maloto anga! ! phukusi la al angizi · monga united states agency for international development...

118
MALOTO ANGA! CHISANKHO CHANGA! PHUKUSI LA ALANGIZI

Upload: others

Post on 23-Oct-2020

2 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

  • 1M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

  • 2 3M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Maloto AngaChisankho ChangaPhukusi La Alangizi Polimbikitsa Atsikana ndi Amayi Achichepere Kuphunzira ndi Kutengera Makhalidwe Owathandiza Kuteteza Miyoyo Yawo

    !

  • 4 5M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Maloto Anga! Chisankho Changa! Ndi phukusi lomwe linalembedwa ndi a Beth Mallalieu ndi a Alice Mkandawire Munthali ndi ukadaulo wochokera kwa a Triza Hara ndi Dr. Alinafe Kasiya. A Chancy Mauluka anathandiziranso mu njira zosiyanasiyana pomwe phukusili limakonzedwa.

    Phukusili linalembedwa kuchokera ku maphukusi ena osiyanasiyana omwe kafukufuku anaonetsa kuti ndiwothandiza kwambiri pakupititsa patsogolo moyo wa atsikana ndi amayi achichepere. Chomwecho tikuthokoza mabungwe omwe anakonza maphukusiwa ndikuchita kafukufuku wofuna kupeza umboni wakuthekera kwawo popeleka masomphenya kwa atsikana ndi amayi achichepere. Maphukusiwa ndi monga ‘SASA! Preventing Violence against Women’ yokonzedwa ndi Raising Voices; ‘Go Girls’ ‘Engaging Community Leaders to Provide a Safe and Supportive Environment for Adolescent Girls and Young Women: A Tool for Facilitating Dialogue’ ndi ‘African Transformation - The Way Forward: Malawi’s Facilitators Guide’ Toolkits wokonzedwa ndi Johns Hopkins Center for Communication Programs; ‘Stepping Stones’ yolembedwa ndi a Alice Welbourn, Medical Research Council; ‘Skillz Girl’ ya Concern WorldWide; ‘Health and Life Skills Curriculum’ yolembedwa ndi Population Council, ndi ena ambiri.

    Tikufunanso tithokoze mabungwe osiyanasiyana omwe anapereka nthawi ndi ukadaulo wawo pothandizira kuti phukusili likonzedwe. Mabungwewa ndi monga United States Agency for International Development (USAID), Johns Hopkins Center for Communication Programs - One Community Project, National AIDS Commission (NAC), Save the Children- ASPIRE Project, Project Concern International (PCI), Family Planning Association of Malawi (FPAM), Population Services International (PSI) Malawi ndi Banja La Mtsogolo (BLM), Otsogolera Ntchito Yolimbana ndi Matenda a EDZI Ku Machinga ndi Zomba, FHI 360, College of Medicine, Management Sciences for Health (MSH) ndi Safe Africa. Kuphatikiza apo, mabungwe komanso sukulu ndi madera awa adatilora kupanga kafukufuku wofuna kumvetsetsa bwino ziphinjo zimene atsikana ndi amayi achichepere amakumana nazo pamiyoyo yawo, komanso kuyesa ngati phukusili lili loyenera kugwiritsidwa ntchito pakati pa atsikana ndi amayi achichepere: Sukulu za sekondale za Liwonde Community ndi Likangala; sukulu za pulaimale za Nkasaulo, Mgwiriza ndi Thondwe, madera a Kawinga ndi Mdeza ku Liwonde komanso Chikapa ndi Simon ku Zomba.

    Tithokonzenso mwapadera atsikana awa omwe anadzipereka kufotokoza nkhani zawo kuti anzawo athe kutengerapo phunziro: Victoria Bamusi, Nellie Inasi, Zephania Dickson, Patuma Justin and Cresencia*.

    Zomwe zalembedwa muphukusi lino zidatheka chifukwa cha thandizo lochokera kwa anthu a America podzera ku bungwe la USAID ndi PEPFAR ndikutsikira ku ntchito ya chitukuko ya SSDI-Communication yomwe imatsogozedwa ndi a Johns Hopkins University Center for Communication Programs. Zonse zimene zalembedwa muphukusili ndimaganizo a SSDI-Communication ndipo sizikuwonetsa maganizo a USAID kapena boma la America.

    Zithunzi komanso nkhani zochokera kumadera zinatoleredwa ndi: a Vitima Ndovi komanso bungwe la Dignitas International.

    Amene akonza bukuli: FD Communications.

    Mukafuna kudziwa zambiri funsani ku:SSDI- Communication ProjectJohns Hopkins Center for Communication Programs Accord CentreP.O. Box 30782Lilongwe.Website: http://ccp.jhu.edu/

    Kuthokoza

  • 6 7M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Za MkatimuChiyambi 10

    Kugwiritsa ntchito phukusi la alangizili 12Zipangizo, zoyenera kudziwa komanso zofunikira zina. 12Nanga ngati akufuna kuti alandire malipiro? 13Dziwani za anthu omwe mukuwafikira 13Dziwani phukusi lanu lophunzitsira 14Kukula kwa gulu 14Unikirani za nthawi yofunikira 14Zigawozi ziphunzitsidwe mu ndondomeko yake 14Dongosolo la kuphunzira potengapo mbali 15Luso loyendetsa maphunziro 16Zomwe mlangizi akuyenera kukumbukira 18Kukambirana zinthu zomwe ena amati ndi zolaula/kapena zochititsa manyazi 18Kuthana ndikukhuzika 19

    Phunziro 1- Kukhazikitsa Maloto ako 22

    Gawo 1.1 – Gawo Lotsegulira 25

    Ntchito 1: Kudziwana 26Ntchito 2: Kumvesetsa Gulu 27Ntchito 3: Kukonza Malamulo a Gulu 28

    Gawo 1.2 – Kumangilira Gulu 32

    Ntchito 1: Kumangilira Gulu 34Ntchito 2: Kukhulupirirana ndi Kusungirana Zinsinsi 35

    Gawo 1.3 – Kudzidziwa Ine Mwini ndi Maloto Anga 38

    Ntchito 1: Kukonda Ine Mwini, Kukondanso Iwe 39Ntchito 2: Kukhazikitsa Masomphenya Anga 40

    Gawo 1.4 – Malo Otetezeka 43

    Ntchito 1: Kujambula Mapu (Chithunzi) Cha Dera Lathu 44Ntchito 2: Kupanga Maubwenzi 45Ntchito 3: Ondilimbikitsa Anga 46

    Phunziro 2- Thupi Lanu, Thanzi Lanu 52

    Gawo 2.1 –Kumvetsetsa Thupi Lanu 55

    Ntchito 1: Kumvetsetsa za Kutha Msinkhu kwa Atsikana 56Ntchito 2: Kumvetsetsa Kutha Msinkhu Mwa Anyamata 58

    Gawo 2.2: Msambo 63

    Ntchito 1: Dongosolo la Kusamba 64Ntchito 2: Ukhondo Panthawi ya Msambo 67

    Gawo 2.3 – Kuunika Mozama za Mimba 72

    Ntchito 1: Zoona Zake Ndi Nkhambakamwa Zokhudza Mimba 73Ntchito 2: Zotsatira Za Mimba Yosakonzekera 75

    Gawo2.4 – Kupewa Kutenga Mimba 78

    Ntchito 1: Kudziwa Njira Zosiyanasiyana Zakulera 79Ntchito 2: Komwe Mungakapeze Njira Za Kulera 86

    Gawo 2.5– Makondomu 88

    Ntchito 1: Nkhambakamwa Ndi Zoona Zenizeni Zakagwiritsidwe Ntchito Ka Makondomu 89Ntchito 2: Zifukwa Zomwe Atsikana Amagwiritsira Kapena Sagwiritsira Ntchito Makondomu 91Ntchito3: Zotsatira Za Kusagwiritsa Ntchito Makondomu 92

    Gawo 2.6 – Kagwiritsidwe Ntchito ka Kondomu 94

    Ntchito 1: Kagwiritsidwe Ntchito ka Kondomu ya Chimuna 95Ntchito 2: Kagwiritsidwe Ntchito ka Kondomu ya Chikazi 99

    Phunziro 3 –Kulumikizana ndi Anthu Ena 106

    Gawo 3.1 –Makhalidwe Okhuza Kulumikizirana Ndi EnaI 109

    Ntchito 1: Makhalidwe Olimbana, Opewa Ndi Ofuna Kupotoloza Ena 110Ntchito 2: Chiwopsezo Chokhudzana ndi Makhalidwe a Mtopola, Opewa ndi Opotoloza . 116

    Gawo 3.2 – Makhalidwe Okhuza Kulumikizirana Ndi Ena II 118

    Ntchito 1: Kudzikhulupilira 119Ntchito 2: Kuphunzira Makhalidwe Odzikhulupilira 121

    Gawo 3.3 – Kumanga Mfundo Zovuta 126

    Ntchito 1: Mfundo ndi Zotsatira Zake 127Ntchito 2: Kumanga Mfundo Polankhula ndi Okondedwa 128

    Phunziro 4: Kukhala Pakati pa Anthu, Mphamvu komanso Kusiyanitsa Pakati pa Amuna ndi Akazi. 136

    Gawo 4.1 – Kumvesetsa Mphamvu 139

    Ntchito 1: Mphamvu 140Ntchito 2: Kumva kuti tili ndi Mphamvu ndi Kumva kuti tilibiretu Mphamvu 143

    Gawo 4.2 – Zimene Anthu komanso Chikhalidwe Chimayembekezera Zokhudzana ndi Kusiyanitsa Pakati Pa Amuna ndi Akazi 145

    Ntchito 1: Kumvetsetsa Kusiyana Pazochitika Pakati Pa Akazi Ndi Amuna 146Ntchito 2: Zochitika Pakati Pa Amayi ndi Abambo Komanso Zomwe Zimayembekezeredwa 147Ntchito 3: Anachita Chinthu Chachilendo 149

    Gawo 4.3 – Maubwenzi ndi Amuna 151

    Ntchito 1: Kudziwa Maubwenzi ndi Maubale Pakati pa Amuna ndi Akazi 152Ntchito 2: Maubwenzi Ogonana omwe Atsikana Amakonda Kuchita 153Ntchito 3: Kulingalira za Maubwenzi Ochitika Pakati pa Anthu Osiyana Mibadwo 154

  • 8 9M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Gawo 4.4 – Nkhanza Yochitirana Chifukwa Wina ndi Mkazi Kapena Mwamuna 158

    Ntchito 1: Nkhanza Komanso Upandu 159Ntchito 2: Zotsatira za Nkhanza 161Ntchito 3: Tingapeze Kuti Thandizo 162

    Gawo 4.5- Maufulu Okhudza Zogonana ndi Ubeleki Wabwino 164

    Ntchito 1: Kumvetsetsa za Ufulu Wachibadwidwe 165Ntchito 2: Ufulu Pa Nkhani Zogonana Komanso Ubereki 167

    Phunziro 5 - Inu ndi HIV 176

    Gawo 5.1 - Kudziwa za HIV 179

    Ntchito 1: Nkhambakamwa ndi Zoona Zake za HIV ndi EDZI 180Ntchito 2: Kodi HIV ndi Edzi Ndichiyani? 186Ntchito 3: Masewera a Momwe HIV Imafalira 187

    Gawo 5.2 – Kuyezetsa HIV 196

    Ntchito 1: Kudziika Pachiopsezo 196Ntchito 2: Kuyezetsa HIV 198Ntchito 3: Zolimbikitsa Ndi Zoletsa Kuyezetsa Magazi 201

    Gawo 5.3 – Kubwera Poyera Ndi M’chitidwe Wosalana 203

    Ntchito 1: Kubwera Poyera Pa Zakupezeka Ndi HIV 204Ntchito 2: Kumvetsa Bwino Za M’chitidwe Wosalana 205

    Gawo 5.4 – Chilimbikitso Ndi Kukhala Moyo Uli Ndi HIV 208

    Ntchito 1: Kukhala Moyo Ndi HIV 208Ntchito 2: Kupereka Chilimbikitso Kwa Omwe Ali Ndi HIV 211

    Phunziro 6 – Tsogolo Lanu 216

    Gawo 6.1: Kuchulukitsa Zisankho 219

    Ntchito 1: Nkhani ya Ngachi 220Ntchito 2: Zisankho 222

    Gawo 6.2 –Kuchilimika pa Masomphenya 224

    Ntchito 1: Kulingalira pa Masomphenya omwe Anakhazikitsidwa 225Ntchito 2: Kulingalira Komaliza 226

  • 10 11M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Cholinga chachikulu komanso za mkati mwa chipangizo cha alangizi cha DREAMS

    ChiyambiTakulandirani alangizi nonse ku phukusi la alangizi!

    Pali ntchito zambiri zomwe zikugwiridwa muno m’Malawi zofuna kupereka kuthekera kwa atsikana ndi amayi achichepere kuti akhale olimbikitsika ndi odzidalira, kuthetsa nkhanza zochitirana chifukwa chakuti wina ndi mkazi kapena mwamuna, komanso kuchepetsa chiwophyezo chakuti atsikana ndi amayi achichepere angatenge HIV ndi mimba zosakonzekera. Ngakhale izi zili chonchi, chiwerengero cha atsikana ndi amayi achichepere omwe akutenga mimba asanakhwimwe, kusiya sukulu, kuchitiridwa nkhanza chifukwa chakuti iwowo ndi akazi komanso kukwatiwa mwachangu chikuchulukirabe.

