo adzayambenso patatha miyezi isanu ndi umodzi atabereka

• Ndiudindowamaikusamalamwana.• Mkazi akamapita koyenda nthawi imene ali ndi pakati amakhala pa chiopsezo

chotaya pakatipo.• Kugonanakoyambakuchokeranthawiyobereka,mwamunaayenerakutayaumuna

kunja kwa thupi la mkazi. Umunawo azoze thupi lonse la mwanayo. (kumupereka mwana kumalo.) amati izi zimathandiza mwanayo kukhala ndi mafupa okhwima (kulimbitsa mwana).

• Amenealibemwanaamatchulidwamainaosiyanasiyana(kukhomerakuDowa;kugwa mu mpapaya; chumba; gocho).

• Mkaziakabereka,njirayaabamboimakhwepandipomwamunasamamvabwino.Izi zimapangitsa amuna kukafuna tianamwali.

• Mkaziakabereka,kukongolakwakekumatha.

> 8:6 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

• Anaamunandiabwinokuposaakazi.• Ukakhalawaulesipameneukuyembekeza,umadzabalaanaaulesi.• Mamunaweniweniamakhalandianaambiri.• Anandichuma.

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilanizi potsindika mfundo izi:

• Palizikhulupilirozambirizomwezimabweramayiakakhalandimimba;kasamalidwe ka mwana; ntchito za amai pakhomopo ndi zina.

• Nkofunikakutianthuadziwekutizosinthazindizofunikakuzimvetsambalizonse ziwiri ndipo mwamuna ndi mkazi ayenera kumvetsetsa kusinthaku.

• Anandimdalitsoochokerakumwamba,kukhalanawokapenakusakhalanawokusasokoneze chikondi chomwe maanja amakhala nacho.

• Maanjaakuyenerakulimbikitsidwakukhalaokondanangakhaleakhalekapenaakhale opanda ana.

• Azimayisakuyenerakutengedwangatizidazoberekaana.Thanzilawolimakhala pa choopsa akabereka ana ambiri.

• MaanjaakuyenerakukhulupilirakutiMulungu/Allahadzawapatsaanamunthawi yake ngati Mulunguyo akufuna.

• Maanjaapitekuchipatalakomweangakawathandizekumvetsetsazamavutoena omwe amapangitsa kuti asakhale ndi ana ndi momwe angathanilane nawo mavutowa.

• Amayiawonetsetsekutiakuzisamalilabeakabereka.• Maanjaazilerakomansoanaazitalikilanamokwanila.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulungu/Allahathandizemaanjakuonansomiyambo,nkhambakamwandi

zoyankhula zomwe takula nazo zomwe timazikhulupilira zomwe zili zotsutsana ndi mawu.

MalembaMasalmo 127:3-4Korani 66:6Korani 16:58-59Korani 61:8-9

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:7

> Ntchito 2: Kumvetsetsa chifukwa chiani ana ali madalitso

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana kuti ndi chifukwa chani tikuti ana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Mothandizidwa ndi mau a Mulungu/Allah amvetsetsa kuti ana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

ZolingaKuwathandiza maanja kumvetsetsa kuti ana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani ntchitoyi. Fotokozani kuti mu ntchito iyi tiona kwambiri nkhani ya ana m’banja ndikukambilana chifukwa chani ana ali madalitso a banja.

Khwerero 2: Funsani anthu kuti akambirane chifukwa chiyani akuganiza kuti ana ndi mdalitso ochokera kwa Mulungu. Lembani mayankho awo pa pepala lalikulu ngati liripo.

Khwerero 3: Anthu onse akatha kukambilana, gawanani nawo malemba awa:

• Korani: 4:1 - “Inu anthu, opani Mbuye wanu yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu m’modzi (Adamu) ndipo analenga mmenemo mkazi wake (Hava), ndipo adafalitsa amuna ndi akazi ambiri kuchokera mwa awiriwo. Ndipo opani Mulungu yemwe kupyolera mwa Iye mumapemphana. Ndipo sungani chibale. Ndithudi Mulungu ndi myangániri pa inu”. - Mneneri Muhammad (mtendere ukhale pa Iye) anati, kwatiranani ndipo muchulukane chifukwa pa tsiku la chiweruzo ndidzanyadira onditsata

pokhala ochuluka kuposa magulu ena. • Genesisi:1:26 -27 - Mulungu analenga munthu mchifanizo chake. - Iye analamula iwo kuti aberekane ndi kukhala ndi udindo. Choncho ana

amatengedwa kuti ndi mdalitso wochokera kwa Mulungu.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• MulunguathandizemaanjakudziwakutianandimdalitsoochokerakwaMulungu.• Muziwakondandikuwalemekezaanaanumongaziwalozabanjalanu.

MalembaYeremia 11:29Masalmo 127:3Korani 42:49Korani 8:28

Ntchito2:Kumvetsetsachifukwachiyanianaalimdalitso

> 8:8 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

> Ntchito 3: Kusintha kumene kumakhalapo ana akayamba kubadwa m’banja

Nthawi: Mphindi 30 Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana zakusintha kumene kumachitika kwa mayi ndi abambo ana akayamba kubadwa mbanja. Akambilananso momwe akuyenera kuchitila ndi kusinthaku ndi cholinga chakuti chikondi chawo chisasokonezeke. Kusokonekela kwa chikondikungapangitse mmodzi wa iwo kutuluka mnyumbamo zomwe zingabweretse HIV.

Zolinga• Kuthandizamaanjakumvetsakutizinamwazosinthazomwezimachitikaana

akayamba kubwera ndi chilengedwe.• Kuwathindizamaanjakuphunzilamomweangachitilendikusinthakomwe

kumabwera ndi madalitso a ana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani zokambilana:

• Awuzenimaanjakutipamakhalazosinthazambirim’banjapameneanaayambakubwera.

• Zosinthazizimakhalazosiyanasiyanakuyambirapamenemaialindipakatikufikiranthawiimenemwanawabadwa.

• Ngakhalekusinthakukulikosangalatsa,nthawizinakukhonzakuyambitsamavuto mbanja

• Ndikofunikakutimaanjaakambilanebwinobwinozazosinthazindikuthesakusamvana kwina kuli konse komwe kungabwere.

Khwerero 2: Gawani anthu m’magulu awiri abambo ndi amayi paokha. Awuzeni maguluwo kuganiza ndi kuyankha mafunso awa:

Abambo• Ndizosinthazitizimenemumazionamwamayiakakhalaoyembekezerakomanso

akabereka? Kusinthaku kukhonza kukhala kwabwino kapena koipa.• Mumapangabwanjindizosinthazi?Khalidwelanulimasinthabwanjikwaakazi

anu? Nanga chikondi chanu chimakhuzidwa bwanji?• Mukuganizakutiakazianuamafunamuzipanganawobwanjiakakhalakutindi

oyembekezera komanso akabereka?

Amayi• Ndizosinthazitizomwemumaonamukakhalandimimbakomansomukabereka?• Mumaonakusinthakwanjimwaamunaanu?Kusinthakukukhonzakukhala

kwabwino kapena koipa.

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:9

• Mumapangabwanjindikusinthaku(kusinthakwawondikwaamunaawo)Khalidwe lanu limasintha bwanji kwa amuna anu? Nanga chikondi chanu chimakhuzidwa bwanji?

• Mumafunakutiamunaanuazipangachanimukakhalandimimbakapenamukabereka?

Khwerero 3: Magulu apereke zomwe ayankha ndipo lolani kuti pakhale zokambilana.

Khwerero 4: Ombani mkota ndi kumalizitsa zokambilanazi potsindika mfundo izi:

• M’musimumulizinamwazosinthazimenezimakhalapomunthawizakambidwapamwambazi:

Za mthupi: • Maonekedwe a mkazi amasintha kumbali ya kawonekedwe ka thupi lake i.e. kusalala kwa thupi; kuoneka bwino. Nthawi zina kusintha kwina kumatha kuchotsa chidwi cha mwamuna pa mkazi wake komanso nthawi zina mwamuna akhonza kuyamba kumuona mkazi wake kukongola kwambiri nthawi yomwe ali oyembekezera. • Madyedwe amkazi amathanso kusintha, amatha kumasilira zakudya zomwe samazikonda, kapena kukanika kudya zakudya zomwe amadya bwinobwino. Nthawi zina amatha, kumalavulalavula. Nthawi zambiri amayi amakhala ndi nselu akakhala oyembekezera, makamaka miyezi itatu yoyambilira ndipo amavutika kudya ndipo amasanza makamaka mmamawa. • Mayi ayenera kupewa zakudya zomwe zingamupatse nselu. • Azidya zakudya zopatsa thanz/zamagulu monga zakudya zopatsa mphamvu (nsima, mbatata, chinangwa mpunga ndi zina) zomanga thupi (nyama, nsomba, nyemba ndi mtedza) ndi zoteteza kumatenda monga (masamba zipatso). • Abambo akuyenera kukhala omvetsetsa kuti mkazi wawo sakupeza bwino ndipo ayenera kumathandiza ntchito za pakhomo.Za maonekedwe: • Maonekedwe a thupi amasintha mwa mkazi, amasowa mtendere pogona kapena pokhala, kusowa tulo. • Agwiritse ntchito mapilo ambili kuti azikhala ndi kugona bwino. • Abambo akuyenera kuwathandiza akazi awo kuti zonse zikhale bwino. • Kusintha kwa thupiku kungathenso kukhuza moyo wawo wogonana. Nkofunika kuti banjali lizikambirana nkhani zokhudza kugonana mnyumbamo. • Alangizeni maanja kuti azisinthasintha pogonana ndipo azigwiritsa ntchito njira yomwe aliyense akhale omasuka nayo pamene ali oyembekezera.Za maganizidwe: • Malinga ndi kusintha kwa zinthu zina mthupi, mkazi amakhala osokonezeka mmaganizo. Mwachitsanzo akhonza kumalira pa zinthu zopanda pake, kapenanso kukhala wawukali. • Izi ndi zinthu zoti sangathe kuziletsa ndipo ndikofunika kuleza naye mtima mu nthawi imeneyi.

