kulengedwa kwa dziko lapansi

9
Phunziro 1 for April 3, 2021

Upload: others

Post on 11-Apr-2022

3 views

Category:

Documents


0 download

TRANSCRIPT

Page 1: Kulengedwa kwa dziko lapansi

Phunziro 1 for April 3, 2021

Page 2: Kulengedwa kwa dziko lapansi

Kulengedwa kwa dziko lapansi

Kulengedwa kwa anthu

Mulungu ndi anthu

Yeso la kukhulupirika

Kulekana komanso chiyemnekezo

Mulungu amakonda kuchezerana. Sizikutanthauza kutiamazimva kuti ali yekha , koma kuti amakonda kulumikizanandi zolengedwa za moyo zina. Anaganiza zolenga mtunduwatsopano wa zolengedwa kuti aukonde komanso akondedwendi iwo.

Adawakonzera nyumba,mwachikondi adawaumba iwo, ndipoadawaphunzitsa momwe angakhalire ndi iye mosangalala.

Iyi ndi nkhani yathu. Tikadatha kukhala osangalala nthawizonse...

Page 3: Kulengedwa kwa dziko lapansi

Mu nkhani ya chilengedwe Genesis 1:1-2:3, Mulungusakuyesera kudzionetsera kuti Iye adalenga dzikolapansi kapena momwe adayambitsira moyo pa dzikolapansi. Koma akutsimikiza kuti adachita zonsezi .

Mwachiziwikire, palibe munthu amene adaona izi, kotero kuvomereza kuti Mulungu adachita izi ndinkhani ya chikhulupiriro (Hebrews 11:3).

Wasayansi wina odziwika bwino (ena amati ndi Bertrand Russell) nthawi inaatakambapo nkhani yokhudza zathambo. Mai wina wokalamba adaimilirandikunena kuti dziko lapansi ndi lanthyathyathya ndipo limathandizidwa ndi fulu. Wasayansiyu adayankha nati, “Kodi fuluyo waima pa chani?” “Ndi tiafulu mpakapansi!”, adatero mzimayiyo. Adakhulupirira izi moona mtima ngakhale analibeumboni weni weni.

Mulungu sapempha chikhulupiriro chakhungu kuchokera kwa ife. Adasiyaumboni kuti chilengedwe chinapangidwa mwa luso, kuti tikathe kukhala nawoumboni ndi kukhulupirira ngati tikufuna kutero.

Page 4: Kulengedwa kwa dziko lapansi

“Mulungu ndipo adalenga munthu mçhifanizo chake, mçhifanizo chaMulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27)

Nyumba yathu itatha kukonzedwa, Mulungu adaumbamwamuna oyamba ndi manja ake. Kenako, Anaumbanso mkazi(Gn. 2:7, 22).

Iyi inali ntchito yotsiriza ya Mulungu pa chilengedwe. Tsopano, zonse zinali “zabwino kwambiri” (Gn. 1:31).

Anthu ali apadera. Adalengedwa mwanjira ina, ndipoiwo ndizolengadwa zokhazo zomwe zidalengedwa “mu chifanizo cha Mulungu.” Kodi izi zimatanthauza chani?

Mlengi wathu amaonekera mu thupi, maganizo ndi uzimu wathu

Timatha kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kupanga zitsanzo zoyenera

Amuna ndi akazi onse amaonetsera chithunzi cha umulungu. Ali ofanana pamaso pa Mulungu (1 Akorinto 11:12)

Page 5: Kulengedwa kwa dziko lapansi

E.G.W. (Patriarchs and Prophets, cp. 2, p. 46)

Page 6: Kulengedwa kwa dziko lapansi

“Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwaiwo, Mubalane, muchuluke, mudzadze dzikolapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsombaza m’nyanja, ndi pambalame za m’mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.” (Genesis 1:28)

Kodi madalitso ndi malangizo a Mulungu kwa Adamundi Hava mu Genesis 1:28-30 akukhudza chani?

Mulungu adayambitsa ubwenzi Wake ndi anthu. Anawadalitsa, komansoadawadalira powapatsa zonse zomweadalenga.

Ubwenzi wawo udakula popita pa nthawi mmene Mulungu ankabwera“kudzayenda munda” madzulo alionse(Genesis 3:8).

Adali okhoza kuchululukanamonga mtundu

Anapatsidwa ntchito: Kusamalira chilengedwe

Anapatsidwa chakudyachoyenera

Anadalira pa chitetezo ndichisamaliro cha Mulungu

Anali ndi zonse zofunika. Sanafunikire kuchita

kalikonse kuti alandire.

Page 7: Kulengedwa kwa dziko lapansi

“koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Genesis 2:17)

Ubwenzi wopambana uyenera kukhazikika pa kukhulupirirana. Kotero, Mulungu adasankha yeso lophweka la kukhulupirika: “Mitengo yonseyimutha kudyako, koma uwu wokha ndi wanga, musadye zipatso zake.”

Anthu atawononga chikhulupiliro cha Mulungu pa iwo, anadziwa kuti choyipa ndi chani. Zotsatira zake, anagonja ku kusalidwa, kusungulumwa, kukhumudwa, ndi imfa.

Ubwenzi wathu ndi Mulungu utha kukhala opambana ndi

wa muyaya pokhapokha titasankha kuchita chifunuro chake.

Mulungu adapereka kwa anthu kuthekera kotha kupanga zisankhozoyenera mwa ufulu, komanso Khumbo la chibadwidwe lofuna kumumvera. Chotero sikunali kovuta kupambana yesoli.

Page 8: Kulengedwa kwa dziko lapansi

“Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyanichimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njokainandinyenga ine, ndipo ndinadya.’” (Genesis 3:13)

Satana akanabwera kwa Hava mwa maonekedwe ake enieni, akanakhalawokaikira. Kotero, anagwiritsa ntchito cholengedwa chomwe chinalichodziwika bwino kuti amunyenge iye(Gn. 3:1). Koma, Adamusananyengedwe; anapanga chisankho chodya chipatsocho mozindikira(Gn. 3:6; 1Tim. 2:14). Kodi zotsatira za ichi zinali chani?

Anatayachiyanjano chawondi Mulungu ndipoadamupewa Iye(Gn. 3:8)

Kukhulupiriranakunatha(Gn. 3:12)

Zotsatira zoyipaza tchimozinawonekera(Gn. 3:16-21)

Ngakhale ubwenzi unasokonekera, Mulungu adawapatsa chiyembekezo: mmodzi mwambadwa za Hava adzagonjetsa tchimo ndi kubwezeretsa ubale omwe unasweka (Gn. 3:15).

Page 9: Kulengedwa kwa dziko lapansi

“Kwa munthu kuluzanitsidwa koyamba kwa

chiombolo kunalengezedwa pa chiweruzo chomwe

chidaperekedwa kwa Satana mu munda (Genesis

3:15). Chiweruzo ichi, makolo athu oyamba

akumva, chinali kwa iwo lonjezano. Ngakhale

chidalosera nkhondo yapakati pa munthu ndi

Satana, chidalengeza kuti mphamvu ya m’dani

wamkulu idzathyoledwa pamapeto pazonse […]

Ngakhale adzasautsidwa ndi mphamvu ya m’dani

wawo wamkulu, adzayang’ana pa chigonjetso

chawo.”E.G.W. (Patriarchs and Prophets, cp. 4, p. 65)