    Cholinga cha phukusi la alangizili ndikuchepetsa zovuta pakati pa atsikana ndi amayi achichepere komanso kuthandiza atsikana ndi amayi achicheperewa kukhala otetezeka. Pofuna kukwanilitsa cholingachi, phukusi la alangizili lakonzedwa kuchokera ku mabuku ophunzitsira osiyanasiyana omwe umboni unasonyeza kuti ndi othandiza monga a Go Girls! Stepping Stones, ndi SASA. Maphunziro onse omwe alembedwa mu phukusi ili akupita kwa atsikana ndi amayi achichepere ndipo likuwapatsa upangiri, luso komanso luntha lothana ndi ziphyinjo zobwera kuchokera kwa anthu akudela kwao, makhalidwe ndi maganizo omwe amawayika pachiwophyezo choti ena awadyere masuku pamutu. Phukusi la alangizili likuwapatsa atsikana ndi amayi achichepere njira yophunzirira yosangalatsa komanso yotetezeka pomwe akuchita chotheka kuti akhale ochilimika, opirira, olimbikitsika ndi ozidalira, opanda HIV ndi EDZI, okhala ndi anthu owalimbikitsa komanso otetezeka!

    Phukusi la alangizili lili ndi maphunziro / mitu yokwana 6 ndi magawo 24. Mwachidule, zolinga za maphunzirowa zafotokozedwa pa tsamba lotsatira:

    Kuchengeta, kupereka chilim

    bikitso ndikudzutsa m’badw

    o wa atsikana ndi am

    ayi achichepere okhala ndi chiyem

    bekezo cha tsogolo la bwino, ozindikira, okhala ndi chilim

    bikitso komanso m

    pamba pa chikhalidw

    e, kulum

    ikizanitsidwa ndi thandizo la chipatala kom

    anso kukhala ndikuthekera kopeza njira zochepetsera chiwopsezo

    chilichonse pom

    we akukula kuchokera ku uchichepere ndikukhala m

    unthu wam

    kulu.

    Atsikana ndi am

    ayi achichepere apeza luso losiyanasiyana,

    upangiri, ndikuthekera kokhala m

    oyo wa phindu, opanda H

    IV

    Atsikana ndi am

    ayi achichepere alum

    ikizana ndi anthu komanso

    m

    agulu osiyanasiyana owapatsa

    chilimbikitso ndi kuzindikira m

    alo

    omw

    e ali otetezeka m’m

    adera aw

    o

    Kulim

    bikitsa atsikana ndi am

    ayi achichepere kulankhula m

    aganizo awo ndikuzindikira

    udindo waw

    o m’m

    adera omw

    e akukhala

    Alum

    ikizanitsidwa kom

    anso

    alimbikitsika kupeza thandizo

    lofunikira la za um

    oyo ndi thandizo lina lopezeka kudera

    Kum

    anga Maloto anu

    Thupi Lanu, Thanzi lanu

    Kulum

    ikizana ndi EnaM

    phamvu ndi K

    usiyana pa zochita pakati pa

    amuna ndi akazi

    HIV

    ndi InuTsogolo lanu

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    utsendera

    malo

    to aw

    o

    •K

    umvetsetsa za

    kufunika koyamb

    a kuchita zinthu zing

    ’ong

    ’ono

    p

    ofuna

    kukwaniritsa

    malo

    to a akulu

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    umvetsetsa

    za HIV

    ndi E

    dzi

    kom

    anso m

    om

    we

    angad

    zitetezere ku H

    IV•

    Aw

    unikire za kuipa

    kom

    anso ub

    wino

    oyezetsa H

    IV•

    Kum

    vetsetsa d

    ong

    oso

    lo

    loyezetsa HIV

    nd

    ikudziw

    a kom

    we

    angakayezetse H

    IV•

    Kum

    vetsetsa zovuta zo

    bw

    era kaamb

    a ka kusalana nd

    i mm

    ene ang

    athanirane nazo

    •K

    uphunzira m

    ’mene

    angab

    werere

    poyera ng

    ati ap

    ezeka ndi H

    IV

    kom

    anso m

    mene

    angathand

    izire ena o

    mw

    e ab

    wera p

    oyera pa

    zakupezeka kw

    awo

    nd

    i HIV

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    uwunikira

    mm

    ene mp

    hamvu

    zimag

    wiritsid

    wira

    ntchito m

    maub

    wenzi

    ndi m

    ’maub

    ale •

    Kuw

    unikira zom

    we

    chikhalidw

    e chim

    ayemb

    ekezera kw

    a atsikana ndi

    amayi, anyam

    ata ndi

    abam

    bo

    ndi m

    om

    we

    izi zimap

    angitsira

    kuti pakhale

    kusiyana mp

    hamvu

    •K

    udziw

    a zipsinjo

    zo

    mw

    e atsikana am

    akumana nazo

    chifukw

    a cha chikhalid

    we nd

    i m

    mene anthu

    amakhalira.

    •K

    umvetsetsa za

    nkhanza zochitirana

    chifukwa w

    ina nd

    i mkazi kap

    ena m

    wam

    una ndi

    kudziw

    a chochita

    po

    mw

    e achitiridw

    a nkhanza

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    umvetsetsa

    makhalid

    we

    osiyanasiyana

    okhud

    zana ndi

    kulumikizana nd

    i anthu

    •K

    ukhala ndi

    kuthekera ko

    lumikizana

    ndi anthu ena

    mo

    dzid

    alira•

    Kup

    hunzira nd

    i kuyeserera kup

    anga nd

    i kum

    anga m

    fundo

    zo

    khwim

    a

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    umvetsetsa za

    do

    ngo

    solo

    la kutha nsinkhu nd

    i m

    mene m

    atupi aw

    o

    amasinthira

    •K

    udziw

    a za kulum

    ikizana kwa

    kutha nsinkhu ndi

    kutenga p

    akati•

    Kuling

    alira za kukhala nd

    i mw

    ana ko

    manso

    udind

    o

    om

    we um

    abw

    era pa

    munthu akakhala nd

    i m

    wana

    •K

    umvetsetsa za

    zovuta zom

    we

    zimab

    wera chifukw

    a cha m

    imb

    a zo

    sakonzekera

    •K

    uphunzira za njira

    zolerera nd

    i kom

    we

    angakap

    eze njirazo•

    Kup

    hunzira kug

    wiritsa ntchito

    m

    akond

    om

    u

    Phunziro

    li lithandiza

    atengam

    bali:

    •K

    udziw

    a zamb

    iri za m

    aphunzirow

    a•

    Kum

    vana nd

    i kuyamb

    a kukhulup

    irirana ndi

    atengam

    bali ena

    •K

    udzim

    vetsetsa o

    kha kom

    anso

    zinthu zom

    we

    zimaw

    apang

    itsa kukhala ap

    aderad

    era•

    Kud

    ziwa m

    bali

    zom

    we am

    achita b

    wino

    kom

    anso

    zofo

    oka zaw

    o

    ndi m

    mene

    angathanirane nazo

    •K

    ukhazikitsa ko

    manso

    kuyika nd

    ond

    om

    eko

    za mo

    mw

    e ang

    akwaniritsire

    malo

    to aw

    o

    •A

    dziw

    e anthu o

    mw

    e angaw

    apatse

    chilimb

    ikitso

    kom

    anso za m

    alo

    otetezeka

  • 12 13M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Kugwiritsa ntchito phukusi la alangizili

    Zigawo zonse mu phukusi la alangizili zikupereka tsatanetsatane wa m’mene mlangizi angagawanirane ndi atengambali pa mitu yosiyanasiyana ya maphunzirowa. Kuti kugawana ndi atengambali pa mituyi kukhale kosavuta, mlangizi akuyenera kukonzekera bwino ndi kumvetsetsa zomwe mutu ulionse ukunena nthawi yamaphunziro isanafike. Pamathero pa gawo lililonse pali ka bokosi koti mlangizi alembe ndemanga kuti awunikire kuti gawo layenda bwanji ndipo ndi ziti zikuyenera kukonzedwa kuti gawo lotsatira lizayende bwino.

    Chigawo chilichonse chili ndi m’ndandanda wotere:• Mutu wachigawo• Nthawi yomwe ikufunikira• Zolinga za gawo• Zipangizo komanso kukonzekera komwe kukufunikira mu chigawocho• Ntchito yotsegulira- yomwe imakhala ngati kadzutsa• Kukumbutsira chigawo- kukumbutsa anthu zomwe zinachitika mu chigawo

    chambuyo• Kudziwitsana za zolinga za gawo - kuthandizira atengambali kumvetsetsa

    zomwe zichitike mu ndime yatsopanoyi• Ntchito yoperekedwa ndi malangizo atsatanetsatane (kawirikawiri pali ntchito

    ziwiri pa chigawo chilichonse komanso pali zigawo zina zomwe zili ndi ntchito zitatu)

    • Kuwunikira gawo – izi zimachitika kuti gawo limveke bwino• Ntchito yotsekera- imachitika kumathero a gawo kuti gawo lithe lidakakoma• Zigawo zonse zilinso ndi:

    o Kabokosi ka zomwe mlangizi akuyenera kudziwao Kabokosi ka malangizo kwa mlangizio Zomwe atengambali akuyenera kudziwa pakutha pa chigawoo Ntchito yoti atengambali atengere kunyumbao Mchangamutsoo Bokosi loti mlangizi alembemo ndemanga

    Zipangizo komanso kukonzekera

    Zipangizo zosiyanasiyana zatchulidwa mu phukusi la alangizili zomwe ndi zothandizira atengambali kuphunzira mitu yosiyanasiyana. Izi zithandizira kuti kuphunzira kukhale kosavuta komanso kosangalatsa kwa atengambali. Zina mwa zipangizozo ndi monga:• Zolembera zowala ndi mapepala akuluakulu (fulipi tchati) omwe afunikire mu

    ma gawo ambiri. • Mabuku a chinsinsi kapena polembapo pena kuti atengambali azitha kulemba

    maganizo awo pa zomwe akuphunzira.• Makondomu amayi komanso abambo ndi zosema zothandizira kuphunsitsira

    kavalidwe ka kondomu.

    • Zowerengawerenga zomwe muzifune pa magawo ena. Konzekeranitu ndikupeza zowerengawerengazi nthawi ya chigawo chomwe zinthuzi zikuyenera kugawidwa isanafike. Ngati zinthuzo ndi zosakwanira kuti aliyense alandire chake chake, pezani zokwanira kuti atengambali angapo athe kugawana chimodzi.

    • Musanayambe chigawo chilichonse, ndibwino kuti mupezeretu zowerenga zina ndi zina zowonjezera kuti mudziwe zambiri ndikuonjezera ukadaulo wanu pa gawo lomwe mukukaphunzitsa. Mitu ina imene inu mukuyenera kuyidziwa ndikuyimvetsa bwino ndi monga: a. Njira zakulerab. Kuyezetsa HIV komanso uphungu wokhuza HIV

    • Mukuyenera kukonza ndondomeko yokhudza alendo apadera omwe apemphedwa kudzalankhula kwa atsikana ndi amayi achicheperewa m’zigawo zosiyanasiyana kuti zonse ziyende bwino.

    • Musanayambe chigawo chilichonse, onetsetsani kuti mukudziwa bwino lomwe malo osiyanasiyana omwe mungatumizeko atsikana ndi amayi achichepere ngati angafune chithandizo chowonjezera.

    Nanga ngati akufuna kuti alandire malipiro?

    Pomemeza anthu kuti atenge nawo mbali pa maphunzirowa, mukuyenera kuwafotokozera mwatchutchutchu kuti atengambali onse salandira ndalama iliyonse pokhala nawo pa maphunzirowa. M’gawo loyamba la maphunzirowa, mlangizi akumbutse atengambali onse kuti ndondomekoyi ndi ya anthu ongozipereka ndipo salandira ndalama iliyonse. Komabe, anthu apindula m’njira zina zosakhuzana ndi ndalama monga kuphunzira luso komanso kupeza nzeru zowathandizira kuchepesa chiwopsezo chotenga HIV.

    Dziwani za anthu omwe mukuwafikira

    Phukusili lakonzedwa ndi cholinga chofikira atsikana komaso amayi achichepere a zaka za pakati pa 10 mpaka 24. M’mene phukusi la alangizili limakonzedwa, zokambirana zakuya zinachitika ndi magulu asanu ndi atatu a atsikana ndi amayi achichepere a m’maboma a Zomba ndi Machinga pofuna kumvetsetsa moyo wa atsikanawa ndi mavuto omwe amakumana nawo. Zokambiranazi zinaonetsa kuti atsikana amatenga nawo mbali pa zinthu zosiyanasiyana mosiyanasiyananso. Izi zili choncho chifukwa chakusiyana:• Muzaka zakubadwa• Munkukhwima kwawo m’maganizo• Mukuzindikira kwawo (monga apasukulu kuyerekeza ndi omwe sali pasukulu)

    Choncho, alangizi akuyenera kuphunzitsa gulu lililonse kutengera ndi m’mene atengambali aliri. Mwachitsanzo, atsikana kapena amayi achichepere omwe sali pasukulu atha kuvutikira kulemba kuyerekeza ndi omwe ali pasukulu komanso

    C H I Y A M B I

  • 14 15M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    atsikana okulirapo atha kukhala patsogolo pa maphunziro ena kuyerekeza ndi atsikana achichepere pa gulu lomwelo.