> 8:10 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

Za makhalidwe: • Kuphatikizapo pa kusintha kwa mmaganizo, amayi amayamba kukhala

opanda chidwi ndi amuna awo ndipo amayika chidwi chawo pa mwana yemwe akumuyembekezera. Akhonzanso osakhala ndi chidwi chozisamalira makamaka ngati akukanika kumvetsetsa za kusintha komwe kukuchitika mmoyo wake. Ndikofunika kuti ngati banja kuziona izi msanga ndi kukambilana momasuka.Zachuma: • Munthu mmodzi amakhala kuti wawonjezereka ofunika kudyetsedwa ndi kusamalidwa. Izi zikutanthauza kuti banja liyenera kusintha zinthu zina ndi cholinga chakuti akwaniritse kumupatsa mwana zosowa zake. Maanja akuyenera kukambilana ndi kukonzekera asanaganize zokhala ndi mwana wina.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaakhalendichikondichenichenikwawinandimzake.• Abamboaziwathandizaakaziawoakakhalandimimbandikusamalamwana.• Abamboagonjetsemiyambondizikhulupilirozinazomwezimawalepheretsa

kuthandiza ndi kuwamvetsetsa akazi awo akakhala ndi mimba komanso akabereka.

MalembaKorani 42:49Korani 64:15Yohane 15:13-14Aroma 12:9-10

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:11

> Ntchito 4: Kuyanjanitsa chikondi kwa mwana ndi wokondedwa

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana mmene angalimbikitsile chikondi chawo kwa wina ndi mzake ngakhale atakhala ndi ana. Maanja awonanso mmene kuthandizana kulera ana kungalimbikitsile chikondi chawo kwa wina ndi mzake.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakuphunzirammeneangalimbikitsilechikondichawokwa

wina ndi mzake ngakhale atakhala ndi ana.• Kuwalimbikitsamaanjakutiazithandizanakuleraana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulilani phunzilo:

• Adziwitseni maanja kuti ntchito iyi ndi yokhuza kupitilizabe kukondana wina ndi mzake ngakhale mbanjamo muli ana.

• Zimachitika kawirikawiri kuti chidwi pa wina ndi mzake mbanja chimazilara ana akayamba kubadwa.

• Ndikofunika kuti maanja azikhala ndi nthawi yocheza wina ndi mzake.

Khwerero 2: Afunseni maanja: • Kubadwa kwa ana mbanja kumasokoneza bwanji chikondi chomwe mayi ndi

bambo anali nacho kwa wina ndi mzake poyamba? Khwerero 2: Maanja akakambilana, ombani mkota pofotokoza mfundo izi:

• Nkofunikakuunikansontchitozamwamunandimkazipameneanaayambakubwera.

• Maanjaayenerakudziwakutimwanandiwawoosatiwamakoloawokapenaachibale awo. Choncho pafunika kugwirizana kuti alere mwanayo.

• Amunaayenerakuperekachithandizochokwanirakwamkaziposamaliramwana. Dziwani kuti udindo wosamalira mwanayo si wa mkazi yekha.

• Amunaamakondakusiyiraudindowumzimayi.Chonchomkaziyoamaonekakuti akuika chidwi kwambiri pa mwana osati mwamunayo.

• Maanjaakuyenerakumakhalandinthawiyapaderayochezangatibanja.• Akaziayenerakulimbikitsidwakuonetsetsakutiakupitirizakudzisamalakuti

adzionekabe bwino. Izi zidzathandiza kuti amuna awo apitilize kuwakonda.• Mwamunayoakuyenerakuonetsetsakutiakuperekazofunikirazonse.• Abamboakuyenerakumvetsetsakutithupilamayilimasinthamwanaakabadwa.

Amayi ndi osiyanasiyana, kwa ena kusinthaku kukhonza kukhala kuwonjezela thupi, kusintha m’maonekedwe kapenanso m’maganizo. Zonse ndi mbali imodzi yakubereka.

> 8:12 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Maanjaasalorekupezekakwaanambanjakutikusokonezechikondichawokwa

wina ndi mzake.• Maanjaazithandizanakuleraanaawo.• Mukhaleolezamtimandiomvetsetsakusinthakukamachitikambanjamwanu

ndikuti Mulungu/Allah akupatseni chilimbikitso kuvomereza kusinthaku moyenerera.

MalembaKorani 16:72Korani 7:189Korani 64:14Korani 8:6-63Genesis 1:27Aroma 12:9-10Yohane 15:13-14

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:13

> Ntchito 5: Ngati m’banja mulibe mwana

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana zina mwa zovuta zimene maanja omwe alibe ana amakumana nazo. Awona zina zomwe zimapangitsa maanja ena kukhala opanda ana. Ntchito iyi ithandiza maanja kukambilananso za zoopsa zomwe zingabwere chifukwa chogwiritsa ntchito malangizo oipa komanso za HIV/Edzi.

Zolinga• Kuwapatsachiyembekezomaanjaomwealibeana.• Kuwathandiza maanja omwe ali ndi ana kumvetsetsa zovuta zomwe maanja

omwe alibe ana amakhala nazo ndi cholinga chakuti awone momwe angathe kumawalimbikitsila.

• Kuwathandizamaanjakumvetsetsakutindichifukwachanimaanjaenasakhalandi ana.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani ntchitoyi:

• Awuzenimaanjakutisionseangathekukhalandiana.• Izizikhonzakuchitakapazifukwazosiyanasiyana,koterondikofunikakumvetsetsa

zomwe winayo akukumana nazo musanamuweruze. • Ngatigulu,tiyambakufufuzazinamwazifukwazimenezindicholingachakuti

tiwamvetsetse ndi kuwalandila okondedwa athu ndi anthu ena.

Khwerero 2: Werengani nkhani yomwe iri mmusiyi kwa anthu onse.

Bambo ndi Mai Papaya akhala m’banja zaka zoposa zisanu koma alibe mwana. Chofunika kudziwa ndi chakuti banjali ndi loopa Mulungu/Allah, limakondana ndipo akhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake. Padakali pano mwamunayo akufunsidwa kwambiri ndi abale ake nayenso mkazi akupanikizidwa kwambiri ndi abale ake. Banja laganiza zokapempha uphungu kwa atsogoleri a chipembedzo.

Khwerero 3: Mukawerenga awuzeni maanja kuti akhale mmagulu ndipo apange timasewero.

Khwerero 4: Agaweni maanja mumagulu ndikuwapatsa nkhani zopangira sewero izi:

• Banjalikulandilachikakamizokuchokerakwaabalendiabwenzikutiakhalendimwana.

• Banjalikukafunamalangizokwamtsogoleriwampingo.

> 8:14 Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja

Khwerero 5: Akamaliza kukonzekera, awuzeni kuti awonetse masewero awo.

Khwerero 6: Akamaliza kuonetsa masewero awo akambilane mafunso awa:

• Kodibanjalilimalandilachikakamizochanjikuchokerakwaachibalendiabwenzi?

• Kodikukakamizidwakukunalindizovutazotanipabanjali?• Munamvauphunguwotanikuchokerakwaatsogoleriampingo?• PolingalirankhaniyaHIVndiEdzi,chiopsezochimenechingagwerebanjali

kamba ka malangizo olakwika chingakhale chotani?

Khwerero 7: Ombani mkota ndi kumalizitsa zokambilanazi powakumbutsa mfundo izi:

• Nkofunikakutigululidziwekutipalizifukwazosiyanasiyanazolepheretsabanjakukhala ndi ana. Zifukwa zina ndi izi;

• Zachipatala:Mayikapenabamboakhonzakukhalandivutolinalachilengedwelomwe lingalepheretse kukhala ndi mwana.