    Ndikoyenera kugwiritsa ntchito zithunzi ndi zizindikiro zosiyanasiyana polemba pa mapepala ndi kugwiritsa ntchito chilankhulo chosavuta kwa atsikana omwe sadziwa kulemba ndi kuwerenga. Onetsetsani kuti malangizo amveka bwino lomwe musanayambe ntchito iliyonse.

    Dziwani phukusi lanu lophunzitsira

    Konzekerani!

    Werengani ndi kumvetsetsa mitu yosiyanasiyana ya mu phukusi la mlangizili.Kumbukirani kuti ili sibuku la malamulo, ndi buku longothandizira kuwunikira chabe.

    Konzekerani kukumana ndi zovuta.

    Maphunziro aliwonse ali ndikuthekera kobweretsa zovuta zosiyanasiyana. Njira ya bwino yopewela zovuta zosiyanasiyana ndi kukonzekera mokwanira.

    Dziwani zomwe mukukaphunzitsa ndipo yeserani kuwongolera ndi kuphunzitsa magawo osiyanasiyana ndi anzanu kapena mlangizi mnzanu.

    Kukula kwa gulu

    Kukula kwa gulu kukuyenera kukhala pakati pa atsikana 15 ndi 20.

    Ndi gulu laling’ono, aliyense atha kukhala ndi mwayi wopereka maganizo ndi kutenga nawo mbali mokwanira mu ntchito komanso zochitika zosiyanasiyana.

    Komanso ngati gulu liri laling’ono sipakhala povuta kuwonetsetsa kuti mayankho onse ayankhidwa ndipo aliyense wamvetsetsa zinthu.

    Unikirani za nthawi yofunikira

    Chigawo chilichonse mu phukusi la alangizili chakonzedwa kuti ndi cha ola limodzi ndi theka, koma magawo ena atha kutenga nthawi yocheperapo kapena yayitaliko kutengera ndi mmene mlangizi akuchitira komanso mmene zokambirana zikuyendera.

    Zigawozi zinakonzedwa kuti zitenge nthawi yayitali chomwechi ndipo zonse zikayenda bwino chigawo chilichonse chikuyenera kuphunzitsidwa pakamodzi.

    Zigawozi ziphunzitsidwe mu ndondomeko yake

    Zigawozi zakonzedwa kuti zizithandizirana kuti chigawo chilichonse

    chiziwonjezera pa zomwe zaphunzitsidwa mu chigawo cha m’mbuyo. Ndiye ndi bwino kuti muphunzitse zigawozi mu ndandanda womwe zayikidwira.

    Dongosolo la kuphunzira potengapo mbali

    Phukusi la alangizili likugwiritsa ntchito dongosolo la kuphunzira potengapo mbali ngati njira yophunzirira ya atengambali.

    Njira zimenezi zimalimbikitsa kuti kuphunzira kuzichitika polola ophunzira kutenga nawo mbali pa china chilichonse chochitika mu gawo lililonse la maphunziro.

    Komanso imapititsa patsogolo kutengapo mbali kwa atengambali pa zinthu komanso zochitika zina zomwe zingawongolere moyo wawo. Zimathandizira kumasula maganizo a atengambali pa zomwe zikuwavuta ndi zoyambitsa zovutazo komanso njirazi zimawathandizira kuti akhale ndi kuthekera kothana ndi zovutazo.

    Mu dongosolo la kuphunzira potengapo mbali, atengambali amathandizira kuti kuphunzitsa ndi kuphunzira kuchitike bwino mmalo mongolandira chiphunzitso kuchokera kwa alangizi. Njirayi imathandizira atengambali kugawana nzeru, kuphunzitsana komanso kuchitira zinthu pamodzi.

    Dongosolo la kuphunzira potengapo mbali limawapatsa anthu ndondomeko ya luso losiyanasiyana lomwe atha kuligwiritsa ntchito mu nyengo zina zomwe amakumana nazo m’moyo ndipo zimawalimbikitsa kuchitapo kanthu kothana ndimavutowa.

    Pogwiritsa ntchito njirazi atengambali akuyembekezereka:• Kutenga mbali mukuphunzira kwawo ndikukhala ndikuthekera kwakukulu

    kokumbukira komanso kugawana ndi ena zachilendo zomwe aphunzira.• Kutenga udindo womvetsetsa zomwe akuphunzira.• Kusunga zomwe aphunzira ndikupitiriza kumvetsetsa zinthu.• Kuphunzira m’mene angakhalire ndi anthu ena pamene akuphunzira pamodzi

    ndi anzawo. • Kukulitsa luso la kaganizidwe kakuya, kukulitsa maluso a moyo, kukhala anthu

    otha kulingalira ndi kuunguza zomwe aphunzira, otha kuchita zinthu pagulu, odziwa kuyendetsa bwino moyo wawo, otha kufufuza zinthu pawokha, komanso atengambali odziwa chomwe akuchita.

    • Kukulitsa luso lawo lolumikizana ndi anthu ena, kusintha khalidwe komanso kutha kulankhulapo maganizo awo m’maubwenzi omwe ali nawo mwabwino komanso motetezeka.

    • Kukulitsa kulimba mtima kwawo pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolumikizirana ndi anthu kuti akhale ndikuthekera kochepetseratu chiwophyezo chowadyera masuku pamutu.

    • Kukhala ndi mtima wofuna kuchita bwino m’moyo wawo komanso kupeza njira zosiyanasiyana zotukulira miyoyo yawo.

    C H I Y A M B I

  • 16 17M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Zitsanzo za dongosolo la kuphunzira potengapo mbali zomwe zagwiritsidwa ntchito mu chipangizo cha alangizi ichi ndi monga:• Ntchito ya pagulu - Apa ndipomwe atengambali akuyenera kuchita zinthu

    onse ngati gulu kapena ayikidwa m’magulu ang’onong’ono a anthu atatu, anayi kapena asanu. Nthawi zina atengambali azichita zinthu awiri awiri. Mlangizi akuyembekezeka kumayendera magulu onse kuthandizira pomwe akuyenera kutero.

    • Kusonkhanitsa maganizo - Iyi ndi ndondomeko yosonkhanitsira maganizo kuchokera ku gulu lonse pa mutu omwe gulu likukambirana kapena pa nkhani ina iliyonse yopatsa chidwi. Atengambali onse akuyenera kupereka maganizo omwe awabwerera. Maganizo onse amalembedwa bwino lomwe ndipo palibe ganizo lomwe limatsutsidwa. Maganizo onse akalembedwa ndi pomwe atengambali onse amaloledwa kuwunikira, kukambirana, komanso kukonza maganizo aliwonse omwe aperekedwa ndikuthandizira kuti amveke bwino.

    • Nkhani zopatsa phunziro - Izi ndi nkhani zongopeka kapena nkhani zenizeni zomwe zinachitikira anthu ena zomwe zimaperedwa kwa atengambali kuti aphunzirepo zina ndi zina.

    • Nyimbo komanso masewera ophunzirira - Izi zagwiritsidwa ntchito kuthandizira kuti maphunziro amveke bwino. Alangizi alimbikitse atengambali kuyambitsa nyimbo ndi masewerawa. Izi zidzathandiza atengambali kuchotsa manyazi ndi mantha komanso kukhala ndi luso loyambitsa zochitika pagulu.

    • Zosemasema - Apa ndi pomwe atengambali amapanga chosema chomwe akufuna pogwiritsa ntchito thupi la munthu wina. Pochita izi, anthu osemawo sakuyenera kulankhula kapena kugwiritsa ntchito mawu ena aliwonse koma kungomupinda munthuyo moyenera kuti asonyeze uthenga omwe akufuna kupereka. Mwachitsanzo, kuti awonetse chithunzi cha munthu akuvina, osemawo akuyenera kupinda ndikutembenuza munthu amene akusemedwayo kuti awoneke ngati akuvina; mwachitsanzo mutha kugwiritsa ntchito manja, mikono, mutu ndi tunthu lonse la thupi kuti liwonetse chithunzi cha munthu akuvina.

    • Timasewero - Atenga mbali akuyembekezereka kutenga mbali zosiyanasiyana zamusewero ndi kuchita zoyenera molingana ndi gawo lomwe akutenga mu kaseweroko. Pokonza sewerolo, atengambali akulimbikitsidwa kuyankha mafunso a “ndi…” asanu otsatirawa kuti apeke sewero lawo:o Ndi chiyani - chomwe chikuchitika mukaseweroka?o Ndikuti - komwe zikuchitikira?o Ndi nthawi yanji – izi zikuchitika?o Ndi chifukwa chiyani - izi zikuchitika?o Ndi ndani – izi zikumukhuza?

    Luso loyendetsa maphunziro

    Kuyendetsa kapena kutsogolera maphunziro ndi luso! Lusoli limathandizira kumaphunziro komanso kutukula anthu kudzera m’njira ndi magawo osiyanasiyana.

    Lusoli limathandizira gulu la anthu kukambirana zinthu, kuzindikira ndikukwaniritsa

    zolinga zosiyanasiyana komanso kumalizitsa ntchito zosiyanasiyana aliyense wa pa gulu atatengapo mbali komaso atakhutira ndi zotsatirazo.

    Luso loyendetsa maphunziro limasiyana kwambiri ndi uphunzitsi wanthawi zonse. Luso loyendetsa maphunziro ndi njira yopereka utsogoleri popanda kuzikundikira mphamvu zonse. Mlangizi amatambasula zomwe sizikumveka, kulondoloza maganizo osiyanasiyana, komanso kuyesayesa kubweretsa kumvetsetsana. Pali ma luso osiyanasiyana omwe mlangizi wabwino amayenera kukhala nawo monga:• Amawawona atengambali ngati akadaulo omwe ali ndi chidziwitso komanso

    luso loti agawane ndi ena, mmalo modzitenga iwo wokha ngati kadaulo yekhayo pamalopo.

    • Kulimbikitsa atengambali kuphunzira kuchokera kwa atengambali ena ndipo amadzitenga kuti ndi ongowongolera zochitikazo osati kuwatenga atengambali ngati zibekete zopanda kathu zomwe zabwera kuti zizadzadze ndi nzeru zochokera kwa mlangizi.

    • Amakhulupirira kuti anthu amaphunzira kudzera mukuchita zinthu, kudutsa mu zinthu zosiyanasiyana, kuyesera ndi kumva zinthu, osati kuloweza, kubwerezabwereza, kapena kukopera chiphunzitso pogwiritsa zipangizo zosiyanasiyana.

    • Amakhala ndi chilichonse m’chimake koma amatha kusintha njira zochitira zinthu molingana ndi zosowa za atengambali.

    • Amakhala ndi chidwi ndi mutu womwe akuphunzitsa komanso ndi atengambali.• Amasunga mapangano awo ndi gulu-kulola atengambali kulankhula, kupita

    kopumulira ndi zina.• Ndi wodekha ndipo amamvetsera.• Atha kuthana ndi mmene anthu amakhudzikira munjira zosiyanasiyana monga

    mkwiyo, chisoni, chikondwerero ndi madandaulo.• Ndi munthu wosangalala.• Sakalipira atengambali.• Amamvetsera ndikuwonetsetsa zinthu.• Chilichonse cha iye chimakhala m’malo ndipo amakonzekera mokwanira.• Ndi omasuka, ofikirika ndipo ndiwodekha.• Amalimbikitsa atengambali onse kutenga mbali pazochitika.• Amalandira maganizo ndi malingaliro a atengambali onse mwansangala.• Nthawi ndi nthawi amabwereza komanso kutsendera mfundo zofunikira.• Amafunsa mafunso kuti atengambali afotokozere zomwe alankhula.• Amawonjezera pa maganizo komanso luntha lomwe atengambali agawana

    ndi gulu.• Amakhala tcheru ndi momwe atengambali akutsatirira zinthu komanso mlingo

    wa mphamvu zawo ndikusintha zochitika kuti zigwirizane ndi izi.• Amatha kusintha kachitidwe ndi kaganizidwe kake ngati ndikoyenera kutero.• Saweruza ena.• Satayana ndi zolinga za maphunziro ndipo chilichonse chomwe amachita

    chimakhala chothandizira kukwaniritsa zolingazo.