• Mwamunakapenamkaziakhonzakukhalakutindiosabereka.Nthawizambirimzimayi ndi amene amanenedwa kuti ali ndi vuto koma zikhonza kutheka kuti mamuna ndi amene ali ndi vuto.

• Zaumunthukapenazachuma:enaamatiakuyambaapitakusukulu,alibechumachokwanira kapena azaberekabe.

• Ndiudindowamwamunandimkaziwakekupangachiganizochakuchulukakwa ana omwe akufuna kukhala nawo komanso nthawi yomwe akufuna kudzakhala ndi anawa.

• Maanjaambirisadziwachifukwachimenesakupezeraanandipoamasowamtendere kwambiri.

• Auzenianthukutisayenerakugonjerazofunazaanthukutiatulukemnyumbachifukwa izi zingaonjezere chiopsezo chotenga HIV.

• Awuzenimaanjakutiakhonzakukhalamakolookondapotengamwanayemwemakolo ake anamwalira kukhala mwana wawo.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• KudziwakutiMulunguamachilitsandipondiameneamatipatsazosowazathu

zonse.• Mulungualimbikitsechikhulupilirochaiwoamenealibeanandikuwapatsa

mtima opilira ndikudikila pa Ambuye ndikudziwa kuti Mulungu amachita zonse kukhala zabwino mu nthawi yake.

• Mulunguawathandizemaanjakuvomerezamomwealirindikupitachitsogolondi moyo wawo podziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitila ubwino iwo amene amamuopa Mulungu. Pemperani kuti mukhale chikondi ndi mtendere mmaanja amenewa.

MalembaKorani 42:50Yeremia 11:29Aroma 8:26Genesis 1:27Mlaliki 3:1

> Phunziro 8: Ana ndi madalitso a banja 8:15

> Kuomba mkota kwa phunziro 8

Nthawi: Mphindi 20

Ndondomeko

Khwerero 1: Akumbutseni maanja kuti ana ndi madalitso ochokera kumwamba, kukhala nawo kapena kusakhala nawo kusamasokoneze chikondi chawo mbanja.

Khwerero 2: Ombani mkota pofotokoza kuti:

• Taonamfundozikuluzikuluzokhuzakukhalakapenakusakhalandiana,mongaizi:

• AnandimdalitsokuchokerakwaMulungu.• Palizifukwazambirizomwezimapangitsaenakutiasakhalendianandipoambiri

mwa iwo saziwa kuti ndi chifukwa chani.• Kugonjerakuchikakamizochakutimukhalendizibwenzizamserikutimukhale

ndi ana kuyenera kupewedwa chifukwa kumachulukitsa chiopsezo chobweretsa HIV mnyumba.

• Maanjaakuyenerakudziwakutipalikusinthakosiyanasiyanakomwekumachitikaana akayamba kubwera mbanja. Zina mwa zosinthazi ndi chilengedwe ndipo maanja akuyenera kukhala okonzeka.

• Zosinthazisizikuyenerakusokonezachikondochomweanalinachokwawinandimzake, koma chikondi chawo chikhalebe cholimba ngakhale pali ana.

Ntchito yakunyumba: Awuzeni maanja kuti akapitilize kukambilana kunyumba za phunziroli. • Funsanianthukutiaonemomweakhalirachiyambirekubweraanam’banjamwao

kapena chifukwa chopanda ana m’banja mwaomo. • Ndizitizimeneakufunikakusintha,kapenakusiyakutiapitirizekukondanawina

ndi mnzake?• Akambilanekutiangakhalebwanjiokhulupilikakwawinandimzake.

MalembaMasalmo 127:3-5; Mateyu. 19:14; Korani 2:233, Korani 65:6

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:1

Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

Iri ndi phunziro lomaliza mbukhuli ndipo atatha kuphunzila zonse zomwe zili mubukhuli, maanja apemphedwa kuti akumbukile zonse zomwe akhala akuphunzila ndi kukonza ndondomeko ya momwe angakagwiritsile ntchito zonse zomwe aphunzira.Pamapeto pake maanja apatsidwa zikalata zonsonyeza kuti amaliza maphunzilo komanso kuti apanganso malumbilo awo abanja.

Phunzilori liri ndi ntchito zomwe zithandize anthu kutengapo mbali ndi kuganiza momwe angagwiritsile ntchito zomwe aphunzila kuti akhale ndibanja lokondwa. Amayi ndi abambo afunsidwa kulemba zomwe akufuna kusiya kuchita ndi zomwe apitilize kuchita.

Phunziro 9

> 9:2 Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

> Phunziro mwachidule

Omwe akuyenera KuphunziraAnthu omwe ali m’banja.

Ntchito1. Mutu wa phunziro2. Phunziro mwachidule3. Kutsegulira phunziro 94. Miyambo ya makolo5. Kuwunikanso zomwe zaphunzilidwa6. Kukhazikitsa ndondomeko7. Kuomba mkota8. Ntchito ya kunyumba9. Malemba owonjezera

Nthawi yofunikaOla limodzi ndi Mphindi 10

Zofunika1. Baibulo/Korani2. Mapepala ndi zolembera

Zokonzekera za Phungu1. Werengani mndandanda wa zokambirana nthawi isanakwane.2. Werengani ndime za muBaibulo/Korani zolingana ndi mutu uno. 3. Ganizilani za zolembedwa zina zowonjezera zomwe zingakhale zothandiza pa

phunziroli.

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:3

> Kutsegulira phunziro 9Nthawi: Mphindi 20

Kukonzekera mwapadera kwa Mlangizi• Irinditsikulapadera.Alimbikitsenimaanjakutiavalebwinondipoawoneke

bwino kwa okondedwa awo. • Konzanimasatifiketiomwemuwapatsechifukwachomalizamaphunzirokoma

chifukwa chakupanganso mapangano aukwati wawo. • Pezanimmodziwaatsogolerikapenaabusa/Sheikhkutiatsogoleremwambo

wopangaso malumbilo a ukwati. • Konzanimwamboojambulazithunzi.• Mukamalizaanthuadyerelimodzi.

Zokambirana mwachiduleAlandileni maanja ku zokambilana ndikuwawuza kuti akhala ndi mwayi wokambilana pa mutu wakuti ‘Kusangalala ndi moyo ndi kukulira limodzi.’ Maanja awunikanso malumbilo awo aukwati ndi kulonjeza kukayamba kuchita zonse zomwe aphunzira mu maphunziro osiyanasiyana amubukhuli.

Zolinga• Kumvetsetsabwinokutimaanjaangakhalebwanjiosangalalandikukulira

limodzi ndi zinthu zomwe zingalimbikitse chiyanjano chabiwno cha banja. • Kukambilanazinthuzomweakayambekuchitandizomweakasinthendi

cholinga chosangalatsana wina ndi mzake.

Ndondomeko

Khwerero 1: Fotokozani za phunziro la kusangalala ndi moyo ndi kukulira limodzi: • Banjamuchipembedzolikuyenerakukhalachiyanjanochamoyowonsendipo

anthu akuyenera kukhala okondwa mbanja osati opilira.• Chitsimikizochakukhalaosangalalambanjachikufunikakuyikachidwipa

mfundo zomwe zimathandiza banja kukhala losangalala. • Kafukufukuakusonyezachiwerengelochamaanjaomweakuthachikuchuluka

kwambiri mofulumira.kodi izi zikutanthauza kuti ndi zosatheka kukhala okondwa mbanja kwa moyo wonse.

Khwerero 2: Awuzeni maanja kuti:

• Maanjaakuyenerakutenganawogawopamaphunzirowa,osangomvetsera.Akuyenera kuthandiza pazokambiranazi pakupereka mfundo ndi kuchita nawo zomwe zakonzedwa.

• Maanjaakuyenerakukambiranamomweakumverandimaganizoawondizinazomwe akuphunzira.

• Maanjaayeserakugwiritsantchitomalusoomweaphunziraomweangawathandize kulimbikitsa ubwenzi wawo ndi wokondedwa wawo.

> 9:4 Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti: • Maanjamomwemulichikondichopambana,kulezamtimakomansokulankhula

kwabwino.

Malemba1 Atesalonika 5:16Yohane 15:13-14Aefeso 5:26-29Korani 30:21

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:5

> Ntchito 1: Miyambo ya makolo

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja ayamba kuyang’ana pa zikhulupiriro kapena zina zomwe anthu amayankhula mdera lawo zokhuza kusangalala ndi moyo ndi kukulira limodzi. Iwo akambirana ngati zimenezi zili zoona kapena ayi ndikupeza thandizo lomwe angalandile kuti athane ndi mavuto amenewa mu chiyanjano chawo.

Zolinga• Kupeza zikhulupiliro, miyambo yosiyanasiyana ndi zina zomwe anthu

samazimvetsetsa zokhuza kusangalala ndi moyo ndi kukulira limodzi. • Kuwafotokozelamfundozoonazomwezingawathandizemaanjakukusangalala

ndi moyo wawo wa mbanja ndi kukulira limodzi.