    C H I Y A M B I

  • 18 19M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Zomwe mlangizi akuyenera kukumbukira

    • Werengani phukusi la mlangizi lonseli maphunziro asanayambe.• Mumvetsetse zigawo zonse maphunziro achigawo chilichonse asanayambe

    ndipo sonkhanitsani zida zonse. • Sinthani ntchito komanso zochitika za muchigawo kuti zigwirizane ndi

    msinkhu komanso maphunziro a atengambali omwe ali pa gululo.• Ganizirani ndi kukonzekera zovuta zomwe zingabwere mu zigawo zonse

    zomwe zikuwoneka kuti ndi “zovuta”.• Khalani ndi malo kapena buku lolembapo zinthu zomwe zatuluka mu

    chigawocho, koma sizikugwirizana ndi zolinga za chigawocho. Muyenera kubwerera ku zinthu zimenezi panthawi yowunikira zomwe zachitika mu chigawocho kapena mungofotokoza pamapeto pa chigawocho kuti zinthuzo ndi zofunikira koma sizimagwirizana ndi maphunzirowo.

    • Malizani ndime mokoma, ndipo atengambali achoke ndi uthenga wachindunji wa chomwe akuyenera kuchita. Ngati kuli kotheka unikirani za zomwe zikubwera kutsogolo komanso njira zomwe atengambali akuyenera kutsatira pothana ndi vuto lomwe lilipo.

    • Onetsetsani kuti inu simukulankhula kwambiri kuposa atengambali. Mukawona kuti inu ndi amene mukulankhula kwambiri kuposa atengambali, alimbikitseni atengambali kuyankha mafunso omwe atengambali ena akufunsa.Mwachitsanzo, ngati wina wafunsa funso, lolani atengambali akambirane powafunsa kuti, “alipo ali ndi yankho ku funsoli?”

    • Zomwe mumachita ndi thupi lanu zitha kukuthandizirani kuwongolera bwino maphunzirowa. Mwachitsanzo, kuwoneka wa chidwi ndikumavomereza atengambali akamalankhula pogwedezera mutu kutha kuwapangitsa atengambali kuti amve kuti zomwe akulankhula ndi zofunikira. Kuyang’ana kumbali kutha kupereka uthenga wachindunji kwa munthu kuti asalankhule kapena kutenganawo mbali. Nthawi zonse muyang’ananeni munthu amene mukulankhula naye.

    • Sangalalani!

    Kukambirana zinthu zomwe ena amati ndi zolaula/kapena zochititsa manyazi

    Zinthu zambiri zomwe zikukambidwa mu phukusi la alangizili zikukhudzana ndi nkhani zokhudza kugonana, maubwenzi, nkhanza, komanso HIV. Izi zikutanthauza kuti atengambali ndi mlangizi azikambirana zinthu zolaula kapena zomwe anthu zitha kuwakhuza kwambiri. Alangizi ena amaganiza kuti pokambirana nkhani zokhuza kugonana komanso nkhani zakulera ndi achinyamata, ndiye kuti akulimbikitsa achinyamata kugonana. Koma zoona zake ndizakuti kukambirana ndi achinyamata nkhani zokhuza kugonana, ndikuwauza zowona zake zokhuza kugonana komanso kulera zimawalimbikitsa kuti asayambe zogonanazo mwamsanga komanso kuti ayambe kuganiza zodzisunga. Mlangizi sakuyenera kungoganiza mwayekha kuti atengambali sakuchita zogonana.

    C H I Y A M B I

    Zina zomwe zingathandizire atengambali kudziwa kuti ndinu omasuka kukambirana zinthuzi ndi izi:• Vomerezani zining’a zomwe amagwiritsa ntchito. Koma osaopa kufunsa

    matanthauzo ngati simukuzidziwa.• Nenani kuti simukudziwa ngati simukudziwadi. Koma auzeni kuti

    muwayankhabe funso lawo; funsani achipatala kapena akadaulo ena omwe angakuthandizeni ndikukapereka yankholo nthawi ina.

    • Musaweruze. Imani pa zoona ndipo musawauze atengambali maganizo anu kapena zomwe mumakhulupirira kapena zomwe mumayimapo.

    • Musayankhe mafunso okhuza moyo wanu wogonana. Ngati mwafunsidwa izi, auzeni a tengambali kuti udindo wanu ngati mlangizi sikukamba za inu.

    • Mvetsetsani mitu yomwe mukuphunzitsa ndikukambirana mituyi ndi alangizi anzanu a mu bungwe lanu kuti mtima wanu udzikhala m’malo pokambirana zinthu zimenezi ndi atengambali.

    • Mukonzekere kuwawuza atsikana koyenera kupita kukalandira thandizo losiyanasiyana lomwe lapezeka kuti ndi lofunikira kuti alandire pomwe maphunzirowa akupitirira. Maulendo okayendera ntchito zosiyanasiyana monga zachipatala ndi njira ina yabwino yodziwira za thandizo lomwe atsikana angapeze kudera lawo.

    Kuthana ndikukhuzika Atengambali atha kukhuzika munjira zosiyanasiyana nthawi yomwe maphunziro akuchitika. Mlangizi akuyenera kukhala tcheru ndikuyendetsa zinthu mwaukadaulo pomwe atengambali akhumudwa mowonekeratu mkati mwamaphunziro. Izi zimathandiza kuti atemtengambaliwo adziwe kuti ndiwotetezeka ndipo sakuchititsidwa manyazi komanso kuti gulu lonse lidutse mu nthawi yodzetsa nthumanziyi mwachangu.

    Njira ina yothanirana ndikukhuzika ndi: • Kusiya kukambirana nkhani zokhumudwitsazo.• Kusintha zokambirana ndikuyamba mutu wina, kapena kupita kopumulira.

    Atengambali atha kukhala ndi chikayiko pa iwo okha kapena atha osamva bwino kukambirana zinthu zokhuza kugonana ndi ena a msinkhu wawo. Zokambirana zitha kuwakumbutsa zovuta zosiyanasiyana zomwe anadutsamo kunyumba kwawo kapena kusukulu maphunziro asanayambe.

    Ngati mtengambali wakhumudwa ndi ntchito yomwe wapatsidwa ngati gawo la maphunzirowa, mlangizi alankhulane naye pambali ndikumva kuti ndi chiyani chomwe chamukhumudwitsa.

    Mlangizi sakuyenera kukakamiza mtengambali kuti alankhule pa zomwe zikumukhumudwitsa. Mvetserani zomwe mtengambali akunena. Ndibwino kumumvetsetsa, kumulimbikitsa komanso kumuthandizira. Musayesere

  • 20 21M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    C H I Y A M B I

    kufotokoza mmene mtengambaliyo akumvera kapena kuyesera kumuuza mmene akuyenera kumvera. Muuzeni kuti kukhumudwa sikolakwika komanso ndi umunthu kukhumudwa.

    Chonde dziwani kuti: konzekerani kumuuza mtengambali yemwe wachitiridwa nkhanza kapena upandu uliwonse za komwe angakalandire thandizo lokhuza uphungu wokhudza nkhawa yomwe ali nayo/kapena kuzunguzika maganizo/mu ubongo. Mukuyenera kukhala ndi maina a malowa ndi mmene angayendere kukafika ku malowa maphunziro a mu chigawo choyamba asanayambe.

    Tsindikani kwa mtengambaliyu kuti ndinu omasuka kulankhula naye ngati angafune kutero. Alimbikitseni atsikana ndi amayi achicheperewa kuyamba kucheza ndi kukhala pa chinzake ndi atsikana ndi amayi achichepere ena m’gulumo ndikupeza munthu wina osati wa pagululo amene angakhale poyang’anirapo pawo. Munthuyo atha kukhala wa kusukulu kwawo, mdera lawo, kapena ku chipembedzo (tchalitchi/kumzikiti).

  • 22 23M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    • Phunziro ili liwadziwitsa atengambali zambiri za phukusi la alangizili komanso lipeleka mpata kwa atengambali kuti adziwane wina ndi mzake. Ndi kofunikira kwambiri kuti pakhale kukhulupirirana ndi kulolerana m’gululi ndi cholinga chakuti anthuwa akhale omasuka ndikutha kugawana wina ndi mzake zinthu zina zomwe anadutsamo. Izi zithandiza kuti atsikana ndi amayi achicheperewa aphunzire kuchokela kwa wina ndi mzake komanso akulire limodzi.

    • Phunziro ili lithandizira atsikana ndi amayi achichepere kukhazikitsa zolinga za tsogolo lawo zomwe akukhumbira atakwaniritsa kudzera mu kutenga nawo mbali mu zigawo zamuphukusili.

    • Phunziro lino lithandizanso atsikana kuzindikira anthu owalimbikitsa, kuwunikira ndikudziwa malo otetezeka, kusukulu ndikudera la kwawo, komanso zithandizo zosiyanasiyana zomwe zili m’dera lakwawo komwe angakapeze chilimbikitso ndi thandizo.

    KukhazikitsaMaloto ako

    P h u n z i r o 1

    Gawo 1.1 – Gawo Lodziwana

    Gawo 1.2 –Kumangilira Gulu

    Gawo 1.3 – Kuzidziwa Ine Mwini ndi Maloto Anga

    Gawo 1.4 – Malo Otetezeka

  • 24 25M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6

    1. Atadziwana komanso kupeza anzawo ocheza nawo pakati pa atengambali ena2. Apitisa patsogolo luso lawo lotha:

    a. Kugwira ntchito ndi anzawo.b. Kutha kuyambitsa zochitika pagulu monga kuyambitsa nyimbo zothandizira

    kuphunzira komanso masewera osiyanasiyana.c. Kucheza komanso kulumikizana ndi atengambali ena.d. Kumasukirana, kuchita zinthu ndi ena komanso kulankhula maganizo awo.

    3. Kudziwa maloto komanso zolinga za moyo wawo, ndikupanga ndondomeko yokwaniritsira malotowo.

    4. Kupeza anthu omwe angawadalire komanso omwe angamakambirane nawo zovuta komanso zinsinsi zawo nthawi ndi nthawi.

    5. Kudziwa malo otetezeka, komwe angakhale mosungiridwa ulemu, komwe maganizo awo angamveke, komanso komwe angapite akafuna thandizo.

    Pakutha pa Phunziro 1, atengambali adzakhala:

    Zomwe Atengambali Akuyenera Kukhala Atadziwa Pakutha pa Phunziro 1

    Zolinga za Gawo

    Pakutha kwagawo lino atengambali:• Amva kuti alandiridwa pagulupo• Adziwa zambiri za maphunzirowa• Adziwana wina ndi mnzake

    Zipangizo komanso Kukonzekera• Mapepala aakulu• Zolembera zowala• Mpira

    Ntchito Yotsekulira

    Alandireni atengambali kumaphunzirowa ndi kuwathokoza kaamba ka kupezeka kwawo.Awuzeni atengambali:• Dzina lanu• Cholinga cha maphunzirowa chomwe chili kuchengetera, kupereka

    chilimbikitso komanso kudzutsa m’badwo wa atsikana ndi amayi achichepere omwe ali oyembekezera zabwino, ozindikira, okhala ndi chilimbikitso cha mphamvu kuchokera ku anthu akudera lawo komanso zochitika ku dera la kwawolo, odziwa komwe angapeze thandizo la chipatala ndi kuthekera kwao pochepetsa chiwopsezo chilichonse pa moyo wawo pomwe akukula ndi kukhala munthu wamkulu.

    • Maphunzirowa ndi a miyezi 6 ndipo atsikana azikambirana zinthu zosiyasiyana monga mimba zosakonzekera, HIV komanso zinthu zina zokhuza m’mene anthu amakhalira ndi kuchitira zinthu zomwe amakumana nazo tsiku ndi tsiku.

    Gawo 1.1

    Gawo Lotsegulira

    K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

    Langizo: Athandizeni atsikana ndi amayi achicheperewa kuti ayambe kutakasuka ndi kumasuka.Atsimikizireni kuti ali kumalo otetezeka ndipo atsikana ndi amayi achichepere onse abwera kumeneko ndi cholinga chakuti aphunzire. Akhale omasuka kufunsa mafunso poti palibe funso lopusa kapena lopanda pake!

  • 26 27M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Kudziwitsana za Zolinga• Mlangizi awerenge zolinga za gawo la tsikulo.• Afotokozere zomwe zolingazo zikutanthauza ndicholinga chakuti

    atengambali amvetsetse tanthauzo la zolingazo. • Funsani ngati atengambali ali ndi mafunso ndikufotokozera pomwe

    sipanamveke.

    Ntchito 1: Kudziwana(Mphindi 20)

    Mtundu wa Zochita: Ntchito za M’magulu.

    Cholinga cha Ntchito: Ntchitozi zili ngati kadzutsa ndipo zithandizire atengambali kuti ayambe kudziwana ndi atsikana ena pagulupo.

    Ntchito 1.1: Ndiwe Ndani?Malangizo1. Auzeni atengambali kuti asewera masewera otchedwa “Ndiwe ndani?”2. Munthu woyamba atchula dzina lake kenako atembenukira munthu yemwe

    wayandikana naye ndikumufunsa “ndiwe ndani?”3. Kenako, munthu wachiwiriyo asananene dzina lake atembenukira munthu

    woyamba uja ndikuuza gulu dzina la munthu woyambayo, kenako atchula dzina lake ndikufunsa munthu wachitatu “ndiwe ndani?”

    4. Munthu wachitatuyo atchula dzina la munthu woyamba ndi wachiwiri asanatchule dzina lake ndikufunsa munthu wachinayi kuti “ndiwe ndani?

    5. Masewerawa apitirira mpaka munthu womaliza. Monga mmene wina aliyense wachitira, munthu womaliza atchula dzina la wina aliyense asanatchule dzina lake.

    6. Munthu womaliza akatchula dzina la aliyense m’chipindacho, auzeni atengambali kuti adzitchule okha dzina lawo, zaka zawo, komanso chomwe amachita m’moyo (monga kuti ali pasukulu, amachita bizinesi kapena amangokhala panyumba).

    Ntchito: 1.2: Munthu ku MunthuMalangizo1. Auzeni atengambali kuti asunthe zinthu pa bwalopo/mchipindamo

    ndikuyika patali zinthu zonse zomwe zingawavulaze. Auzeni kuti asewera masewera otchedwa “munthu ku munthu.”

    2. Auzeni atengambali kuti ayendeyende m’chipindamo kulowera mbali ina iliyonse yomwe akufuna.

    3. Mwa apo ndi apo mlangizi akuwe kuti ‘munthu ku munthu.’4. Atengambali akuyenera kupita kwa munthu amene ali naye pafupi

    ndikukhala awiriawiri, auzana mayina awo mwachidule ndikuuzana chinthu chimodzi chomwe aliyense amakonda kuchita.

    5. Pitirizani kusewera masewerawa mpaka atengambali ambiri atadziwana ndi anthu ambiri.

    6. Aloleni atengambali abwerere ndikukhala mubwalo, kenako adziwitse kugulu lonse anthu awiri kapena atatu omwe anacheza nawo.

    Funso lowunikiraAfunseni atengambali:• Kodi ndi kofunika bwanji kuti tidziwane wina ndi mnzake?

    Ntchito 2: Kumvetsetsa Gulu (Mphindi 20)

    Mtundu wa Zochita: Gulu Lonse

    Cholinga cha Ntchito: Kumvetsetsa kuti gululo ndi lotani.

    Malangizo1. Atengambali akhale pansi koma bwalo lisaphwasuke.2. Auzeni atengambali mwa chidule za ndondomeko yonse ya maphunzirowa,

    nthawi yoyambira ndi kuweruka, nthawi yopuma ndi zina, komanso zina ndi zina zokhuza mmene maphunzirowa ayendere kuphatikizapo:• Malo ndi nthawi yomwe gulu lizikumana.• Kuti pa mkumano uliwonse pazikhala ntchito zochitira limodzi kwa

    pafupifupi ola limodzi ndi theka.• Fotokozani kuti ntchito zonse ndi zoti anthu atengepo mbali ndipo

    apempheni ndikuwalimbikitsa atengambali kulankhula, kugawana nzeru, kukambirana komanso kusangalala ndi kusewera.

    • Longosolani cholinga cha maphunzirowa.• Akumbutseni atengambali kuti ali pa maphunzirowa modzipereka ndipo

    salandira malipiro aliwonse.3. Perekani mpata kuti gulu lifunse mafunso.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 28 29M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Mafunso owunikira:• Kodi ndikofunikira bwanji kuti tizikumana ngati atsikana ndi amayi

    achichepere?• Kodi misonkhano ngati imeneyi ingatithandizire bwanji kuchepetsa zovuta

    zomwe timakamuna nazo?

    Chonde tsindikani kuti cholinga cha maphunzirowa ndikuthandizira atsikana ndi amayi achichepere kuti akhale:

    Ochilimika:Kukhala atsikana ndi amayi achichepere okhwima maganizo ndi odziwa chomwe akufuna.

    Opilira:Olimba mtima, omwe maso awo alunjika pakukwaniritsa masomphenya awo komanso zolinga za moyo wawo.

    Olimbikitsika ndi ozidalira: Kuphunzira maluso amoyo omwe achepetse chiwopsezo chokumana ndi zovuta zosiyansiyana.

    Opanda HIV ndi Edzi:Kuchepetsa chiwopsezo chotenga HIV pogwiritsa ntchito maluso a moyo omwe aphunzire.

    Okhala ndi owunikilidwa / Otsogoleredwa:Alimbikitsidwe, awongoleredwe, athandizidwe ndi anzawo komanso anthu ena kunja kwa gululi.

    Otetezeka:Kukhala atsikana omwe ali wotetezeka ku ziwopsezo zosiyanasiyana zomwe zimawapangitsa kupezeka mu zovuta komanso kutayidwa kumbali.

    Maphunzirowa ndi a anthu omwe adzipereka ndipo wina aliyense asayembekezere kuti alandira malipiro pokhala nawo pa maphunzirowa. Koma, pakutha pakutenga nawo mbali mu zigawo zonsezi atengambali akhala ataphunzira luso komanso nzeru zowathandizira kuchepetsa chiwopsezo chowadyera masuku pamutu.

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Ntchito 3: Kukonza Malamulo a Gulu(Mphindi 30)

    Mtundu wa Zochita: Ntchito ya Gulu Lonse.

    Cholinga cha Ntchito: Kukhazikitsa malamulo oyendetsera gulu.

    Ntchito 3.1: Masewera Opanda Malamulo.

    Malangizo1. Auzeni atengambali kuti asankhe masewera omwe angafune kusewera ngati

    gulu (monga mpira wa miyendo kapena mpira wa manja).2. Agaweni atengambali kuti akhale m’magulu awiri (maguluwo atha kukhala

    ofanana kapena gulu lina litha kukhala lalikulu kuposa lina).3. Apatseni mpira kuti agwiritse ntchito posewera masewera omwe

    asankhidwa ndipo mlangizi akhale oyimbira masewerawa.4. Popanda kukambirana kulikonse kapena kukonzekera, auzeni atengambali

    kuti asewere masewerawa.5. Masewerawa ali mkati, mlangizi azipereka malikisi/zigoli, zilango komanso

    chenjezo ku maguluwo momwe akufunira.6. Akasewera kwa ka nthawi imitsani masewerawa ndikuyambitsa zokambirana

    potsatira mafunso otsatirawa:• Kodi chomwe chikutika pa masewerawa ndi chiyani?• Kodi zotsatira za zomwe zikuchitika pa masewerawa ndi chiyani?• Ndi chiyani chomwe chingasinthe kuti masewerawa akhale

    mwachilungamo?• Kodi kugwiritsa ntchito malamulo kungakometse bwanji masewerawa?

    Ntchito 3.2: Masewera Okhala ndi Malamulo.Malangizo1. Auzeni atengambali kuti tsopano asewera masewera ena ndipo akuyenera

    kutsatira malamulo onse.2. Agaweni atengambali m’magulu awiri ofanana.3. Afunseni ngati akudziwa malamulo onse amasewerawa ndipo agwirizane za

    malamulo omwe agwiritse ntchito pamasewerawa.4. Lolani gulu lilonse likonzekere ndikuuzana chochita.5. Lolani atengambali kuti asewere masewerawa potsatira malamulo onse

    omwe agwirizana. Kenako afunseni atengambali mafunso otsatirawa.• Chimachitika m’masewerawa ndi chiyani?• Kodi masewera asintha bwanji titabweretsa malamulo?• Kodi kubwera kwa malamulo kwathandiza bwanji?

    6. Funsani, molingana ndi masewera onse omwe aseweredwa:• Kodi kufunikira kokhala ndi malamulo ndikotani?• Ndichifukwa chiyani gululi likuyenera kukhala ndi malamulo?• Kodi malamulowa angathandize bwanji?• Kodi zotsatira zosatsata malamulo pa gulu ndi chiyani?

    Ntchito 3.3 Kukhazikitsa MalamuloMalangizo1. Atengambali adziwe kuti tsopano apereka maganizo awo pa malamulo

    omwe akuganiza kuti atha kuthandizira kuti aliyense atengepo mbali pogwira ntchito zosiyanasiyana limodzi ngati gulu.

    2. Malamulo onse ayikidwe pamodzi, avomerezedwe ndikulembedwa pa pepala lalikulu. Lolani mtengambali yemwe angathe kulemba ndi kuwerenga kuti alembe mndandanda wa malamulowa.

    3. Malamulowa akalembedwa, uzani atengambali onse kuti alembe dzina lawo, kaya kusayinira kapena kuyika chizindikiro chilichonse pa pepala la malamulolo kusonyeza kuzipereka komanso kuvomerezana ndi malamulowo.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 30 31M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Uthenga kwa a atengambali

    Awuzeni atengambali kuti cholinga cha phukusili ndi maphunzirowa ndi kulola atsikana ndi amayi achichepere kuonjezera upangili, nzeru ndi kuthekera pokhala moyo wopindulitsa, opanda HIV, wochilimika kutengapo mbali komanso kutha kunena nkhanza zina zilizonse pamene ali m’njira yokonza tsogolo lawo.

    Ndemanga za mlangizi pa momwe gawoli layendera:

    Ndi zinthu ziti zomwe zayenda bwino?

    Ndi zinthu ziti zomwe zitha kukonzedwa?

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Tsindikani kwa atengambali kuti:Malamulo ndi ndondomeko za kakhalidwe zomwe gulu limakhazikitsa ndikugwirizana maphunziro asanayambe. Malamulowa amakhala ngati ndondomeko zowongolera kachitidwe ka zinthu. Malamulo amakonzedwa ndicholinga chakuti mtengambali aliyense amve kuti ndi wotetezeka komanso wofanana ndi aliyense nthawi zonse.Ena mwa malamulo omwe akuyenera kukhalapo ndi monga:• Kutenga mbali mofanana.• Kusunga ndi kulondoloza nthawi (kuyamba ndi kumaliza zinthu pa

    nthawi yake).• Kulemekezana wina ndi mnzake.• Wina aliyense asanyozetse kapena kupeputsa wina chifukwa cha

    maganizo ake, zomwe zikuwakhuza, kapena zomwe adutsamo. • Kumvetsera.• Kupatsana mpata wolankhula munthu m’modzi pa nthawi (osaseka,

    kunyogodola kapena kulowerera pomwe wina akulankhula).

    Langizo: Matani m’ndandanda wa malamulo poyera ndipo kumbutsani atengambali za malamulowa potsegulira chigawo chilichonse.

    Ntchito Yotsekera: Dzina langa ndi… ndipo ndimakonda ku….

    • Auzeni atengambali ayimilire ndikupanga bwalo.• Funsani aliyense aganizire chinthu chomwe amakonda kuchita

    ndikuyesezera mmene chinthucho chimachitikira (monga kusewera mpira, kuphika ngakhale kuvina).

    • Munthu mmodzi asunthira mkati mwa bwalo pang’ono ndikunena. “Dzina Langa ndi.............ndipo ndimakondaku… (ayesezere chinthucho) kenako ndikutchula chinthucho ndikubwerera mmalo mwake.

    • Aliyense asunthira mkati pang’ono ndikubwereza zomwe munthu uja ananena ndikunena pogwiritsa ntchito zizindikiro, kalankhulidwe ndi zichitochito zomwe munthu uja anachita. Aliyense kuphatikiza mlangizi azidziwitse yekha ku gulu lonse kudzera m’njirayi.

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Tsindikani zinthu izi kwa atengambali:• Atengambali atha kukupezani pambali ngati akufuna kulankhula nanu

    mwapadera kapena ngati akufuna thandizo pa vuto lomwe ali nalo.• Maphunzirowa akhala opindulitsa pokhapokha ngati atengambali

    apezeke nthawi zonse pamaphunzirowa ndikutenga nawo mbali pa zochitika zonse.

    Athokozeni atengambali pobwera kumaphunzirowa ndikuwakumbutsa za tsiku, nthawi ndi malo omwe adzakumanenso popitiriza ndi maphunzirowa.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 32 33M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Zolinga za GawoPakutha pa gawo lino atengambali:

    • Amvetsetsa zakufunikira kogwirira ntchito limodzi pagulu• Alumikizana ndi anthu ena pagulupo ndikuyamba kukhulupirirana

    Zipangizo komanso Kukonzekera• Mapepala akuluakulu (fulipi tchati)• Zolembera zowala• Mipando, mabokosi kapena miyala yayikulu kapena chilichonse chomwe

    chingawoneke mosavuta pa bwalo lalikulu chomwe anthu akuyenera kupewa akamayenda

    • Zomangira nkhope kuti munthu asawone

    Ntchito Yotsekulira

    Masewera: Kambuzi kali m’khonde mee! Fisi watopa wuwii!• Auzeni atengambali kuti asewera masewera otchuka achiMalawi,

    Kambuzi kali m’khonde.• Uzani atengambali ozipereka awiri kuti ayime pambali ndipo wina

    akhala mbuzi ndipo winayo akhala fisi.• Atengambali ena onse ayimilira ndikupanga bwalo, ndipo agwirane

    manja• Mtengambali yemwe akhale mbuzi akhala mkati mwa bwalo ndipo

    yemwe akhale fisi akhala kunja kwa bwalo.• Cholinga ndi chakuti gulu lonse liteteze mbuziyo uku fisi akuchita

    chilichonse chomwe angathe kuti agwire mbuziyo. Ngati fisi wakwanitsa kulowa m’bwalomo, mbuziyo ikuyenera ithawire kunja kwa bwalolo mwachangu. Ngati fisi agwira mbuziyo, awiriwa atha kusinthana kuti yemwe anali mbuzi akhale fisi ndipo fisi akhale mbuzi. Muthanso kusankha anthu ena ozipereka kulowa mmalo mwa awiriwa.