Ndondomeko

Khwerero 1: Awuzeni maanja kuti akambirana za zikhulupiriro ndi zoyankhulidwa zokhuza kusangalala ndi moyo ndi kukulira limodzi. Pokambirana mwakuya tisiyanitsa zabodza ndi zoona.

Khwerero 2: Afunseni maanja kuti atchule miyambo ndi zikhulupiriro zomwe zokhuza moyo wachisangalalo m’banja.

Khwerero 3: Zina mwa mfundo zomwe zingatchulidwe ndi zomwe ziri mmusizi. Werengani mfundo zomwe sizinatchulidwe ku gulu.

• Ndizosathekaanthuambanjakukhalaokondwa.• Ngati mwamuna akumuthandiza mkazi wake ntchito za pakhomo kapena

akumukonda mkazi wake kwambiri ndiye kuti anadyetsedwa mankhwala.

Khwerero 4: Ombani mkota pa zokambilanizi potsindika mfundo izi:

• Palimaanjaambiriomweamakhalabeokondwambanja.Ngakhaleizizilizotheka,ena zikachitika izi, amachiona chovuta kumvetsetsa ndipo amanena kuti “anthu awa amakondana ngati adakali pachibwenzi’’. (“angokhala ngati ndi chibwenzi” kapena “banja sangakondane choncho”).

• Ndizothekakukhalandibanjalokondwangatiawiriwoapitilizakukondanangatim’mene amkakonderana ali pa chibwenzi.

• Kumukondawokondedwawanundikumuthandizantchito sizikutanthauzakutiwapatsidwa mankhwala koma waganiza zomuthandiza wokondedwa wako ndi kukhala ndi banja lokondwa.

> 9:6 Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti:• Mulunguathandizemaanjakusiyamiyambo,nkhambakamwandizoyankhula

zomwe takula nazo zomwe timazikhulupilira zomwe ziri zotsutsana ndi mawu komanso zimakulepheretsani kumumvetsetsa okondedwawanu.

MalembaMateyu 19:5-6Korani 33:21

Mtumiki Muhammad mtendere ukhale ndi iye, Abu Sufyan Sakhri anayankha pamene amafunsidwa ndi mfumu Heraclius zomwe mtumiki amawawuza kuti azichita? “ Kupembedza Mulungu yekha osaphatikiza ndi zina, kusiya zikhalidwe/ miyambo zoipa za makolo athu.(Al-Bukhar).

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:7

> Ntchito 2: Kuyang’ana zomwe zaphunziridwa

Nthawi: Mphindi 20

Zokambirana mwachiduleMaanja awunikanso maphunziro omwe aphunzira mbuyomu ndikuona kuti angakhale bwanji okondwa moyo wawo wonse.

Zolinga• Kuwathandizamaanjakukumbukilazomweanaphunzilamumagawo

ammbuyomu ndikukonza ndondomeko ya mmene angagwiritsile ntchito zomwe aphunzila.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani phunziro. Adziwitseni maanja kuti tikhala tikuyang’ananso zomwe takhala tikuphunzira mbuyomu.

Khwerero 2: Gawani amuna ndi akazi m’magulu awiri.

• Anthuasinkhesinkhezamituimeneaphunzirandikugawanazofunikirazazimene aphunzira.

• Afunsenikutialembezinthuizi:-

• Ndizithuzitizimeneakayambekuchitakutimuwawonetseokondedwaanukutimumawakonda ndi kuwanyadila?

• Ndizinthuzitizimeneakufunawokondedwawawoazichitakutiapitilizekukhala osangalala.

Khwerero 3: Onse abwere pamodzi ndipo afotokoze zomwe akambilana.

Khwerero 4: Afotokozereni maanja kuti:

• Mfundoizindizokhuzagululonsendipondikofunikabanjalirilonsekuganizirazomwe iwo angapange paokha.

Khwerero 5: Awuzeni maanja kuti akhale paokha paokha ndipo banja liri lonse likambilane mafunso omwe aja:

• Ndizinthuzitizimeneakayambekuchitakutiawawonetseokondedwaawokutiamawakonda ndi kuwanyadila?.

• Ndizinthuzitizimeneakufunawokondedwawawoazichitakutiapitilizekukhala osangalala.

> 9:8 Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

Khwerero 6: Maanjawa akamaliza kukambilana, abwererenso mmalo mwawo. Ombani mkota wa zokambilananzi powakumbutsa maanja: • Ndikofunikakukhalaomasukandiwachilunamopokambazomwe

zingakupangeni kukhala osangalala mbanja.• Ngatichinachakesichikukusangalatsani,mukuyenerakukambilanandi

okondedwa wanu.• Ngatiokondedwawanualindivutomukuyenerakudekhandikukhala

omvetsetsa. Ndikofunika kumvetsera ndi kusintha ngati kuli kotheka. • Mbaliimodziyakukhalambanjandikukhalaololakusintha.Izizikhonza

kuthandiza banja lanu kukhala lolimba.

ZopemphereraPempherani ngati banja kuti: • Maanjaathekuchitazomweakhalaakuphunzilakutimtenderendichikondi

zipitilire pakati pawo.

MalembaMateyu 19:5-61 Akorinto 7:10Korani 25:54

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:9

> Ntchito 3: Kumanga mfundo

Nthawi: Mphindi 30

Zokambirana mwachiduleMaanja akambilana mmene angapititsile patsogolo banja lawo. Ntchitoyi ithandiza maanja paokha paokha kuganizila za momwe akhala kukhalira ndi mbali zomwe akuyenera kusintha.

ZolingaKuthandiza maanja kukonza ndondomeko ya momwe angakhalire mokondwa moyo wawo wonse.

Ndondomeko

Khwerero 1: Tsegulirani ntchitoyi. Adziwitseni maanja kuti tikhala tikuonanso za maphunziro omwe taphunzira mmbuyomu poyang’ana za m’mbuyo komanso za mtsogolo.

Khwerero 2: Akumbutseni mofulumila maphunziro omwe akhala akuphunzira mbuyomu. Gwiritsani ntchito mfundo zomwe zili kumapeto a maphunzirowa ngati mukufuna kuti mukumbukile mosavuta.

Khwerero 3: Awuzeni maanja kuti banja liri lonse likhale palokha. Awuzeni kuti asinkhesinkhe zomwe akhala akuphunzila ndipo ayankhe mafunso awa:

• Ganizilanizamomwemwakhalamukukhalirangatimwamunandimkazimusanaphunzire za m’bukhuli. Ndi zinthu ziti zimene mwazitulukira zimene simumachita bwino?

• Ndizinthuzitizachilendozimenemwaphunzirandipomukukonzazokayambakuzigwiritsa ntchito? Lembani zimenezi ndi kuzisunga pabwino – mchipinda mwanu kapena pena paliponse mnyumba mwanu.

Khwerero 4: Kumaliza zokambirana ndi kuomba mkota pa mfundo zikuluzikulu.

• Amayindiabamboayenerakulimbikirakusangalatsawokondedwawawokutibanja lawo likhale lamphamvu ndiponso lokwanira.

• Banja,mongachilichonsechamtengochimafunanthawindintchito.Mwamunandi mkazi adziwe kuti banja lawo likhale losangalala ndi lapamwamba limafunika kudyetsera pafupipafupi.

• Mwamunandimkaziaonetsetsekutiakumapezanthawiyokhalalimodzi.Adziwenso kuti mdani wa banja ndi kutangwanika ndi zinthu zambira mpaka osapeza nthawi yosangulutsana. Pa moyo wathu timakonda kunyozera ubale. Koma tiyenera kupereka nthawi yokwanira ku banja lathu.

• Maanjaamalepherapamenemwamunandimkaziakulepherakuperekazimenewokondedwa wawo akufuna monga chikondi, kuyamikiridwa, ndinso kupereka mpata wakuti aliyense azipita patsogolo.

• Mfundozotsatilazizikuombamkotapamomwebanjalokondwaliyenerakukhalira:

> 9:10 Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi

• Kudzipereka: Mu chiyanjano chomwe chili chabwino, mamuna ndi mkazi amazindikila kuti anapanga chiyanjano chomwe chili cha moyo wawo wonse. Amadzipereka kusamalilana ndi kuthandizana mmavuto.Maanja momwe zinthu zikuyenda bwino mamuna kapena mkazi samaganiza za iwo okha, koma amaganiza kwambiri za zomwe zili zokomera onse awiri limodzi; amakhala odzipereka kwa wina ndi mzake. • Kukwanitsidwa: Mu chiyanjano chomwe chiri chabwino, onse amakhala okwanitsidwa ndipo amakhala moyo wosangalala. Amakhala okwanitsidwa ndi moyo wawo, komanso chiyanjano chawo wina ndi mzake. • Kulankhulana: Maanja omwe chiyanjano chawo chili bwino, amadziwa

mmene akuyenera kuyankhulilana wina ndi mzake mwaulemu komanso molorelana. Anaphunzira kulankhula bwino. • Kuthetsa kusamvana: Mu chiyanjano china chili chonse anthu amatha kuyambana/kusemphana. Mu chiyanjano chabwino, aliyense amayesesa kuthetsa mavutowo akadali ang’ono, kuti mavutowo asakule ndikusokoneza chiyanjano chawo. • Palibe nkhanza: nkhanza zikhonza kukhala kumenyana kapena kukankhana, kapena nkhanza za mmaganizo kapena kuyankhulidwa mwa nkhanza. Nkhanza sizabwino mu chiyanjano china chili chonse. Mbanja

lomwe muli chikondi nkhanza sizingakhalemo. • Kukwanitsidwa ndi moyo wogonana: Kukhulupilirana ndi kofunikila mu chiyanjano chomwe chili chabwino. Pamene pali kukayikila mbanja, banjalo limakhala pamavuto. • Nthawi yopambana: Mu chiyanjano mwamuna ndi mkazi amakhla ndi nthawi yocheza wina ndi mzake ndikupanga zinthu zomwe onse amazikonda limodzi. • Chikondano ndi kuthandizana mmaganizo: mmbanja mmene chiyanjano chawo chili bwino amathandizana ndipo amasamalana mwachikondi komanso amathandizana maganizo. Amaonetserana chikondi munjira zosiyanasiyana, osati mukugonana kokha. • Kusamala ana: mu banja momwe chiyanjano chawo ndi chabwino amadzipereka kusamala ana awo, obereka okha kapena omwe akulera. Ndizotheka kukhala mbanja opanda mwana, koma ngati ana alipo, banja labwino amathandiza kulera ana aja bwino.

Khwerero 5: Tsopano popeza mwamaliza maphunzilo onse, ndi nthawi yachisangalalo. Monga momwe mungathere, konzani mwambo wachikondwerero ndi maanja onse, ndikufotokoza zomwe aphunzira.

ZopemphereraPempherani ngati banja:• Maanjaagwiritsentchitozomweaphunzirammaanjamwawondikugawanandi

anzawo.• Maanjakhaleokondwamoyowawowonse,kulemekezamawuaMulungu/

Allah, kukonda ndi kulemekeza wokondedwa wanu.

> Phunziro 9: Kusangalala ndi moyo komanso kukulira limodzi 9:11

MalembaYohane 15:13-14Mateyu 19:5-6Genesis 2:24Korani 3:103Korani 66:6Korani 9:71

> 12 Banja la chisangalalo

> Kuomba mkota pa bukhuliBukhuli launika zinthu zingapo zimene zimakhudza anthu pa nkhai ya ukwati.

1. Mutu woyamba waunika zinthu zina zimene achinyamata akuyenera kuziganizira pamene aganiza zolowa m’banja. Izi ndi zinthu zomwe zingathandize pa moyo wawo wa m’banja kukhala wamsangala kapenanso wamazunzo. Achinyamata alangizidwa kuti asanyozere zinthuzi kamba koti zidzapangitsa moyo wawo kukhala wabwino kapenanso wamavuto. Alangizidwanso kumasuka kuthetsa ubwenzi ngati aona kuti mathero ake akhala ovuta. Alangizidwa momwenso angachitire pakusiyanaku.

2. Mutu wachiwiri waunika banja monga mphatso yochokera kwa Mulungu/Allah ndi kufunika kolilemekeza. Mutuwu wathandandiza maanja kukumbukira udindo wawo ndi kufunika kosunga malonjezo aukwati. Maanja analinso ndi mwai wokambirana momwe angasonyezerane chikondi kwa wina ndi mnzake ndi kupanga moyo wawo wa m’banja kukhala wokhathamira ndi wa chikondi.

3. Mutu wachitatu waunika momwe maanja angakhalire moyo wosangalala m’banja lawo. Mutu wakhunzanso nkhani yofunika kwambiri ya kulumikizana. Maanja akumbutsidwa kufunika kwa kulumikizana m’banja ndi momwe kuperewera kwa kulumikizana kungasokonezere banja. Mutuwu unayang’ananso zimene zimayambitsa mavuto a kulumikizana pakati pa mwamuna ndi mkazi ndi zomwe angachite kuti kulumikizana kuyambenso kuyenda bwino.

4. Mutu wachinayi ukuona za kugonana ngati mphatso imene Mulungu/Allah anapereka kwa anthu apabanja ndi momwe mwamuna ndi mkazi angapangire moyo wawo wogonana kukhala wokoma. Mutuwu wayang’ananso momwe kulumikizana kwabwino kungathandizile kuti banja likhale ndi moyo wogonana wokwanitsidwa.

5. Mutu wachisanu ukuona zimene zimayambitsa ndi zotsatira za kukhala ndi zibwenzi kunja kwa banja. Mutuwu ukuwunikila zinthu zomwe zimayambitsa mchitidwe wokhala ndi zibwenzi kawirikawiri ndi momwe izi zingapewedwere. Zotsatirazi zikuphatikizapo kutenga HIV imene imapatsiridwa kwa mnzanu wosalakwa. Mutuwu ukuthandizanso maanja kumvetsa kuopsa kokhala mu chipwirikiti cha kugonana.

6. Mutu wachisanu ndi chimodzi maanja apatsidwa mwai wounika zimene zimachititsa kuti m’modzi pabanja apezeke ndi HIV pamene wina alibe. Maanja alangizidwa momwe angayilandilire nkhaniyi pakuti sikutanthauza kuti m’modziyo anali wosakhulupirika. Mutuwu ukukambanso nkhani zokhudza kufala kwa HIV kuchokera kwa mai kupita kwa mwana (PMTCT) kuti mwamuna ndi mkazi adzipanga chiganizo akudziwa chimene akuchita.

7. Mutu wachisanu ndi chiwiri waunika momwe tingathetsere kusamvana. Mu phunzilo ili nkhanza ndi kuthetsa banja zaletsedwa. M’malo mwake maanja apatsidwa luso la momwe angathetsere kusamvana kwawo kuti banja lawo likhalebe lokondwa. Maanja akumbutsidwanso kuti ayenera kuyembekezera kuti kusamvana kuzikhalapo m’banjamo.

8. Mutu wachisanu ndi chitatu ukukamba zakuti ana ndi mdalitso wochokera kwa Mulungu/Allah ndipo kuti kusowa kwa ana kapena kupezeka kwao kusasokoneze chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi. Mutuwu ukukambanso za zosinthika zina zimene zimabwera mbanja ana akayamba kubwera mnyumba, udindo wawo pa anawo ndi kulimbikitsa azimayi kuonetsetsa kuti akuzisamalirabe ngakhale abereka.

9. Mutu womaliza ukuomba mkota pa zonse zimene zakambidwa mu bukhuli ndipo ukupempha mwamuna ndi mkazi kuti kusinkhasinkha pa zonse zimene aphunzira ndi kukambirana momwe angazigwiritsire ntchito kuti akhale moyo wabanja wosangalala mpaka kalekale.

> Banja la chisangalalo 13

> Tiuzeni maganizo anu pa za mlozowu

Tifunitsitsa kumva maganizo anu!Chonde lembani maganizo anu m’munsimu. Izi zidzatithandiza kuknza zofunika kusintha mu mlozomu.

Tumizani maganizo anu ku:John Hopkins University Bloommberg School of Public HealthCentre for Communications ProgramsBridge Project,P O Box 30782Lilongwe 3, Malawi.Fax No: 01750496

1. Chongani gulu lomwe inu mwagwiritsamo ntchito mlozowu:-

Magulu a achinyamata

Magulu a kudera lanu

Magulu a abambo

Magulu asakaniza amayi ndi abambo

Magulu a zipembedzo

Atsogoleri a zipembedzo

Ana asukulu

Olandira uphungu

Ena

2. Fotokozani za phindu lomwe mlozowu ukuwonetsa kwa ophunzira pa maganizo komanso makhalidwe a ophunzira?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

3. Kodi ophunzira anena kapena kuchita chiyani kuti inu muyankhe funso la mwambali m’mene mwaliyankhira?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

> 14 Banja la chisangalalo

4. Ndi ntchito ziti zomwe munapindula nazo kwambiri? Fotokozani.

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

5. Kodi ndi ntchito ziti zomwe sizidapindule kwambiri pophunzitsa? Fotokozani.

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

6. Kodi munakumana ndi mabvuto ati pogwiritsa ntchito mlozo umenewu.

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

7. Kodi pali zosintha zomwe munakonza pophunzitsa? Fotokozani

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

8. Kodi ndi zosintha ziti zomwe mukufuna tikonze kuti mlozowu ukomerekomere?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

> Banja la chisangalalo 15

9. Kodi inuyo kapena bungwe lanu mukusowa maphunziro ena akagwiritsidwe ntchito ka mlozowu? (chongani chimodzi) Inde Ayi

10. Ngati mukufuna maphunzirowa, fotokozani kuti maphunziro ake ndi a mtumu wanji? Nanga ndati adzaphunzitsidweyo?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

11. Kodi amene akuyenera kupindula ndi maphunziro amenewa ndi ndani?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

12. Maganizo ena?

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––––

Dzina lanu:

Bungwe:

Adilesi:

Foni:

Fax:

Imelo:

ZIKOMO

> Banja la chisangalalo 16

> Zolemba zofotokozera

1. KODI HIV IMAFALA BwANJI?

HIV imafala kuchokera kwa munthu amene ali nayo kupita kwa wina kudzera mu:• Magazi(kuphatikizaamsambo)• Umuna• Chikazi• Mkakawammawere

Magazi amakhala ndi tizirombo tambiri, motsatidwa ndi umuna, motsatidwa ndi chikazi, motsatidwa ndi mkaka wa m’mawere.