    • Masewerawa akamachitika atengambali onse akuyenera kuyimba:Otsogolera: Kambuzi kali m’khondeOnse: MeeeeOtsogolera: Fisi WatopaOnse: wuwii

    Masewerawa akatha tsogolerani zokambirana poyankha mafunso otsatirawa:• Kodi gulu lonse linagwira ntchito bwanji poteteza munthu yemwe anali

    ngati mbuzi?

    • Kodi “iweyo amene umasewera ngati fisi” umamva bwanji pokhala kunja kwa gulu?

    • Kodi “iweyo amene umasewera ngati mbuzi” unamva bwanji potetezedwa ku fisi?

    • Kodi gulu linakwanitsa kuteteza munthu yemwe anali ngati mbuzi? Ngati eya, munamuteteza bwanji? Ngati ayi, munalephera pati?

    • Kodi kunali kofunikira bwanji kuti mugwire ntchito limodzi ngati gulu kuti muteteze mbuzi?

    • Kodi ndikofunikira bwanji kuti tigwire ntchito limodzi ngati gulu?• Kodi masewerawa akufanana bwanji ndi zomwe zimachitika mmoyo

    mwanu pa nkhani yogwirira ntchito limodzi ngati gulu?

    Kukumbutsana• Funsani atengambali kuti akhale awiriawiri. Mu uwiri wawo

    auzeni atengambali kuti akambirane mmene akonzekera kukhala: ochilimika, opirira, olimbikitsika ndi kuzidalira, opanda HIV, okhala ndi oyang’anirapo ndi owateteza?

    • Akatha kukambirana, sankhani magulu angapo kuti agawane ndi gulu lonse zomwe akambirana.

    Kudziwitsana za ZolingaAloleni atengambali kuti awerenge zolingazi mokweza.

    • Afunseni atengambali ndemanga zawo pa zolingazo kuti muwone ngati amvetsetsa zolingazo.

    • Mlangizi afotokozere zolingazo ndikuyankha mafunso onse omwe angakhalepo. • Atengambali adziwe kuti chigawochi chiwunika kwambiri pa

    kugwilira ntchito limodzi ngati gulu komanso kufunikira kwa kukhulupirirana pa gulu.

    • Tsindikani kuti ndikofunikira kwambiri kuti akhale okhulupirirana pagululo ndikugwilira ntchito limodzi podziwa kuti m’miyezi ikubwerayi azikambirana zinthu zambiri zochititsa manyazi kapena zolaula, zina zomwe ena amaganiza kuti siziyenera kukambidwa pagulu komanso zina zomwe sangafune kuti anthu akunja kwa gululi adziwe.

    • Pokhulupirirana wina ndi mnzake, maphunzirowa akhala malo omwe atengambali angakhale omasuka kugawana ndi ena nkhawa zawo ndipo akhala ndi chikhulupiriro chakuti anthu a mugululo sakauza anthu apadera.

    Gawo 1.2

    Kumangilira Gulu

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 34 35M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Ntchito 1: Kumangilira Gulu(Mphindi 30)

    Mtundu wa Zochita: Ntchito ya Awiriawiri

    Cholinga cha Ntchito: Kuthandizira atengambali kuyamba kuchitira zinthu limodzi ngati gulu komanso kuti akhale odalirana

    Malangizo1. Kuti masewerawa ayende bwino pafunika malo akulu; ngati kuli kotheka

    ndi bwino kusewerera panja. Ikani malire ndipo mkati mwa malirewo muyikemo zinthu zosiyanasiyana (monga mipando, ndi zipangizo zina zomwe zingatchinge njira) zomwe zingalepheretse munthu kuyenda mwachindunji kapena kuti mosakhotakhota komanso zoti zitha kugwetsa anthu. Onetsetsani kuti pali mpata wokwanira woti munthu atha kudutsa pakati pa zinthuzo.

    2. Auzeni atengambali kuti akhale awiriawiri ndi munthu amene sakumudziwa kapena sacheza naye kwambiri, ndipo mu uwiri wawo atengambali agawane kuti wina akhale ‘A’ wina ‘B’.

    3. Ma “A” amange nkhope za ma “B” kuti asamaone, ndipo ma “B” ndi omwe aziyenda, ndipo sakuloledwa kulankhula kapena kusuzumira pansi pa nsalu yomwe yakulunga nkhope yawo.

    4. Ma “A” akhale kunja kwa malire anayikidwa aja koma azitha kuwawongolera ma “B” powauza chochita kuti asagunde zinthu zomwe zinayikidwa mkati mwa malire pomwe akuyenda kuchokera mbali imodzi ya bwalo kupita mbali ina. Adziwitseni kuti ngati agunda chinthu chilichonse iwo akuyenera kubwerera kukayambiranso kumayambiriro.

    5. Asanayambe apatseni mphindi zingapo kuti agwirizane chochita.6. Perekani mphindi khumi kwa munthu aliyense mwa awiriwo kenako

    asinthana kuti winayo nde amangidwe nkhope ndipo yemwe anali womangidwa uja akhala owongolera anzawo.

    7. Onse awiri akamaliza, gulu lonse libwere pamodzi ndi kukambirana.8. Tsogolerani zokambirana powunikira mafunso awa:

    • Kodi ndi chiyani chimachitika apa?• Kodi ndi chiyani chinapangitsa kuti zinthu zisavute pomwe

    anakumangani nkhope?• Kodi ndi chiyani chomwe chimavuta atakumangani nkhope?• Kodi munthu m’modzi akanatha kudutsa dera lonse payekha?• Kodi kugwirira ntchito limodzi mu uwiri wanu kunali kofunika bwanji pa

    masewerawa?• Kodi kukhulupirirana kunali ndi gawo lanji pamasewerawa?• Kodi kugwirira ntchito limodzi ngati gulu komanso kukhulupirirana

    kungatithandize bwanji ngati gulu?

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Tsindikani kwa atengambali kuti kugwirira ntchito limodzi pa gulu ndi chinthu chofunikira kwambiri. Gulu siligwira ntchito moyenera ndipo silikwaniritsa zambiri ngati siligwirira ntchito limodzi. Kugwirira ntchito limodzi kumabweretsa mgwirizano pa gulu ndikuthandiza anthu kuphunzira kugwirira ntchito limodzi. Zimalimbikitsa munthu aliyense payekhapayekha, zimathandizira kupeza mayankho amavuto osiyanasiyana, ndipo zimakulitsa chimvano.

    Langizo: Zitha kukhala bwino kuti gulu liyambe kuganizira dzina, kapena mawu woti gululo lizidziwika nawo.

    Ntchito 2: Kukhulupirirana ndi Kusungirana Zinsinsi(Mphindi 40)

    Mtundu wa Zochita: Magulu Ang’onoang’ono

    Cholinga cha Ntchito: Atengambali apeze munthu m’modzi amene angamukhulupirire kumasuka naye ndi kumuuza zinsinsi zawo.

    Malangizo1. Uzani gulu kuti ligawane ndi kukhala m’magulu anayi. 2. Lipatseni gulu lililonse vuto loti alipezere yankho:

    • Ndinu mtsikana wa zaka 15 ndipo mwapezeka ndi mimba yosakonzekera.

    • Makolo anu aganiza zoti musiye sukulu kuti muziwathandiza pakhomo.• Bambo wachikulire akukufunani chibwenzi koma inu

    sizikukusangalatsani.• Mwamva abale anu akukambirana kuti nthawi yoti mukwatiwe yakwana.

    Simuli okonzeka kukwatiwa ndipo mudakakonda kukhalabe ndi abale anu.

    3. Longosolani kuti akuyenera kupeza thandizo kwa munthu, akhoza kukhala wachibale kapena oyandikana nawo nyumba, kapena wachipatala.

    4. Gulu lilonse likambirane ndi kuyankha mafunso otsatirawa: • Angakalankhule ndi ndani pa nkhani imeneyi?• Angakamuuze chiyani munthuyo? • Ndichifukwa chiyani angakauze munthu ameneyu osati munthu wina?

    5. Pakatha mphindi 15 kapena 20, ayitanitseni onse kuti abwerere mu bwalo lija ndikuwafunsa kuti afotokoze zomwe akambirana pa gulu lawo pa vuto lomwe anapatsidwa.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 36 37M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    6. Kambiranani mayankho osiyanasiyana ndikutsindika zomwe zikufanana. 7. Tsogolerani zokambirana powunikira mafunso awa:

    • Ndi ndani yemwe munamusankha kuti mumuuze vuto lanu?• Ndichifukwa chiyani munasankha kuti muuze munthu ameneyu za vuto

    lanu?• Mukuganiza kuti mungamve bwanji mutamuuza munthuyo za vuto

    lanu?• Ndikangati munthu anakuuzanipo inuyo za mavuto ake?• Kodi mumachita chiyani kuthandizira anthu kuti akukhulupirireni? • Kodi ndi angati mwa ife tili ndi zinthu m’moyo mwathu zomwe zili

    zovuta kuuza anthu ena ndipo sitifuna ena adziwe pokhapokha titadziwa kuti asunga chinsinsi?

    • Kodi ubwino onena nkhani zomwe zikutikhuza pagulu ndi chiyani?• Kuwophya konena nkhani zomwe zimatikhuza kwambiri pagulu ndi

    chiyani? • Kodi ngati gulu tingatani kuti tipindule ndi kuuzana nkhani zotikhuza

    uku tikuchepetsa chiwophyezo chilichonse chomwe chingakhalepo?

    Ntchito Yotsekera: Munthu ku Munthu

    1. Auzeni atengambali kuti abwerenzenso ntchito ija ya munthu ku munthu. 2. Auzeni kuti azungulirezungulire m’chipindacho/pabwalopo.3. Mlangizi akakuwa kuti munthu ku munthu, atengambali akhale awiriawiri

    ndikulingalira komaliza poganizira mafunso awa:• Kodi kugwirira ntchito limodzi ndikofunikira bwanji pa gulu?• Ndikofunikira bwanji kukhala ndi munthu yemwe ungamukhulupirire

    ndikutha kumuuza mavuto ako?4. Apatseni mpata atengambali kuti akambirane.

    Athokozeni atengambali pokhala nawo pamaphunzirowa ndikuwakumbutsa za tsiku, nthawi komanso malo omwe mudzakumaniranenso popitiriza maphunzirowa.

    Ntchito yoti atengambali atengere kunyumba

    Akumbutseni atengambali kuti abweretse mabuku awo achinsinsi kapena madayale kuti adzagwiritse mu chigawo chinacho Apempheni atengambali kuti adzakhale ndi chidwi pa momwe iwo kapena anthu omwe ali nawo pafupi akugwirira ntchito limodzi ngati gulu.

    Ndemanga za mlangizi pa momwe gawoli layendera:

    Ndi zinthu ziti zomwe zayenda bwino?

    Ndi zinthu ziti zomwe zitha kukonzedwa?

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 38 39M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Gawo 1.3

    Kudzidziwa Ine Mwini ndi Maloto AngaZolinga za GawoPakutha pa gawo lino atengambali adzatha:

    • Kudziwa chomwe ali ngati munthu komanso kumvetsetsa zomwe zimawapangitsa kukhala munthu wapaderadera

    • Kuzindikira mphamvu komanso zofooka zawo ndi mmene angathanirane nazo

    • Kukhazikitsa zolinga m’moyo ndi kuyika m’malo ndondomeko zokwaniritsira masomphenyawo

    Zipangizo komanso Kukonzekera• Mapepala akuluakualu• Mpira• Zolembera zowala• Mabuku a chinsinsi

    Ntchito Yotsekulira

    Masewera: ‘Tiuze’ • Auzeni atengambali kuti apange bwalo ndikupempha mtengambali

    mmodzi kuti azipereke kuyambitsa masewerawa.• Atengambali onse atchule dzina la munthu wodziperekayo pakamodzi

    ndikumuuza munthuyo kuti alankhule ponena kuti “Chimwemwe tiuze”.• Kenako Chimwemwe auze gulu lonse chili chonse chimene amakonda mwa

    iye mwini• Kenako gulu litchula dzina la munthu wina, mwachitsanzo munthu yemwe

    wayima kumanja kwa Chimwemwe.• Masewerawa akuyenera kupitirira mpaka wina aliyense atanena chinthu

    chimodzi chomwe amakonda.

    KukumbutsanaAfunseni atengambali kuti:

    • Atchule malamulo oyendetsera gulu omwe anakhazikitsidwa pachiyambi paja.

    • Akawatchula onse, kapena ngati ena ayiwalika, mataninso pepala lomwe panalembedwa malamulo aja pakhoma ndikuwunikiranso lamulo lililonse.

    • Afunseni ngati pali malamulo ena omwe akuyenera kuwonjezeredwa ndipo

    malamulo amenewa akhala omalizira ndipo akuyenera kukumbukiridwa mu ndime iliyonse.