Machitidwe amene amathandiza kufala kwa HIV• KugonanamosadzitetezandimunthuamenealindiHIV.• Kukhudzanakwamagazi,kuphatikizapomasinganooperekeramankhwala

mzipatala, kupatsana magazi, pangozi, malo operekera chithandizo cha kuchipatala kapena zinthu zina zokhudzana ndi magazi.

• Kuchokakwamaikupitakwamwana(nthawiyoyembekezerakapenayoberekakapenso kudzera mu mkaka wa m’mawere).

Kugonana (kutsogolo ndi kumbuyo komwe): kudzera kumaliseche akutsogolo ndi kumbuyo, HIV imatha kulowa mthupi mwamutnhu mosavuta kudzera mukakhungu kakang’ono kamene kamakhala mkati kapena kutsogolo kwa maliseche amayi kapena abambo. HIV ingathenso kulowa mthupi kudzeranso muzilonda zimene zimadza kamba kakutemeka nthawi ya kugonana (timabala totemekati nthawi zambiri sitimaoneka). Kugonana kosaziteteza kugwiritsa ntchito maliseche akutsogolo kapena kumbuyo ndi koopsa.

Kuchoka kwa mai kupita kwa mwana: nkotheka kuti mai amene ali ndi HIV

apatsire mwana wake kachiromboka asanabereke kapena nthawi yobereka, kapenanso nthawi yoyamwitsa mkaka wa m’mawere. Mkaka wa m’mawere umakhala ndi HIV, ndipo ngakhale mkaka wa mmawere supereka chiopsezo kwa akuluakulu, kwa ana ang’onoang’ono, mkakawu ndi woopsa kwambiri.

Madzi a mthupi awa sangafalitse HIV:• Malovu• Misonzi• Thukuta• Chimbudzi• Mkodzo

> 17 Banja la chisangalalo

2. Chimpwirikiti cha chiwerewere

Liu loti kangaude wa zibwenzi limatanthauza mchitidwe wokhala ndi zibwenzi zambiri zogona nazo nthawi imodzi. Izi zimachitika pamene munthu uli ndi mkazi kapena mwamuna wako, koma ndikukhalanso ndi akazi kapena amuna ena omwe umagonana nawo. Kukhala ndi zibwenzi zingapo zolumikizana munjira imeneyi kumapanga kangaude wa zibwenzi kapena chimpwirikiti chachiwerewere. Chotero kukhala ndi akazi kapena amuna ambiri ogonana nawo kumamupanga minthu kukhala nawo mu chimpwirikiti kapena kangaude wa chiwerewereyu. Omwe ali mu chimpwirikiti cha chiwerewerewa angathe kudziwa munthu mmodzi kapena awiri okha omwe amagonana nawo, osadziwa kuti aliponso ena ambiri. Ngati munthu akugonana ndi munthu mmodzi- mkazi kapena mwamuna wake yekha-koma mzako wa bnajayo ali ndi mabwenzi ena ogonana nawo, ndiye kuti inunso muli nawo mu wa kangaude wa zibwenziyu ngakhale atakhala kuti akudziwa kapena ayi.

Kangaude wa zibwenzi akuthandiza kwambiri pa kufala kwa matenda opatsirana pogonana, makamaka HIV muno mu Africa.Kangaude wa zibwenzi kapena chimpwirikiti cha chiwerewere chingakulitse mliri wa edzi, kuchuluka kwa anthu omwe angamatenge HIV pa nthawi imodzi, komanso kupezeka kwa HIV pakati pa anthu. Munthu mmodzi akhonza kupatsila HIV anthu ambiri kudzera mu kangaude wa zibwenziyu, omwenso angapatsile anthu ena ambiri, amenenso angakapatsile anthu enanso ambiri, zomwe zimapangitsa kuti HIV ifale kwambiri mu kanthawi kochepa.. HIV imafala kwambiri kuchokera kwa munthu wina kupita kwa wina miyezi yoyambirila yomwe munthu watenga HIV, koma iwo amakhala asakudziwa kuti atenga HIV kotero saganiza zogwiritsa ntchito njira zozitetezera kuti ateteze okondedwa wawo.

> Banja la chisangalalo 18

3. Kukhala m’banja lomwe m’modzi ali ndi HIV

Ndi zotheka kukhala mbanja momwe wina ali ndi HIV wina alibe. I zi zimatanthauza kuti wina ali ndi HIV mthupi mwake pamene wina alibe. Kugonana kopanda kugwiritsa ntchito njira yodzitetezera ndi njira yoyamba imene imafalitsa HIV. Kufala kwa HIV kumachitika mosiyanasiyana. Choncho, nkotheka kwambiri kwa anthu amene akhala pa banja nthawi yayitali kukhala ndi zotsatira zosiyana za momwe mthupi mwao muliri. Izi ziri chonchi chifukwa chakuti HIV simafala nthawi zonse pamene munthu amene ali ndi HIV wagonana ndi munthu amene alibe. Monga momwe zimakhalira ukakhalapafupi ndimunthu amene ali ndi chimfine, ungathekutenga chimfinechokapena ayi.

Zimene zingapangitse munthu kutenga HIV ndi:Kuchuluka kwa HIV mthupi mwamunthu amene ali ndi HIV• Munthu angathe kupatsira mnzake HIV masiku ake oyambilira atangokatenga

kumene ndipo thupi lisanazindikire kuti mthupi muli HIV. HIV imatengerapo mwai wodzichulukitsa, ndipo pakutha tsiku limodzi imatha kuswana ndi kukwana ma miliyoni a tizirombo tina. Tizirombo tikachuluka, mpata wopatsira ena umakhalanso wochuluka. Anthu angathe kupatsirana HIV ngakhale isanayambe kupezeka mmagazi mwawo akayezedwa. Izi zikufotoka chifukwa HIV ikufala mwachangu.

• Pafupifupi theka la anthu amene akutenga HIV, amatenga kuchokera kwa anthu amene angotenga kumene HIV ndipo ali m’masiku oyambilira, Lipoti la UN-AIDS likunena kuti 75 mwa anthu 100 amene akutenga kachiromboka amakhala pa ubwenzi wokhazikika kapena maanja. Choncho, pamene m’modzi azembera mnzake ndi kukatenga HIV, adzatha kupatsira mnzakeyo masiku oyambilira mosavuta.

• Patapita miyezi itatu, thupi limazindikira kuti mwalowa kachirombo (HIV) ndipo limatulutsa asilikali kuti amenyane nako. Izi zimachepetsa chiwerengero cha HIV koma siyimatheratu. Chitetezo cha mthupi mwa munthu chikakhala cha mphamvu chonchi, mwai wopatsira ena kachiromboka umakhalanso wochepa.

• Ngati munthu yemwe ali ndi HIV koma ali ndi asilikali okwanira mthupi mwake, akakwatira munthu yemwe alibe HIV, mwai wotenga HIV kwa munthu yemwe alibeyo umakhala ochepa.

> 19 Banja la chisangalalo

Kugwiritsa Ntchito ma ARV • Patatha nthawi, HIV imagonjetsa chitetezo cha mthupi ndipo zimapangitsa kuti HIV ichulukane kwambiri. Izi zikachitika, thupi limafuna kuthandizidwa kuti limenyane ndi HIVyo , kotero kuti imafuna munthuyo kuti ayambe kumwa makhwala owonjezera chitetezo. Mankhwalawa amathandiza kuchepetsa HIV mthupi zomwe zimapangitsanso kuti mwayi wakuti munthuyo afalitseHIV kuti ifale, ukhale ochepa. Kumwa mkhwala otalikitsa moyowa kumathandiza kuchepetsa kufala kwa HIV. Pakutero, kusiyana kwa zotsatira za kuyezetsa HIV kwa anthu awiri omwe ali mbanja akayezedwa kungakhalepo pamene m’modzi amene ali ndi HIV ayamba kumwa ma ARV mokhulupilika. Izi sizikutanthauza kuti munthu amene ali pa ma ARV sanga patsile HIV mbale wake koma kuti amakhala ndi mwayi ochepa opatsira mnzake HIV.• Choyenera kudziwa ndi chakuti, mwamuna ndi mkazi omwe ali pa banja sangakhale osiyana zotsatila za magazi awo mpaka kalekale. Ngati akugonana mosadziteteza winayo amakhalabe pa chiopsezo chotenga HIV. Ichi ndi chifukwa chake kuli kofunika kugonana moziteteza ndi kugwiritsa ntchito makondomu ngati mmodzi wa inu ali ndi HIV wina alibe.

Nkhani ya Kusakhulupirika• Munthu m’modzi mbanja kupezeka HIV sikukutanthauza kuti wina wachita kusakhulupirika ayi. Monga momwe tafotokozera pa mwambapa, munthu yemwe ali ndi HIV angathe kukhala kuti anatenga HIV kudzera mu njira zina osati kusakhulupilika. Kapenanso munthuyo akhonza kukhala kuti anatenga HIV mmene amalowa mbanja koma samadziwa kuti ali ndi HIV.Anthu amene amakondana angathe kukhala mbanja bwinobwino ngakhale wina ali ndi HIV.• Choncho, nkofunika kupita kukayezetsa musanalowe m’banja ndi kukatsimikizirana patapita miyezi itatu kuti mudziwe momwe mthupi mwa aliyense muliri musanalowe m’banja. Izi zidzathandiza kupanga ziganizo zabwino za moyo wawo pamene ali m’banja. Mwamuna ndi mkazi ayeneranso kudziwa kuti m’banja, awiriwo sangatenge HIV nthawi yofanana. Choncho, momwe muliri mthupi mwa mnzanuyo sizikutanthauza kuti mwanunso muli choncho. Chotero ndikofunika kuti nonse mukayezetse. Kuyezetsa HIV ndikofunikabe ngakhale mutakhala limodzi nthawi yayitali.

Moyo wakugonana pamene wina ali ndi HIV wina alibe• Banjali, monga maanja ena onse amakhala ndi zilakolako za kugonana zofunika

kuzikwaniritsa. Ali ndi ufulu wokhala ndi moyo wogonana wokwanitsidwa. Komabe, ayenera kusamala kuti amene alibe HIV asayitenge.

• Nkofunikakudziwakutianthuawiriomwem’modzialindiHIVsangadzakhalechoncho mpaka kalekale. Malingana ngati mwamuna ndi mkazi akugonana mosadziteteza winayo akhonza kudzatenga HIV.

• Chofunikakwambiripabanjalindichakutiayenerakudzitetezapogwiritsantchitomakondomu nthawi zonse pogonana.

• Banjali liyenerakumafunsauphunguwachipatalapamoyowawowakugonanandi momwe angakhalire limodzi mopanda kupatsirana HIV.

• MunthuyemwealindiHIVangathensokutengaHIVyamtunduwinawosiyanandi yomwe ali nayo kale ngati akugonana mosaziteteza ndi anthu ena omwe alinso ndi HIV. HIV ya mtundu winayo ikhonza kukana kumva makhwala omwe munthuyo akumwa. Izi zikutanthauza kuti kuchuluka kwa HIV yatsopanoyi kungathe kuchuluka mwamsanga mthupi la munthuyo. Chotero ngati angakhalire limodzi ndi okondedwa wawo yemwe alibe HIV amakhala ndi mwayi wawukulu

> Banja la chisangalalo 20

womupatsila mosavuta.• Nkofunika kuti onse awiri akambirane momasuka udindo wawo wotetezana,

koma awonetsetse kuti aliyense akukhutitsidwa ndi kugonana m’banjamo.• Onse awiri akhale okhulupirika kwawina ndimnzake ndipo apewe kugonana

mosateteza.• Makhalidwe ena monga kumwa mowa mwauchidakwa ndi mankhwala ena

osokoneza maganizidwe apewedwe poopa kugwa m’mayesero ogonana mosatetezana ndi wokondedwa wanu.

Kubereka AnaMkazi angathe kutenga pathupi ngati awiri omwe mmodzi ali ndi HIV wina alibe agonana mosadziteteza. Ngati banjali likufuna kukhala ndi mwana akapeze uphungu kuchipatala ndi cholinga choti apewe kupatsira mwanayo HIV ndi kuti mayi oyembekezera ngati ali ndi HIV akhale moyo wathanzi.

Mavuto a m’banja limene m’modzi ali ndi HIV wina AlibeZotsatira zakuti wina ali ndi HIV ndipo wina alibe, ndi zovuta kuzivomera. Nkovutanso kwa wachipatala kufotokoza, koma zimachitika kawirikawiri. Nkofunika kumvetsa bwino kuti izi zikutanthauza chani, ndipo mwamuna ndi mkazi angapange bwanji atapezeka ndi zotsatila zoterezi. Zotsatira za kuyezetsa zikatero, nkofunika kwa mwamuna ndi mkazi kukhalabe limodzi ndi kupitiliza kupeza uphungu wa momwe angakhalire limodzi mosangalala popanda kupatsana HIV.

Kuvomereza ndi kumvetsa kuti m’modzi wa inu ali ndi HIV ndipo wina alibe kumathandiza mwamuna ndi mkazi ndi anthu ena kupeza njira zothandizirana mdera mwao. Maanja otere alimbikitsidwe kupewa kupatsira wina yemwe alibe HIV. Ngati apitilira kugonana mosatetezana, yemwe alibeyo amakhala pa chiopsezo chotenga HIV.

Kukhala mbanja momwe wina ali HIV wina alibe ndi nkhani yovuta kwa ena okhudzidwa komanso achibale. Iwo amakhala pa chiopsezo chosalidwa ndi kusowa chithandizo. Izi zimakhala choncho chifukwa chakuti anthu ambiri amalumikiza HIV ndi kusakhulupirika. Kutha kwa banja ndi vuto linanso limene lingabwere. Izi zimachitika kawirikawiri ngati amene wapezeka ndi HIV ali mkazi. Ndi kofunika kwambiri kuwapatsa chilimbikitso ndi chithandizo maanja oterewa kuti amvetsetse za nkhaniyi ndikuti apitilize kukhala moyo wachikondi, wokwanitsidwa ndi banja labwino .

Kuthandizana pamene wina ali ndi HIV pamene wina AlibeNkofunika kuti banjali lithandizane ndi kutetezana kuti akhale mokondwa limodzi. Ayenera kukhala olimba pakuthandiza ndipo apewe zolankhula za anthu ena monga achibale ndi anthu ena a mdera lawo omwe angabweretse vuto lakusalana.• Pameneazindikiraiziatalandirauphungundikuyezetsa,banjaliliyenerakupeza

uphungu wa momwe angakhalire mmoyo wawo wa banja. Angathe kupezanso makondomu aulere malo omwewo ayezetserawo ndi muzipatala.

• Pamene anthu oterewa aganiza kuyamba banja, chithandizo chodalirikachingapezeke ku chipatala pa njira zomwe angatsate ndi mavuto omwe angakhalepo, mmene angapewere kupatsirana komanso kupatsira mwana HIV.

> 21 Banja la chisangalalo

• Pa nkhani yakuyezetsa ndi kuyezetsanso, banjali liyenera kufunsa uphungulimodzi ku chipatala.

Chidziwitso ChofunikiraChofunika kwambiri ndi chakuti HIV ingathe kupatsidwa kwa m’modzi yemwe alibeyo nthawi ina iliyonse.Akatswiri amalangiza amene ali ndi HIV m’banjali kuti atsate ndondomeko ya mankhwala ndipo awiriwa azigwiritsa ntchito makondomu pamene akugonana ndipo akafunse uphungu wa dotolo ngati akufuna kukhala ndi mwana.

> Banja la chisangalalo 22

4. HIV ndi kutenga pathupiKubwera kwa mankhwala a HIV otalikitsa moyo, a ARV ndi kuvomereza kwa ma dotolo kuti mai amene ali ndi HIV angathe kukhala ndi pakati, ndikumusunga mwanayo mpaka kubadwa osamupatsira HIV kunabweretsa chiyembekezo kwa amayi ambiri otha kukhala pa banja labwino ndi kukhala ndi ana. Mantha opatsira HIV mwana amene sanabadwe nthawi imene ali ndi pakati, pobereka ndi poyamwitsa, amakhala akulu kwa amai ambiri. Izi zadzetsa chiyembekezo chatsopano kwa amai chokhala ndi mwana. Komabe, HIV ndi kukhala ndi pakati zili ndi ziopsezo zake. Koma ngati amai akuzindikira kuopsaku ndi kukhala pafupi ndi madotolo, palibe chifukwa chakuti HIV iwalepheretse kukhala ndi mwana.

Kufala kwa HIV kuchokera kwa mai kupita kwa mwanaKufala kwa HIV kupita kwa mwana ndi pamene mai amene ali ndi HIV apatsira mwana wake HIV. Izi zingachitike nthawi imene maiyo ali woyembekezera, yobereka kapena yoyamwitsa mwanayo mkaka wa m’mawere. Popanda mankhwala, ana 15 kapena 30 pa 100 aliwonse angathe kutenga HIVnthawi yobereka. Ana 5 kapena 20 mwa 100 aliwonse angatenge HIV kudzera mu mkaka wa m’mawere.