    Kudziwitsana za Zolinga• Pemphani mtengambali mmodzi kuti awerenge zolinga zonse mokweza/

    kapena mlangizi awerenge zolingazi ku gulu lonse.• Afunseni atengambali ndemanga zawo pa zolingazo kuti muwone ngati

    amvetsetsa.• Mlangizi afotokozere zolingazo ndikuyankha mafunso onse omwe alipo.

    o Atengambali adziwe kuti chigawochino chikhazikika poti atengambali adzimvetsetse wokha komanso zolinga za moyo wawo.

    o Tsindikani kuti ndikofunika kwambiri kuti aliyense azidziwe yekha komanso kuti masomphenya awo ndiwotani. Izi zithandiza atsikana kulunjika pa zomwe akufuna komanso kutsogozedwa ndi zolinga za moyo wawo uku akuchita china chilichonse kuti akwaniritse masomphenya awo.

    Ntchito 1: Kukonda Ine Mwini, Kukondanso Iwe (Mphindi 20)

    Mtundu wa Zochita: Payekha Payekha.

    Cholinga cha Ntchito: Kuti atengambali athe kuziwona okha kuti ndi anthu apamwamba pounikira zabwino zomwe ali nazo ngati munthu, luso losiyanasiyana lomwe ali nalo, komanso zomwe zitha kuwathandiza kukuza chikhulupiliro chawo mwa iwo mwini.

    Malangizo:1. Gawani makope kapena uzani atengambali kuti atenge mabuku awo

    achinsinsi ndipo onetsetsani kuti aliyense ali ndi cholembera. Afunseni kuti akhale pawokha ndikulemba kapena kujambula zinthu zisanu zomwe amakonda mwa iwo eni ngati munthu.• Ngati atengambali ena sadziwa kuwerenga, athandizireni kujambula

    zithunzi kapena muwapezere munthu amene angawathandize kujambula zithunzi.

    2. Longosolani kuti izi zitha kukhala umunthu wawo, zomwe akwaniritsa mmoyo, mawonekedwe ndi chilichonse chomwe chabwera m’maganizo awo.• Kuti mupewe kuwauzira, ndikofunikira kuti atengambali apange maganizo

    awo awo ndikuziganizira wokha zinthu zabwino.

    Langizo: Fufuzani ngati pali atengambali omwe samatha kulemba ndi kuwerenga. Ngati alipo akhale limodzi ndi munthu amene amadziwa kulemba ndi kuwerenga.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 40 41M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    3. Aliyense akalemba mndandanda kapena kujambula zithunzi, funsani anthu anayi kapena asanu kuti auze gulu mndandanda wa zinthu zomwe alemba. Afunseni ena onse ngati ali ndi zinthu zofanana ndi izi pa mdandanda wawo kapena ngati ali ndi zinthu zina zosiyana.

    4. Afunseni atengambali kuti alembe zinthu zisanu zomwe zimawapangitsa kumva bwino kapena kukondwa. Bwerezaninso kuti zinthu izi zitha kukhala anthu, maubale ndi maubwenzi, zinthu zomwe amaimapo kapena kukhulupilira, mmene anthu amawaonera ndi zinthu zina. Kumbukirani kuti simukuyenera kupereka zitsanzo za chindunji.

    5. Aliyense akapanga mndandanda wake, funsani anayi kapena asanu kuti auze gulu lonse zinthu zomwe zili pa mndandanda wawo. Afunseni ena ngati ali ndi zinthu zomwezo pamndandanda wawo kapena ngati ali ndi zina zosiyana.

    6. Pamathero a nchitoyi, tsogolerani zokambirani powunikira mafunso awa:• Kodi ndikofunikira bwanji kuti mumvetsetse zinthu zomwe mumakonda pa

    inu mwini?• Kodi zinthu zimenezi zingakuthandizeni bwanji kukwaniritsa zolinga za

    moyo wanu?• Ndi zinthu ziti zomwe mumazitenga kuti ndi zofooka zanu?• Mungachite chiyani kuti mukonze zofookazo?

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Onetsetsani kuti atengambali amvetsetsa kuti ndikofunikira kuti aziganizira zinthu zomwe zili zofunikira m’moyo mwawo komanso zomwe zingawapangitse kukhala munthu wokondwa chifukwa kawirikawiri anthu amavomereza zinthu zomwe sizikuwasangalatsa. Ulendo wokhala ndi moyo wokondwa komanso kukhala ndi maubwenzi abwino umayamba ndi kumvetsetsa kuti aliyense ndi munthu wapaderadera ndi kuzindikira zinthu zomwe zimakupangitsa kuti ukhale wokondwa. Zikatero utha kupeza njira yoti utsate paulendo wopangitsa miyoyo yambiri kukhala yokondwa.

    Mchangamutso: Pemphani mtengambali m’modzi kuti ayambitse masewera kapena nyimbo yayifupi yomwe aliyense atha kutenga nawo mbali.

    Ntchito 2: Kukhazikitsa Masomphenya Anga (Mphindi 50)

    Mtundu wa Zochita: Ntchito ya M’magulu Ang’onong’ono

    Cholinga cha Ntchito: Kuthandizira atengambali kukhala ndi zolinga zomwe akufuna kukwaniritsa mu nthawi yoyikika

    Langizo: Onetsetsani kuti mwalemba maganizo onse pa pepala lalikulu kuti gulu lidzaonenso maganizowa kanthawi kena. Ngati atengambali ena samatha kulemba ndikuwerenga, athandizeni!Yenderani magulu onse kuwonetsetsa kuti atengambali akukambirana zoyenera.

    Ntchito Yotsekera: ‘Tiuze’

    • Bwerezani masewera a ‘Tiuze’ omwe anachitika koyambirira kwachigawochi koma panopa atengambali azinena za zolinga zawo m’moyo.

    Thokozani atengambali kaamba kokhala nawo pamaphunzirowa ndikuwakumbutsa za malo, nthawi komanso tsiku lomwe mudzakumanenso popitiriza ndi maphunzirowa.

    Malangizo1. Auzeni atengambali ayendeyende m’chipindacho/pa bwalolo. Asayime

    mpaka mutawauza kuti atero2. Akuyenda choncho, auzeni kuti aganizire chinthu chomwe akufuna achite

    kapena amalizitse m’mwezi umodzi, kapena chomwe akufuna achite asanafike zaka 26, kapena mu nthawi ina iliyonse.

    3. Pakadutsa mphindi zingapo pomwe mukuganiza kuti atengambali atha kukhala ataganizira chinthu chimodzi kapena ziwiri, auzeni ayime ndikulemba kapena kujambula maganizo awo mu kope kapena polemba pomwe ali napo. Kenako abwerere kugulu ndikupanga bwalo.

    4. Funsani atengambali kuti agawane maganizo awo:a. Lembani zomwe akunenazo pa pepala lalikulu.

    5. Kenako agaweni atengambali kuti akhale m’magulu a anthu anayianayi. M’magulu awowo ayankhe mafunso otsatirawa:a. Zomwe zingandithandizire kukwaniritsa maloto anga ndi chiyani?b. Zomwe zingandilepheretse kukwaniritsa maloto anga ndi chiyani?c. Kodi zopinga zimenezi ndingathane nazo bwanji?

    6. Zokambirana za m’maguluzi zikatha, atengambali abwerere m’malo ndikugawana ndi gulu lonse zomwe akambirana.

    7. Onetsetsani kuti mupereke ndemanga pomwe pakufunika kutero.8. Afunseni atengambali kufunikira koti atsikana azikhala ndi masomphenya

    m’moyo?

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 42 43M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    • Longosolani kuti ndikoyenera kuti aliyense akhale ndi zolinga m’moyo ndi kuganizira kuti angazikwaniritse bwanji komanso kuti ndi zopinga zanji zomwe zingalepheretse kukwaniritsa zolingazo. Anthu atha kukhala ndi zolinga zomwe akufuna akwaniritse m’chaka chimodzi, zaka zisanu, zaka khumi kapena m’moyo mwawo. Zolingazi zimatha kusintha munthu akamakula koma ndi bwino kuzilemba ndi kumalingalira za zolingazo.

    • Tsindikani kuti kukhala ndi zolinga kumawapatsa atengambaliwo chinthu choti azilakalaka atachifikira. Ndikofunikira kwambiri kuti azindikire luso lomwe ali nalo komanso phindu lake, komanso chilimbikitso chochokera kwa anthu ena chomwe chingawathandizire kukwaniritsa maloto awo. Onetsetsani kuti mwatsindika kuti ndikofunikira kuwunikira zolingazi nthawi ndi nthawi kuwonetsetsa kuti zolingazo zikukwaniritsidwa komanso kuti asatayane ndi zolinga zomwe zitha kutenga zaka zambiri kuti azikwaniritse.

    Ntchito yoti atengambali atengere kunyumba

    M’masiku akubwerawa atengambali aganizire kwambiri: • Pa momwe angafikire zolinga za m’moyo mwao• Ndondomeko zomwe akuyenera kutsata kuti izi zitheke• Zokoma zina zomwe akuyenera kuzisiya (kuzichita nsembe) kuti izi

    zitheke

    Gawo 1.4

    Malo OtetezekaZolinga za GawoPakutha pa gawo lino atengambali adzatha:

    • Kudziwa malo osiyanasiyana komwe atsikana amakhala otetezeka• Kudziwa anthu omwe angawapatse atsikana chilimbikitso ndikuwapangitsa kumva

    kuti ndiwotetezeka

    Zipangizo komanso Kukonzekera• Mapepala akuluakulu• Zolembera zowala za mitundu yosiyanasiyana• Pepala lalikulu lomwe analembapo malamulo mu ndime ya m’mbuyo

    Ntchito Yotsekulira

    Pemphani mtengambali kuti ayambitse nyimbo, gule kapena masewera aliwonse omwe ali otchuka mderalo kuti aliyense athe kutengapo mbali.

    Kukumbutsana• Auzeni atengambali kuti akhale m’magulu a anthu anayianayi• M’magulu mwawo akambirane mmene angathanirane ndi zofooka zawo kuti

    akwaniritse zolinga zawo.

    Kudziwitsana za Zolinga• Mlangizi/ Mtengambali awerenge zolingazo mokweza.• Atengambali akhale awiriawiri ndikukambirana zomwe zolingazo zikutanthauza• Kenako fotokozerani zolingazo.

    o Tsindikani kuti gawo lino liwunika za malo otetezeka. Malo otetezeka amenewa ndi malo omwe atsikana/azimayi amayenera kukumana ndi kuchita zinthu zomwe zimawasangalatsa. Malo otetezekawa akuyenera kuteteza atsikana ndi amayi ku nkhanza za kuthupi, zokhuza kugonana, komanso kunyazitsidwa. Chitsanzo cha malo otetezeka ndi monga ‘gulu lino’.

    Ndemanga za mlangizi pa momwe gawoli layendera:

    Ndi zinthu ziti zomwe zayenda bwino?

    Ndi zinthu ziti zomwe zitha kukonzedwa?

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 44 45M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Ntchito 1: Kujambula Mapu (Chithunzi) Cha Dera Lathu(Mphindi 30)

    Mtundu wa Zochita: Ntchito ya Magulu Ang’onong’ono

    Cholinga cha Ntchito: Ntchitoyi ithandizira atsikana ndi amayi achichepere kukhazikitsa komanso kudziwa malo omwe ali otetezeka ku dera lawo. Ntchitoyi ithandiziranso atsikana ndi amayi achicheperewa kudziwa anthu omwe angawathandizire kukhala otetezeka ndikutha kulankhula za kukhosi kwawo, kuchita zinthu momasuka, ndikulankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana. Kudziwa malo otetezeka amenewa, kuthandiza atsikana kumva kuti ndiwotetezeka pomwe ayamba ulendo wokhala anthu odzikhulupirira, amphamvu, oyima pawokha, okhala ndi cholinga ndikutha kupewa ziphyinjo zomwe zimawayika pachiwophyezo chowadyera masuku pamutu

    Malangizo1. Auzeni atengambali apange bwalo ndikukhala pansi.2. Auzeni atengambali kuti achita ntchito yotchedwa kujambula mapu

    kapena chithunzi cha dera lawo.3. Auzeni kuti muntchitoyi ajambula mapu kapena chithunzi cha dera, komwe

    asonyeze malo onse komwe atsikana ndi amayi achichepere amakhala otetezeka komanso malo omwe atsikana ndi amayi achichepere sakhala otetezeka.

    Langizo: Alimbikitseni atengambali kujambula mapu omwe awonetse malo ambiri mderalo monga kusukulu, ku mjigo, ku tchalitchi, ku mzikiti, kuchipatala ku msika ndi malo ena.

    Aloreni atengambali kuti ajambule mapu akulu. Zitha kukhala bwino mapuwa atajambulidwa pa mapepela akuluakulu oti atha kumatidwa pakhoma.

    4. Magulu onse akagawana ndi gulu lonse zomwe anakonza, tsogolerani zokambirana potsatira mafunso owunikira awa:• Ndichifukwa chiyani malo omwe asonyezedwa kuti ndi ‘otetezeka’ ali

    malo omwe atsikana amakhala otetezeka?• Ndichifukwa chiyani malo omwe asonyezedwa kuti ndi “osatetezeka” ali

    malo omwe atsikana sakhala otetezeka?• Tingatani ngati atsikana kuti tipewe malo osatetezekawa?• Tidzitani tikakumana ndi zovuta/chiwopsezo m’malo osatetezekawa?• Tingakanene kuti kapena tingauze ndani tikakumana ndi chiopsezo

    kumalo osatetezekawa?

    • Kodi tingatani kuti gulu lino likhale malo otetezeka kwa aliyense m’gululi?

    • Kodi malo otetezeka angatithandizire bwanji kukwaniritsa zolinga za moyo wathu?

    • Kodi malo otetezeka amenewa angatithandizire bwanji kukhala ochilimika, opirira, olimbikitsika ndi kuzidalira, opanda HIV ndi Edzi, okhala ndi anthu oyang’anirapo ndi otetezeka?

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Tsindikani kuti malo otetezeka ndi kumalo komwe atsikana amamva kuti ndi otetezeka, kuthupi komanso m’maganizo. M’malo otetezekawa atsikana amakhala omasuka kulumikizana ndi kucheza ndi atsikana ena, kugawana maganizo ndikulimbikitsana pomwe akuchita kuthekera kulikonse kuti akhale amphamvu.

    Malo otetezeka amakhala• Komwe sikuchitidwa nkhanza za m’maganizo komanso za kuthupi• Apadera komanso achinsinsi.• Ovomerezeka ndi makolo molingana ndi chikhalidwe koma makolo

    sakhala ndi mphamvu pa zochitika za kumaloko.• Komwe amuna ngakhale ena omwe sakukhuzana ndi zochitika

    kumaloko salowererapo.

    Mchangamutso: Afunseni atengambali kuti ayambitse/kuphunzitsa masewera.

    Ntchito 2: Kupanga Maubwenzi(Mphindi 30)

    Mtundu wa Zochita: Payekhapayekha

    Cholinga cha Ntchito: Kuti atengambali apitirize kupeza anzawo ndikupanga maubwenzi ndi atengambali ena m’gululo

    Malangizo1. Auzeni atengambali kuti aganizire munthu yemwe akumuwona kuti atha

    kukhala mnzawo wabwino, kapena yemwe akufuna atakhala mnzawo. Ndichifukwa chiyani munthu ameneyo angakhale mnzawo wabwino? Ndichifukwa chiyani mukufuna munthu ameneyo kuti akhale mnzanu?

    2. Tsopani auzeni atengambali kuti akonze mauthenga/malonda a pawayilesi otchedwa “Ndikufuna mnzanga” omwe kutalika kwake kusaposere theka la phindi imodzi. Sakuyenera kulemba uthengawu/malondawa, ndipo sukuyenera kuchita kukhala wovuta. Uthengawu ungonena zomwe

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 46 47M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    munthuyo akhale kuti amakonda, makhalidwe, komanso zina zabwino zomwe munthu mukufunayo akuyenera kukhala nazo.

    3. Auzeni atengambali kuti agawane ndi gulu lonse uthenga wawo uja. Pongofuna kukometsera, yesezerani kugwiritsa ntchito chojambulira mawu cha pawayilesi.

    4. Kuti muwongolere zokambirana, tsatirani mafunso owunikira awa:a. Kodi ndi zinthu ziti zabwino zomwe atengambali akuyang’ana mwa

    mnzawo?b. Kodi zinthu zimenezo ndizofunikira bwanji? (Atengambali atha kunena

    zinthu monga, kukhulupirirana, amawafunira zabwino nthawi zonse, sangawakakamize kuchita zinthu zomwe sakufuna).

    c. Mukuganiza kuti anyamata ndi atsikana amayang’ana zinthu zofanana mwa m’nzawo? Ngati eya: ndichifukwa chiyani, ngati ayi: ndichifukwa chiyani?

    d. Anzanu amapeza ubwino wanji mwa inu?e. Kodi maubwenzi atithandizira bwanji m’gulu lino?

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    Limbikitsani atengambali kuti mu gawo linalo, atengambali akuyenera kupeza mzawo wa paderadera ndikukhala awiri ngati anthu ali operewera ena atha kukhala atatu. Alimbikitseni atengambali kupeza munthu amene sanachezepo naye. Komanso akuyenera kupeza munthu yemwe sanapeze kale mnzake wa pa gululo.

    Ntchito 3: Ondilimbikitsa Anga(Mphindi 10)

    Mtundu wa Zochita: Payekhapayekha

    Cholinga cha Ntchito: Kuwapatsa mpata atengambali kuganizira munthu amene atha kumukhulupirira ndipo atha kulankhula naye pa chinthu chilichonse chomwe chikuwavuta

    Malangizo1. Atengambali atenge makope awo kapena polemba pomwe ali napo

    ndikupeza malo awokha pomwe angathe kukhala ndikulemba komanso kulingalira.

    2. M’makope mwawomo alingalire za munthu yemwe anamupeza mu gawo 2 yemwe amati atha kumuuza zinsinsi zawo uja (monga zokhudza mimba, maphunziro, kugonana, zibwenzi, kutha nsinkhu, mantha awo kapena zomwe akwaniritsa m’moyo). Atha kulemba za munthuyo, athanso kumujambula.

    3. Atengambali aganizirenso kuti ndichifukwa chiyani munthuyu ali woyenera kuti azikambirana naye zinthu ngati zimenezi.

    4. Akamaliza kulingalira ayitaneni atengambali kuti akhale pamodzi.

    Zoyenera kuti mlangizi adziwe

    • Akumbutseni atengambali kuti m’dera lawo muli anthu ambiri makamaka amayi omwe akuchita zinthu zosiyanasiyana kuthandizira anyamata ndi atsikana achisodzera kuti akhale ozidalira, kuthetsa mabanja a ana ang’onong’ono, kuthandizira achinyamata kubwerera kusukulu ndi kupitiriza maphunziro komanso kuthetsa nkhanza zopangirana chifukwa wina ndi mkazi kapena mwamuna. Ndi anthu ngati amenewa omwe atengambali angathe kulankhula nawo pa za zinsinsi zawo, mantha awo, zikhulupiriro zomwe zikuwakhuza popanda kuweruzidwa. Anthu amenewa atha kukhala: Amayi omwe mumayang’anirapo, amayi a m’magulu a azimayi (mother group) aphunzitsi, aphungu akuchipempembezo, azakhali, achemwali, mayi athu, ngakhale alangizi amaphunziro ano.

    • Zinthu zina zabwino zomwe tikuyenera kuwona mwa munthu yemwe tikuyang’anirapo ndi monga, kudalirika, kudekha, kukhala omasuka m’kachitidwe ka zinthu, otha kupereka chitsogozo ndi malangizo, amawona kuthekera komanso kukhala ndi chiyembekezo choti zinthu ziyenda bwino m’moyo ndipo ndi munthu wapaderadera.

    • Alimbikitseni atengambali kumasukirana wina ndi mnzake, kukhala anthu odalirika komanso kuthandizana pa zinthu zosiyanasiyana zomwe amakambirana pa gulu lawo.

    • Auzeni atengambali kuti asankha anthuwo mwakufuna kwawo. Atha kuuza anthu ena maina a anthu omwe asankhawo ngati afuna kutero.

    Ntchito Yotsekera: Aliyense yemwe...?

    1. Mumasewera awa, atengambali onse akhala pansi kupatula munthu mmodzi. Munthu ameneyu ayimilira ndipo atsogolera masewerawa ndikunena kuti ‘aliyense yemwe…’ ndipo amaliza chiganizochi ndi chilichonse chomwe chabwera kukhosi kwake chokhuza maonekwe kapena chilichonse chomwe wina pagulupo anachita (monga yemwe wavala zofiira, yemwe wavala masandasi, yemwe wavala ndolo ndi zina).

    2. Anthu omwe atchulidwawo asinthana malo monga omwe avala zofiira asinthana malo, onse omwe anadya nsima dzulo asinthana malo.

    3. Masewera akamapitirira, mlangizi alimbikitse atengambali kugwiritsa ntchito zomwe zakambidwa mu ndimeyi. Mwachitsanzo, omwe akhazikitsa zolinga za tsogolo lawo asinthane malo kapena omwe akufuna apeze munthu ouzana naye zinsinsi asinthane malo.

    Athokozeni atengambali chifukwa chokhala nawo pa maphunzirowa ndikuwakumbutsa za tsiku, nthawi komanso malo omwe mudzakumanso nthawi ina popitiriza ndi maphunzirowa.

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 48 49M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    I N t R O d U C t O R Y s e s s I O N

    Victoria Bamusi amaganizira kuti kutenga mimba kwake adakali wamng’ono kunamuphunzitsa phunziro lalikulu m’moyo ndipo amalingaliraso kuti ndi chinthu chomwe chinachitika m’moyo wake wakale. Maso ake ali pa maphunziro omwe anawasiya mu 2013-2014 pa nthawi yomwe anatenga mimba ndikupita kunyumba kukabereka. Pano Victotia akufuna kugometsa anthu aku dera lakwao ndi dziko lonse kuti msinkhu simalire ndipo naye atha kupita patsogolo ndi maphunziro ake komaso atha kudzakwaniritsa maloto ake odzakhala oyimilira milandu.

    Victoria anabwerera ku sukulu ya Nkasaulo Primary, m’boma la Machinga ndipo ali mu sitandade 7 limodzi ndi anyamata ndi atsikana ocheperapo komanso ena okulirapo. “Ndimakhala bwinobwino ndi ophunzira anzanga, amanditenga kuti ndine mzawo ndipo amandilimbikitsa,” amatero Victoria kulankhupapo za ophunzira anzake kuphatikizapo Yasmin yemwe ndi wamn’gono kwa Victoria ndi zaka pafupifupi zisanu ndi chimodzi. Ngakhale ali ndi zaka 18 komanso ali ndi mwana, Victoria amachita nawo chilichonse chomwe ophunzira anzake amachita m’kalasi mwawo komanso pasukulupo.

    Ntchito yoti atengambali atengere kunyumba

    Atengambali apite kwa anthu omwe awasankha kuti atha kumasukirana nawo ndikukawauza za ganizo lomwe apanga ndikukagawana nawo nkhani zilizonse zomwe aganiza.

    Atengambali apeze mnzawo wapaderadera pa gululo yemwe azitha kukambirana naye maganizo awo pa za maphunzirowa, kukumbutsana zomwe aphunzira ndi kulimbikitsana zina ndi zina.

    Ndinalakwitsa, koma mayi anga anandilimbikitsa kuti ndipitebe chitsogoloVictoria Bamusi

    Ndemanga za mlangizi pa momwe gawoli layendera:

    Ndi zinthu ziti zomwe zayenda bwino?

    Ndi zinthu ziti zomwe zitha kukonzedwa?

    P H U N Z I R O 1 P H U N Z I R O 2 P H U N Z I R O 3 P H U N Z I R O 4 P H U N Z I R O 5 P H U N Z I R O 6 K U K H A Z I K I t s A M A L O t O A K O

  • 50 51M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i M a l o t o a n g a ! C h i s a n k h o C h a n g a ! P h u k u s i L a a L a n g i z i

    Pakuyankhulapo zakutenga mimba anakali wamng’ono, anati “ndinazindikira kuti ndinalakwitsa ndipo ndinabwerera kusukulu kudzaphunzira ndipo ndikupitiriza kuchokera pomwe ndinasiyira,” Victoria anatero. Iye amavomereza kuti ankadziwa bwino lomwe kuti atha kutenga mimba ngati achita zogonana mosadziteteza koma amangowona ngati linali chabe tsiku la tsoka chifukwa anakhala akuchita zogonana mosadziteteza pogwiritsa ntchito makondomu kangapo konse. Atangobereka mwana wa mwamuna m’chaka cha 2014, mayi ake omwe ndi a Mfumu a Chikwakwata kwa mfumu yayikulu Nsanama ananenetsa kuti Victoria abwererenso kusukulu ndipo sankafuna kumva chilichonse chokhudza ukwati wa Victoria ndi mwamuna yemwe anampatsa mimbayo. “Panali ambiri omwe anayesera kundikhumudwitsa kuti ndisakayambirenso sukulu koma ndinasankha kumvera mayi anga mpaka ndidzakwanitse maloto anga oti ndidzakhale woyimilira anthu pa milandu” amakumbukira motero.

    Pokhala ku dera komwe kukwatiwa usanakhwime, mimba zosakonzekera ndi chikhalidwe choyika atsikana pampanipani, Victoria akufuna kukhala wosiyana ndi ena kuti adzagwire ntchito zolimbikitsa atsikana omwe anabereka ali pasukulu kubwereranso kusukulu.

    1. Kodi ndi chiyani chinamupangitsa Victoria kuti asagonje, mpakana abwererenso kusukulu?

    2. Kodi ndi ndani anamulimbikitsa Victoria kuti abwerere kusukulu? 3. Kodi mukanakhala kuti mukudutsa mu zomwe Victoria anadut