Mwana amatenga bwanji HIV?• Kupatsirana magazi nthawi imene mayi ali ndi pakati HIV imachoka mwa mai kupita kwa mwana pamene mwanayo akukula m’mimba

mwa mai wake.Magazi amayi yemwe ali ndi HIV amayenda yendanso mthupi la mwana wosabadwayo, kuika mwanayo pa chiopsezo chotenga HIV.

• Nthawi yobereka- mwana amakhuzana ndi madzi osiyanasiyana omwe amatuluka mthupi la mayi nthawi yobereka. Ena mwa madziwa ndi magazi amayiyo ndipo amakhala ndi HIV. Mwana wobadwayo angathe kutenga HIV mosavuta ngati mwanayu wakhalitsa mumadziwa. Nthawi imene, mayi akubereka ndipo mwana akubadwa, amakhala ndi mabala otemeka. Mwana amadulidwa mchombo ndipo ngati mchombowo sunadulidwe bwino, ungathe kukhala njira yomwe HIV ingalowere mosavuta.

• Nthawi yoyamwitsa - HIV imapita kwa mwana kudzera mu mkaka wa m’mawere. Mkaka wa m’mawere umakhala ndi tizirombo tambiri ta HIV, ndipo popanda kusamala, chiopsezo chopatsira mwanayo nthawi imene akuyamwa chimakhala chachikulu. Mwanayo amatenga HIV poyamwa kudzera m’timabowo timene timapezeka kunsonga ya mawere.

Kupewa Koyenera kwa kufala kwa HIV kuchoka kwa Mai kupita kwa Mwana (PMTCT) Pali njira zambiri zothandizila kupewa kufala kwa HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana:

• Makolo apewe kutenga HIV – Makolo akuyenera kupewa kutenga HIV pokhala okhulupilika kwa wina ndi mzake. Akuyeneranso kupita kukayezetsa kuti adziwe momwe mthupi mwawo muliri. Ngati mmodzi mbanjamo ali ndi HIV, agwiritse ntchito makondomu nthawi zonse akamagonana. Akaganiza kuti akhale ndi mwana, akafunse chithandizo kuchokera kwa a zaumoyo.

• Amayi oyembekezera apewe kutenga pathupi mosakonzekera – amai

omwe ali ndi HIV akuyenera kupatsidwa uphungu woyenera ndi chisamaliro

> 23 Banja la chisangalalo

chowayenereza kupanga ziganizo akuzindikira.

• Kupita ku sikelo ya amayi kukalandila chithandizo kuwonjezerapo kuyezetsa magazi-Amayi oyembekezera akuyenera kulandila choyenera kuchokera kuchipatala ndi kuonetsetsa kuti ayezetsa magazi awo ngati sakudziwa za momwe mthupi mwawo muliri. Ngati ali ndi HIV, achpatala angawapatse uphungu wa momwe angapewere kumupatsila mwana wawo HIV.

• Kupewa kufala kwa HIV kuchokera kwa amayi amene ali ndi HIV kupita kwa ana nthawi yomwe ali ndi pakati, yobereka ndi nthawi yoyamwitsa. Bungwe lowona za umoyo pa dziko lonse lapansi lakhazikitsa ndondomeko ya tsopano yopewera kufala kwa HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana. Amayi onse oyembekezera omwe alindi HIV adziyambilatu kumwa ma ARV posayang’ana kuchuluka kapena kuchepa kwwa chitetezero chawo cha mthupi. Ndi njira yatsopanoyi amayi ali ndi ufulu woyamwitasa anawo momwe angafunile osati kwa miyezi isanu ndi umodzi okha ngati momwe zinaliri ndi njira yoyamba.

- Nthawi yomwe mai ali ndi pakati-kugwiritsa ntchito ma ARV Amai apakati amalimbikitsidwa kutsata ndondomeko pa kamwedwe ka makhwala. Ngati mai wapakati akumwa mankhwala amene ali ndi Retrovir (AZT) amachepetsa

chiopsezo chopatsira mwana wake HIV. - Nthawi yoyamwitsa-uphungu ndi ulangizi pa kayamwitsidwe ka mwana

kwa amai amene ali ndi HIV zimaperekedwa. Kale Amai amapatsidwa mwai wosankha kuyamwitsa mwana mwakathithi kwa miyezi isanu ndi umodzi kapena kumupatsa mkaka wogula.

Mu njira ya tsopano yomwe yakhazikitsidwa, amayi omwe ali ndi HIV akulimbikitsidwa kuyamwitsa mwana momwe angafunile.

> Banja la chisangalalo 24

5. Maluso amoyo

Kupanga zisankha zabwino: Mumoyo wa tsiku ndi tsiku timapanga zisankho zosiyansiyana. Kupanga chisankho ndi ndondomeko yosonkha chomwe ukufuna kupanga poganizila zotsatila zosiyanasiyana za zisankho zina zomwe ungapange. Timangwiritsa ntchito maluso akupanga zisankho zabwino kuthana ndi mavuto posankha yankho limodzi pa mayankhoa aambiri omwe timankhala nawo. Chomwe chimakhala chovuta ndi kusankha chinthu chimodzi chomwe ubwino wake uli oposa zina zonse. (werengani zolemba zowonezera kumapeto kwa bukhuli)Ndikofunikila kwa omwe ali pa chibwenzi kupanga zisankho zawo zokhuza moyo wawo kusiyana ndi kugonjera ku zikakamizo zomwe amalandila kuchokera kwa anthu ena. Achinyamata sakuyenera kuvomera china chili chonse chomwe anthu akunena. Koma akuyenera kuchiunika kaye. Ndi kupanga chisakho chabwino.Achinyamata akuyeneranso kupanga chisankho cha abwenzi omwe okhala nawo. Abwenzi oyipa maphunzitsa khalidwe loipa.

Kuzidalira wekha: Kuzidalira wekha kukutanthauza kutha kufokotokoza za kukhosi kwako momasuka ndi mowona komanso moganizila nkhawa za anthu ena. Zikutanthauzanso kukhala chomwe iw uli, kukhal aowona ku zomwe umakhulupilira, ndikukhal aolimba mtima kuyankhula pakafunika kutero.Kupanga zinthu mozidalira kungathe kuonjezera mwayi wokhala ndi maubwenzi achilungamo, kukuthandiza kumva bwinommoyo wako, komanso kukupatsa mphamvu pazochitika zonse mmoyowako.

Kukwanitsa kuyankhula momasuka zomwe umakhulupilira kungakuthandize kukhakuchepetsa nkhawa, kugonjetsa zikakamizo za muchibwenzi kapena zochokera kunja kwa chibwenzi. Zingakuthandizenso kua kuti ndiwe munthu ofunikila, kuthandiza kuti uzipanga ziganizo zabwino komanso ndikukhala olimba mtima ndi ozidalila mu ubwenzi wanu.

Anthu ambiri amavutika kuti akhale ozidalira okha chifukwa amaganiza kutia libe ofulu oterowo, alibe maluso owathandiza kukhala ozidalira, kapena amakhala ndi mantha ozikhulupilira okha. Akhonzanso kukanika chifukwa momwe akulila komanso chikhalidwe chawo. Anthu oetrewa amagonjetsedwa mosavuta ndi zikakamizo zomwe amakumana nazo.

Kuyankhula ndi kukhala bwino ndi anthu: kukhala bwino ndi anthu ndi maluso a moyo omwe timagwiritasa ntchito nthawi zonse tikamayankhulana ndi kupanga maubwenzi ndi anthu osiyanasiya, paokha kapena ngati gulu. Kukhala bwino ndi anthuku sikungokhuza kuyankhuala bwino kokha komanso, komanso kuzidalira kwathu, komanso kutha kumvetsera ndi kumvetsetsa.

Luso lokana kapena kukambilana: kukambialana ndi chinthu chomwe timachita nthawi zonse, mwachitsanzo, timagwiritsa nthcito mu ubwenzi wathu poanga chisankho cha nthawi yokumana kapena malo omwe tingapite kukdya nkhomaliro limodzi. Kukambilana kukutanthauza kuti kukambilana ndikugwirizana chinthu chimodzi chokomera nonse. Kukambilanakungathe kukhala pakati pa nthu awiri kapena gulu. Mungathe kugwiritsa ntchito kukambilana kuti mupeze zomwe mukufuna.

Ngati mukulandila zikakamizo mu ubwenzi wanu kapena kuchokera kunja mungathe

> 25 Banja la chisangalalo

kukambilana ndi kugwiriza chimodzi.

Kukhala ndi cholinga mmoyo-masomphenya: izi zikhonza kukuthandizani kudziwa za komwe mukupita ndi zomwe mukufuna mmoyo

> Banja la chisangalalo 26